Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 10

Pangano lokhazikika pakati pa anthu ndi Mulungu

1 Okhomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,

2 Seraya, Azariya, Yeremiya,

3 Pasuri, Amariya, Malikiya,

4 Hatusi, Sebaniya, Maluki,

5 Harimu, Meremoti, Obadiya,

6 Daniele, Ginetoni, Baruki,

7 Mesulamu, Abiya, Miyamini,

8 Maaziya, Biligai, Semaya, ndiwo ansembe.

9 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele;

10 ndi abale ao: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,

11 Mika, Rehobu, Hasabiya,

12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya,

13 Hodiya, Bani, Beninu.

14 Akulu a anthu: Parosi, Pahatimowabu, Elamu, Zatu, Bani,

15 Buni, Azigadi, Bebai,

16 Adoniya, Bigivai, Adini,

17 Atere, Hezekiya, Azuri,

18 Hodiya, Hasumu, Bezai,

19 Harifi, Anatoti, Nebai,

20 Magapiyasi, Mesulamu, Heziri,

21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa,

22 Pelatiya, Hanani, Anaya,

23 Hoseya, Hananiya, Hasubu,

24 Halohesi, Piliha, Sobeki,

25 Rehumu, Hasabuna, Maaseiya,

26 ndi Ahiya, Hanani, Anani,

27 Maluki, Harimu, Baana.

28 Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m’kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m’dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,

29 amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m’temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m’chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;

30 ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m’dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;

31 ndipo mitundu ya anthu a m’dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku laSabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.

32 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

33 kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.

34 Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m’chilamulo;

35 ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;

36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m’chilamulo, ndi oyamba a ng’ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m’nyumba ya Mulungu wathu;

37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m’midzi yonse yolima ife.

38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.

39 Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/10-e2907d3749ba6ac9a9dd19e9230ebcd2.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 11

Ena akhala mu Yerusalemu, ena m’midzi ina

1 Ndipo akulu a anthu anakhala muYerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m’mizinda ina.

2 Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala mu Yerusalemu.

3 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m’midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m’midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m’kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.

4 Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;

5 ndi Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.

6 Ana onse a Perezi okhala mu Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.

7 Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya.

8 Ndi wotsatana naye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

9 Ndi Yowele mwana wa Zikiri ndiye woyang’anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang’anira mzinda.

10 Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini,

11 Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi mtsogoleri wa m’nyumba ya Mulungu;

12 ndi abale ao ochita ntchito ya m’nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya;

13 ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri;

14 ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang’anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu.

15 Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni;

16 ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang’anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu;

17 ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

18 Alevi onse m’mzinda wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.

19 Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

20 Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m’midzi yonse ya Yuda, yense m’cholowa chake.

21 Koma antchito a m’kachisi anakhala mu Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang’anira antchito a m’kachisi.

22 Ndipo woyang’anira wa Alevi mu Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang’anira ntchito ya m’nyumba ya Mulungu.

23 Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake.

24 Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.

25 Ndi ana ena a Yuda anakhala m’midzi ya kuminda yao, mu Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ndi mu Diboni ndi midzi yake, ndi mu Yekabizeele ndi midzi yake,

26 ndi mu Yesuwa, ndi mu Molada, ndi Betepeleti,

27 ndi mu Hazara-Suwala, ndi mu Beereseba ndi midzi yake,

28 ndi mu Zikilagi, ndi mu Mekona ndi midzi yake,

29 ndi mu Enirimoni, ndi mu Zora, ndi mu Yaramuti,

30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi midzi yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu.

31 Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi midzi yake,

32 pa Anatoti, Nobi, Ananiya,

33 Hazori, Rama, Gitaimu,

34 Hadidi, Zeboimu, Nebalati,

35 Lodi, ndi Ono, chigwa cha amisiri.

36 Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/11-f3c4f10c7ab83f701f0e3e896f785769.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 12

Maina a ansembe ndi Alevi ofika ku Yerusalemu pamodzi ndi Zerubabele

1 Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,

2 Amariya, Maluki, Hatusi,

3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti,

4 Ido, Ginetoyi, Abiya,

5 Miyamini, Maadiya, Biliga,

6 Semaya, ndi Yoyaribu, Yedaya.

7 Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akulu a ansembe ndi abale ao m’masiku a Yesuwa.

