Categories
MIYAMBO

MIYAMBO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli liphunzitsa nzeru zosiyanasiyana zothandiza anthu ndi kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira yokomera Mulungu ndi anzao. Mau ake ambiri akuwoneka ngati miyambi. Mau oyamba akuti, “Kudziwa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mau ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika.” Kenaka bukuli likupereka malangizo osiyanasiyana okhudza makhalidwe, kusunga mwambo, kupatsana ulemu ndi kukhalirana mwamtendere, kutsata choona ndi chilungamo, moyo wa pa banja, pa ntchito, pa malonda, pa maphwando ndi pa zochitika zina zilizonse. Nzeru ndizo zimene akuluakulu a Israele ankaphunzitsa anthu ao pa masiku akale. Wofuna kutsata nzeruzo ayenera kudzilamulira, kudzichepetsa, kuleza mtima, kulemekeza osauka ndi kukhala okhulupirika pa chibwenzi.

Za mkatimu

Bukuli lili ndi zigawo zingapo:

Mau oyamikira nzeru

1.1—9.18

Miyambi ya Solomoni

10.1—29.27

Mau a Aguri

30.1-33

Mau ena osiyanasiyana

31.1-31

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 1

Zochitira miyambo

1 Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele.

2 Kudziwa nzeru ndi mwambo;

kuzindikira mau ozindikiritsa;

3 kulandira mwambo wakusamalira machitidwe,

chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika;

4 kuchenjeza achibwana,

kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;

5 kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;

ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;

6 kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake,

mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.

Munthu asalole oipa amchete

7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa;

opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

8 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,

ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;

9 pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako,

ndi mkanda pakhosi pako.

10 Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.

11 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,

tilalire osachimwa opanda chifukwa;

12 tiwameze ali ndi moyo ngati manda,

ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13 tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake,

tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

14 udzachita nafe maere,

tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi.

15 Mwananga, usayende nao m’njira;

letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16 pakuti mapazi ao athamangira zoipa,

afulumira kukhetsa mwazi.

17 Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe;

18 ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao.

19 Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere;

chilanda moyo wa eni ake.

Chenjezo la Nzeru

20 Nzeru ifuula panja;

imveketsa mau ake pabwalo;

21 iitana posonkhana anthu polowera pachipata;

m’mzinda inena mau ake,

22 Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu?

Onyoza ndi kukonda kunyoza,

opusa ndi kuda nzeru?

23 Tembenukani pamene ndikudzudzulani;

taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,

ndikudziwitsani mau anga.

24 Chifukwa ndaitana, ndipo munakana;

ndatambasula dzanja langa,

ndipo panalibe analabadira;

25 koma munapeputsa uphungu wanga wonse,

ndi kukana kudzudzula kwanga.

26 Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu,

ndidzatonyola pakudza mantha anu;

27 pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,

ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu;

pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.

28 Pamenepo adzandiitana,

koma sindidzavomera;

adzandifunatu, osandipeza ai;

29 chifukwa anada nzeru,

sanafune kuopa Yehova;

30 anakana uphungu wanga,

nanyoza kudzudzula kwanga konse;

31 momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,

nadzakhuta zolingalira zao.

32 Pakuti kubwerera m’mbuyo kwa achibwana kudzawapha;

ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.

33 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,

nadzakhala phee osaopa zoipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/1-32cef618ad9ecae5edf89bcb3338ccd7.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 2

Ukoma ndi phindu lake la Nzeru

1 Mwananga, ukalandira mau anga,

ndi kusunga malamulo anga;

2 kutcherera makutu ako kunzeru,

kulozetsa mtima wako kukuzindikira;

3 ukaitananso luntha,

ndi kufuulira kuti ukazindikire;

4 ukaifunafuna ngatisiliva,

ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;

5 pompo udzazindikira kuopa Yehova

ndi kumdziwadi Mulungu.

6 Pakuti Yehova apatsa nzeru;

kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.

7 Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;

ndiye chikopa cha oyenda molunjika;

8 kuti atchinjirize njira za chiweruzo,

nadikire khwalala la opatulidwa ake.

9 Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo,

zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.

