Categories
MLALIKI

MLALIKI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli lipereka maganizo a Mphunzitsi wina amene adayesetsa kumvetsa za moyo wa munthu; poona kuti moyowo sukhalira kutha ndiponso ndi wodzaza ndi mavuto, poonanso kuti zinthu siziyenda motsata chilungamo monga momwe mwini wake ankayembekezera. Mlalikiyo atafufuza zonsezi anagoti, “Zachabechabe…zachabechabe zonse ndi chabe.” Sankamvetsa njira zake za Mulungu, amene amaongolera moyo wa anthu ndi zinthu zina zonse mwa njira yodziwa Iye yekha, potsata zomwe Iye amaganizira pa chiyambi. Komabe Mlalikiyo akuwauza anthu kuti agwire ntchito molimbika ndiponso azikondwerera mphatso za Mulungu mpaka kukhutira pa nthawi yonse ya moyo wao.

Mwina anthu sangavomerezane ndi maganizo ambiri a Mlaliki, poona kuti maganizowo ngokayikitsa ndi otayitsa mtima. Komabe popeza kuti bukuli lipezeka mu Baibulo, ndiye kuti ngakhale maganizo amenewa angathe kuthandiza anthu ambiri kumvetsa za m’mene moyo wao uliri, akamasinkhasinkha mau ena ambiri a mu Baibulo momwemo onena za madalitso aakulu amene Mulungu wasungira anthu okhulupirira Iyeyo.

Za mkatimu

Kodi moyo uli ndi cholinga?

1.1—2.26

Zonena zokhudza moyo

3.1—11.8

Malangizo otsiriza

11.9—12.8

Mau omaliza

12.9-14

Categories
MLALIKI

MLALIKI 1

Za pansi pano nzachabe

1 Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya muYerusalemu.

2 Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.

3 Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?

4 Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.

5 Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako.

6 Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.

7 Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.

8 Zinthu zonse zilemetsa; munthu sangathe kuzifotokoza; maso sakhuta m’kuona, ndi makutu sakhuta m’kumva.

9 Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.

10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.

11 Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m’tsogolomo, sadzazikumbukirai.

12 Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu.

13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.

14 Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

15 Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe.

16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.

17 Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.

18 Pakuti m’nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/1-dd0ec0fb2ee2fa728bfb140a46f68729.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 2

Za m’moyo uno sizitha kukondweretsa mtima

1 Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.

2 Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?

3 Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

4 Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;

5 ndinakonza mphanje ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundumitundu;

6 ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m’nkhalango momeramo mitengo;

7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing’ono kupambana onse anakhala muYerusalemundisanabadwe ine;

8 ndinakundikansosilivandi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.

9 Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.

10 Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m’ntchito zanga zonse ndi limeneli.

11 Pamenepo ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

12 Ndipo ndinatembenuka kukayang’ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.

13 Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

14 Wanzeru maso ake ali m’mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.

15 Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.

16 Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m’tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.

17 Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

18 Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata.

19 Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.

20 Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.

21 Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.

22 Pakuti munthu ali ndi chiyani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?

23 Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe.

24 Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.

25 Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.

26 Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/2-7e1af7472df83fb66d8bdf327a368b14.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 3

Zilizonse zili ndi nyengo yake, Mulungu ndi kuziika zonse

1 Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;

2 mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;

3 mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;

4 mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;

5 mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;

6 mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;

7 mphindi yakung’amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;

8 mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.

9 Wogwira Ntchito aona phindu lanji m’chomsautsacho?

10 Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo.

11 Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.

12 Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo.

13 Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

14 Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.

15 Chomwe chinaoneka, chilikuonekabe; ndi chomwe chidzaoneka chinachitidwa kale; Mulungu anasanthula zochitidwa kale.

16 Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.

17 Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.

18 Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zichitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ake kuti ndiwo nyama zakuthengo.

19 Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.

20 Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.

21 Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?

