Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 40

Yeremiya apita kwa Gedaliya ku Mizipa

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m’maunyolo pamodzi ndi am’nsinga onse aYerusalemundi Yuda, amene anatengedwa am’nsinga kunka nao ku Babiloni.

2 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano;

3 ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.

4 Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.

5 Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira mizinda ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.

6 Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m’dziko.

Gedaliya wolamulira mu Yerusalemu aphedwa ndi Ismaele

7 Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m’minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m’dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni;

8 pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.

9 Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m’dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.

10 Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m’mbiya zanu, nimukhale m’mizinda imene mwailanda.

11 Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m’maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;

12 pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.

13 Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m’minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,

14 nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.

15 Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m’tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?

16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usachite ichi; pakuti unamizira Ismaele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/40-310a59eaaf6183bc4b662472b4423a5a.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 41

Gedaliya ndi ena aphedwa ndi Ismaele

1 Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi mu Mizipa.

2 Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.

3 Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.

4 Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,

5 anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang’amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndilubanim’manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.

6 Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka mu Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mzinda, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m’mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

9 Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.

10 Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.

11 Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazichita Ismaele mwana wa Netaniya,

12 anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pamadzi ambiri a mu Gibiyoni.

13 Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismaele anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera.

14 Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa mu Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya.

15 Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;

17 ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,

18 chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m’dzikomo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/41-b9aaab098fe54b2eec566100a7bba58e.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 42

Yeremiya achenjeza anthu asapite ku Ejipito

1 Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono, kufikira wamkulu, anayandikira,

2 nati kwa Yeremiyamneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m’malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

3 kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi chomwe tichite.

4 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.

5 Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.

6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

7 Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.

8 Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu,

9 nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pake,

10 Ngati mudzakhalabe m’dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.

11 Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m’dzanja lake.

12 Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu.

13 Koma mukati, Sitidzakhala m’dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;

14 ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;

15 chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe mu Ejipito, kukakhala m’menemo;

16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m’menemo m’dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa.

17 Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.

18 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala muYerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.

19 Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe mu Ejipito; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.

20 Pakuti mwanyenga m’miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.

21 Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m’chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.

22 Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/42-c6969a88995b6bfbbdfc609f69f439a7.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 43

Amtenga Yeremiya napita naye ku Ejipito

1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

2 pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m’menemo;

3 koma Baruki mwana wake wa Neriya atisonkhezera zoipa za inu, mutipereke m’dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am’nsinga ku Babiloni.

4 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m’dziko la Yuda.

5 Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m’dziko la Yuda;

6 ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;

7 ndipo anadza nalowa m’dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

Yeremiya aneneratu kuti Nebukadinezara adzagonjetsa Ejipito

8 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya mu Tapanesi, kuti,

9 Tenga miyala yaikulu m’dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba yaFaraomu Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;

10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.

11 Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.

12 Ndidzayatsa moto m’nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m’menemo ndi mtendere.

13 Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m’dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/43-30549cf0aa0d720b379d0c2e21ee1ce8.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 44

Achenjeza mowaopsa Ayuda amene adathawira ku Ejipito

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m’dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m’dziko la Patirosi, akuti,

2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa mizinda yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;

3 chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.

4 Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.

5 Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina.

6 Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m’mizinda ya Yuda ndi m’miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.

7 Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;

8 popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m’dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwaamitunduonse a dziko lapansi?

9 Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazichita m’dziko la Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu?

10 Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m’chilamulo changa, kapena m’malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

11 Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang’anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.

12 Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m’dziko la Ejipito akhale m’menemo, ndipo adzathedwa onse; m’dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.

13 Ndipo ndidzalanga iwo okhala m’dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri;

14 kuti otsala a Yuda, amene ananka kudziko la Ejipito kukhala m’menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere kudziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m’menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.

15 Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m’dziko la Ejipito, mu Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,

16 Koma mau amene wanena ndi ife m’dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

17 Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m’kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m’mizinda ya Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.

18 Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi njala.

19 Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?

20 Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti,

21 Zofukizira zanu m’mizinda ya Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m’dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m’mtima mwake?

22 Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.

23 Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m’chilamulo chake, ndi m’malemba ake, ndi m’mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.

24 Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m’dziko la Ejipito.

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m’kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu.

26 Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m’dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m’kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m’dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.

27 Taonani, ndiwayang’anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m’dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.

28 Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kutuluka kudziko la Ejipito kulowa m’dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m’dziko la Ejipito kuti akhale m’menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.

29 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m’malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa.

30 Yehova atero: Taonani, ndidzaperekaFaraoHofira mfumu ya Aejipito m’manja a adani ake, ndi m’manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m’manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/44-53f99c37c8099d292a837badf50b8e7f.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 45

Mau a Mulungu kwa Baruki

1 Mau amene ananena Yeremiyamnenerikwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m’buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

2 Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:

3 Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

4 Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m’dziko lonseli.

