Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Nyimbo ya Solomoni

ndi mndandanda wa ndakatulo za chikondi, ndipo zambiri mwa izo zili ngati nyimbo zimene mwamuna amalankhula kwa mkazi, kapena mkazi kwa mwamuna. Ambiri amakhulupirira kuti Solomoni ndiye analemba nyimboyi.

Ayuda amakhulupirira kuti nyimbozi zikuonetsa za ubale wa Mulungu ndi anthu ake, pamene Akhristu amakhulupirira kuti zikuonetsa za ubale wa Yesu ndi mpingo. Nyimbo zake zilipo zisanu ndi imodzi.

Za mkatimu

Nyimbo yoyamba

1.1—2.7

Nyimbo yachiwiri

2.8—3.5

Nyimbo yachitatu

3.6—5.1

Nyimbo yachinai

5.2—6.3

Nyimbo yachisanu

6.4—8.4

Nyimbo yachisanu ndi chimodzi

8.5-14

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 1

Mkwatibwi anena ndi ana a Yerusalemu za mkwati

1 Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni.

2 Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m’kamwa mwake;

pakuti chikondi chako chiposa vinyo.

3 Mafuta ako anunkhira bwino;

dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;

chifukwa chake anamwali akukonda.

4 Undikoke; tikuthamangire;

mfumu yandilowetsa m’zipinda zake:

Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.

Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo:

Akukonda molungama.

5 Wakuda ine, koma wokongola,

ana aakazinu a kuYerusalemu,

ngati mahema a Kedara,

ngati nsalu zotchinga za Solomoni.

6 Musayang’ane pa ine, pakuti ndada,

pakuti dzuwa landidetsa.

Ana aamuna a amai anandikwiyira,

anandisungitsa minda yamipesa;

koma munda wangawanga wamipesa sindinausunge.

7 Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,

umaweta kuti gulu lako?

Umaligonetsa kuti pakati pa usana?

Pakuti ndikhalirenji ngati wosochera

pambali pa magulu a anzako?

8 Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,

dzituluka kukalondola bande la gululo,

nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.

Mkwati ndi mkwatibwi akambirana za chikondano chao

9 Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,

ngati akavalo a magaleta aFarao.

10 Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,

ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.

11 Tidzakupangira nkhata zagolide

ndi njumu zasiliva.

12 Pokhala mfumu podyera pake,

naridowanga ananunkhira.

13 Wokondedwa wanga mnyamatayo

ali kwa ine ngati thumba lamure,

logona pakati pa mawere anga.

14 Wokondedwa wanga ali kwa ine

ngati chipukutu cha maluwa ofiira

m’minda yamipesa ya ku Engedi.

15 Taona, wakongolatu, bwenzi langa;

namwaliwe taona, wakongola,

maso ako akunga a nkhunda.

16 Taona, wakongolatu, bwenzi langa,

mnyamatawe, inde, wakongoletsa;

pogona pathu mpa msipu.

17 Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza,

ndi mapaso athu nga mlombwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/1-f44648ae3302899dea72d80c85d1d64d.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 2

1 Ndine duwa lofiira la ku Saroni,

ngakhale kakombo wa kuzigwa.

2 Ngati kakombo pakati pa minga

momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.

3 Ngati maula pakati pa mitengo ya m’nkhalango,

momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna.

Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake,

zipatso zake zinatsekemera m’kamwa mwanga.

4 Anandifikitsa kunyumba ya vinyo,

mbendera yake yondizolimira inali chikondi.

5 Mundilimbikitse ndi mphesa zouma,

munditonthoze mtima ndi maula,

pakuti ndadwala ndi chikondi.

6 Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu,

dzanja lake lamanja ndi kundifungatira.

7 Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a kuYerusalemu,

pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo,

kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,

mpaka chikafuna mwini.

8 Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,

alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.

9 Wokondedwa wanga akunga mphoyo,

pena mwana wa mbawala:

Taona, aima patseri pakhoma lathu.

Apenyera pazenera,

nasuzumira pamade.

10 Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,

tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.

11 Pakuti, taona, chisanu chatha,

mvula yapita yaleka;

12 maluwa aoneka pansi;

nthawi yoimba mbalame yafika,

mau a njiwa namveka m’dziko lathu.

13 Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima,

mipesa niphuka,

inunkhira bwino.

Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.

14 Nkhunda yangawe, yokhala m’ming’alu ya thanthwe,

mobisika motsetsereka,

ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako;

pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.

15 Mutigwirire ankhandwe, ngakhale aang’ono,

amene akuononga minda yamipesa;

pakuti m’minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.

16 Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake:

aweta zake pakati akakombo.

17 Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,

bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo

pena mwana wa mbawala

pa mapiri a mipata.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/2-c40816a30125b8a4d20f98f602d2fcad.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 3

Mkwatibwi apeza mkwati

1 Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:

Ndinamfunafuna, koma osampeza.

2 Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m’mzinda,

m’makwalala ndi m’mabwalo ake,

ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:

Ndimfunafuna, koma osampeza.

3 Alonda akuyendayenda m’mzinda anandipeza:

Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?