22 M’mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/3-8e358d8041764b8562c5445f8022c926.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 4

Matsoka ndi mavuto a moyo uno

1 Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.

2 Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;

3 inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno.

4 Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

5 Chitsiru chimanga manja ake, ndipo chidya nyama yakeyake.

6 Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti thoo pali vuto ndi kungosautsa mtima.

7 Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zachabe kunja kuno.

8 Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.

9 Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m’ntchito zao.

10 Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.

11 Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?

12 Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.

13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

14 Pakuti atuluka m’nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m’dziko lake asauka.

15 Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m’malo mwake.

16 Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m’mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/4-ea0ce4db12a609a9f25f50b4fe08a092.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 5

Malangizo osiyana akuwasamalira anthu m’moyo uno

1 Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.

2 Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.

3 Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno.

4 Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.

5 Kusawinda kupambana kuwinda osachita.

6 Usalole m’kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

8 Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.

9 Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza;

10 Wokondasilivasadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

11 Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?

12 Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.

13 Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;

14 koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m’dzanja lake mulibe kanthu.

15 Monga anatuluka m’mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m’dzanja lake.

16 Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?

17 Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.

18 Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.

19 Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

20 Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m’chimwemwe cha mtima wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/5-496d7a038ca21e3be0705ca3db35eaa1.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 6

Ngakhale Mulungu apatsa munthu zonse azikhumba koma mtima sukhuta nazo

1 Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu,

2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.

3 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;

4 pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake.

5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;

6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?

7 Ntchito zake zonse munthu angogwirira m’kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta.

8 Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?

9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

10 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.

11 Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?

12 Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m’tsogolo mwake kunja kuno?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/6-36290b2c86cc0e37329dd7049368d6a2.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 7

Kumva zowawa nkokoma, nzeru ndi kudziletsa momwemo

1 Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.

2 Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.

3 Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.

4 Mtima wa anzeru uli m’nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m’nyumba ya kuseka.

5 Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.

6 Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.

7 Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.

8 Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.

9 Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.

10 Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.

11 Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa; akuona dzuwa apindula nayo.

12 Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.

13 Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?

14 Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m’tsogolo mwao.

15 Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m’chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m’kuipa kwake.

16 Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?

17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?

18 Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.

19 Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m’mzinda.

20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.

21 Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;

22 pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.

23 Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru; koma inanditalikira.

24 Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?

25 Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;

26 ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.

27 Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m’kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;

28 chomwe moyo wanga uchifuna chifunire, koma osachipezai ndi ichi, mwamuna mmodzi mwa chikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeze.

29 Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/7-f7d5b47f5a89cf9f8809f560ca047ea2.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 8

Langizo la kumvera mfumu

1 Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.

2 Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m’kulumbira Mulungu.

3 Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda.

4 Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?

5 Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

6 pakuti kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake; popeza zoipa za munthu zimchulukira;

7 pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa?

8 Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.

9 Zonsezi ndaziona ndi kuyang’anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.

Woipa salangidwa pakuchita pomwepo; mwina wolungama aona nsautso

10 Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m’manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.

11 Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.

12 Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;

13 koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.

14 Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe.

15 Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.

16 Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;

17 pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/8-594f57f167273c052efbc8fb9252c95c.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI 9

Okoma ndi oipa amamva zomwezo. Khalani nazo zakupatsa Mulungu mokondwera

1 Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m’manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m’tsogolo mwao.

2 Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.

3 Ichi ndi choipa m’zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m’mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.

4 Pakuti woyang’ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa.

5 Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.

6 Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.

7 Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.

8 Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.

9 Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m’moyo ndi m’ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.

10 Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.

Nzeru ya mwini ilanditsa ena

11 Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m’nthawi mwake.

12 Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.

13 Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu;

14 panali mzinda waung’ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikulu, nawuzinga ndi nkhondo, nkumanga malinga aakulu;

15 koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.

16 Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.

17 Mau a anzeru achete amveka koposa kufuula kwa wolamulira mwa zitsiru.

18 Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/9-1c8c49bdff765158ebbeffe8acb88cf4.mp3?version_id=1068—