8 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.

9 Ndi Bakibukiya ndi Uni, abale ao, anawayang’anira maulonda.

10 Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada,

11 ndi Yoyada anabala Yonatani, ndi Yonatani, anabala Yaduwa.

12 Ndi m’masiku a Yoyakimu ansembe aakulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya;

13 wa Ezara, Mesulamu; wa Amariya, Yehohanani;

14 wa Maluki, Yonatani; wa Sebaniya, Yosefe;

15 wa Harimu, Adina; wa Meraiyoti, Helikai;

16 wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu;

17 wa Abiya, Zikiri; wa Miniyamini, wa Mowadiya, Pilitai;

18 wa Biliga, Samuwa; wa Semaya, Yehonatani;

19 ndi wa Yoyaribu, Matenai; wa Yedaya, Uzi;

20 wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi;

21 wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netanele.

22 M’masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya.

23 Ana a Levi, akulu a nyumba za makolo, analembedwa m’buku la machitidwe, mpaka masiku a Yohanani mwana wa Eliyasibu.

24 Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.

25 Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubu, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za chuma zili kuzipata.

26 Awa anakhala m’masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m’masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.

Kuperekedwa kwa linga la Yerusalemu

27 Ndipo popereka linga laYerusalemuanafunafuna Alevi m’malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.

28 Ana a oimbirawo anasonkhana ochokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi kumidzi ya Anetofa,

29 ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.

30 Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.

31 Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;

32 ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akulu a Yuda,

33 ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,

34 Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya,

35 ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,

36 ndi abale ake: Semaya, ndi Azarele, Milalai, Gilalai, Maai, Netanele, ndi Yuda, Hanani, ndi zoimbira za Davide munthu wa Mulungu; ndi Ezara mlembiyo anawatsogolera;

37 ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum’mawa.

38 Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng’anjo, mpaka kulinga lachitando;

39 ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.

40 Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m’nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine;

41 ndi ansembe, Eliyakimu, Maaseiya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya, ndi Hananiya, ali nao malipenga;

42 ndi Maaseiya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanani, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezere. Ndipo oimbira anaimbitsa Yezeraya ndiye woyang’anira wao.

43 Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali.

Akonzanso za kupereka limodzi la magawo khumi

44 Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m’mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.

45 Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomoni mwana wake.

46 Pakuti m’masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.

47 Ndi Aisraele onse m’masiku a Zerubabele, ndi m’masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/12-d60c071c94d49bac6f5232f0a30014b0.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 13

Tobiya achotsedwa ku Kachisi

1 Tsiku lomwelo anawerenga m’buku la Mose m’makutu a anthu, napeza m’menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;

2 popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.

3 Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.

4 Chinkana ichi, Eliyasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anachita chibale ndi Tobiya,

5 namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa,lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.

6 Koma pochitika ichi chonse sindinkakhale kuYerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;

7 ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira choipa anachichita Eliyasibu, chifukwa cha Tobiya, ndi kumkonzera chipinda m’mabwalo a nyumba ya Mulungu.

8 Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m’nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m’chipindamo.

9 Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi lubani.

10 Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m’mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake.

11 Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwaika m’malo mwao.

12 Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma.

13 Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.

14 Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.

Tsiku la Sabata likhalanso lopatulika

15 Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m’choponderamo tsiku laSabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.

16 Anakhalanso m’menemo a ku Tiro, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa tsiku la Sabata kwa ana a Yuda ndi mu Yerusalemu.

17 Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?

18 Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mzinda uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata.

19 Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata.

20 Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri.

21 Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata.

22 Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.

Nehemiya awadzudzula pa kukwatira akazi akunja

23 Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu,

24 ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse.

25 Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.

26 Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwaamitunduambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.

27 Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo?

28 Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.

29 Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi.

30 Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake;

31 ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/13-fea8a3addb8ee063b35c35b39c807f29.mp3?version_id=1068—