10 Pakuti nzeru idzalowa m’mtima mwako,

moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,

11 kulingalira kudzakudikira,

kuzindikira kudzakutchinjiriza;

12 kukupulumutsa kunjira yoipa,

kwa anthu onena zokhota;

13 akusiya mayendedwe olungama,

akayende m’njira za mdima;

14 omwe asangalala pochita zoipa,

nakondwera ndi zokhota zoipa;

15 amene apotoza njira zao,

nakhotetsa mayendedwe ao.

16 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere,

kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;

17 wosiya bwenzi la ubwana wake,

naiwalachipanganocha Mulungu wake.

18 Nyumba yake itsikira kuimfa,

ndi mayendedwe ake kwa akufa;

19 onse akunka kwa iye sabweranso,

safika kunjira za moyo;

20 nzeru idzakuyendetsa m’njira ya anthu abwino,

kuti usunge mayendedwe a olungama.

21 Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko,

angwiro nadzatsalamo.

22 Koma oipa adzalikhidwa m’dziko,

achiwembu adzazulidwamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/2-cf23f208ad1a7192340fc8e2c2fe8d53.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 3

Malangizo a kuopa, kukhulupirira, ndi kumvera Yehova

1 Mwananga, usaiwale malamulo anga,

mtima wako usunge malangizo anga;

2 pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,

ndi zaka za moyo ndi mtendere.

3 Chifundo ndi choonadi zisakusiye;

uzimange pakhosi pako;

uzilembe pamtima pako;

4 motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino,

pamaso pa Mulungu ndi anthu.

5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,

osachirikizika pa luntha lako;

6 umlemekeze m’njira zako zonse,

ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

7 Usadziyese wekha wanzeru;

opa Yehova, nupatuke pazoipa;

8 mitsempha yako idzalandirapo moyo,

ndi mafupa ako uwisi.

9 Lemekeza Yehova ndi chuma chako,

ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;

10 motero nkhokwe zako zidzangoti thee,

mbiya zako zidzasefuka vinyo.

11 Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,

ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;

12 pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;

monga atate mwana amene akondwera naye.

Phindu la Nzeru

13 Wodala ndi wopeza nzeru,

ndi woona luntha;

14 pakuti malonda a nzeru aposa malonda asiliva,

phindu lake liposa golide woyengeka.

15 Mtengo wake uposa ngale;

ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.

16 Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake;

chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere.

17 Njira zake zili zokondweretsa,

mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.

18 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;

wakuiumirira ngwodala.

19 Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;

naika zamwamba ndi luntha.

20 Zakuya zinang’ambika ndi kudziwa kwake;

thambo ligwetsa mame.

21 Mwananga, zisachokere kumaso ako;

sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;

22 ndipo mtima wako udzatengapo moyo,

ndi khosi lako chisomo.

23 Pompo udzayenda m’njira yako osaopa,

osaphunthwa phazi lako.

24 Ukagona, sudzachita mantha;

udzagona tulo tokondweretsa.

25 Usaope zoopsa zodzidzimutsa,

ngakhale zikadza zopasula oipa;

26 pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,

nadzasunga phazi lako lingakodwe.

Malangizo ena osiyana

27 Oyenera kulandira zabwino usawamane;

pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.

28 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,

ndipo mawa ndidzakupatsa;

pokhala uli nako kanthu.

29 Usapangire mnzako chiwembu;

popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.

30 Usakangane ndi munthu chabe,

ngati sanakuchitire choipa.

31 Usachitire nsanje munthu wachiwawa;

usasankhe njira yake iliyonse.

32 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;

koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.

33 Yehova atemberera za m’nyumba ya woipa;

koma adalitsa mokhalamo olungama.

34 Anyozadi akunyoza,

koma apatsa akufatsa chisomo.

35 Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao;

koma opusa adzakweza manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/3-e517f48ff8327cd8228c94a3e6c5b797.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 4

Chenjezo lakuti afune Nzeru nalewe njira za oipa

1 Ananu, mverani mwambo wa atate,

nimutchere makutu mukadziwe luntha;

2 pakuti ndikuphunzitsani zabwino;

musasiye chilangizo changa.

3 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,

wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina.

