Categories
YAKOBO

YAKOBO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Wolemba kalatayi alembera Akhristu achiyuda obalalika kumaiko osiyanasiyana. Apereka malangizo amitundumitundu owathandiza kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira ya Chikhristu. Aziwonetsa makhalidwe abwino pa zochita zao zonse, pakuti “chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.” (2.17)

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1

Za chikhulupiriro ndi nzeru 1.2-8

Za umphawi ndi chuma 1.9-11

Za kuyesedwa ndi zovuta kapena zinyengo 1.12-18

Za kumva ndi kuchita zimene Mulungu anena 1.19-27

Awachenjeza kuti asamachite tsankho 2.1-13

Za chikhulupiriro ndi ntchito zake 2.14-26

Za kuwongolera lilime potsata nzeru zochokera kumwamba 3.1-18

Za kuchita chibwenzi ndi pansi pano 4.1—5.6

Za kuyembekeza mopirira ndi kupempherera odwala 5.7-20

Categories
YAKOBO

YAKOBO 1

1 Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye YesuKhristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m’chibalaliko: ndikupatsani moni.

Za mayesero

2 Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu;

3 pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.

4 Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

5 Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

6 Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

7 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;

8 munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse.

9 Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake;

10 ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu.

11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m’mayendedwe ake.

12 Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

13 Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:

14 koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.

15 Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.

16 Musanyengedwe, abale anga okondedwa.

17 Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

18 Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.

Tikhale akuchita a mau

19 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.

20 Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

21 Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.

22 Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

23 Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole;

24 pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani.

25 Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.

26 Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

27 Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/1-2befdb6b7b5e71c1747b0e4d1087eeb5.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 2

Asachite tsankho pakati pa anthu

1 Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu YesuKhristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.

2 Pakuti akalowa m’sunagogemwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa;

3 ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;

4 kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

5 Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?

6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu?

7 Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?

8 Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:

9 koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa.

10 Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.

11 Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

12 Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

13 Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Chikhulupiriro chopanda ntchito zake chikhala chopanda pake

14 Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa?

15 Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake,

16 ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?

17 Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.

18 Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga.

19 Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.

20 Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?

21 Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe?

22 Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro;

23 ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

24 Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.

25 Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?

26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/2-292c9914e17fa02a3992da014148541a.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 3

Azichenjera ndi pakamwa pao

1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

3 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m’kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.

4 Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling’ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.

5 Kotero lilimenso lili chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!

6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndiGehena.

7 Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam’nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;

8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

9 Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;

10 Mochokera m’kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

11 Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa?

12 Kodi mkuyu ukhoza kubalaazitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.

Nzeru yochokera Kumwamba

13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.

14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.

15 Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.

16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.

17 Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.

18 Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/3-91e9b88f1bda5bdcf04695d91b72bb18.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 4

Adziletse polakalaka zoipa

1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu?

2 Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simungathe kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.

3 Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.

4 Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?

6 Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.

7 Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

10 Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

11 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.

12 Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

Sikudziwika ngati zidzachitika zofuna ifezi

13 Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;

14 inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

15 Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.

16 Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.

17 Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/4-0097d69dd02d4537bb4a32eb9d733dec.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 5

Achuma ouma mtima atsutsidwa

1 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.

2 Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete.

3 Golide wanu ndisilivawanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

4 Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m’minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m’makutu a Ambuye wa makamu.

5 Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.

6 Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu.

Apirire. Za kulumbira, kupemphera, kubweza wosochera

7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.

8 Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

9 Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

10 Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.

11 Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.

12 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m’chiweruziro.

13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.

14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu aMpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye:

15 ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.

16 Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake.

17 Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

18 Ndipo anapempheranso; ndipo m’mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.

19 Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake;

20 azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/5-ff1832cb27ea435e04dd90535a98e3ac.mp3?version_id=1068—