Categories
OWERUZA

OWERUZA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba zochitika zina ndi zina kuyambira nthawi imene Aisraele analowa m’dziko la Kanani kufikira nthawi yokhazikitsa ufumu. Pa nthawi yonseyo Aisraele anakhala akuzunzika kwambiri chifukwa chokhala pakati pa anthu a mitundu ina, anthu ofunkha ndi ankhanza, kotero kuti panali chisokonezo. Bukuli litchedwa

Oweruza

, kunena anthu angapo amene Yehova awaitana kuti azitsogolera Aisraele anzao pa nkhondo yomenyana ndi adani. Woweruza wina wodziwika kwambiri ndi Samisoni amene zochita zake zikukambidwa pamutu 13 mpaka 16.

Phunziro lopezeka m’bukuli ndilo lakuti, Israele akakhala okhulupirika kwa Yehova, amakhala pa mtendere. Koma akafulatira Mulungu ndi kumamchimwira, amagwa m’mavuto aakulu. Komabe ngakhale iwo apandukira Yehova ndi kugwa m’mavuto, Mulungu ali wokonzeka kuwapulumutsa anthu akewo, ataona kuti atembenuka ndi kubwerera kwa Iyeyo.

Za mkatimu

Zochitika zina kufikira nthawi ya imfa ya Yoswa

1.1—2.10

Za oweruza ena ndi ena

2.11—16.31

Zochitika zinanso

17.1—21.25

Categories
OWERUZA

OWERUZA 1

Aisraele aonjeza kugonjetsa Akanani

1 Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?

2 Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m’dzanja lake.

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m’dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.

5 Ndipo anapeza Adoni-Bezeki mu Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.

6 Koma Adoni-Bezeki anathawa; ndipo anampirikitsa, namgwira, namdula zala zazikulu za m’manja ndi za m’mapazi.

7 Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m’manja ndi m’mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye kuYerusalemu, nafa iye komweko.

8 Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda ndi moto.

9 Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha.

10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala mu Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11 Pochoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Debiri, koma kale dzina la Debiri ndilo mudzi wa Kiriyati-Sefere.

12 Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake.

13 Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng’ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

14 Ndipo kunali, m’mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pabulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

15 Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.

16 Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m’mzinda wa m’migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m’chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.

17 Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala mu Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mzindawo analitcha Horoma.

18 Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake.

19 Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsa nzika za kuchigwa, popeza zinali nao magaleta achitsulo.

20 Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana aamuna atatu a Anaki.

21 Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22 Ndipo anakwera iwo a m’nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao.

23 Ndipo iwo a m’nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mzindawo ndilo Luzi.

24 Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m’mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m’mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.

25 Nawaonetsa polowera m’mzinda iye, naukantha mzinda iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lake lonse amuke.

26 Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mzinda, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.

Aisraele aleka kugonjetsa Akanani ena

27 Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m’dziko muja.

28 Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.

29 Ndipo Efuremu sanaingitse Akanani okhala mu Gezere; koma Akanani anakhala mu Gezere pakati pao.

30 Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera.

31 Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu;

32 koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse.

33 Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera.

34 Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalole atsikire kuchigwa;

35 Aamori anakhumbanso kukhala kuphiri la Heresi, ku Ayaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m’nyumba ya Yosefe linawagonjetsa, nakhala iwo akupereka msonkho.

36 Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/1-0ff455f23c670f97faaea4ae62cf22d5.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 2

Mngelo wa Mulungu adzudzula Aisraele

1 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyolachipanganochanga nanu ku nthawi yonse;

2 ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m’dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?

3 Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m’nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

4 Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.

5 Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

Aisraele alowerera atamwalira Yoswa

6 Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao.

7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.

8 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi.

9 Ndipo anamuika m’malire a cholowa chake mu Timnati-Heresi, ku mapiri a Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.

10 Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.

11 Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;

12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m’dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.

13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndiAsitaroti.

