Categories
MATEYU

MATEYU 20

Fanizo la antchito olembedwa mwinamwina

1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m’munda wake wampesa.

2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.

3 Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo;

4 ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.

5 Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi.

6 Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?

7 Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.

8 Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.

9 Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi.

10 Ndipo m’mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.

11 Koma m’mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,

12 nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.

13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?

14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.

15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?

16 Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.

Funso la ana a Zebedeo

17 Ndipo pamene Yesu analikukwera kuYerusalemu, anatengaophunzirakhumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,

18 Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipoMwana wa Munthuadzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,

19 nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.

20 Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.

21 Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.

22 Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.

23 Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.

24 Ndipo m’mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.

25 Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.

26 Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

27 ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:

28 monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

Akhungu a ku Yeriko

29 Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye.

30 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m’mphepete mwa njira; m’mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide.

31 Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.

32 Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?

33 Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye.

34 Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/20-f62cb8509cd814b40546f113af6fba13.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 21

Yesu alowa mu Yerusalemu

1 Ndipo pamene iwo anayandikira kuYerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumizaophunziraawiri,

2 nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.

3 Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.

4 Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndimnenerikuti,

5 Tauzani mwana wamkazi waZiyoni,

Taona, mfumu yako idza kwa iwe,

wofatsa ndi wokwera pabulu,

ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.

6 Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza;

7 nabwera ndi bulu ndi mwana wake, naika pa iwo zovala zao, nakhala Iye pamenepo.

8 Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m’njiramo.

9 Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!

10 Ndipo m’mene adalowa mu Yerusalemu mzinda wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?

11 Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.

Yesu ayeretsa Kachisi kachiwiri

12 Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

13 nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

14 Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa.

15 Koma ansembe aakulu ndi alembi, m’mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,

16 nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

17 Ndipo Iye anawasiya, natuluka m’mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.

Mkuyu wofota

18 Ndipo mamawa, m’mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.

19 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.

20 Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?

21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa.

22 Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.

Ubatizo wa Yohane

23 Ndipo m’mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?

24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:

25 Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?

26 Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.

27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.

Fanizo la ana aamuna awiri

28 Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.

29 Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita.

30 Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite.

31 Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kutiamisonkhondi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.

32 Popeza Yohane anadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m’mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.

Fanizo la olima munda wampesa

33 Mveranifanizolina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.

35 Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.

36 Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo.

37 Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu.

38 Koma olimawo m’mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.

39 Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.

40 Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?

41 Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.

42 Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m’malembo,

Mwala umene anaukana omanga nyumba

womwewu unakhala mutu wa pangodya:

Ichi chinachokera kwa Ambuye,

ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu?

43 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.

44 Ndipo iye wakugwa pamwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.

45 Ndipo ansembe aakulu ndiAfarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo.

46 Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/21-357443a40e1bd9b8689f2630fef23159.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 22

Fanizo la ukwati

1 Ndipo Yesu anayankha, nalankhulanso kwa iwo m’mafanizo, nati,

2 Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati,

3 natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza.

4 Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng’ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati.

5 Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake:

6 ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.

7 Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.

8 Pomwepo inanena kwa akapolo ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenere.

9 Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo aliyense amene mukampeze, itanani kuukwatiku.

10 Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya.

11 Koma mfumuyo m’mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati;

12 nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau.

13 Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.

14 Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.

Za kupereka msonkho kwa Kaisara

15 PomwepoAfarisianamuka, nakhala upo wakumkola Iye m’kulankhula kwake.

16 Ndipo anatumiza kwa Iyeophunziraao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang’anira pa nkhope ya anthu.

17 Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwaKaisara, kapena iai?

18 Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?

19 Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka.

20 Ndipo Iye anati kwa iwo, Ncha yani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?

21 Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.

22 Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo.

Asaduki ndi kuuka kwa akufa

23 Tsiku lomwelo anadza kwa IyeAsaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,

24 nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.

25 Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake;

26 chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri.

27 Ndipo pomalizira anamwaliranso mkaziyo.

28 Chifukwa chake m’kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse anakhala naye.

29 Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.

30 Pakuti m’kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngatiangeloa Kumwamba.

31 Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,

32 Ine ndili Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki,

ndi Mulungu wa Yakobo?

Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.

33 Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi chiphunzitso chake.

Lamulo lalikulu

34 Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.

35 Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa malamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,

36 Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo?

37 Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

38 Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.

39 Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

40 Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.

Khristu ndiye Mwana wa Davide

41 Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,

42 nati, Muganiza bwanji zaKhristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.

43 Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena,

44 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,

ukhale padzanja lamanja langa,

kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.

45 Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.

46 Ndipo sanalimbike mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/22-03aa0d45a9b679125d5a67f52b1fb712.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 23

Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi

1 Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndiophunziraake,

2 nanena, Alembi ndiAfarisiakhala pa mpando wa Mose;

3 chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.

4 Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.

