Categories
YEREMIYA

YEREMIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneri Yeremiya adalalikira kwa zaka zambiri, mzinda wa Yerusalemu usanapasuke (586 BC), ndiponso zaka zina zingapo mzindawo utapasuka. Mau ake ambiri ngochenjeza Ayuda akuti likubwera tsiku pamene Mulungu adzawalanga ndi kuwononga Yerusalemu, chifukwa cha machimo ao ndi kupembedza milungu ina. Tsono zimenezi zidachitikadi pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adadzazinga mzindawo nkuwuononga pamodzi ndi Kachisi wa Yehova; anthu ake ambiri pamodzi ndi mfumu yomwe adawatenga ukapolo nkupita nawo ku Babiloni, Yeremiya uja akuwona. Iye adalankhulanso mau ena onena kuti tsiku lina anthu otengedwa ku ukapolowo adzabwerera kwao ndi kukhalanso pabwino.

Yeremiya anali munthu wachifundo, wokonda Ayuda anzake kwambiri; ankawamvera chisoni ndipo nchifukwa chake ankayenera kuwadzudzula ndi kuwachenjeza. Mau ake aonetsa kuti ntchito imene Yehova adamupatsa inkawawitsa mtima wake. Mau a Yehova ankayaka ngati moto mumtima mwake, kotero kuti sankathanso kusunga mauwo mumtima mwake mpaka atalengeza zonse.

Mau ena a m’bukuli aloza zakutsogolo pamene Yehova adzakhazika chipangano chatsopano, cholembedwa m’mitima ya anthu, mwakuti anthuwo sadzasowanso mphunzitsi wowakumbutsa zimenezi (31.31-34).

Za mkatimu

Bukuli lili ndi zigawo zingapo:

Kuitanidwa kwa Yeremiya

1.1-19

Mau a Yehova kwa atsogoleri ao

2.1—25.38

Mau ena a Yehova ndipo zochitika zina ndi zina

26.1—45.5

Mau ena otsutsa mitundu ina ya anthu

46.1—51.64

Mau oonjezera osimba za kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu

52.1-34

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 1

Kuitanidwa kwa Yeremiya akhale mneneri

1 Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m’dziko la Benjamini;

2 amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.

3 Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a kuYerusalemuanatengedwa ndende mwezi wachisanu.

4 Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,

5 Ndisanakulenge iwe m’mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhalemneneriwa mitundu ya anthu.

6 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.

7 Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.

8 Usaope nkhope zao; chifukwa Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.

9 Ndipo Yehova anatulutsa dzanja lake, nakhudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m’kamwa mwako;

10 penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.

Masomphenya oyamba a Yeremiya

11 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona nthyole ya katungurume.

12 Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwachita.

13 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto.

14 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kuchokera kumpoto choipa chidzatulukira onse okhala m’dziko.

15 Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.

16 Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.

17 Koma iwe ukwinde m’chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.

18 Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mzinda walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, padziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m’dziko.

19 Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/1-3c7f9e24786a2511d8c5cc6fc791deb2.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 2

Yehova adzudzula anthu a Israele

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,

2 Pita nufuule m’makutu aYerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m’chipululu m’dziko losabzalamo.

3 Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoyamba za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.

4 Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele;

5 atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?

6 Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m’chipululu, m’dziko loti see ndi la maenje, m’dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m’dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?

7 Ndipo ndinakulowetsani m’dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.

8 Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwaBaala, natsata zinthu zosapindula.

9 Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

10 Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere.

11 Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.

12 Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova.

13 Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong’aluka, zosakhalamo madzi.

14 Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m’nyumba? Afunkhidwa bwanji?

15 Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.

16 Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamutu pako.

17 Kodi sunadzichitire ichi iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?

18 Tsopano uli nacho chiyani m’njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a mtsinje wa Nailo? Uli nacho chiyani m’njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a mtsinje wa Yufurate?

19 Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

20 Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.

21 Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?

22 Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

23 Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m’chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwengamirayothamanga yoyenda m’njira zake;

24 mbidzi yozolowera m’chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m’mwezi wake.

25 Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m’mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.

26 Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;

27 amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m’nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

28 Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m’nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, Yuda iwe.

29 Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova.

30 Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.

31 Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?