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m’manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m’dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.

15 Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.

16 Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m’dzanja la iwo akuwafunkha.

17 Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m’njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.

18 Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m’dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.

19 Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m’mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.

20 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;

21 Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu;

22 kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.

23 Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereke m’dzanja la Yoswa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/2-2505c2e715f0948e077fe96f11a42d82.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 3

Amitundu otsala akuyesa nao Aisraele

1 Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani;

2 chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale;

3 anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m’phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati.

4 Amenewo anakhala choyesera Israele kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ake, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.

5 Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;

6 nakwatira ana aakazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana aamuna a iwowa natumikira milungu yao.

Otiniyeli alanditsa Aisraele m’dzanja la Kusani

7 Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaalandi zifanizo.

8 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m’dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.

9 Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng’ono wake wa Kalebe.

10 Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m’dzanja lake; ndi dzanja lake linamgonjetsa Kusani-Risataimu.

11 Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniyele mwana wa Kenazi anafa.

Ehudi awalanditsa m’dzanja la Egiloni

12 Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova.

13 Ndipo anadzisonkhanitsira ana a Amoni ndi a Amaleke, namuka nakantha Israele, nalanda mzinda wa m’migwalangwa nakhalamo.

14 Ndipo ana a Israele anatumikira Egiloni mfumu ya Mowabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.

15 Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m’dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu.

16 Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konsekonse utali wake mkono; nalimangirira pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja.

17 Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu.

18 Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo achoke.

19 Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo.

20 Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m’chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake.

21 Ndipo Ehudi anatulutsa dzanja lake lamanzere nagwira lupanga ku ntchafu ya kulamanja nampyoza m’mimba mwake;

22 ndi chigumbu chake chinalowa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolole lupanga m’mimba mwake; nilituluka kumbuyo.

23 Pamenepo Ehudi anatuluka kukhonde namtsekera pamakomo pa chipinda chosanja nafungulira.

24 Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo ake; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m’chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo.

25 Ndipo analindirira mpaka anachita manyazi; koma taonani, sanatsegule pamakomo pa chipinda chosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.

26 Ndipo Ehudi anapulumuka pakuchedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira.

27 Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye.

28 Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m’manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke.

29 Ndipo anakantha Amowabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuke ndi mmodzi yense.

30 Motero anagonjetsa Mowabu tsiku lija pansi padzanja la Israele. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu.

31 Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng’ombe; nayenso anapulumutsa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/3-60ebbecb9e2f6fe0959ab541362c07a2.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 4

Debora ndi Baraki alanditsa Aisraele m’dzanja la Yabini

1 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.

2 Ndipo Yehova anawagulitsa m’dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti waamitundu.

3 Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.

4 Ndipo Debora,mneneriwamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija.

5 Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze.

6 Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?

7 Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m’dzanja lako.

8 Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.

9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m’dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

10 Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.

11 Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa mu Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.

12 Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori.

13 Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni.

14 Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m’dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.

15 Ndipo Yehova anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.

16 Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.

17 Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni.

18 Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m’hema, namfunda ndi chimbwi.

19 Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang’ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, namfunda.

20 Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.

21 Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m’dzanja lake namdzera monyang’ama, nakhomera chichiri chilowe m’litsipa mwake; ndipo chinapyoza kulowa m’nthaka; popeza anali m’tulo tofa nato ndi kulema; nafa.

22 Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m’litsipa mwake.

23 Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele.

24 Ndipo dzanja la ana a Israele linankabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/4-6c3dd0c90a55cbda0d7382cc4f081d51.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 5

Nyimbo ya Debora

1 Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinowamu anaimba tsiku lomwelo ndi kuti,

2 Lemekezani Yehova

pakuti atsogoleri mu Israele anatsogolera,

pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.

3 Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu;

ndidzamuimbira ine Yehova, inetu;

ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.

4 Yehova, muja mudatuluka mu Seiri,

muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu,

dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,

inde mitambo inakha madzi.

