Categories
NUMERI

NUMERI 10

Adzipangira malipenga awiri asiliva

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m’zigono.

3 Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo lachihema chokomanako.

4 Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a mu Israele, azisonkhana kuli iwe.

5 Mukaliza chokweza ayende a m’zigono za kum’mawa.

6 Mukalizanso chokweza, a m’zigono za kumwera ayende; alize chokweza pakumuka.

7 Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai.

8 Ana aamuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.

9 Ndipo pamene mupita kunkhondo m’dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.

10 Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Aisraele achoka ku Sinai

11 Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa chihema cha mboni.

12 Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m’chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m’chipululu cha Parani.

13 Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.

14 Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang’anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.

15 Ndi pa gulu la fuko la ana a Isakara panali Netanele mwana wa Zuwara.

16 Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.

17 Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.

18 Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang’anira Elizuri mwana wa Sedeuri.

19 Ndi pa gulu la fuko la ana a Simeoni anayang’anira Selumiele mwana wa Zurishadai.

20 Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang’anira Eliyasafu mwana wa Deuwele.

21 Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.

22 Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang’anira Elisama mwana wa Amihudi.

23 Ndi pa gulu la fuko la ana a Manase anayang’anira Gamaliele mwana wa Pedazuri.

24 Ndi pa gulu la fuko la ana a Benjamini anayang’anira Abidani mwana wa Gideoni.

25 Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m’mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang’anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.

26 Ndi pa gulu la fuko la ana a Asere anayang’anira Pagiyele mwana wa Okarani.

27 Ndi pa gulu la fuko la ana a Nafutali anayang’anira Ahira mwana wa Enani.

28 Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao.

Mose apempha Hobabu awaperekeze

29 Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.

30 Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.

31 Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m’chipululu, ndipo udzakhala maso athu.

32 Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe.

33 Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipolikasa la chipanganocha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.

34 Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono.

35 Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.

36 Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/10-32ca20667530fb06da5fd7ec8e3acae1.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 11

Kudandaula kwa Aisraele

1 Ndipo anthu anaipa, namadandaula m’makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.

2 Pamenepo anthu anafuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazima.

3 Ndipo anatcha malowo dzina lake Tabera; popeza moto wa Yehova udayaka pakati pao.

4 Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?

5 Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;

6 koma tsopano moyo wathu waphwa; tilibe kanthu pamaso pathu komamanaawa.

7 Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola.

8 Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m’mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

9 Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo.

Mose adandaula pa katundu wake

10 Ndipo Mose anamva anthu alikulira m’mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

11 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?

12 Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?

13 Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.

14 Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.

15 Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang’ane tsoka langa.

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao kuchihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.

17 Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.

18 Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m’makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino mu Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.

19 Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;

20 koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m’mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?

21 Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

22 Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng’ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m’nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?

23 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai.

24 Ndipo Mose anatuluka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akulu a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa chihema.

25 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.

26 Koma amuna awiri anatsalira m’chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m’chigono.

27 Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m’chigono.

28 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.

29 Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!

30 Ndipo Mose ndi akulu onse a Israele anasonkhana kuchigono.

31 Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, n’kudza nazo zinziri zochokera kunyanja, ndipo zidagwa kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.

32 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang’ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono.

33 Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.

34 Ndipo anatcha malowo dzina lake Kibroti-Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka.

35 Kuchokera ku Kibroti-Hatava anthuwo anayenda kunka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/11-12a108c7cccf4da0a1422d54689bb562.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 12

Miriyamu ndi Aroni aukira Mose

1 Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.

2 Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva.

3 Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza kuchihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.

5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri.

6 Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhalamneneripakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m’masomphenya, ndinena naye m’kulota.

7 Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m’nyumba mwanga monse.

8 Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.

9 Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye.

10 Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.

11 Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.

12 Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wake watha potuluka iye m’mimba mwa make.

13 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mchiritsenitu, Mulungu.

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.

15 Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu.

16 Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m’chipululu cha Parani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/12-642d409a0d6a8b7aa744c1537788ef5e.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 13

Atumidwa amuna 12 kukazonda Kanani

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.

3 Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.

4 Maina ao ndi awa: wa fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri.

5 Wa fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori.

6 Wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.

7 Wa fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe.

8 Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni.