32 Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

33 Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna chilakolako? Chifukwa chake waphunzitsa akazi oipa njira zako.

34 Ndiponso m’nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.

35 Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwe.

36 Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.

37 Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m’menemo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/2-f863902411da98e07298fb7bdbd0ea62.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 3

1 Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.

2 Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m’chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.

3 Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.

4 Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?

5 Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero.

Abwere kwa Yehova anthu olowererawo

6 Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m’mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.

7 Ndipo ndinati atachita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwake wonyenga, Yuda, anaona.

8 Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m’mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.

9 Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.

10 Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga.

12 Pita; nulalikire mau awa kuyang’ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang’anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.

13 Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.

14 Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mzinda uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani kuZiyoni;

15 ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.

16 Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m’dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse,Likasa la chipanganocha Yehova; silidzalowa m’mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse.

17 Pa nthawi yomweyo adzatchaYerusalemumpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m’kuumirira kwa mtima wao woipa.

18 Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.

19 Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.

20 Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova.

21 Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.

22 Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.

23 Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.

24 Ndipo chochititsa manyazi chinathetsa ntchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao aamuna ndi aakazi.

25 Tigone m’manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/3-0a89844ace5a25b1b7a21b64ce1f8ccc.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 4

1 Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.

2 Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m’zoonadi, m’chiweruziro, ndi m’chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.

Adani achilendo adzagwera dziko la Yuda

3 Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwaYerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.

4 Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.

5 Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m’dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m’mizinda ya malinga.

6 Kwezani mbendera kuyang’ana kuZiyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu.

7 Mkango wakwera kutuluka m’nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m’mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.

8 Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.

9 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.

10 Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.

11 Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m’chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa;

12 mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.

13 Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka.

14 Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?

15 Pakuti mau anena mu Dani nalalikira nsautso m’phiri la Efuremu:

16 Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera mizinda ya Yuda mau ao.

17 Monga adindo a m’munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

18 Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.

19 Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m’kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

20 Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m’kamphindi.

21 Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?

22 Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.

23 Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.

24 Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.

25 Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.

26 Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo mizinda yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.

27 Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.

28 Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.

29 Mzinda wonse uthawa m’phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m’nkhalango, adzakwera pamiyala; mizinda yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m’menemo.

30 Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.

31 Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/4-5551d613fb2f1bba364043c0d98fb43c.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 5

Malango a Mulungu pa Ayuda chifukwa cha zoipa zao zonse

1 Thamangani inu kwina ndi kwina m’miseu yaYerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m’mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.

2 Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.

3 Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.

4 Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao.

5 Ine ndidzanka kwa akulu, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi chiweruzo cha Mulungu wao. Koma awa anavomerezana nathyola goli, nadula zomangira zao.

6 Chifukwa chake mkango wotuluka m’nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m’mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.

7 Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m’nyumba za adama.

8 Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake.

9 Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?

10 Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.

11 Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.

12 Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; choipa sichidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;

13 ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.

14 Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m’kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.

15 Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.

16 Phodo lao lili ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba.

17 Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.

18 Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.

19 Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m’dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m’dziko silili lanu.

20 Nenani ichi m’nyumba ya Yakobo, lalikirani mu Yuda, kuti,

21 Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;

22 Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.

23 Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka.

24 Ndipo sanena m’mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m’nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.

25 Mphulupulu zanu zachotsa zimenezi, ndi zochimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.

26 Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.

27 Monga chikwere chodzala ndi mbalame, chomwecho nyumba zao zadzala ndi chinyengo; chifukwa chake akula, alemera.

28 Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.

29 Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?

30 Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m’dzikomo;

31 aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/5-f31ee4790f5c590a1df317025bf84bd5.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 6

Achenjezedwa kuti adani adzamangira Yerusalemu misasa

1 Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati paYerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m’mpoto ndi kuononga kwakukulu.

2 Ndidzachotsa mwana wamkazi waZiyonimkazi wokoma ndi wololopoka.

3 Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake.

4 Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.

5 Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zake.

6 Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mzinda wakudzalangidwa ndi uwu; m’kati mwake modzala nsautso.

7 Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m’kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

8 Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.

9 Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m’madengu ake.

10 Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.

11 Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.

12 Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m’dziko, ati Yehova.

13 Pakuti kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambiramnenerikufikira wansembe onse achita monyenga.

14 Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onong’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.

15 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.