5 Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,

Sinai lili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israele.

6 Masiku a Samigara, mwana wa Anati,

masiku a Yaele maulendo adalekeka

ndi apanjira anayenda mopazapaza.

7 Midzi idalekeka mu Israele, idalekeka.

Mpaka ndinauka ine Debora,

ndinauka ine amai wa Israele.

8 Anasankha milungu yatsopano,

pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata.

Ngati chikopa kapena nthungo zidaoneka

mwa zikwi makumi anai a Israele?

9 Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a mu Israele,

amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu.

Lemekezani Yehova.

10 Inu akuyenda okwera pa abulu oyera,

inu akukhala poweruzira,

ndi inu akuyenda m’njira, fotokozerani.

11 Posamveka phokoso la amauta potunga madzi,

pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova,

zolungama anazichita m’madera ake, mu Israele.

Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.

12 Galamuka, Debora, galamuka,

galamuka, galamuka, unene nyimbo;

uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.

13 Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu;

Yehova ananditsikira pakati pa achamuna.

14 Anafika Aefuremu amene adika mizu mu Amaleke;

Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako.

Ku Makiri kudachokera olamulira,

ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.

15 Akalonga a Isakara anali ndi Debora;

monga Isakara momwemo Baraki,

anawatuma m’chigwa nanka choyenda pansi.

Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikulu.

16 Wakhaliranji pakati pa makola,

kumvera kulira kwa zoweta?

Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikulu.

17 Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani;

ndi Dani, akhaliranji m’zombo?

Asere anakhala pansi m’mphepete mwa nyanja,

nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja.

18 Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa,

Nafutali yemwe poponyana pamisanje.

19 Anadza mafumu nathira nkhondo;

pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani.

Mu Taanaki, ku madzi a Megido;

osatengako phindu la ndalama.

20 Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba,

m’mipita mwao zinathirana ndi Sisera.

21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,

mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni.

Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.

22 Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda.

Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu.

23 Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova,

mutemberere chitemberere nzika zake;

pakuti sanadzathandize Yehova,

kumthandiza Yehova pa achamuna.

24 Wodalitsika, woposa akazi, akhale Yaele

mkazi wa Hebere Mkeni.

Akhale wodalitsika woposa akazi a m’hema.

25 Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka,

anamtengera mafuta a mkaka m’chotengera cha mfulu.

26 Dzanja lake analitambasulira kuchichiri,

ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito,

nakhomera Sisera, nakantha mutu wake,

inde, anaphwanya napyoza m’litsipa mwake.

27 Pa mapazi ake anabzong’onyoka, anagwa, anagona;

pa mapazi ake anabzong’onyoka, anagwa;

pobzong’onyokapo, pamenepo wagwa wafa.

28 Anapenyerera ali pazenera,

nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake,

achedweranji galeta wake?

Zizengerezeranji njinga za magaleta ake?

29 Akazi anzake omveka anzeru anamyankha;

koma anadziyankhira yekha mau.

30 Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha?

Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense.

Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera;

chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa,

nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse,

kwa chofunkha cha khosi lake.

31 Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo.

Koma iwo akukonda Inu

akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake.

Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/5-b7c4b6c396c76e3cf64902a6c6e904a8.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 6

Midiyani agonjetsa Aisraele

1 Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m’dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri.

2 Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming’ang’ala ya m’mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.

3 Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum’mawa, inde amawakwerera;

4 nawamangira misasa, namaononga zipatso za m’dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala mu Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng’ombe, kapena bulu.

5 Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kuchuluka kwao; iwowa ndingamirazao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m’dziko kuliononga.

6 Ndipo Israele anafooka kwambiri chifukwa cha Midiyani; ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova.

7 Ndipo kunali, pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova chifukwa cha Midiyani,

8 Yehova anatuma munthumnenerikwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera mu Ejipito, ndi kukutulutsani m’nyumba ya ukapolo;

9 ndipo ndinakulanditsani m’dzanja la Aejipito, ndi m’dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;

10 ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lao; koma simunamvere mau anga.