4 Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,

mtima wako uumirire mau anga;

sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

5 Tenga nzeru, tenga luntha;

usaiwale, usapatuke pa mau a m’kamwa mwanga;

6 usasiye nzeru, ndipo idzakusunga;

uikonde, idzakutchinjiriza.

7 Nzeru ipambana, tatenga nzeru;

m’kutenga kwako konseko utenge luntha.

8 Uilemekeze, ndipo idzakukweza;

idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

9 Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako;

idzakupatsa korona wokongola.

10 Tamvera mwananga, nulandire mau anga;

ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.

11 Ndakuphunzitsa m’njira ya nzeru,

ndakuyendetsa m’mayendedwe olungama.

12 Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;

ukathamanga, sudzaphunthwa.

13 Gwira mwambo, osauleka;

uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.

14 Usalowe m’mayendedwe ochimwa,

usayende m’njira ya oipa.

15 Pewapo, osapitamo;

patukapo, nupitirire.

16 Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona;

ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.

17 Pakuti amadya chakudya cha uchimo,

namwa vinyo wa chifwamba.

18 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha,

kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.

19 Njira ya oipa ikunga mdima;

sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.

20 Mwananga, tamvera mau anga;

tcherera makutu ku zonena zanga.

21 Asachoke kumaso ako;

uwasunge m’kati mwa mtima wako.

22 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,

nalamitsa thupi lao lonse.

23 Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;

pakuti magwero a moyo atulukamo.

24 Tasiya m’kamwa mokhota,

uike patali milomo yopotoka.

25 Maso ako ayang’ane m’tsogolo,

zikope zako zipenye moongoka.

26 Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;

njira zako zonse zikonzeke.

27 Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere;

suntha phazi lako kusiya zoipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/4-4bebf0641029010d0e0755c15bc99f54.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 5

Achenjere naye mkazi woipa

1 Mwananga, mvera nzeru yanga;

tcherera makutu ku luntha langa;

2 ukasunge zolingalira,

milomo yako ilabadire zomwe udziwa.

3 Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi;

m’kamwa mwake muti see koposa mafuta.

4 Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo,

ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse.

5 Mayendedwe ake atsikira kuimfa;

mapazi ake aumirira kumanda;

6 sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;

mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye.

7 Ndipo tsopano ana, mundimvere,

musapatuke ku mau a m’kamwa mwanga.

8 Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo,

osayandikira ku khomo la nyumba yake;

9 kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,

ndi zaka zako kwa ankhanza;

10 kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,

ndi kuti usagwire ntchito m’nyumba ya wachilendo;

11 ungalire pa chimaliziro chako,

pothera nyama yako ndi thupi lako;

12 ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,

mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo;

13 ndipo sindinamvere mau a aphunzitsi anga;

ngakhale kutcherera makutu kwa akundilanga mwambo!

14 Ndikadakhala m’zoipa zonse,

m’kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.

15 Imwa madzi a m’chitsime mwako,

ndi madzi oyenda a m’kasupe mwako.

16 Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,

ndi mitsinje ya madzi m’makwalala?

17 Ikhale ya iwe wekha,

si ya alendo okhala nawe ai.

18 Adalitsike kasupe wako;

ukondwere ndi mkazi wokula nayo.

19 Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo,

maere ake akukwanire nthawi zonse;

ukodwe ndi chikondi chake osaleka.

20 Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere,

ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?

21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,

asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.

22 Zoipa zakezake zidzagwira woipa;

adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.

23 Adzafa posowa mwambo;

adzasochera popusa kwambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/5-bbbe90f0618659e9199c566ac200b145.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 6

Za kuperekera mnzake chikole

Zisanu ndi ziwiri zoipira Mulungu

1 Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole,

ngati wapangana kulipirira mlendo,

2 wakodwa ndi mau a m’kamwa mwako,

wagwidwa ndi mau a m’kamwa mwako.

3 Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse;

popeza walowa m’dzanja la mnzako,

pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako.

4 Usaone tulo m’maso mwako,

ngakhale kuodzera zikope zako.

5 Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki,

ndi mbalame kudzanja la msodzi.

6 Pita kunyerere, waulesi iwe,

penya njira zao nuchenjere;

7 zilibe mfumu,

ngakhale kapitao, ngakhale mkulu;

8 koma zitengeratu zakudya zao m’malimwe;

ndipo zituta dzinthu zao m’masika.