16 Yehova atero, Imani m’njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m’menemo muli njira yabwino, muyende m’menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.

17 Ndipo ndinaika alonda oyang’anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera.

18 Chifukwa chake tamverani,amitunduinu, dziwani, msonkhano inu, chimene chili mwa iwo.

19 Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.

20 Lubaniandifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.

21 Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.

22 Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.

23 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi waZiyoni.

24 Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.

25 Usatulukire kumunda, usayenda m’njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m’mbali zonse.

26 Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m’phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.

27 Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.

28 Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda;

29 mvukuto yatenthedwa ndi moto; mtovu watha ndi moto wa ng’anjo; ayenga chabe; pakuti oipa sachotsedwa.

30 Anthu adzawatcha nthale yasiliva, pakuti Yehova wakana iwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/6-5930f3b8ce7f427ff501a337ed07b27b.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 7

Mneneri alikuima pa chipata cha Kachisi, atchula mau akulonjeza ndi akuopsa

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Ima m’chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m’menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m’zipata izi kuti mugwadire Yehova.

3 Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m’malo ano.

4 Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.

5 Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake;

6 ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m’malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo;

7 ndipo ndidzakukhazikani inu m’malo muno, m’dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya.

8 Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.

9 Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwaBaala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa,

10 ndi kudza ndi kuima pamaso panga m’nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi?

11 Kodi nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova.

12 Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m’mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.

13 Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamve; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankhe;

14 chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.

15 Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.

16 Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.

17 Kodi suona iwe chimene achichita m’mizinda ya Yuda ndi m’miseu yaYerusalemu?

18 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.

19 Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?

20 Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m’munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.

21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.

22 Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;

23 koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m’njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.

24 Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m’kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m’tsogolo.

25 Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m’dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;

26 koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.

27 Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.

28 Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.

Zoopsa za Tofeti

29 Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.

30 Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m’nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.

31 Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m’chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m’moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m’mtima mwanga.

32 Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya mu Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.

33 Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.

34 Ndipo ndidzaletsa m’mizinda ya Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/7-f163bd0fafc7b42eaaf2c7dee0a0d9e3.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 8

1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzatulutsa m’manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akulu ake, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m’Yerusalemu,

2 ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.

3 Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m’malo monse m’mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu.

Kulowerera kwa anthu a Mulungu, kulangidwa kudzafikadi

4 Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?

5 Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.

6 Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m’nkhondo.

7 Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang’anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova.

8 Bwanji muti, Tili ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga.

9 Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?

10 Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambiramnenerikufikira wansembe onse achita zonyenga.

11 Ndipo analipoletsa pang’ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.

12 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang’aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.

13 Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.

14 Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m’mizinda yamalinga, tikhale chete m’menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.

15 Tinayang’anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

16 Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.

17 Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.

18 Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m’kati mwa ine.

19 Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi muZiyonimulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?

20 Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.

21 Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.

22 Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing’anga m’menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/8-4a165454f83e51ecd48bc16941660447.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 9

1 Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!

2 Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m’chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.

3 Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m’dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.

4 Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.

5 Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa.

6 Ukhala pakati pa manyengo m’manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.

Achenjezedwa za kuonongeka ndi kutengedwa ukapolo

7 Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?

8 Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m’mtima mwake amlalira.

9 Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?

10 Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng’ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.

11 Ndipo ndidzayesaYerusalemumiyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.

12 Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?

13 Ndipo Yehova ati, Chifukwa asiya chilamulo changa ndinachiika pamaso pao, ndipo sanamvere mau anga, osayenda m’menemo;

14 koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndiBaala, monga makolo ao anawaphunzitsa;

15 chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.

16 Ndidzawabalalitsanso mwaamitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.

17 Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze;

18 afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.

19 Pakuti mau a kulira amveka muZiyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.

20 Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pake, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzake maliridwe ake.

21 Pakuti imfa yakwera m’mazenera athu, yalowa m’nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.

22 Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.

23 Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m’nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m’mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m’chuma chake;

24 koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi, pakuti m’menemo ndikondwerera, ati Yehova.

25 Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m’kusadulidwa kwao;

26 Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m’mphepete mwa tsitsi lao, okhala m’chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m’mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/9-722819d1a476ea0f868b0eeb14e05150.mp3?version_id=1068—