Mngelo wa Mulungu amdzera Gideoni

11 Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala mu Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m’mopondera mphesa, awabisire Amidiyani.

12 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.

13 Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi? Ndipo zili kuti zodabwitsa zake zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweze kodi Yehova kuchokera mu Ejipito? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m’dzanja la Midiyani.

14 Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israele m’dzanja la Midiyani. Sindinakutume ndi Ine kodi?

15 Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka mu Manase, ndipo ine ndine wamng’ono m’nyumba ya atate wanga.

16 Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.

17 Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.

18 Musachoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kutulutsa chopereka changa ndi kuchiika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.

19 Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m’lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.

20 Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero.

21 Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m’dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m’thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.

22 Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.

23 Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.

24 Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.

Gideoni agamula guwa la nsembe la Baala

25 Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng’ombe ya atate wako, ndiyo ng’ombe yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe laBaalandilo la atate wako, nulikhe chifanizo chili pomwepo;

26 numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng’ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.

27 Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku.

28 Ndipo pakuuka mamawa amuna akumudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi chifanizo chinali pomwepo chitalikhidwa ndi ng’ombe yachiwiri yoperekedwa paguwa la nsembe adalimanga.

29 Nanenana wina ndi mnzake, Wachita ichi ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yowasi wachita ichi.

30 Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo.

31 Koma Yowasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? Iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m’mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lake la nsembe.

32 Chifukwa chake anamutcha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenere mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lake la nsembe.

33 Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum’mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m’chigwa cha Yezireele.

34 Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye.

35 Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Asere, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafutali; iwo nadzakomana nao.

36 Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena,

37 taonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena.

38 Ndipo kunatero; pakuti anauka mamawa, nafinya chikopacho, nakamula mame a pachikopa, madzi ake odzala mbale.

39 Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.

40 Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pachikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/6-afa12d2564e06808671f6e2a4c8f0504.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 7

Gideoni apirikitsa nkhondo ya Amidiyani

1 Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, paphiri la More m’chigwa.

2 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m’dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.

3 Ndipo tsopano, kalalike m’makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke paphiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.

4 Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.

5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa.

6 Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.

7 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidiyani m’dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwake.

8 Pamenepo anthu anatenga kamba m’dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m’chigwa.

9 Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m’dzanja lako.

10 Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;

11 nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m’misasa.

12 Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum’mawa ali gonere m’chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndingamirazao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.

13 Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzake loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulirakunkhulira m’misasa ya Midiyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala chigwere.

14 Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m’misasa onse m’dzanja lake.

15 Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m’misasa a Midiyani m’dzanja lanu.

16 Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m’manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m’kati mwa mbiyazo.

17 Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa chilekezero cha misasa, kudzali, monga ndichita ine, momwemo muzichita inu.

18 Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.

19 Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m’manja mwao.

20 Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m’dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.

21 Ndipo anaima yense m’mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m’misasa onse, nafuula, nathawa.

22 Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m’misasa monse; ndi a m’misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.

23 Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.

24 Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efuremu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidiyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Betebara ndi Yordani. Potero amuna onse a Efuremu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betebara, ndi Yordani.

25 Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/7-17171600689ad907b37788d840bfdd1e.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 8

1 Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.

2 Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?

3 Mulungu anapereka m’dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.

A ku Sukoti ndi a ku Penuwele anyoza Gideoni nalangidwa naye

4 Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere.

5 Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani.

6 Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m’dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?

7 Ndipo Gideoni anati, Chifukwa chake, Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m’dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m’chipululu ndi mitungwi.

8 Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.

9 Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penuwele ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi.

10 Zeba ndi Zalimuna ndipo anali mu Karikori, ndi a m’misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum’mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.

11 Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m’mahema kum’mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.