5 Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,

6 nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m’masunagoge,

7 ndi kulonjeredwa m’misika, ndi kutchedwa ndi anthu,Rabi.

8 Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.

9 Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

10 Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu.

11 Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.

12 Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

13 Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.

15 Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m’mene akhala wotere, mumsandutsa mwana waGehenawoposa inu kawiri.

16 Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira.

17 Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?

18 Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira.

19 Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

20 Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake.

21 Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo.

22 Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.

23 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.

24 Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumezangamira.

25 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.

26 Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m’kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.

27 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m’katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.

28 Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m’kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.

29 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,

30 ndi kuti, Ife tikadakhala m’masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri.

31 Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.

32 Dzazani inu muyeso wa makolo anu.

33 Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena?

34 Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;

35 kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.

36 Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.

37 Ha,Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafune ai!

38 Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.

39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena,

Wolemekezedwa Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/23-8066f2fba357947549ab68c0f85291c2.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 24

Yesu anenera zam’tsogolo. Chiyambi cha masautso

1 Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipoophunziraake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo.

2 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.

3 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?

4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang’anirani, asasokeretse inu munthu.

5 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndineKhristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.

6 Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.

7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.

8 Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.

9 Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.

10 Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.

11 Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri.

12 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.

13 Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.

14 Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.

Chisautso chachikulu

15 Chifukwa chake m’mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danielemneneri, chitaima m’malo oyera (iye amene awerenga m’kalata azindikire)

16 pomwepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri:

17 iye ali pamwamba pa tsindwi, asatsikire kunyamula za m’nyumba mwake;

18 ndi iye wa m’munda asabwere kutenga chofunda chake.

19 Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m’masiku awo!

20 Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena paSabata;

21 pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.

22 Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.

23 Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musamvomereze;

24 chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

25 Chifukwa chake akanena kwa inu,

26 Onani, Iye ali m’chipululu; musamukeko. Onani, ali m’zipinda; musavomereze.

27 Pakuti monga mphezi idzera kum’mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwaMwana wa Munthu.

28 Kumene kulikonse kuli mtembo, miimba idzasonkhanira konko.

Kudza kwake kwa Mwana wa Munthu

29 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:

30 ndipo pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

31 Ndipo Iye adzatumizaangeloake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.

32 Koma phunzirani ndi mkuyufanizolake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira;

33 chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.

34 Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.

35 Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.

Awachenjeza adikire

36 Koma za tsiku ili ndi nthawi yake saidziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.

37 Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.

38 Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa,

39 ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.

40 Pomwepo adzakhala awiri m’munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:

41 awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

42 Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.

43 Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.

44 Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m’mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.

Fanizo la akapolo awiri

45 Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?

46 Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.

47 Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.

48 Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa;

49 nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;

50 mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,

51 nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/24-40e421c79f64c6db17626109d9a91d53.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 25

Fanizo la anamwali asanu ochenjera ndi asanu opusa

1 Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.

2 Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera.

3 Pakuti opusawo, m’mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta;

4 koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.

5 Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.

6 Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye.

7 Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao.

8 Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima.

9 Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.

10 Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.

11 Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, mbuye, mutitsegulire ife.

12 Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.

13 Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.

Fanizo la ndalama za matalente

14 Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.

15 Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.

16 Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.

17 Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri.

18 Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake.

19 Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.

20 Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu.

21 Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.

22 Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri.

23 Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.

24 Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze;

25 ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo.

26 Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze;

27 chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake.

28 Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.

29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.

30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Moyo wosatha ndi kulanga kosatha

31 Koma pameneMwana wa Munthuadzadza mu ulemerero wake, ndiangeloonse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:

32 ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;

33 nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.

34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:

35 pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;

36 wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.

37 Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?

38 Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani?

39 Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?

40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine.

41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:

42 pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatse Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetse Ine:

43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandire Ine; wamaliseche ndipo simunandiveke Ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadze kundiona Ine.

44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?

45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang’onong’ono, munalibe kundichitira ichi Ine.

46 Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/25-07908513c1ca256cdd1c96486b4e26f5.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 26

Akulu a Ayuda apangana amgwire Yesu

1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwaophunziraake,

2 Mudziwa kuti akapita masiku awiri,Paskaafika, ndipoMwana wa Munthuadzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.

3 Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;

4 nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe.

5 Koma ananena iwo, pa nthawi ya chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.

Yesu m’nyumba ya Simoni wakhate

6 Ndipo pamene Yesu anali mu Betaniya, m’nyumba ya Simoni wakhate,

7 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m’mene Iye analikukhala pachakudya.

8 Koma m’mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku?

9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi.

10 Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino.

11 Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

12 Pakuti mkaziyo, m’mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga.

13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m’dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.

Mphotho ya kumpereka Yesu

14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,

15 nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasilivamakumi atatu.

16 Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.

Paska wotsiriza

17 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye?

18 Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.