4 Nditawapitirira pang’ono,

ndinampeza amene moyo wanga umkonda:

Ndinamgwiritsitsa, osamfumbatula,

mpaka nditamlowetsa m’nyumba ya amai,

ngakhale m’chipinda cha wondibala.

5 Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a kuYerusalemu,

pali mphoyo, ndi mbawala yakuthengo,

kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,

mpaka chikafuna mwini.

Ulendo wa ukwati

6 Ndaniyu akwera kutuluka m’chipululu ngati utsi wa tolo,

wonunkhira ndimurendilubani,

ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?

7 Taonani, ndi machira a Solomoni;

pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,

a mwa ngwazi za Israele.

8 Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:

Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake,

chifukwa cha upandu wa usiku.

9 Solomoni mfumu anadzipangira machira okhalamo tsonga

ndi matabwa a ku Lebanoni.

10 Anapanga timilongoti take ndisiliva,

cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira,

pakati pake panayalidwa za chikondi

cha ana aakazi a ku Yerusalemu.

11 Tulukani, ana aakazi inu aZiyoni,

mupenye Solomoni mfumu,

ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake,

ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/3-1a31c7bcd35df394c8dc95d3a80502bc.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 4

Mkwati alemekeza mkwatibwi

1 Taona, wakongola, bwenzi langa,

namwaliwe, taona, wakongola;

maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako.

Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,

zooneka paphiri la Giliyadi.

2 Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,

zokwera kuchokera kosamba;

yonse ili ndi ana awiri,

palibe imodzi yopoloza.

3 Milomo yako ikunga mbota yofiira,

m’kamwa mwako ndi kukoma:

Palitsipa pako pakunga phande la khangaza

paseri pa chophimba chako.

4 Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida,

apachikapo zikopa zikwi,

ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu.

5 Mawere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi,

akudya pakati pa akakombo.

6 Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,

ndikamuka kuphiri lamure,

ndi kuchitunda chalubani.

7 Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe,

mulibe chilema mwa iwe.

8 Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi,

kuchokera nane ku Lebanoni:

Unguza pamwamba pa Amana,

pansonga ya Seniri ndi Heremoni,

pa ngaka za mikango,

pa mapiri a anyalugwe.

9 Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi;

walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,

ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.

10 Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi!

Kodi chikondi chako sichiposa vinyo?

Kununkhira kwa mphoka yako

ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!

11 M’milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi,

uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako;

kununkhira kwa zovala zako

ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.

12 Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa;

ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.

13 Mphukira zako ndi munda wamakangaza,

ndi zipatso zofunika, bonongwe ndinarido.

14 Narido ndi chikasu,

nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani;

mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.

15 Ndiwe kasupe wa m’minda,

chitsime cha madzi amoyo,

ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.

Ayankha mkwatibwi

16 Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe,

nudze, mphepo iwe ya kumwera;

nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo.

Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m’munda mwake,

nadye zipatso zake zofunika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/4-81cf6194500e89d5b7e58635224e8862.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 5

1 Ndalowa m’munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi:

Ndatcheramurewanga ndi zonunkhiritsa zanga;

ndadya uchi wanga ndi chisa chake;

ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.

Idyani, atsamwalinu,

imwani, mwetsani chikondi.

Alekana nthawi

2 Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso:

Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati,

nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga,

nkhunda yanga, wangwiro wanga.

Pakuti pamutu panga padzala mame,

patsitsi panga pali madontho a usiku.

3 Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji?

Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenji?

4 Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera,

mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye.

5 Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;

pamanja panga panakha mure.

Ndi pa zala zanga madzi a mure,

pa zogwirira za mpikizo.

6 Ndinamtsegulira bwenzi langalo;

koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka.

Moyo wanga unalefuka polankhula iye:

Ndinamfunafuna, osampeza;

ndinamuitana, koma sanandivomere.

7 Alonda akuyenda m’mzinda anandipeza,

nandikantha, nanditema;

osunga makoma nandichotsera chophimba changa.

8 Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a kuYerusalemu,

mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani?

Kuti ndadwala ndi chikondi.

9 Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,

mkaziwe woposa kukongola?

Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,

kuti utilumbirira motero?

10 Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,

womveka mwa zikwi khumi.

11 Mutu wake ukunga golide, woyengetsa,

tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khwangwala.

12 Ana a maso ake akunga nkhunda

pambali pa mitsinje ya madzi;

otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.

13 Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo,

ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:

Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.

14 Manja ake akunga zing’anda zagolide

zoikamo zonyezimira zoti biriwiri.

Thupi lake likunga chopanga cha minyanga

cholemberapo masafiro.

15 Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,

zogwirika m’kamwa mwa golide:

Maonekedwe ake akunga Lebanoni,

okometsetsa ngati mikungudza.

16 M’kamwa mwake muli mokoma; inde,

ndiye wokondweretsa ndithu.

Ameneyu ndi wokondedwa wanga,

ameneyu ndi bwenzi langa,

ana aakazi inu a ku Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/5-7c017417172149a537199e139929db71.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 6

1 Bwenzi lako wapita kuti,

mkaziwe woposa kukongola?