12 Ndipo Zeba ndi Zalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midiyani Zeba ndi Zalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.

13 Pamenepo Gideoni mwana wa Yowasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.

14 Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.

15 Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m’dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?

16 Ndipo anagwira akulu a m’mzinda ndi minga ya kuchipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.

17 Ndipo anagamula nsanja ya Penuwele, napha amuna akumzinda.

18 Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.

19 Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.

20 Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.

21 Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwangamirazao.

Gideoni akana kulowa ufumu

22 Pamenepo anthu a Israele anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m’dzanja la Amidiyani.

23 Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.

24 Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele.

25 Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo chovala, naponyamo yense maperere a mwa zofunkha zao.

26 Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao.

27 Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m’mzinda mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.

28 Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m’masiku a Gideoni.

29 Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m’nyumba ya iye yekha.

30 Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.

31 Ndipo mkazi wake wamng’ono wokhala mu Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Abimeleki.

32 Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m’manda a Yowasi atate wake, mu Ofura wa Aabiyezere.

33 Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israele anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-Beriti mulungu wao.

34 Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m’dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;

35 osachitira chifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anachitira Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/8-a6be2e9727e28464d018e0d24de7334e.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 9

Abimeleki awapha abale ake

1 Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti,

2 Nenanitu m’makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana aamuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.

3 Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m’makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.

4 Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m’nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.

5 Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng’ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.

6 Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili mu Sekemu.

Fanizo la Yotamu

7 Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.

8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.

9 Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?

10 Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

11 Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?

12 Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

13 Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?

14 Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

15 Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m’nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni.

16 Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake;

17 pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wake, nakupulumutsani m’dzanja la Amidiyani;

18 koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;

19 ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;

20 koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.

21 Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beere, nakhala komweko, chifukwa cha Abimeleki mbale wake.

Mpanduko wa Gaala

22 Abimeleki atakhala kalonga wa Israele zaka zitatu,

23 Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika;

24 kuti chiwawa adachitira ana aamuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.

25 Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.

26 Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.

27 Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m’mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m’nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.

28 Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?

29 Mwenzi anthu awa akadakhala m’dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke.

30 Pamene Zebuli woyang’anira mzinda anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.

31 Natuma mithenga kwa Abimeleki ku Aruma monyenga nati, Taonani Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mzinda.

32 Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;

33 ndipo kukhale kuti m’mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mzindawo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako.

34 Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.

35 Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mzinda; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m’molalira.

36 Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.

37 Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati padziko, ndi gulu limodzi lidzera njira ya ku thundu wa alauli.

38 Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao.

39 Ndipo Gaala anatuluka pamaso pao pa eni ake a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.

40 Koma Abimeleki anampirikitsa, nathawa iye pamaso pake; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa chipata.

41 Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anaingitsa Gaala ndi abale ake kuti asakhale mu Sekemu.

42 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti anthu anatuluka kunka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.

43 Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m’minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m’mzinda; nawaukira iye nawakantha.

44 Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa chipata cha mzinda; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m’munda, nawakantha.

45 Ndipo Abimeleki analimbana ndi mzinda tsiku lija lonse; nalanda mzinda nawapha anthu anali m’mwemo; napasula mzinda; nawazapo mchere.

46 Ndipo pamene eni ake onse a Nsanja ya ku Sekemu anachimva, analowa m’ngaka ya nyumba ya Eliberiti.

47 Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a Nsanja ya ku Sekemu asonkhana.

48 Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m’dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.

49 Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a Nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi.

Imfa ya Abimeleki

50 Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebezi, naumangira Tebezi misasa, naulanda.

51 Koma m’mzindamo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ake onse a mzindawo, nadzitsekereza m’mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.

52 Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.

53 Ndipo mkazi wina anaponya mwala wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake.

54 Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.

55 Pamene amuna a Israele anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwake.

56 Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri.

57 Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/9-3a3ca7324ffff31ab209fdb44f2633d1.mp3?version_id=1068—