9 Udzagona mpaka liti, waulesi iwe?

Udzauka kutulo tako liti?

10 Tulo tapang’ono, kuodzera pang’ono,

kungomanga manja pang’ono, ndi kugona;

11 ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,

ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

12 Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu;

amayenda ndi m’kamwa mokhota.

13 Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake,

amalankhula ndi zala zake;

14 zopotoka zili m’mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka;

amapikisanitsa anthu.

15 Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka;

adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.

16 Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida;

ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:

17 Maso akunyada, lilime lonama,

ndi manja akupha anthu osachimwa;

18 mtima woganizira ziwembu zoipa,

mapazi akuthamangira mphulupulu m’mangum’mangu;

19 mboni yonama yonong’ona mabodza,

ndi wopikisanitsa abale.

20 Mwananga, sunga malangizo a atate wako,

usasiye malamulo a mai ako;

21 uwamange pamtima pako osaleka;

uwalunze pakhosi pako.

22 Adzakutsogolera ulikuyenda,

ndi kukudikira uli m’tulo,

ndi kulankhula nawe utauka.

23 Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika;

ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.

24 Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa,

ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.

25 Asakuchititse kaso m’mtima mwako,

asakukole ndi zikope zake.

26 Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama,

udzamaliza ndi nyenyeswa;

ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.

27 Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake,

osatentha zovala zake?

28 Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,

osapsa mapazi ake?

29 Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake;

womkhudzayo sadzapulumuka chilango.

30 Anthu sanyoza mbala ikaba,

kuti ikhutitse mtima wake pomva njala;

31 koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;

idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.

32 Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru;

wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.

33 Adzalasidwa nanyozedwa;

chitonzo chake sichidzafafanizidwe.

34 Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,

ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.

35 Sadzalabadira chiombolo chilichonse,

sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/6-002dadb40a0570935a603f53806bf402.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 7

Achenjere naye mkazi woipa

1 Mwananga, sunga mau anga,

ukundike malangizo anga,

2 Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo;

ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.

3 Uwamange pa zala zako,

uwalembe pamtima pako.

4 Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongo wanga;

nutche luntha mbale wako.

5 Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere,

kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.

6 Pakuti pa zenera la nyumba yanga

ndinapenyera pamwamba pake;

ndinaona pakati pa achibwana,

7 ndinazindikira pakati pa aang’ono

mnyamata wopanda nzeru,

8 alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,

ndi kuyenda panjira ya kunyumba yake;

9 pa madzulo kuli sisiro,

pakati pa usiku pali mdima.

10 Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira,

atavala zadama wochenjera mtima,

11 ali wolongolola ndi wosaweruzika,

mapazi ake samakhala m’nyumba mwake.

12 Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo,

nabisalira pa mphambano zonse.

13 Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona;

nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe,

14 nsembe zamtendere zili nane;

lero ndachita zowinda zanga.

15 Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira,

kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.

16 Ndayala zofunda pakama panga,

nsalu zamawangamawanga za thonje la ku Ejipito,

17 ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira amure

ndi chisiyo ndi sinamoni.

18 Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamawa;

tidzisangalatse ndi chiyanjano.

19 Pakuti mwamuna kulibe kwathu,

wapita ulendo wa kutali;

20 watenga thumba la ndalama m’dzanja lake,

tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.

21 Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake,

ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.

22 Mnyamatayo amtsata posachedwa,

monga ng’ombe ipita kukaphedwa;

ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru;

23 mpaka muvi ukapyoza mphafa yake;

amtsata monga mbalame yothamangira msampha;

osadziwa kuti adzaononga moyo wake.

24 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,

labadirani mau a m’kamwa mwanga.

25 Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo,

usasochere m’mayendedwe ake.

26 Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa;

ndipo ophedwa ndi iye achulukadi.

27 Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda,

yotsikira kuzipinda za imfa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/7-27422fd7823f7b616ef37a976cfa2d76.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 8

Nzeru ipambana m’kuchita kwake

1 Kodi nzeru siitana,

luntha ndi kukweza mau ake?

