Categories
OWERUZA

OWERUZA 20

Aisraele abwezera chilango fuko la Benjamini

1 Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.

2 Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga.

3 Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israele adakwera kunka ku Mizipa. Nati ana a Israele, Nenani, choipa ichi chinachitika bwanji?

4 Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibea wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng’ono, kugonako.

5 Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng’ono, nafa iye.

6 Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng’ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m’dziko lonse la cholowa cha Israele, pakuti anachita chochititsa manyazi ndi chopusa mu Israele.

7 Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israele, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno.

8 Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwake, kapena kupatukira nyumba yake,

9 koma tsopano ichi ndicho tidzachitira Gibea: tidzaukwerera ndi kulota maere.

10 Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mafuko onse a Israele; ndi zana limodzi pa zikwi chimodzi, ndi chikwi chimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibea wa Benjamini, auchitire monga mwa chopusa chonse unachita mu Israele.

11 Potero amuna onse a Israele anasonkhanira mzindawo, olunzika ngati munthu mmodzi.

12 Ndipo mafuko a Israele anatuma anthu mwa fuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Choipa chanji ichi chinachitika mwa inu?

13 Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala mu Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele.

14 Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kuchokera kumizinda kunka ku Gibea, kuti atuluke kulimbana ndi ana a Israele.

15 Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m’mizinda tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala mu Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.

16 Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.

17 Ndipo anawerenga amuna a Israele, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okhaokha.

18 Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.

19 Nauka ana a Israele m’mawa, naumangira Gibea misasa.

20 Ndipo amuna a Israele anatuluka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israele anawandandalikira nkhondo ku Gibea.

21 Pamenepo ana a Benjamini anatuluka mu Gibea, naononga a Israele tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi.

22 Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.

23 Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.

24 Potero ana a Israele anayandikira ana a Benjamini m’mawa mwake.

25 Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m’mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.

26 Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

27 Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakutilikasa la chipanganola Mulungu linakhala komweko masiku aja,

28 namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m’dzanja lako.

29 Ndipo Israele anaika olalira Gibea pozungulira pake.

30 Ndipo ana a Israele anakwerera ana a Benjamini tsiku lachitatu, nanika pa Gibea monga nthawi zina.

31 Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mzinda, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu aamuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m’makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo.

32 Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israele anati, Tithawe, tiwakokere kutali ndi mzinda kumakwalala.

33 Nauka amuna onse a Israele m’malo ao nanika ku Baala-Tamara; natuluka Aisraele olalira aja m’malo mwao, kumwera kwa Geba.

34 Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika mu Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza.

35 Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israele; ndi ana a Israele anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.

36 Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea.

37 Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mzinda wonse ndi lupanga lakuthwa.

38 Koma kunali chizindikiro choikika pakati pa amuna a Israele ndi olalirawo, ndicho chakuti afukitse mtambo wa utsi kumzinda.

39 Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.

40 Koma pamene mtambo unayamba kukwera m’mzinda ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.

41 Natembenuka amuna a Israele; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti chidawagwera choipa.

42 Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israele kunka njira ya chipululu; koma nkhondo inawalondetsa; ndi aja otuluka m’mizinda anawaononga pakati pao.

43 Anawazinga Abenjamini, anawapirikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibea, kotulukira dzuwa.

44 Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi.

45 Natembenuka iwo, nathawira kuchipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m’makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.

46 Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi.

47 Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kuchipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m’thanthwe la Rimoni miyezi inai.

48 Ndipo amuna a Israele anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m’mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/20-3473e48a1aa3b2a9558011a484fae612.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 21

Fuko la Benjamini limangidwanso

1 Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake.

2 Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.

3 Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji mu Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi mu Israele?

4 Ndipo kunali m’mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.

5 Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.

6 Ndipo ana a Israele anamva chifundo chifukwa cha Benjamini mbale wao, nati, Fuko limodzi lalikhidwa pa Israele leroli.

7 Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao?

8 Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano.

9 Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala mu Yabesi-Giliyadi.

10 Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala mu Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana aang’ono.

11 Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye.

12 Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m’dziko la Kanani.

13 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m’thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.

14 Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-Giliyadi; koma sanawafikire.

15 Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang’amba mafuko a Israele.

16 Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti mu Benjamini?

17 Nati iwo, Pakhale cholowa cha iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe fuko mu Israele.

18 Koma ife sitingathe kuwapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.

19 Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum’mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona.

20 Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m’minda yampesa;

21 nimuyang’ane, ndipo taonani, atatuluka ana aakazi a Silo kuvinavina, pamenepo mutuluke m’minda yampesa ndi kudzigwirira yense mkazi wake mwa ana aakazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.

22 Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.

23 Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo.

24 Ndipo ana a Israele anachokako nthawi ija yense kunka ku fuko lake, ndi banja lake, natulukako yense kunka ku cholowa chake.

25 Panalibe mfumu mu Israele masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/21-d2e034550e44b4aaab9af4ec430846a9.mp3?version_id=1068—