5 Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m’malo monse m’mene mupitamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/45-0b689bc167264163b21b6bf2565be91d.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 46

Aneneratu kuti mfumu ya ku Babiloni idzagonjetsa Aejipito

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiyamneneriakunena zaamitundu.

2 Za Ejipito: kunena za nkhondo yaFaraoNeko mfumu ya Aejipito, imene inali pamtsinje wa Yufurate mu Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.

3 Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.

4 Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.

5 Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m’mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.

6 Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pamtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.

7 Ndani uyu amene auka ngati mtsinje, madzi ake ogavira monga mitsinje?

8 Ejipito auka ngati mtsinje, madzi ake agavira ngati mitsinje; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mizinda ndi okhalamo ake.

9 Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.

10 Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m’dziko la kumpoto pamtsinje wa Yufurate.

11 Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.

12 Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.

13 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.

14 Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.

15 Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa.

16 Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.

17 Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira.

18 Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.

19 Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.

20 Ejipito ndi ng’ombe yaikazi yosalala; chionongeko chotuluka kumpoto chafika, chafika.

21 Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang’ombe a m’khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.

22 Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.

23 Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka.

24 Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m’manja a anthu a kumpoto.

25 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati, Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;

26 ndipo ndidzawapereka m’manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m’manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.

27 Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m’mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye.

28 Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/46-d06c551d0b144f7a2231002a4b099d55.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 47

Aneneratu za chitsutso cha Afilisti

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiyamnenerionena za Afilisti,Faraoasanakanthe Gaza.

2 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m’mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m’dziko adzakuwa.

3 Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao;

4 chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.

5 Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m’chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?

6 Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m’chimake; puma, nukhale chete.

7 Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m’mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/47-efc82fcd73fad87d54951dff763e4861.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 48

Chitsutso cha Mowabu

1 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.

2 Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

3 Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!

4 Mowabu waonongedwa; ang’ono ake amveketsa kulira.

5 Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.

6 Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m’chipululu.

7 Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

8 Ndipo wakufunkha adzafikira pa mizinda yonse, sudzapulumuka mzinda uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9 Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

10 Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.

11 Mowabu wakhala m’mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.

12 Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.

13 Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.

14 Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?

15 Mowabu wapasuka, akwera kulowa m’mizinda yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.

16 Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu.

17 Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!

18 Iwe mwana wamkazi wokhala mu Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

19 Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?

20 Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.

21 Chiweruzo chafika padziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati;

22 ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu;

23 ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;

24 ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa mizinda yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi.

25 Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.

26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzamvimvinika m’kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.

27 Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.

28 Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m’thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.

29 Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang’wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.

30 Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachite kanthu.

31 Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi.

32 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mphakasa ndi mphesa zako.

33 Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.

34 Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.

35 Ndiponso ndidzaletsa mu Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake.

36 Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika.

37 Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.

38 Pamwamba pa matsindwi a Mowabu ndi m’miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m’mene mulibe chikondwero, ati Yehova.

39 Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.

40 Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake.

41 Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42 Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

43 Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala mu Mowabu, ati Yehova.

44 Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m’dzenje; ndi iye amene atuluka m’dzenje adzagwidwa m’khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

45 Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m’kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.

46 Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako aamuna atengedwa ndende, ndi ana ako aakazi atengedwa ndende.

47 Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/48-a708b8159b4351a9714f0ec1fc95ba51.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 49

Chitsutso cha Aamoni

1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M’mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m’mizinda mwake?

2 Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo midzi yake idzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

3 Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana aakazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m’ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

4 Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m’mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?

5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera.

6 Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

Za kulangidwa kwa Aedomu

7 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?

8 Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.

9 Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?

10 Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye.

11 Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.

12 Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.

13 Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwaamitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

15 Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng’ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.

16 Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m’mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.

17 Ndipo Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse.

18 Monga m’kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m’menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m’menemo.

19 Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang’anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20 Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang’ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

21 Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira.

22 Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

Chitsutso cha Damasiko

23 Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.

24 Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.

25 Alekeranji kusiya mzinda wa chilemekezo, mzinda wa chikondwero changa?

26 Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m’miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.

27 Ndipo Ine ndidzayatsa moto m’khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Benihadadi.

Chitsutso cha Kedara ndi Hazori

28 Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m’mawa.

29 Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndingamirazao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.

30 Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala mu Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.

31 Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha.

32 Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng’ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m’mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova.

33 Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

Chitsutso cha Elamu

34 Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiyamneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

36 Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.

37 Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;

38 ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga mu Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.

39 Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/49-47c3d8ad9be05146370e0b170fc41d10.mp3?version_id=1068—