9 Wa fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu.

10 Wa fuko la Zebuloni, Gadiele mwana wa Sodi.

11 Wa fuko la Yosefe, wa fuko la Manase, Gadi mwana wa Susi.

12 Wa fuko la Dani, Amiyele mwana wa Gemali.

13 Wa fuko la Asere, Seturi mwana wa Mikaele.

14 Wa fuko la Nafutali, Nabi mwana wa Vofusi.

15 Wa fuko la Gadi, Geuwele mwana wa Maki.

16 Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.

17 Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwera, nimukwere kumapiri;

18 mukaone dziko umo liliri; ndi anthu akukhala m’mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofooka, ngati achepa kapena achuluka;

19 ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri mizindayo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m’malinga;

20 ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m’dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.

21 Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.

22 Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)

23 Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.

24 Malowa anawatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsangolo ana a Israele analichekako.

25 Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.

26 Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.

27 Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.

28 Komatu anthu okhala m’dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.

29 Aamaleke akhala m’dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m’mphepete mwa Yordani.

30 Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.

31 Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitingathe kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu.

32 Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu.

33 Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m’maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m’maso mwao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/13-d620e29d0c4d84a342462225540f9556.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 14

Aisraele afuna kubwerera kunka ku Ejipito

1 Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

2 Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m’dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m’chipululu muno!

3 Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Ejipito?

4 Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito.

5 Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele.

6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang’amba zovala zao;

7 nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.

8 Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

9 Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m’dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

10 Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m’chihema chokomanakokwa ana onse a Israele.

Mose atetezera anthu kwa Mulungu

11 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?

12 Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa.

13 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aejipito adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwachotsa pakati pao;

14 ndipo adzawauza okhala m’dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.

15 Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepoamitunduamene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,

16 Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m’dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m’chipululu.

17 Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti,

18 Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

19 Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.

20 Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:

21 koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;

22 popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m’chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;

23 sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;

24 koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m’dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.

25 Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m’chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Odandaulawo saloledwa kulowa dziko la Kanani

26 Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

27 Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.

28 Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m’makutu mwanga;

29 mitembo yanu idzagwa m’chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

30 simudzalowa inu m’dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m’mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

31 Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

32 Koma inu, mitembo yanu idzagwa m’chipululu muno.

33 Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m’chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m’chipululu.

34 Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.

35 Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m’chipululu muno, nadzafamo.

36 Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko,

37 amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.

38 Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.

39 Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri.

40 Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba paphiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa.

41 Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?

42 Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.

43 Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m’mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.

44 Koma anakwera pamwamba paphiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.

45 Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m’phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/14-ca3ac19e86ab15a442ff559dac38bf5c.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 15

Malamulo a pa nsembezo

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mukakalowa m’dziko lokakhalamo inu, limene ndilikupatsa inu,

3 ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng’ombe kapena nkhosa;

4 pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;

5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wamwanawankhosammodzi.

6 Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini.

7 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la hini, achitire Yehova fungo lokoma.

8 Ndipo pamene mukonza ng’ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;

9 abwere nayo, pamodzi ndi ng’ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini.

10 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.

11 Kudzatero ndi ng’ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.

12 Monga mwa kuwerenga kwake kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwake.

13 Onse akubadwa m’dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma.

14 Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso,

15 Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.

16 Pakhale chilamulo chimodzi ndi chiweruzo chimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.

17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

18 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene mulowa m’dziko limene ndilikukulowetsani,

19 kudzali, pakudya inu mkate wa m’dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.

20 Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumachitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza,

21 Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.

22 Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;

23 ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova analamula, ndi kunkabe m’mibadwo yanu;

24 pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng’ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.

25 Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.

26 Ndipo khamu lonse la ana a Israele, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linachichita osati dala.

27 Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo.

28 Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa.

29 Kunena za wobadwa m’dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.

30 Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m’dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.

31 Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye.

Alangidwa wosasunga Sabata

32 Ndipo pokhala ana a Israele m’chipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku laSabata.

33 Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.

34 Ndipo anayamba wamsunga, popeza sichinanenedwe choyenera kumchitira iye.

35 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa chigono.

36 Pamenepo khamu lonse linamtulutsa kunja kwa chigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.

Pakhale chizindikiro pa zovala zao

37 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

38 Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m’mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m’mphepetemo thonje lamadzi.

39 Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang’anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m’mtima mwanu, ndi za m’maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;

40 kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu.

41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukutulutsani m’dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/15-9d0140c4b5be3255e8abd33f2cd93ab6.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 16

Kora, Datani, ndi Abiramu aukira Mose

1 Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

2 ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

3 Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?

4 Pamene Mose anamva ichi anagwa nkhope yake pansi;

5 nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M’mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.

