Yefita alanditsa Israele
1 Yefita Mgiliyadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Giliyadi adabala Yefita.
2 Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m’nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.
3 Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m’dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi.
4 Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anachita nkhondo ndi Israele,
5 ndipo kunatero, pamene ana a Amoni anathira nkhondo pa Israele, akulu a Giliyadi anamuka kutenga Yefita m’dziko la Tobu;
6 nati kwa Yefita, Tiye ukhale kazembe wathu kuti tilimbane ndi ana a Amoni.
7 Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Simunandide kodi, ndi kundichotsa m’nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m’kusauka?
8 Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala mu Giliyadi.
9 Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Mukandifikitsanso kwathu kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkulu wanu kodi?
10 Ndipo akulu a Giliyadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kuchita monga momwe wanena.
11 Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
12 Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi chiyani ndi inu ndi kuti mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?
13 Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere.
14 Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;
15 nanena naye, Atero Yefita, Israele sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la ana a Amoni;
16 pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m’chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;
17 pamenepo Israele anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati padziko lanu; koma mfumu ya Edomu siinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Mowabu; nayenso osalola; ndipo Israele anakhala mu Kadesi.
18 Pamenepo anayenda m’chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum’mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.
19 Ndipo Israele anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israele, Tikupemphani tipitire pakati padziko lanu, kunka kwathu.
20 Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele.
21 Ndipo Yehova Mulungu wa Israele anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m’dzanja la Israele, ndipo anawakantha, ndi Israele, analandira cholowa chake, dziko lonse la Aamori, nzika za m’dziko lija.
22 Ndipo analandira akhale cholowa chao, malire onse a Aamori, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira chipululu mpaka Yordani.
23 Motero Yehova Mulungu wa Israele anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ake Israele, ndipo kodi liyenera kukhala cholowa chanu?
24 Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu.
25 Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu; anatengana konse ndi Israele iyeyu kodi, kapena kuchita nao nkhondo konse kodi?
26 Pokhala Israele mu Hesiboni ndi midzi yake, ndi mu Aroere ndi midzi yake ndi m’mizinda yonse yokhala m’mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?
27 Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni.
28 Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvere mau a Yefita anamtumizirawo.
Chowinda cha Yefita
29 Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni.
30 Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m’dzanja langa,
31 ndipo kudzali kuti chilichonse chakutuluka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kuchokera kwa ana a Amoni, chidzakhala cha Yehova, ndipo ndidzachipereka nsembe yopsereza.
32 Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m’dzanja lake;
33 nawakantha kuyambira ku Aroere mpaka ufika ku Miniti, ndiyo mizinda makumi awiri, ndi ku Abele-Keranimu, makanthidwe aakulu ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israele.
34 Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang’ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
35 Ndipo kunali, pakumuona anang’amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.
36 Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtsegulira Yehova pakamwa panu, mundichitire ine monga umo mudatulutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakuchitirani inu chilango pa adani anu, pa ana a Amoni.
37 Ndipo anati kwa atate wake, Andichitire ichi, andileke miyezi iwiri, kuti ndichoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga.
38 Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzake, nalirira unamwali wake pamapiri.
39 Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wake amene anamchitira monga mwa chowinda chake anachiwinda; ndipo sanamdziwe mwamuna. Motero unali mwambo mu Israele,
40 kuti ana aakazi a Israele akamuka chaka ndi chaka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Giliyadi, masiku anai pa chaka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/11-23113561ae659784b23e39b308ae2a3c.mp3?version_id=1068—