Categories
NUMERI

NUMERI 20

Imfa ya Miriyamu; madzi a Meriba

1 Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m’chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.

2 Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.

3 Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!

4 Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m’chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?

5 Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa mu Ejipito, kutilowetsa m’malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.

6 Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo lachihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.

7 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

8 Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m’thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.

9 Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye.

10 Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m’thanthwe umu?

11 Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.

12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m’dziko ndinawapatsali.

13 Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.

Mose apempha njira kwa Aedomu

14 Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;

15 kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala mu Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.

16 Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.

17 Tipitetu pakati padziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m’zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.

18 Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.

19 Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.

20 Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

21 Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira.

Imfa ya Aroni

22 Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m’phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,

24 Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m’dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.

25 Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m’phiri la Hori;

26 nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.

27 Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m’phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.

28 Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m’phirimo.

29 Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/20-997bf2cfae0036812dbc4f5f060078cb.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 21

Aisraele aononga Akanani

1 Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.

2 Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m’dzanja langa, ndidzaononga mizinda yao konse.

3 Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.

Njoka yamkuwa

4 Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.

5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m’chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.

6 Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israele.

7 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.

8 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto, nuiike pa mtengo wake; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.

9 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.

Achoka kunka ulendo wao

10 Pamenepo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema mu Oboti.

11 Ndipo anachoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyeabarimu, m’chipululu chakuno cha Mowabu, kotulukira dzuwa.

12 Pochokapo anayenda ulendo, namanga mahema m’chigwa cha Zeredi.

13 Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m’chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.

14 Chifukwa chake, ananena m’buku la Nkhondo za Yehova,

Waheba mu Sufa,

ndi miyendo ya Arinoni;

15 ndi zigwa za miyendoyo

zakutsikira kwao kwa Ari,

ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.

16 Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.

17 Pamenepo Israele anaimba nyimbo iyi,

Tumphuka chitsime iwe;

muchithirire mang’ombe;

18 chitsime adakumba mafumu,

adachikonza omveka a anthu;

atanena mlamuli, ndi ndodo zao.

Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana;

19 atachoka ku Matana ku Nahaliyele; atachoka ku Nahaliyele ku Bamoti;

20 atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m’dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.

Aisraele alanda dziko la Aamori

21 Ndipo Israele anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,

22 Ndipitire pakati padziko lako; sitidzapatuka kulowa m’munda, kapena m’munda wampesa, sitidzamwako madzi a m’zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako.

23 Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m’malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m’chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele.

24 Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.

25 Ndipo Israele analanda mizinda iyi yonse; nakhala Israele m’mizinda yonse ya Aamori; mu Hesiboni ndi midzi yake yonse.

26 Popeza Hesiboni ndiwo mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m’dzanja lake kufikira Arinoni.

27 Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti,

Idzani ku Hesiboni,

mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.

28 Popeza moto unatuluka mu Hesiboni,

chirangali cha moto m’mzinda wa Sihoni;

chatha Ari wa Mowabu,

eni misanje ya Arinoni.

29 Tsoka kwa iwe, Mowabu!

Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu,

anapereka ana ake aamuna opulumuka,

ndi ana ake aakazi akhale ansinga,

kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

30 Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni,

ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa.

Ndiwo wakufikira ku Medeba.

31 Chomwecho Israele anakhala m’dziko la Aamori.

32 Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda midzi yake, napirikitsa Aamori a komweko.

Aisraele alanda dziko la Basani

33 Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya ku Basani anatuluka kukumana nao, iye ndi anthu ake onse, kudzachita nao nkhondo ku Ederei.

34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m’manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.

35 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/21-153816cdf374f671075357116b766512.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 22

Za Balamu ndi Balaki

1 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m’zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko.

2 Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israele anachitira Aamori.

3 Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele.

4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng’ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m’dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m’dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

7 Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m’dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

8 Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.

9 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?

10 Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,

11 Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.

12 Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.

13 Ndipo Balamu anauka m’mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu.

14 Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe.

15 Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ochuluka, ndi omveka koposa awa.

16 Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu chinthu chakukuletsa kudza kwa ine;

17 popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.

18 Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndisilivandi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.

19 Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane.

20 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.

21 Pamenepo Balamu anauka m’mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu.

22 Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m’njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pabulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.

23 Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m’njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m’njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.

24 Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m’njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga.

25 Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.

26 Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.

27 Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo.

28 Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?

29 Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m’dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.

30 Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.

31 Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m’njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.

32 Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;

33 koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.

34 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m’njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.

35 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

36 Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m’mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.

37 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?

38 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m’kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.

39 Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati-Huzoti.

40 Pamenepo Balaki anapha ng’ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.

41 Ndipo kunali kuti m’mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje yaBaala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/22-94f83caa4e965d0c823e45d0c7cbd79b.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 23

1 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

2 Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka paguwa la nsembe lililonse ng’ombe ndi nkhosa yamphongo.

