Categories
TITO

TITO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Tito sanali Myuda koma wa mitundu ina. Atatembenuka ndi kulowa mu mpingo, adasanduka mnzake wa Paulo womthandiza pa ntchito yolalikira, namuperekeza pa maulendo ake. Paulo adamsiya ku chilumba cha Krete kuti aziyang’anira mpingo kumeneko.

Pomulembera kalatayi, Paulo akumukumbutsa za makhalidwe oyenera atsogoleri a mpingo, makamaka ku Krete poti anthuwo mbiri yao sinali yabwino. Kenaka akumufotokozera kuti iye ayenera kuphunzitsira magulu ena a Akhristu: azibambo okalamba, amai okalamba (kuti iwonso aziphunzitsa amai achitsikana), achinyamata ndipo akapolo. Potsiriza Paulo alangiza Tito pa za mayendedwe a Chikhristu, kuti adziwe kuyanjanitsa anthu ndi kukopa mitima yao, apewe zilizonse zimene zingabweretse kukangana kapena kupatukana mu mpingo.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-4

Za atsogoleri a mpingo 1.5-16

Ntchito yosamalira magulu osiyanasiyana mu mpingo 2.1-15

Malangizo ndi mau ena ochenjeza 3.1-11

Mau omaliza 3.12-15

Categories
TITO

TITO 1

1 Paulo, kapolo wa Mulungu, ndimtumwiwa YesuKhristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,

2 m’chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;

3 koma pa nyengo za Iye yekha anaonetsa mau ake muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:

4 kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.

Asenzetsa Tito udindo wakusunga Mpingo wa ku Krete. Atsutsa aphunzitsi onyenga

5 Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m’midzi yonse, monga ndinakulamulira;

6 ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.

7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;

8 komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

9 wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.

10 Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe,

11 amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.

12 Wina wa mwa iwo, ndiyemneneriwa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zilombo zoipa, aumbombo, aulesi.

13 Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m’chikhulupiriro,

14 osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.

15 Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.

16 Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/TIT/1-e0ea9c6fabc561b7d3999df629e672ce.mp3?version_id=1068—

Categories
TITO

TITO 2

Machenjezedwe a okalamba ndi anyamata ndi akapolo. Akhale chitsanzo yekha Tito

1 Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa:

2 okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.

3 Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;

4 kuti akalangize akazi aang’ono akonde amuna ao, akonde ana ao,

5 akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.

6 Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;

7 m’zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m’chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko,

8 mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.

9 Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m’zonse; osakana mau ao;

10 osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.

11 Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,

12 ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

13 akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu YesuKhristu;

14 amene anadzipereka yekha m’malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.

15 Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/TIT/2-d63b8b5db3d7ce3073bd5a624611247e.mp3?version_id=1068—

Categories
TITO

TITO 3

1 Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;

2 asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.

3 Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m’dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.

4 Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka,

5 zosati zochokera m’ntchito za m’chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

6 amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa YesuKhristuMpulumutsi wathu;

7 kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.

8 Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;

9 koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe.

10 Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize,

11 podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.

12 Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu.

13 Zena nkhoswe ya milandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu,

14 Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.

15 Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m’chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/TIT/3-cfcb0f893943058a29a045b40318586f.mp3?version_id=1068—