Categories
RUTE

RUTE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likamba nkhani ya Rute, mkazi wachimowabu amene adakwatiwa ndi mwamuna wa ku Israele. Mwamuna wake atamwalira, iye atsatira mpongozi wake Naomi ku Betelehemu kwao chifukwa chokhulupirira Mulungu wa Aisraele.

Nkhani yabwinoyi yochitika panthawi ija yankhanza ya

Oweruza

, iwonetsa kuti ngakhale amitundu nawonso adzalandira madalitso a Mulungu, akakhulupirira Mulungu wa Israele ndi kusanduka anthu ake.

Za mkatimu

Naomi abwerera ku Betelehemu pamodzi ndi Rute

1.1-22

Rute akumana ndi Bowazi

2.1—3.18

Rute akwatiwa ndi Bowazi Davide

4.1-22

Categories
RUTE

RUTE 1

Naomi ndi apongozi ake awiri

1 Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m’dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m’dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.

2 Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m’dziko la Mowabu, nakhala komweko.

3 Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri.

4 Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.

5 Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake aamuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.

6 Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m’dziko la Mowabu; pakuti adamva m’dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.

7 Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda.

8 Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.

9 Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.

10 Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu.

11 Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m’mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?

12 Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindingathe kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana aamuna;

13 kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.

14 Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira.

15 Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako.

16 Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;

17 kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.

18 Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye.

19 Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?

20 Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.

21 Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?

22 Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/1-6ea412b45d6cf5ccf1075e8415460ded.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 2

Rute akunkha m’munda wa Bowazi

1 Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi.

2 Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.

3 Namuka iye, nakatola khunkha m’munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.

4 Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.

5 Nati Bowazi kwa mnyamata woyang’anira ochekawo, Mkazi uyu ngwa yani?

6 Ndipo mnyamata woyang’anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;

7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m’mawa mpaka tsopano; koma m’nyumba samakhalitsamo.

8 Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m’munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.

9 Maso ako akhale pamunda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauze anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,

10 Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?

11 Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

12 Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.

13 Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.

14 Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m’vinyo wosasayo. Nakhala iye m’mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.

15 Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi.

16 Ndiponso mumtayire za m’manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula.

17 Natola khunkha iye m’munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo; napeza ngati efa wa barele,

18 nalisenza nalowa kumzinda; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.

19 Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.

20 Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.

21 Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m’minda.

22 Nati Naomi kwa Rute mpongozi wake, Nchabwino, mwana wanga, kuti uzituluka nao adzakazi ake, ndi kuti asakukomane m’munda wina uliwonse.

23 Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/2-73a3f0dd9226b7c545ff303860ec9440.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 3

Bowazi anena za kumuombolera Rute cholowa

1 Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?

2 Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

3 Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.

4 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe.

5 Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzachita.

6 Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza.

7 Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona.

8 Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ake pagona mkazi.

9 Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.

10 Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsate anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.

11 Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakuchitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.

12 Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.

13 Gona usiku uno, ndipo kudzali m’mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m’mawa.

14 Nagona ku mapazi ake mpaka m’mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.

15 Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m’mzinda.

16 Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wake, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamchitira munthuyo.

17 Natinso, Miyeso iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu.

18 Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga, mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/3-3b6f17c0d7b2c929f8b5357fd28c0a89.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 4

Bowazi akwatira Rute nabadwa Obedi

1 Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi.

2 Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mzinda, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

3 Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki;

4 ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

5 Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo padzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.

6 Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7 Koma kale mu Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe mu Israele.

8 Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake.

9 Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, padzanja la Naomi.

10 Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.

11 Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m’nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;

12 ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

13 Momwemo Bowazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wake; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.

14 Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake mu Israele.

15 Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana aamuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.

16 Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pachifuwa pake, nakhala mlezi wake.

17 Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide.

18 Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;

19 ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu;

20 ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni;

21 ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi;

22 ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala Davide.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/4-2464e9df2763cb283373dace0f0da481.mp3?version_id=1068—