Miyambo yosiyanasiyana
Miyambo ya Solomoni:
1 Mwana wanzeru akondweretsa atate;
koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.
2 Chuma cha uchimo sichithangata;
koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.
3 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;
koma amainga chifuniro cha wochimwa.
4 Wochita ndi dzanja laulesi amasauka;
koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5 Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzeru;
koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.
6 Madalitso ali pamutu pa wolungama;
koma m’kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
7 Amayesa wolungama wodala pomkumbukira;
koma dzina la oipa lidzavunda.
8 Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;
koma chitsiru cholongolola chidzagwa.
9 Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;
koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.
10 Wotsinzinira achititsa chisoni;
koma wodzudzula momveka achita mtendere.
11 M’kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;
koma m’kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
12 Udani upikisanitsa;
koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.
13 Nzeru ipezedwa m’milomo ya wozindikira;
koma wopusa pamsana pake nthyole.
14 Anzeru akundika zomwe adziwa;
koma m’kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.
15 Chuma cha wolemera ndi mzinda wake wolimba;
koma umphawi wao uononga osauka.
16 Ntchito za wolungama zipatsa moyo;
koma phindu la oipa lichimwitsa.
17 Wosunga mwambo ali m’njira ya moyo;
koma wosiya chidzudzulo asochera.
18 Wobisa udani ali ndi milomo yonama;
wonena ugogodi ndiye chitsiru.
19 Pochuluka mau zolakwa sizisoweka;
koma wokhala chete achita mwanzeru.
20 Lilime la wolungama likungasilivawosankhika;
koma mtima wa oipa uli wachabe.
21 Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;
koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22 Madalitso a Yehova alemeretsa,
saonjezerapo chisoni.
23 Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa;
koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24 Chomwe woipa achiopa chidzamfikira;
koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.
25 Monga kavumvulu angopita, momwemo woipa kuli zii;
koma olungama ndiwo maziko osatha.
26 Ngati vinyo wowawa m’mano, ndi utsi m’maso,
momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma.
27 Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;
koma zaka za oipa zidzafinimpha.
28 Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe;
koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.
29 Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;
koma akuchita zoipa adzaonongeka.
30 Wolungama sadzachotsedwa konse;
koma oipa sadzakhalabe m’dziko.
31 M’kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;
koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;
koma m’kamwa mwa oipa munena zokhota.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/10-6640647a67135114988aab0e34b398f7.mp3?version_id=1068—