Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Nehemiya

tingathe kuligawa mu magawo anai: Gawo loyamba ndi pamene Nehemiya akubwerera ku Yerusalemu, atatumizidwa ndi mfumu ya ku Persiya kuti akakhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda. Gawo lachiwiri ndi pamene akumanganso malinga a Yerusalemu. Lachitatu ndi pamene Ezara akuwerenga Malamulo a Mulungu anthuwo nalapa machimo. Gawo lachinai ndi ntchito zina zimene Nehemiya anazichita pokhala bwanamkubwa wa ku Yuda.

Chinthu chodziwika bwino mu bukuli ndi mbiri ya moyo wa Nehemiya wodalira pa Mulungu komanso kukonda kupemphera.

Za mkatimu

Nehemiya abwerera ku Yerusalemu

1.1—2.20

Kumangidwanso kwa makoma a Yerusalemu

3.1—7.73

Lamulo liwerengedwa, ndipo anthu akonzanso mapangano ao

8.1—10.39

Ntchito zina za Nehemiya

11.1—13.31

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 1

Nehemiya apempherera ana a Israele kwa Mulungu

1 Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,

2 anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi zaYerusalemu.

3 Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto.

4 Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,

5 ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;

6 mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.

7 Tachita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulira mtumiki wanu Mose.

8 Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;

9 koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.

10 Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba.

11 Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/1-35fa40ae186ac5964313b6748afde4d4.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 2

Arita-kisereksesi alola Nehemiya akamange linga la Yerusalemu

1 Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.

2 Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha aakulu.

3 Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.

4 Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.

5 Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumzinda wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.

6 Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi.

7 Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse makalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;

8 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.

9 Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.

10 Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.

11 Motero ndinafika kuYerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.

12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m’mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.

13 Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang’ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.

14 Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera.

15 Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang’ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso.

16 Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi.

17 Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m’mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.

18 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.

19 Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?

20 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam’mwamba, Iye ndiye adzatilemeretsa; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, mu Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/2-fcf0168cc29ad4b4756c1d382e516969.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 3

Mamangidwe a malinga ndi zipata za Yerusalemu

1 Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.

2 Ndi pambali pake anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imuri.

3 Ndi Chipata cha Nsomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.

4 Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.

5 Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao.

6 Ndi Chipata Chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.

7 Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje.

8 Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsaYerusalemumpaka linga lachitando.

9 Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.

10 Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.

11 Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng’anjo.

12 Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi.

13 Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala mu Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.

14 Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake.

15 Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.

16 Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.

17 Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.

18 Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila.

19 Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.

20 Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe.

21 Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu.

22 Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kuchidikha.

23 Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake.

24 Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya.

25 Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.

26 Koma antchito a m’kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum’mawa, ndi nsanja yosomphokayo.

27 Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele.

28 Kumtunda kwa Chipata cha Akavalo anakonza ansembe, yense pandunji pa nyumba yake.

29 Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga Chipata cha Kum’mawa.

30 Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake.

31 Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m’kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.

32 Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/3-35a363f328f24b75697f847a2b9df5e2.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 4

Adani ayesa kuwaletsa kumanga malinga

1 Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete.

2 Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?

3 Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.

4 Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m’dziko la ndende;

5 ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.

6 Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.

7 Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga aYerusalemuanakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;

8 napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m’menemo.

9 Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa.

10 Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.

11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.

12 Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.

Ankhondo atchinjiriza antchito

13 Chifukwa chake ndinawaika potera m’kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.

14 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Ambuye wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.

15 Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.

16 Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m’mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.

17 Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida;

18 ndi omanga linga aliyense anamangirira lupanga lake m’chuuno mwake, nagwira ntchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.

19 Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Ntchito ndiyo yochuluka ndi yachitando, ndi ife tili palakepalake palingapo, yense atalikizana ndi mnzake;

20 paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.

21 Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.

22 Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone mu Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana.

23 Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/4-38be6d4224d9a6addda239215b6fd0dd.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 5

Nehemiya atchinjiriza aumphawi opsinjika

1 Pamenepo panamveka kulira kwakukulu kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.

2 Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.

3 Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi.

4 Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.

5 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu aakazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.

6 Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri.

7 Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.

8 Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwaamitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.

9 Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m’kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?

10 Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.

11 Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao yaazitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.

12 Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa.

13 Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati,Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.

14 Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m’dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe.

15 Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndisilivamasekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.

16 Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.

17 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.

18 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng’ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.

19 Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/5-8f7b93e64342364ce1095bfb4cc368e7.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 6

Adani ayesa kunyenga ndi kuopsa Nehemiya

1 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);

2 anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa.

3 Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?

4 Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.

5 Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata yosatseka m’dzanja mwake;

6 m’menemo mudalembedwa, Kwamveka mwaamitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.

7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe kuYerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.

8 Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.

9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.

10 Pamenepo ndinalowa m’nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m’kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.

11 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa mu Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.

12 Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.

13 Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.