3 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.

4 Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng’ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.

5 Ndipo Yehova anaika mau m’kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.

6 Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yake, iye ndi akalonga onse a Mowabu.

7 Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ku Aramu ananditenga Balaki,

mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum’mawa,

Idza, udzanditembererere Yakobo.

Idza, nudzanyoze Israele.

8 Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere?

Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze?

9 Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya,

pokhala pa zitunda ndimuyang’ana;

taonani, ndiwo anthu akukhala pa okha.

Osadziwerengera pakati paamitunduena.

10 Adzawerenga ndani fumbi la Yakobo,

kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israele?

Ndipo ine ndife monga amafa oongoka mtima,

chitsiriziro changa chifanane nacho chake!

11 Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.

12 Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m’kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi?

13 Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.

14 Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng’ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.

15 Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi Iye uko.

16 Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m’kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.

17 Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?

18 Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ukani, Balaki, imvani;

ndimvereni, mwana wa Zipori.

19 Mulungu sindiye munthu, kuti aname;

kapena mwana wa munthu, kuti aleke;

kodi anena, osachita?

20 Kapena kulankhula, osachitsimikiza?

Taonani, ndalandira mau akudalitsa,

popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha.

21 Sayang’anira mphulupulu ili mu Yakobo,

kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele.

Yehova Mulungu wake ali ndi iye,

ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.

22 Mulungu awatulutsa mu Ejipito;

mphamvu yake ikunga ya njati.

23 Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo,

kapena ula mwa Israele;

pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele,

chimene Mulungu achita.

24 Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi,

nadzitukumula ngati mkango waumuna.

Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira,

utamwa mwazi wa zophedwa.

25 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.

26 Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?

27 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

28 Ndipo Balaki ananka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi chipululu.

29 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

30 Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng’ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/23-42770d9b2f6a92a1e744765762e72eaf.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 24

1 Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zina zija, ku nyanga zolodzera, koma anayang’ana nkhope yake kuchipululu.

2 Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

3 Pamenepo ananena fanizo lake, nati,

Balamu mwana wa Beori anenetsa,

ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

4 wakumva mau a Mulungu anenetsa,

wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,

wakugwa pansi maso ake openyuka.

5 Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo;

zokhalamo zako, Israele!

6 Ziyalika monga zigwa,

monga minda m’mphepete mwa nyanja,

monga khonje wooka Yehova,

monga mikungudza m’mphepete mwa madzi.

7 Madzi adzayenda natuluka m’zotungira zake,

ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri,

ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi,

ndi ufumu wake udzamveketsa.

8 Mulungu amtulutsa mu Ejipito;

ali nayo mphamvu yonga ya njati;

adzawadyaamitundu, ndiwo adani ake.

Nadzamphwanya mafupa ao,

ndi kuwapyoza ndi mivi yake.

9 Anaunthama, nagona pansi ngati mkango,

ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani?

Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe,

wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.

10 Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m’manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.

11 Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.

12 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,

13 Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndisilivandi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?

14 Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza.

15 Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Balamu mwana wa Beori anenetsa,

ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;

16 anenetsa wakumva mau a Mulungu,

ndi kudziwa nzeru ya Wam’mwambamwamba,

wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,

wakugwa pansi wopenyuka maso.

17 Ndimuona, koma tsopano ai;

ndimpenya, koma si pafupi ai;

idzatuluka nyenyezi mu Yakobo,

ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele,

nidzakantha malire a Mowabu,

nidzapasula ana onse a Seti.

18 Ndi Edomu adzakhala akeake,

Seiri lomwe lidzakhala lakelake,

ndiwo adani ake;

koma Israele adzachita zamphamvu.

19 Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu;

nadzapasula otsalira m’mizinda.

20 Ndipo anayang’ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati,

Amaleke ndiye woyamba wa amitundu;

koma chitsiriziro chake,

adzaonongeka ku nthawi zonse.

21 Ndipo anayang’ana Akeni, nanena fanizo lake, nati,

kwanu nkokhazikika,

wamanga chisa chako m’thanthwe.

22 Koma Kaini adzaonongeka,

kufikira Asiriya adzakumanga nsinga.

23 Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ha! Adzakhala ndi moyo ndani pakuchita ichi Mulungu?

24 Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu,

ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi,

koma iyenso adzaonongeka.

25 Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/24-3a90975a87000f3acdf783f185f9c614.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 25

Aisraele achita chigololo napembedza mafano ku Sitimu

1 Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;

2 popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.

3 Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele.

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.

5 Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.

6 Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo lachihema chokomanako.

7 Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m’dzanja lake;

8 natsata munthu Mwisraele m’hema, nawapyoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m’mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.

9 Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.

10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

11 Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawathe ana a Israele m’nsanje yanga.

12 Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;

13 ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.

14 Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.

15 Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo mu Midiyani.