6 Chitani ichi; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lake lonse;

7 nimuikemo moto, muikenso chofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.

8 Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;

9 kodi muchiyesa chinthu chaching’ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku gulu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya chihema cha Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

10 ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? Ndipo kodi mufunanso ntchito ya nsembe?

11 Chifukwa chake, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?

12 Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:

13 kodi ndi chinthu chaching’ono kuti watikweza kutichotsa m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m’chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

14 Ndiponso sunatilowetse m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yampesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako.

15 Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.

16 Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;

17 nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m’mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.

18 Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo lachihema chokomanakopamodzi ndi Mose ndi Aroni.

19 Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.

Alangidwa oukirawo

20 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

21 Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m’kamphindi.

22 Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24 Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kuchoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.

25 Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata.

26 Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m’zochimwa zao zonse.

27 Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna, ndi makanda ao.

28 Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m’mtima mwangamwanga.

29 Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumize ine.

30 Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.

31 Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang’ambika pansi pao;

32 ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.

33 Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.

34 Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.

35 Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.

Alanditsa mbale zofukiza za oukirawo

36 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

37 Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali: pakuti zili zopatulika;

38 mbale zofukizazo za iwo amene adachimwira moyo waowao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, chifukwa chake zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala chizindikiro kwa ana a Israele.

39 Ndipo Eleazara wansembe anatenga mbale zofukiza zamkuwa, zimene anthu opsererawo adabwera nazo; ndipo anazisula zaphanthiphanthi zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe;

40 chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.

Anthu adandaula, mliri uwaononga

41 Koma m’mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.

42 Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.

43 Ndipo Mose ndi Aroni anadza kukhomo kwa chihema chokomanako.

44 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

45 Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m’kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi.

46 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.

47 Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera.

48 Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka.

49 Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.

50 Ndipo Aroni anabwera kwa Mose ku khomo la chihema chokomanako; ndi mliri unaleka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/16-32ede4777061826d04644deec21e5393.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 17

Ndodo ya Aroni iphuka

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.

3 Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.

4 Ndipo uziike m’chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu.

5 Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.

6 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.

7 Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m’chihema cha mboni.

8 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti Mose analowa m’chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n’kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n’kubereka akatungurume.

9 Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake.

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.

11 Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza, momwemo anachita.

12 Pamenepo ana a Israele ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.

13 Yense wakuyandikiza chihema cha Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/17-125ef890b3b305f0d60f69a097cacfce.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 18

Udindo wa ansembe ndi Alevi, ndi zolandira zao

1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.

2 Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.

3 Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa chihema chonse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.

4 Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wachihema chokomanako, kuchita ntchito yonse ya chihema; koma mlendo asayandikize inu.

5 Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele.

6 Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.

7 Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m’kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.

9 Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako aamuna.

10 Muzizidya izi monga zopatulika kwambiri; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika.

11 Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m’banja lako adyeko.

12 Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.

13 Zipatso zoyamba zonse zili m’dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m’banja lako adyeko.

14 Zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zako.

15 Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.

16 Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.

17 Koma ng’ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.

18 Ndipo nyama yake ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.

19 Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.

20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m’dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele.

Limodzi la magawo khumi ndilo gawo la ansembe

21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.

22 Ndipo kuyambira tsopano ana a Israele asayandikize chihema chokomanako, angamasenze uchimo kuti angafe.

23 Koma Alevi azichita ntchito ya chihema chokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale nacho cholowa pakati pa ana a Israele.

24 Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele.

25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

26 Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.

27 Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.

28 Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

29 Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.

30 Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.

31 Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m’chihema chokomanako.

32 Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/18-aa1725f0db0916c8067886115c5cebb5.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 19

Za ng’ombe yaikazi yofiira ndi madzi oyeretsa nao

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng’ombe yaikazi yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m’goli;

3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.

4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pachihema chokomanako.

5 Pamenepo atenthe ng’ombe yaikaziyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake.

6 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndihisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng’ombe yaikazi.

7 Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8 Ndipo iye wakutentha ng’ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9 Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng’ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m’malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.

10 Ndipo wakuola mapulusayo a ng’ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

11 Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;

12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.

13 Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.

14 Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m’hema, yense wakulowa m’hemamo, ndi yense wakukhala m’hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

15 Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.

16 Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

17 Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m’chotengera madzi oyenda;

18 ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m’madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.

19 Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala woyera madzulo.

20 Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.

21 Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

22 Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/19-f0ea25e1a90155dc929b1d78188541aa.mp3?version_id=1068—