Categories
NAHUMU

NAHUMU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli ndi ndakatulo yokondwerera kupasuka kwa Ninive, mzinda waukulu wa Aasiriya amene ankazunza Aisraele kuyambira kale. Kupasuka kwa mzindawo kuwoneka ngati chilango cha Mulungu chogwera anthu onyada ndi ankhanza.

Za mkatimu

Chauta aimba Ninive mlandu

1.1-15

Kupasuka kwa mzindawo

2.1—3.19

Categories
NAHUMU

NAHUMU 1

Chilungamo ndi chifundo cha Mulungu. Adzaononga adani ndi kulanditsa anthu ake

1 Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

2 Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake.

3 Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m’kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.

4 Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala.

5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m’mwemo.

6 Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.

7 Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

8 Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.

9 Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

10 Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.

11 Mwa iwe watuluka wina wolingalira choipa chotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pake.

12 Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nachuluka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Chinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.

13 Koma tsopano ndidzathyola ndi kukuchotsera goli lake, ndipo ndidzadula zomangira zako.

14 Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m’nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.

15 Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NAM/1-9e429d61b8c465db9f9a40f9abc7a2ae.mp3?version_id=1068—

Categories
NAHUMU

NAHUMU 2

Ninive amangidwa misasa nalandidwa

1 Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang’anira panjira, limbitsa m’chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.

2 Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.

3 Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.

4 Magaleta achita mkokomo m’miseu, akankhana m’makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.

5 Akumbukira omveka ake; akhumudwa m’kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka.

6 Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka.

7 Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao.

8 Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.

9 Funkhanisiliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse.

10 Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m’zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.

11 Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?

12 Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.

13 Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake mu utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako padziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NAM/2-a3ae7af6dcbd71c31d97042bb6690d10.mp3?version_id=1068—

Categories
NAHUMU

NAHUMU 3

Zoipa za Ninive ndi kupasuka kwake

1 Tsoka mzinda wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza.

2 Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;

3 munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong’anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

4 chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsaamitundumwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake.

5 Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.

6 Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo.

7 Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza?

8 Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pamtsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja?

9 Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza.

10 Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo.

11 Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani.

12 Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m’kamwa mwa wakudya.

13 Taona, anthu ako m’kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.

14 Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng’anjo yanjerwa.

15 Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe.

16 Wachulukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; chirimamine anyambita, nauluka, nathawa.

17 Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m’matchinga tsiku lachisanu, koma likatuluka dzuwa ziuluka ndi kuthawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.

18 Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.

19 Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NAM/3-3ee4e47dfc76afa9f7c724171064fb7f.mp3?version_id=1068—