16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

17 Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha;

18 popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m’chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m’chija cha Peori.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/25-2268008534910ad26d12eecead70269e.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 26

Awerengedwa Aisraele

1 Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,

2 Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo mu Israele.

3 Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m’zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m’dziko la Ejipito.

5 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

6 Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.

7 Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

8 Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9 Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova;

10 ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.

11 Koma sanafe ana aamuna a Kora.

12 Ana aamuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

13 Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo.

14 Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri.

15 Ana aamuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni;

16 Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;

17 Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.

18 Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.

19 Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m’dziko la Kanani.

20 Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

21 Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.

22 Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.

23 Ana aamuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni;

24 Yasubu, ndiye kholo la banja la Ayasubu; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi.

25 Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu.

26 Ana aamuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele.

27 Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.

28 Ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.

29 Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi.

30 Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;

31 ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;

32 ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere.

33 Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

34 Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

35 Ana aamuna a Efuremu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekere, ndiye kholo la banja la Abekere; Tahani, ndiye kholo la banja la Atahani.

36 Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.

37 Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.

38 Ana aamuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;

39 Sefufamu ndiye kholo la banja la Asefufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu.

40 Ndipo ana aamuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani.

41 Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.

42 Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.

43 Mabanja onse a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai.

44 Ana aamuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Aimina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya.

45 Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele.

46 Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Asere ndiye Sera.

47 Iwo ndiwo mabanja a ana aamuna a Asere monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

48 Ana aamuna a Nafutali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeele, ndiye kholo la banja la Ayezeele; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;

49 Yezere, ndiye kholo la banja la Ayezere; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.

50 Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.

51 Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

Magawidwe a dziko

52 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

53 Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.

54 Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake.

55 Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.

56 Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere.

57 Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.

58 Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu.

59 Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.

60 Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni.

61 Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova.

62 Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.

63 Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m’zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.

64 Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m’chipululu cha Sinai.

65 Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m’chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/26-6b523b856c37a7d3f77e56c277e97ff3.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 27

Ana aakazi a Zelofehadi

1 Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.

2 Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pachihema chokomanako, ndi kuti,

3 Atate wathu adamwalira m’chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.

4 Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.

5 Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.

6 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

7 Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.

8 Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi.

9 Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ake cholowa chake.

10 Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wake cholowa chake.

11 Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale wake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.

Aikidwa Yoswa m’malo mwa Mose

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m’phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele.

13 Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;

14 popeza munapikisana nao mau anga m’chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m’chipululu cha Zini.

15 Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati,

16 Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo,

17 wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.

18 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;

19 numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.

20 Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israele ammvere.

21 Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.

22 Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;

23 namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/27-075e919676b2dfbd47132f5c049260e8.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 28

Nsembe yopsereza yosalekeza

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.

3 Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.

4 Mwanawankhosammodziyo umpereke m’mawa, ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo;

5 ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera.

6 Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

7 Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m’malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.

8 Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m’mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

Nsembe yopsereza ya pa tsiku la Sabata

9 Ndipo tsiku laSabataanaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;

10 ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.

11 Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng’ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;

12 ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa ng’ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;

13 ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ikhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

14 Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng’ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.

15 Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.

Za zikondwerero zomveka

16 Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi paliPaskawa Yehova.

17 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa.

18 Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena;

19 koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng’ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;

20 ndi nsembe yao ya efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng’ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;

21 upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi; uzitero ndi anaankhosa asanu ndi awiri;

22 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu.

23 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m’mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza.

24 Momwemo mupereke chakudya cha nsembe yamoto cha fungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, chakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.

25 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

26 Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m’chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

27 Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng’ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;

28 ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng’ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi,

29 limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;

30 tonde mmodzi wakutetezera inu.

31 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/28-21a6f970c777b93732f80fd6033619d1.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 29

1 Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.

2 Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;

3 ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng’ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,

4 ndi limodzi la magawo khumi likhale lamwanawankhosammodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;

5 ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo, yakutetezera inu;

6 pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

7 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;

8 koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng’ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;

9 ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng’ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;

10 limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;

11 tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.

12 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;

13 ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng’ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;

14 ndi nsembe yake yaufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng’ombe imodzi, momwemo nazo ng’ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;

15 ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo nao anaankhosa khumi ndi anai;

16 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

17 Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng’ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema;

18 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

19 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.

20 Ndi tsiku lachitatu ng’ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema;

21 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

22 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

23 Ndi tsiku lachinai ng’ombe khumi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;

24 nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

25 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

26 Ndi tsiku lachisanu ng’ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;

27 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

28 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

29 Ndi tsiku lachisanu ndi chimodzi ng’ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;

30 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

31 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

32 Ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri ng’ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;

33 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng’ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

34 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

35 Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena;

36 koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng’ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri, a chaka chimodzi, opanda chilema;

37 nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng’ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;

38 ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosakeleza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

39 Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.

40 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/29-6bda6024a48b42bc9555b20d2b226789.mp3?version_id=1068—