Categories
MATEYU

MATEYU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Mateyu

limafotokoza za uthenga wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, amene kudzera mwa iye Mulungu anakwaniritsa malonjezano ake amene adanena kwa anthu ake mu Chipangano Chakale. Uthenga Wabwinowu si wa mtundu wa Ayuda okha ai, umene Yesu anabadwira ndi kukhala pakati pao, koma ndi wa dziko lonse.

Buku la

Mateyu

ndi lolembedwa mwadongosolo. Likuyamba ndi kubadwa kwa Yesu, kenaka ndi kulongosola za ubatizo ndi mayesero ake, komanso ndikudzanena za utumiki wake wolalikira, kuphunzitsa ndi kuchiritsa m’dera la Galileya. Zitatha izi, Uthengawu ukunena za ulendo wa Yesu kuchoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu ndiponso zochitika mu sabata yomaliza ya utumiki wa Yesu, ndi kudzatsendera ndi kupachikidwa kwake pamtanda komanso kuukitsidwa kwake.

Bukuli likumuonetsa Yesu ngati Mphunzitsi wamkulu, amene ali ndi mphamvu zomasulira Malamulo a Mulungu ngati mwini wake, komanso amene amaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Zambiri mwa ziphunzitso zake zimagawidwa m’magulu asanu: Choyamba ndi chiphunzitso cha paphiri, chimene chikunena za khalidwe labwino, maudindo, cholowa ndi matsiriziro ake a mzika za Ufumu wa Kumwamba (mutu 5 mpaka 7); Chachiwiri ndi malangizo kwa ophunzira ake 12 pa za utumiki wao (mutu 10); Chachitatu ndi mafanizo a Ufumu wa Kumwamba (mutu 13); Chachinai ndi chiphunzitso kuti kutsata Yesu kumatanthauza chiyani (mutu 18) ndipo chachisanu ndi chiphunzitso cha chimaliziro cha nthawi ino komanso kubweranso kwa Ufumu wa Kumwamba (mutu 24 mpaka 25).

Za mkatimu

Kubadwa kwa Yesu Khristu ndi mbiri ya makolo ake

1.1—2.23

Utumiki wa Yohane Mbatizi

3.1-12

Yesu abatizidwa nayesedwa

3.13—4.11

Utumiki wa Yesu ku Galileya

4.12—18.35

Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu

19.1—20.34

Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira

1.1—27.66

Ambuye auka kwa akufa naonekera kwa anthu

28.1-20

Categories
MATEYU

MATEYU 1

Makolo a Yesu Khristu monga mwa thupi

1 Buku la kubadwa kwa YesuKhristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

2 Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;

3 ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;

4 ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni;

5 ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;

6 ndi Yese anabala Davide mfumuyo.

Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;

7 ndi Solomoni anabala Rehobowamu; ndi Rehobowamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;

8 ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;

9 ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;

10 ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;

11 ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni.

12 Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele;

13 ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;

14 ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi;

15 ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;

16 ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye.

17 Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18 Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

19 Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m’mtima kumleka iye m’tseri.

20 Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani,mngelowa Ambuye anaonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.

21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.

22 Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwamneneri, ndi kuti,

23 Onani namwali adzaima,

nadzabala mwana wamwamuna,

ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele.

Ndilo losandulika, Mulungu nafe.

24 Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;

25 ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/1-e89841c80421bb3611a8c1a8a2be86f8.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 2

Anzeru a kum’mawa

1 Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m’masiku aHerodemfumu, onani, Anzeru a kum’mawa anafika kuYerusalemu,

2 nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

3 Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.

4 Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kutiKhristuyo?

5 Ndipo anamuuza iye, Mu Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndimneneri, kuti,

6 Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya,

sukhala konse wamng’onong’ono mwa akulu a Yudeya.

Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe,

amene adzaweta anthu anga Aisraele.

7 Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m’tseri, nafunsitsa iwo nthawi yake idaoneka nyenyeziyo.

8 Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.

9 Ndipo iwo, m’mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum’mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza nkuima pamwamba pomwe panali kamwanako.

10 Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu.

11 Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndilubanindimure.

12 Ndipo iwo, pochenjezedwa m’kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao panjira ina.

Athawira ku Ejipito

13 Ndipo pamene iwo anachoka, onani,mngelowa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m’kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.

14 Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito;

15 nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti,

Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.