19 Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska.

20 Ndipo pakufika madzulo, Iye analinkukhala pachakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;

21 ndipo m’mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22 Ndipo iwo anagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye mmodzimmodzi, Kodi ndine, Ambuye?

23 Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m’mbale, yemweyu adzandipereka Ine.

24 Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

25 Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine,Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.

Mgonero wa Ambuye

26 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m’mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa.

27 Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse,

28 pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.

29 Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.

30 Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.

Yesu achenjeza Petro

31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,

Ndidzakantha mbusa,

ndipo zidzabalalika

nkhosa za gulu.

32 Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

33 Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.

34 Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.

35 Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.

Yesu mu Getsemani

36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.

37 Ndipo anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru.

38 Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.

39 Ndipo anamuka patsogolo pang’ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.

40 Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m’tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simungathe kuchezera ndi Ine mphindi imodzi?

41 Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.

42 Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.

43 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m’tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.

44 Ndipo anawasiyanso, napemphera kachitatu, nateronso mau omwewo.

45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m’manja a ochimwa.

46 Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.

Amgwira Yesu

47 Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.

48 Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.

49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.

50 Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.

51 Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.

52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.

53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe aangelooposa khumi ndi awiri?

54 Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?

55 Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.

56 Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.

Yesu kubwalo la akulu a Ayuda

57 Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe.

58 Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro.

59 Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;

60 koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri,

61 nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu.

62 Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe?

63 Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiweKhristu, Mwana wa Mulungu.

64 Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.

65 Pomwepo mkulu wa ansembe anang’amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;

66 muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha.

67 Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu,

68 nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?

Petro akana Yesu

69 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.

70 Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa.

71 Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.

72 Ndipo anakananso ndi chilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo.

73 Ndipo popita nthawi yaing’ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.

74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.

75 Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/26-c3f0823e2303af0b9882362048008b5e.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 27

Yudasi adzipachika yekha

1 Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;

2 ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.

3 Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasilivamakumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu,

4 nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.

5 Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.

6 Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m’chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.

7 Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo.

8 Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino.

9 Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiyamneneri, ndi kuti,

Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu,

mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake,

amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;

10 ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya,

monga anandilamulira ine Ambuye.

Yesu kwa Pilato

11 Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.

12 Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu.

13 Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?

14 Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.

15 Ndipo pa chikondwerero kazembe adazolowera kumasulira anthu mmodzi wandende, amene iwo anafuna.

16 Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lake Barabasi.

17 Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwaKhristu?

18 Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.

19 Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m’kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.

20 Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu.

21 Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Barabasi.

22 Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.

23 Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda.

24 Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.

25 Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.

26 Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.

27 Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.

28 Ndipo anavula malaya ake, namveka malaya ofiira achifumu.

29 Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m’dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!

30 Namthira malovu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

31 Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda.

Ampachika Yesu

32 Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.

33 Ndipo pamene anadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, Malo a Bade,

34 anamwetsa Iye vinyo wosakaniza ndi ndulu; ndipo Iye, m’mene analawa, sanafune kumwa.

35 Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:

36 nakhala iwo pansi, namdikira kumeneko.

37 Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.

38 Pamenepo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, mmodzi kudzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.

39 Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,

40 nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.

41 Chomwechonso ansembe aakulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe, nati,

42 Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.

43 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.

44 Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi.

45 Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.

46 Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena,Eli, Eli, lama sabakitani?ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

47 Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya.

48 Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye.

49 Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.

50 Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau aakulu, anapereka mzimu wake.

51 Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang’ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang’ambika;

52 ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;

53 ndipo anatuluka m’manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m’mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.

54 Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.

55 Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang’anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye;

56 mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.

Amuika Yesu kumanda

57 Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzirawa Yesu;

58 yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.

59 Ndipo Yosefe anatenga mtembo, naukulunga m’nsalu yabafuta yoyeretsa,

60 nauika m’manda ake atsopano, osemedwa m’mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.

61 Ndipo Maria wa Magadala anali pamenepo, ndi Maria winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawo.

62 Ndipo m’mawa mwake, ndilo tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndiAfarisianasonkhana kwa Pilato,

63 nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.

64 Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapenaophunziraake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho.

65 Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa.

66 Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/27-22074afdf55f92e99978acaeae04aa61.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 28

Yesu auka kwa akufa

1 Ndipo popita tsiku laSabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda.

2 Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakutimngelowa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.

3 Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;

4 ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.

5 Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa.

6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m’mene anagonamo Ambuye.

7 Ndipo pitani msanga, muuzeophunziraake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.

8 Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.

9 Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.

10 Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.

Mau omveka mwa Ayuda

11 Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.

12 Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri,

13 nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m’mene ife tinali m’tulo.

14 Ndipo ngati ichi chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.

15 Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

Yesu aoneka mu Galileya

16 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.

17 Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.

18 Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.

19 Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

20 ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/28-cc01068682d7a153971601df37171ede.mp3?version_id=1068—