2 Iima pamwamba pa mtunda,

pa mphambano za makwalala;

3 pambali pa chipata polowera m’mudzi,

polowa anthu pa makomo ifuula:

4 Ndinu ndikuitanani, amuna,

mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.

5 Achibwana inu, chenjerani,

opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;

6 imvani, pakuti ndikanena zoposa,

ndi zolungama potsegula pakamwa panga.

7 Pakuti m’kamwa mwanga mudzalankhula ntheradi,

zoipa zinyansa milomo yanga.

8 Mau onse a m’kamwa mwanga alungama;

mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.

9 Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;

alungama kwa akupeza nzeru.

10 Landirani mwambo wanga, sisilivaai;

ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika.

11 Pakuti nzeru iposa ngale,

ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo.

12 Ine Nzeru ndikhala m’kuchenjera, ngati m’nyumba yanga;

ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.

13 Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;

kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa,

ndi m’kamwa mokhota, ndizida.

14 Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;

ndine luntha; ndili ndi mphamvu.

15 Mwa ine mafumu alamulira;

akazembe naweruza molungama.

16 Mwa ine akalonga ayang’anira,

ndi akulu, ngakhale oweruza onse a m’dziko.

17 Akundikonda ndiwakonda;

akundifunafuna adzandipeza.

18 Katundu ndi ulemu zili ndi ine,

chuma chosatha ndi chilungamo.

19 Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka;

phindu langa liposa siliva wosankhika.

20 Ndimayenda m’njira ya chilungamo,

pakati pa mayendedwe a chiweruzo,

21 kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale cholowa chao,

ndi kudzaza mosungira mwao.

Nzeru ndiyo ya nthawi yosayamba

22 Yehova anali nane poyamba njira yake,

asanalenge zake zakale.

23 Anandiimika chikhalire chiyambire,

dziko lisanalengedwe.

24 Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine,

pamene panalibe akasupe odzala madzi.

25 Mapiri asanakhazikike,

zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa.

26 Asanalenge dziko, ndi thengo,

ngakhale chiyambi cha fumbi la dziko.

27 Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo;

pamene analemba pazozama kwetekwete;

28 polimbitsa Iye thambo la kumwamba,

pokula akasupe a zozama.

29 Poikira nyanja malire ake,

kuti madzi asapitirire pa lamulo lake;

polemba maziko a dziko.

30 Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri;

ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku,

ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;

31 ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu,

ndi kusekerera ndi ana a anthu.

32 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,

ngodala akusunga njira zanga.

33 Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.

34 Ngwodala amene andimvera,

nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku,

ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;

35 pakuti wondipeza ine apeza moyo;

Yehova adzamkomera mtima.

36 Koma wondichimwira apweteka moyo wake;

onse akundida ine akonda imfa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/8-65b70aedaa5e09db561e00a6b605e874.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 9

Madyerero a Nzeru

1 Nzeru yamanga nyumba yake,

yasema zoimiritsa zake zisanu ndi ziwiri;

2 yaphera nyama yake, nisakaniza vinyo wake,

nilongosolanso pa gome lake.

3 Yatuma anamwali ake, iitana

pa misanje ya m’mudzi.

4 Wazibwana yense apatukire kuno;

iti kwa yense wosowa nzeru,

5 Tiyeni, idyani chakudya changa;

nimumwe vinyo wanga ndamsakaniza.

6 Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo;

nimuyende m’njira ya nzeru.

7 Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi;

yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yakeyake.

8 Usadzudzule wonyoza kuti angakude;

dzudzula wanzeru adzakukonda.

9 Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake;

ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.

10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova;

kudziwa Woyerayo ndiko luntha.

11 Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka,

zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.

12 Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo?

Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.

13 Utsiru umalongolola,

ngwa chibwana osadziwa kanthu.

14 Ukhala pa khomo la nyumba yake,

pampando pa misanje ya m’mudzi,

15 kuti uitane akupita panjira,

amene angonkabe m’kuyenda kwao,

16 wachibwana ndani? Apatukire kuno.

Ati kwa yense wopanda nzeru,

17 madzi akuba atsekemera,

ndi chakudya chobisika chikoma.

18 Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko;

omwe achezetsa utsiru ali m’manda akuya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/9-f14cb55a6d54b6ebae11a55edb662d4b.mp3?version_id=1068—