14 Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiyamneneriwamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.

15 Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.

16 Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.

17 Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso makalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso makalata ake a Tobiya.

18 Pakuti ambiri mu Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

19 Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza makalata kuti andiopse ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/6-008ca1ec27add51061ee2ed3de4c9646.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 7

Alonda adikira Yerusalemu

1 Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;

2 ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa paYerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.

3 Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala mu Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.

4 Mzindawo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m’mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.

Maina a oyamba kubwerera kuchokera ku Babiloni

5 Ndipo Mulungu wanga anaika m’mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m’mwemo.

6 Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:

7 ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo:

8 ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.

9 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

10 Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

11 Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu.

12 Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.

13 Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

14 Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

15 Ana a Binuyi, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

16 Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

17 Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri.

18 Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri.

19 Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.

20 Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.

21 Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.

22 Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

23 Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.

24 Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

25 Ana a Gibiyoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu.

26 Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi atatu.

27 Amuna a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

28 Amuna a ku Betazimaveti, makumi anai kudza awiri.

29 Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.

30 Amuna a ku Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

31 Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

32 Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.

33 Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri.

34 Ana a Elamu winayo, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.

35 Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

36 Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

37 Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

38 Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu.

39 Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

40 Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

41 Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

42 Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

43 A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai.

44 Oimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

45 Odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.

46 Antchito a m’kachisi: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

47 ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni,

48 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai,

49 ana a Hanani, ana a Gidele, ana a Gahara,

50 ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda,

51 ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya,

52 ana a Besai, ana a Meunimu, ana a Nefusesimu,

53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,

54 ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa,

55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,

56 ana a Neziya, ana a Hatifa.

57 Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,

58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele,

59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Amoni.

60 Antchito onse a m’kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.

61 Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele;

62 ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.

63 Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.

64 Awa anafunafuna maina ao m’buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.

65 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndiUrimu ndi Tumimu.

66 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,

67 osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri mphambu makumi anai kudza asanu ndi mmodzi.

68 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu;

69 ngamirazao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu ao zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.

Zopereka za akulu

70 Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.

71 Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso yasilivazikwi ziwiri mphambu mazana awiri.

72 Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.

73 Nakhala m’midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi antchito a m’kachisi, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m’midzi mwao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/7-8915f37d6a4d4d188f73b896500d8fdb.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 8

Ezara awerengera anthu buku la chilamulo

1 Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.

2 Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri.

3 Nawerenga m’menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.

4 Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo;ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.

5 Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.

6 Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti,Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.

7 Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.

8 Nawerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa chowerengedwacho.

9 Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo.

10 Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

11 Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni.

12 Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.

Chikondwerero cha Misasa

13 Ndipo m’mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo.

14 Napeza munalembedwa m’chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m’misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri,

15 ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m’midzi mwao monse ndi muYerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi zaazitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.

16 Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m’mabwalo ao, ndi m’mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.

17 Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m’ndende anamanga misasa, nakhala m’misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yoswa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israele sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu.

18 Anawerenganso m’buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/8-2c060b46a43c1448f2617e73e586b4eb.mp3?version_id=1068—

Categories
NEHEMIYA

NEHEMIYA 9

Msonkhano wa kusala ndi kupemphera

1 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndikuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi.

2 Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.

3 Naimirira poima pao, nawerenga m’buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao.

4 Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao.

5 Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.

6 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m’mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.

7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa mu Uri wa kwa Akaldeya, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;

8 ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.

9 Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,

10 nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsaFaraondi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m’dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.

11 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m’madzi olimba.

12 Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m’njira akayendamo.

13 Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;

14 ndiSabatalanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;

15 ndi mkate wochokera m’mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m’thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.

16 Koma iwo ndi makolo athu anachita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu,

17 nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m’kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.

18 Ngakhale apa atadzipangira mwanawang’ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu;

19 koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m’chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m’njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.

20 Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamanemanaanu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.

21 Ndipo munawalera zaka makumi anai m’chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinathe, ndi mapazi ao sanatupe.

22 Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m’madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.

23 Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m’mwamba, nimunawalowetsa m’dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.

24 Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m’dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m’dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m’dziko, kuti achite nao chifuniro chao.

25 Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda yaazitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.

26 Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m’mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.

27 Chifukwa chake munawapereka m’dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m’dzanja la adani ao.

28 Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m’dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva mu Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;

29 ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.

30 Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m’dzanja la mitundu ya anthu a m’dziko.

31 Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawathe, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.

32 Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.

33 Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;

34 ndi mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunge chilamulo chanu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawachitira umboni nazo.

35 Popeza sanatumikire Inu mu ufumu wao, ndi mu ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m’dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa.

36 Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zake ndi zokoma zake, taonani, ife ndife akapolo m’menemo.

37 Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.

38 Ndipo mwa ichi chonse tichita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikhomera chizindikiro.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/9-c7809a61e3fe57e74c91cf1d3f4e9932.mp3?version_id=1068—