Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 30

Chivomerezo, pemphero ndi malangizo a Aguri

1 Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga.

Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu;

ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;

2 pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,

ndilibe luntha la munthu.

3 Sindinaphunzire nzeru

ngakhale kudziwa Woyerayo.

4 Ndani anakwera kumwamba natsikanso?

Ndani wakundika nafumbata mphepo?

Ndani wamanga madzi m’malaya ake?

Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?

Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.

5 Mau onse a Mulungu ali oyengeka;

ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

6 Usaonjezere kanthu pa mau ake,

angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.

7 Zinthu ziwiri ndakupemphani,

musandimane izo ndisanamwalire:

8 Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza;

musandipatse umphawi, ngakhale chuma,

mundidyetse zakudya zondiyenera;

9 ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?

Kapena ndingasauke ndi kuba,

ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

10 Usanamizire kapolo kwa mbuyake,

kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.

11 Pali mbadwo wotemberera atate ao,

osadalitsa amai ao.

12 Pali mbadwo wodziyesa oyera,

koma osasamba litsiro lao.

13 Pali mbadwo wokwezatu maso ao,

zikope zao ndi kutukula.

14 Pali mbadwo mano ao akunga malupanga,

zibwano zao zikunga mipeni;

kuti adye osauka kuwachotsa kudziko,

ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.

15 Msundu uli ndi ana aakazi awiri ati, Patsa, patsa.

Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,

ngakhale zinai sizinena, Kwatha:

16 Manda, ndi chumba,

dziko losakhuta madzi,

ndi moto wosanena, Kwatha.

17 Diso lochitira atate wake chiphwete,

ndi kunyoza kumvera amake,

makwangwala a kumtsinje adzalikolowola,

ana a mphungu adzalidya.

18 Zinthu zitatu zindithetsa nzeru,

ngakhale zinai, sindizidziwa:

19 Njira ya mphungu m’mlengalenga,

njira ya njoka pamwala,

njira ya ngalawa pakati pa nyanja,

njira ya mwamuna ndi namwali.

20 Chomwecho njira ya mkazi wachigololo;

adya, napukuta pakamwa, nati,

Sindinachite zoipa.

21 Chifukwa cha zinthu zitatu dziko linthunthumira;

ngakhale chifukwa cha zinai silingathe kupirira nazo;

22 chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu;

ndi chitsiru chitakhuta zakudya;

23 chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa;

ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.

24 Zilipo zinai zili zazing’ono padziko;

koma zipambana kukhala zanzeru:

25 Nyerere ndi mtundu wosalimba,

koma zitengeratu zakudya zao m’malimwe.

26 Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu,

koma ziika nyumba zao m’matanthwe.

27 Dzombe lilibe mfumu,

koma lituluka lonse mabwalomabwalo.

28 Buluzi ungamgwire m’manja,

koma ali m’nyumba za mafumu.

29 Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya;

ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:

30 Mkango umene uposa zilombo kulimba,

supatukira chinthu chilichonse;

31 tambala wolimba m’chuuno, ndi tonde,

ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.

32 Ngati wapusa podzikweza,

ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.

33 Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo;

ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo,

ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/30-db9df611125b9f92b067f0360681c25b.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 31

Malangizo a mai wa Lemuwele

1 Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa.

2 Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga?

Chiyani mwana wa zowinda zanga?

3 Musapereke mphamvu yako kwa akazi,

ngakhale kuyenda m’njira yoononga mafumu.

4 Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo;

akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?

5 Kuti angamwe, naiwale malamulo,

naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

6 Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali,

ndi vinyo kwa owawa mtima;

7 amwe, naiwale umphawi wake,

osakumbukiranso vuto lake.

8 Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula,

ndi mlandu wa amasiye onse.

9 Tsegula pakamwa pako

nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.

10 Mkazi wangwiro ndani angampeze?

Pakuti mtengo wake uposa ngale.

11 Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira,

sadzasowa phindu.

12 Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa,

masiku onse a moyo wake.

13 Afuna ubweya ndi thonje,

nachita mofunitsa ndi manja ake.

14 Akunga zombo za malonda;

nakatenga zakudya zake kutali.

15 Aukanso kusanake,

napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito.

16 Asinkhasinkha za munda, naugula;

naoka mipesa ndi zipatso za manja ake.

17 Amanga m’chuuno mwake ndi mphamvu,

nalimbitsa mikono yake.

18 Azindikira kuti malonda ake ampindulira;

nyali yake sizima usiku.

19 Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake,

nafumbata mtengo wake.

20 Aolowera chikhato chake osauka;

natambasulira aumphawi manja ake.

21 Saopera banja lake chipale chofewa;

pakuti banja lake lonse livala mlangali.

22 Adzipangira zimbwi zamawangamawanga;

navala bafuta ndi guta wofiirira.

23 Mwamuna wake adziwika kubwalo,

pokhala pakati pa akulu a dziko.

24 Asoka malaya abafuta, nawagulitsa;

napereka mipango kwa ogulitsa malonda.

25 Avala mphamvu ndi ulemu;

nangoseka nthawi ya m’tsogolo.

26 Atsegula pakamwa pake ndi nzeru,

ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.

27 Ayang’anira mayendedwe a banja lake,

sadya zakudya za ulesi.

28 Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala;

mwamuna wake namtama, nati,

29 Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro,

koma iwe uposa onsewo.

30 Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe;

koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

31 Mumpatse zipatso za manja ake;

ndi ntchito zake zimtame kubwalo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/31-3d11d4411361f4cf307575b7480eae73.mp3?version_id=1068—