Categories
MIKA

MIKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneriyu adalalika mau ake ku Yuda panthawi ya mneneri Yesaya. Iye ankadziwiratu kuti ufumu wa Yuda nawonso udzawonongedwa. Monga muja Yehova adalangira ufumu wakumpoto chifukwa Aisraelewo ntchito zao zinali zopanda chilungamo, momwemonso adzalanga ndi Ayuda omwe chifukwa cha zochita zao zosalungama. Komabe pa mau ake Mika akuonetsa chikhulupiriro chakuti Mulungu adzakonzanso zinthu kutsogoloko kuti zidzakhale bwino.

Kutsogoloko Mulungu adzakhazikitsanso ufumu wake kudzera mwa mmodzi mwa zidzukulu za Davide, ndipo adzadzetsa mtendere ponseponse (5.2-4).

Mau ena ofunikira kwambiri amene akunena mwachidule zimene aneneri anali kulalikira ndi awa akuti, “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (6.8)

Za mkatimu

Mau a Yehova otsutsa Aisraele ndi Ayuda

1.1—3.12

Mau ena a Yehova olonjeza zabwino

4.1—5.15

Mau ena a Yehova ochenjeza anthu, mau ena otsutsa chikhulupiriro

6.1—7.20

Categories
MIKA

MIKA 1

Mau akuchenjeza Israele ndi Yuda chifukwa cha machimo ao

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndiYerusalemu.

2 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m’mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.

3 Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m’malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.

4 Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang’ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetsereka.

5 Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu?

6 Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m’munda, ngati zooka m’munda wampesa; ndipo ndidzataya miyala yake m’chigwa, ndi kufukula maziko ake.

7 Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere.

8 Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

9 Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.

10 Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m’nyumba ya Afira ndinagubuduka m’fumbi.

11 Pitiratu, wokhala mu Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala mu Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake.

12 Pakuti wokhala mu Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.

13 Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala mu Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi waZiyonindi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe.

14 Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele.

15 Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.

16 Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/1-dd0804d9b0b670726b7ec842db775a3e.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 2

Mau akutsutsa akulanda za eni

1 Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m’mawa achichita, popeza chikhozeka m’manja mwao.

2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

3 Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.

4 Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.

5 Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m’msonkhano wa Yehova.

6 Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.

7 Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka?

8 Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.

9 Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.

10 Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.

11 Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiyemneneriwa anthu ake.

12 Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.

13 Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/2-bae0082b6ea1ed09cf70abcdcf3f139c.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 3

Chilangizo cha Mulungu chifukwa cha atsogolera ndi aneneri onyenga

1 Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?

2 Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;

3 inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

4 Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.

5 Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m’kamwa mwao, amkonzera nkhondo;

6 chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.

7 Ndipo alauli adzachita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

8 Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.

9 Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.

10 AmangaZiyonindi mwazi, ndiYerusalemundi chisalungamo.

11 Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.

12 Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m’nkhalango.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/3-bfd32fbc93b47b106e48b12587cc5ecf.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 4

Kuitanidwa kwa amitundu

1 Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.

2 Ndipoamitunduambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake; pakuti kuZiyonikudzatuluka chilamulo, ndi kuYerusalemumau a Yehova.

3 Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.

4 Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.

5 Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.

6 Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzamemeza wakutsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo, ndi iye amene ndinamsautsa;

7 ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m’phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.

8 Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.

9 Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?

10 Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m’mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m’manja a adani ako.

11 Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.

12 Koma sadziwa zolingirira za Yehova, kapena kuzindikira uphungu wake; pakuti anawasonkhanitsa ngati mitolo kudwale.

13 Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/4-badb7f0515bb48122b4a78b506a35223.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 5

1 Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.

Aneneratu za kubadwa kwa woweruza mu Israele

2 Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng’ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

3 Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.

4 Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.

5 Ndipo ameneyo adzakhala mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m’dziko lathu, ndi pamene adzaponda m’zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.

6 Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m’dziko lathu, pamene aponda m’kati mwa malire athu.

7 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.

8 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwaamitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.

9 Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.

10 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m’kati mwako, ndi kutha magaleta ako;

11 ndipo ndidzaononga mizinda ya m’dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;

12 ndipo ndidzaononga zanyanga za m’dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

13 ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.

14 Ndipo ndidzazula zifanizo zako m’kati mwako, ndi kutha mizinda yako.

15 Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera chilango mu mkwiyo waukali.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/5-0ec30371f0ae0a7cdc9963307c21cf90.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 6

Mulungu atsutsana ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao

1 Tamverani tsono chonena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako.

2 Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele.

3 Anthu anga inu, ndakuchitirani chiyani? Ndakulemetsani ndi chiyani? Chitani umboni wonditsutsa.

4 Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m’nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.

5 Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.

6 Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam’mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang’ombe a chaka chimodzi?

7 Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?

8 Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.

9 Mau a Yehova aitana mzinda, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.

10 Kodi m’nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?

11 Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?

12 Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m’kamwa mwao.

13 Chifukwa chake Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula chifukwa cha zochimwa zako.

14 Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzachotsa koma osalanditsa; ndi ichi wachilanditsa ndidzachipereka kulupanga.

15 Udzafesa koma osacheka; udzapondaazitonakoma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.

16 Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/6-9c401742239e12ba75a0b48e74239333.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 7

Za kuipa kwakukulu kwa Aisraele, ndi chifundo cha Mulungu

1 Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m’mwamvu, atakunkha m’munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.

2 Watha wachifundo m’dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.

3 Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.

4 Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.

5 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m’fukato mwako.

6 Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m’nyumba yake.

7 Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.

8 Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.

9 Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.

10 Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m’miseu.

11 Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali.

12 Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Ejipito, kuyambira ku Ejipito kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri.

13 Koma dziko lidzakhala labwinja chifukwa cha iwo okhalamo, mwa zipatso za machitidwe ao.

14 Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m’nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.

15 Monga masiku a kutuluka kwako m’dziko la Ejipito ndidzamuonetsa zodabwitsa.

16 Amitunduadzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m’makutu mwao mudzagontha.

17 Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m’ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.

18 Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.

19 Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m’nyanja yakuya.

20 Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/7-0919be8687bc3cbebb193b4e6b7c45ee.mp3?version_id=1068—