Bwenzi lako wapatukira kuti,

tikamfunefune pamodzi nawe?

2 Bwenzi langa watsikira kumunda kwake,

kuzitipula za mphoka,

kukadya kumunda kwake, ndi kutchera akakombo.

3 Ndine wake wa wokondedwa wanga,

wokondedwa wanganso ndiye wa ine;

aweta zake pakati pa akakombo.

Mkwati ndi mkwatibwi alemekezana

4 Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza,

wokoma ngatiYerusalemu,

woopsa ngati nkhondo ndi mbendera.

5 Undipatutsire maso ako,

pakuti andiopetsa.

Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,

zigona pambali pa Giliyadi.

6 Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi,

zikwera kuchokera kosamba;

yonse ili ndi ana awiri,

palibe imodzi yopoloza.

7 Palitsipa pako pakunga phande la khangaza

paseri pa chophimba chako.

8 Alipo akazi aakulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi,

kudza akazi aang’ono makumi asanu ndi atatu,

ndi anamwali osawerengeka.

9 Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;

ndiye wobadwa yekha wa amake;

ndiye wosankhika wa wombala.

Ana aakazi anamuona, namutcha wodala;

ngakhale akazi aakulu a mfumu,

ndi akazi aang’ono namtamanda.

10 Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha,

wokongola ngati mwezi,

woyera ngati dzuwa,

woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?

11 Ndinatsikira kumunda wa mtedza,

kukapenya msipu wa m’chigwa,

kukapenya ngati pamipesa paphuka,

ngati pamakangaza patuwa maluwa.

12 Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimika

pakati pa magaleta a anthu anga aufulu.

13 Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe;

bwera, bwera, tiyang’ane pa iwe.

Muyang’aniranji pa Msulami,

ngati pa masewero akuguba?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/6-0164c8d0b6458e7aab941d11404b254f.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 7

1 Ha, mapazi ako akongola m’zikwakwata,

mwana wamkaziwe wa mfumu!

Pozinga m’chuuno mwako pakunga zonyezimira,

ntchito ya manja a mmisiri waluso.

2 Pamchombo pako pakunga chikho choulungika,

chosasowamo vinyo wosanganika:

Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu

wozingidwa ndi akakombo.

3 Mawere ako akunga ana awiri a nswala

anabadwa limodzi.

4 Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;

maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,

a pa chipata cha Batirabimu;

mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni

imene iloza ku Damasiko.

5 Mutu wako ukunga Karimele,

ndi tsitsi la pamutu pako likunga nsalu yofiirira;

mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam’nsinga.

6 Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,

bwenziwe, m’zokondweretsa!

7 Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa,

mawere ako akunga matsango amphesa.

8 Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo,

ndikagwira nthambi zake:

Mawere ako ange ngati matsango amphesa,

ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula.

9 M’kamwa mwako munge ngati vinyo woposa,

womeza tseketseke bwenzi langa,

wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.

10 Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo,

ndine amene andifunayo.

11 Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda;

titsotse m’midzi.

12 Tilawire kunka kuminda yamipesa;

tiyang’ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso,

makangaza ndi kutuwa maluwa ake;

pompo ndidzakupatsa chikondi changa.

13 Mankhwala a chikondi anunkhira,

ndi pamakomo pathu zipatso zabwino,

za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano,

zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/7-1055d898df24daffdf8b6c36d7568e92.mp3?version_id=1068—

Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 8

1 Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga,

woyamwa pa bere la amai!

Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;

osandinyoza munthu.

2 Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m’nyumba ya amai,

kuti andilange mwambo;

ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,

ndi madzi a makangaza anga.

3 Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu,

lamanja lake ndi kundifungatira.

4 Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a kuYerusalemu,

muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi,

chisanafune mwini.

5 Ndaniyu achokera kuchipululu,

alikutsamira bwenzi lake?

Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:

Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe,

pomwepo wakukubala anali m’pakati pa iwe.

6 Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro,

nundikhomenso chizindikiro pamkono pako;

pakuti chikondi chilimba ngati imfa;

njiru imangouma ngati manda:

Kung’anima kwake ndi kung’anima kwa moto,

ngati mphezi ya Yehova.

7 Madzi ambiri sangazimitse chikondi,

ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola:

Mwamuna akapereka katundu yense wa m’nyumba yake

ngati sintho la chikondi,

akanyozedwa ndithu.

8 Tili ndi mlongo wathu wamng’ono,

alibe mawere;

timchitirenji mlongo wathu

tsiku lokhoma unkhoswe wake?

9 Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:

Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.

10 Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake:

Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.

11 Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni;

nabwereka alimi mundawo;

yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.

12 Koma munda wanga wamipesa,

uli pamaso panga ndiwo wangatu;

nacho chikwicho, Solomoni iwe,

koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.

13 Namwaliwe wokhala m’minda,

anzako amvera mau ako:

Nanenanso undimvetse.

14 Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,

dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala

pa mapiri a mphoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/8-2edcd607c87b9c7f04e8ec5a0bb46e37.mp3?version_id=1068—