Aphedwa ana mu Betelehemu

16 Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m’midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating’ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.

17 Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,

18 Mau anamveka mu Rama,

maliro ndi kuchema kwambiri;

Rakele wolira ana ake,

wosafuna kusangalatsidwa,

chifukwa palibe iwo.

Abwera kuchokera ku Ejipito

19 Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m’kulota kwa Yosefe mu Ejipito,

20 nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako.

21 Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m’dziko la Israele.

22 Koma pakumva iye kutiArkelaoanali mfumu ya Yudeya m’malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m’kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,

23 nadza nakhazikika m’mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/2-b5132ed34898587b8f1d1f99f947b589.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 3

Yohane Mbatizi

1 Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m’chipululu cha Yudeya,

2 nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

3 Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesayamneneri, kuti,

Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

4 Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.

5 Pamenepo panamtulukira iye a kuYerusalemu, ndi Yudeya yense, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani;

6 nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.

7 Ndipo iye pakuona ambiri aAfarisindi aAsadukiakudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8 Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:

9 ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.

10 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.

11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

12 chouluzira chake chili m’dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m’nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.

Abatizidwa Yesu

13 Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.

14 Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?

15 Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.

16 Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;

17 ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/3-bc833b10ac131099146792f8c1078711.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 4

Yesu ayesedwa m’chipululu

1 Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.

2 Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.

3 Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.

4 Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,

Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha,

koma ndi mau onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.

5 Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,

6 nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,

Adzalamulaangeloake za iwe,

ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe,

ungagunde konse phazi lako pamwala.

7 Yesu ananena naye,

Ndiponso kwalembedwa,

Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

8 Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;

9 nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.

10 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, ChokaSatana, pakuti kwalembedwa,

Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,

ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.

11 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.

Yesu mu Galileya. Ophunzira oyamba

12 Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;

13 ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m’malire a Zebuloni ndi Nafutali:

14 kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesayamneneri, kuti,

15 Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,

njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani,

Galileya wa anthu akunja,

16 anthu akukhala mumdima

adaona kuwala kwakukulu,

ndi kwa iwo okhala m’malo a mthunzi wa imfa,

kuwala kunatulukira iwo.

17 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

18 Ndipo pamene Yesu analikuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m’nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.

19 Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

20 Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.

21 Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m’ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.

22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.

Yesu aphunzitsa, nalalika, nachiritsa

23 Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m’masunagogemwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.

24 Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.

25 Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi kuYerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/4-7eb8ec56f14f23a9494a1c6e35ca3ddc.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 5

Chiphunzitso cha paphiri. Madalitso

1 Ndipo m’mene Iye anaona makamu, anakwera m’phiri; ndipo m’mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iyeophunziraake;

2 ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:

3 Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

4 Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.

5 Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.

6 Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.

7 Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.

8 Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.

9 Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

10 Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

11 Odala muli inu m’mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.

12 Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Ophunzira ake ali mchere wa dziko ndi kuunika kwa dziko

13 Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.

14 Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.

15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m’mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m’nyumbamo.

16 Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Makwaniridwe a Malamulo ndi Aneneri

17 Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa.

18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.

19 Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang’onong’ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng’onong’ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba.

20 Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndiAfarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

21 Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:

22 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamulaGehenawamoto.

23 Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,

24 usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.

25 Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m’nyumba yandende.

26 Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko.

27 Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo;

28 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

29 Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena.

30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.

31 Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye kalata yachilekaniro:

32 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.

33 Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:

34 koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu;

35 kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchulaYerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu.

36 Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbuu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.

37 Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.

38 Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:

39 koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.

40 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.

41 Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.

42 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

43 Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:

44 koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;

45 kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.

46 Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhaleamisonkhosachita chomwecho?

47 Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho?

48 Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/5-da40326507f0c0a89ed9a4b974295f61.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 6

Za zopereka zachifundo; za kupemphera; za kudzikana kudya

1 Yang’anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.

2 Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m’masunagoge, ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

3 Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja;

4 kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam’tseri; ndipo Atate wako wakuona m’tseri adzakubwezera iwe.

5 Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m’tseri, ndipo Atate wako wakuona m’tseri adzakubwezera iwe.

7 Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwao.

8 Chifukwa chake inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.

9 Chifukwa chake pempherani inu chomwechi:

Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.

11 Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.

12 Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.

13 Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.

15 Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

16 Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

17 Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:

18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m’tseri: ndipo Atate wako wakuona m’tseri adzakubwezera iwe.

Za chuma cha mu Mwamba, diso langwiro, ambuye awiri, malabadiro a moyo uno

19 Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:

20 koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;

21 pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

22 Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa.

23 Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu!

24 Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

25 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?

26 Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

27 Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?

28 Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa akuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota:

29 koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa.

30 Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono?

31 Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani?

32 Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.

33 Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

34 Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/6-6c3f19d398acf997e34c479328f4b83d.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 7

Za kuweruza mnzake, kulimbika m’kupemphera, zipata ziwiri, aneneri onyenga, kumva ndi kuchita

1 Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.

2 Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

3 Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwe mwini suuganizira?

4 Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m’diso lakoli.

5 Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.

6 Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang’ambe inu.

Pemphani, Funani, Gogodani

7 Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;

8 pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.

9 Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala?

10 Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi?

11 Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?

12 Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Chipata chopapatiza

13 Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.

14 Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.

Za aneneri onyenga

15 Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwao ali mimbulu yolusa.

16 Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?

17 Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.

18 Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.

19 Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.

20 Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

21 Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.

22 Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?

23 Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.

Za anthu awiri omanga nyumba

24 Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;

25 ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.

26 Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga;

27 ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.

28 Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:

29 pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/7-25923732c7dd64a4f36550a597ac6763.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 8

Yesu achiritsa wakhate

1 Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu.

2 Ndipo onani, wakhateanadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.

3 Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.

4 Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.

Kenturiyo wa ku Kapernao

5 Ndipo m’mene Iye analowa mu Kapernao anadza kwa Iyekenturiyo, nampemba Iye,

6 nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m’nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa.

7 Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye.

8 Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.

9 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.

10 Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.

11 Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum’mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;

12 koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

13 Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.

Mpongozi wa Petro

14 Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.

15 Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.

16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;

17 kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesayamneneri, kuti,

Iye yekha anatenga zofooka zathu,

nanyamula nthenda zathu.

Matsatidwe ake a Yesu

18 Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamuliraophunziraamuke kutsidya lina.

19 Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako.

20 Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zao, komaMwana wa Munthualibe potsamira mutu wake.

21 Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine ndiyambe ndamuka kuika maliro a atate wanga.

22 Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.

Yesu aletsa namondwe

23 Ndipo pamene Iye atalowa m’ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye.

24 Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m’tulo.

25 Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika.

26 Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang’ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.

27 Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Ogwidwa ndi ziwanda a ku Gadara

28 Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu panjira imeneyo.

29 Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?

30 Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya.

31 Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m’gulu la nkhumbazo.

32 Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m’nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m’nyanjamo, ndipo linafa m’madzi.

33 Koma akuziweta anathawa, namuka kumzinda, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja.

34 Ndipo onani, mzinda wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m’mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m’malire ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/8-a5ffb0a35c1132199afbfc101155b8e0.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 9

Munthu wamanjenje wa ku Kapernao

1 Ndipo Iye analowa m’ngalawa, naoloka, nadza kumzinda kwao.

2 Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.

3 Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano.

4 Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m’mitima yanu?

5 Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?

6 Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvuMwana wa Munthupansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.

7 Ndipo ananyamuka, napita kunyumba kwake.

8 Ndipo m’mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.

Yesu aitana Mateyu

9 Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.

10 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m’nyumba, onani,amisonkhondi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndiophunziraake.

11 NdipoAfarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?

12 Ndipo m’mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing’anga ai, koma odwala.

13 Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.

Za kusala kudya

14 Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala?

15 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.

16 Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka kuchofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu.

17 Kapena samathira vinyo watsopano m’matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m’matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.

Mwana wamkazi wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu

18 M’mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.

19 Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe.

20 Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;

21 pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira.

22 Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

23 Ndipo Yesu polowa m’nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,

24 ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m’tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.

25 Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka.

26 Ndipo mbiri yake imene inabuka m’dziko lonse limenelo.

Yesu achiritsa akhungu awiri ndi wosalankhula

27 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.

28 Ndipo m’mene Iye analowa m’nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.

29 Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu.

30 Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang’anirani, asadziwe munthu aliyense.

31 Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m’dziko lonselo.

32 Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda.

33 Ndipo m’mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.

34 Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.

Zotuta ndi antchito

35 Ndipo Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagogemwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

36 Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.

37 Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka.

38 Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/9-eded64c7d01e63afbd32280de03dbc39.mp3?version_id=1068—