Categories
MASALIMO

MASALIMO 80

Apempha Mulungu alanditse anthu ake m’chisautso chao

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Syosyanimu; lochita mboni. Salimo la Asafu.

1 Mbusa wa Israele, tcherani khutu;

inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa;

inu wokhala paakerubi, walitsani.

2 Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase,

ndipo mutidzere kutipulumutsa.

3 Mutibweze, Mulungu;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

4 Yehova, Mulungu wa makamu,

mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?

5 Munawadyetsa mkate wa misozi,

ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

6 Mutiika kuti atilimbirane anzathu;

ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha.

7 Mulungu wa makamu, mutibweze;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

8 Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito,

munapirikitsaamitundundi kuuoka uwu.

9 Mudasoseratu pookapo,

idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.

10 Mthunzi wake unaphimba mapiri,

ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu.

11 Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja,

ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje.

12 Munapasuliranji maphambo ake,

kotero kuti onse akupita m’njira atcherako?

13 Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba,

ndi nyama za kuchidikha ziudya.

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu;

suzumirani muli m’mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

15 ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka,

ndi mphanda munadzilimbikitsira.

16 Unapserera ndi moto, unadulidwa;

aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu;

pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

18 Potero sitidzabwerera m’mbuyo kukusiyani;

titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/80-f7f6ebf5a67b2478f0a50131ab76fbd1.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 81

Mulungu atonza Aisraele pa kusamvera kwao

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gititi. Salimo la Asafu.

1 Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu;

fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo.

2 Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka,

zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.

3 Ombani lipenga, pokhala mwezi,

utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.

4 Pakuti ichi ndi cholemba cha kwa Israele,

chiweruzo cha Mulungu wa Yakobo.

5 Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe,

pakutuluka iye kudziko la Ejipito.

Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

6 Ndinamchotsera katundu paphewa pake,

manja ake anamasuka ku chotengera.

7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;

ndinakuvomereza mobisalika m’bingu;

ndinakuyesa kumadzi a Meriba.

8 Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni;

Israele, ukadzandimvera!

9 Kwanu kusakhale mulungu wofuma kwina;

nusagwadire mulungu wachilendo.

10 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza

kukuchotsa kudziko la Ejipito;

yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.

11 Koma anthu anga sanamvere mau anga;

ndipo Israele sanandivomere.

12 Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,

ayende monga mwa uphungu waowao.

13 Ha! Akadandimvera anthu anga,

akadayenda m’njira zanga Israele!

14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga,

ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga,

koma nyengo yao ikadakhala yosatha.

16 Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa,

ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m’thanthwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/81-7a6d9c36607a2edf7841f2afaaa781b5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 82

Oweruza aweruza bwino

Salimo la Asafu.

1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,

aweruza pakati pa milungu.

2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,

ndi kusamalira nkhope ya oipa?

3 Weruzani osauka ndi amasiye;

weruzani molungama ozunzika ndi osowa.

4 Pulumutsani osauka ndi aumphawi;

alanditseni m’dzanja la oipa.

5 Sadziwa, ndipo sazindikira;

amayendayenda mumdima;

maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,

ndi ana a Wam’mwambamwamba nonsenu.

7 Komatu mudzafa monga anthu,

ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.

8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;

pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/82-51f5963a0b1ec07d9942f2c0062d9534.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 83

Amitundu apangana kuononga Aisraele. Apempha Mulungu awalanditse

Nyimbo. Salimo la Asafu.

1 Mulungu musakhale chete;

musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.

2 Pakuti taonani, adani anu apokosera,

ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.

3 Apangana mochenjerera pa anthu anu,

nakhalira upo pa obisika anu.

4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;

ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.

5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;

anachitachipanganocha pa Inu.

6 Mahema a Edomu ndi a Aismaele;

Mowabu ndi Ahagiri;

7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleke;

Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.

8 Asiriya anaphatikana nao;

anakhala dzanja la ana a Loti.

9 Muwachitire monga munachitira Midiyani;

ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,

10 amene anaonongeka ku Endori;

anakhala ngati ndowe ya kumunda.

11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;

mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,

12 amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.

13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;

ngati ziputu zomka ndi mphepo.

14 Monga moto upsereza nkhalango,

ndi monga lawi liyatsa mapiri.

15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,

nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.

16 Achititseni manyazi pankhope pao;

kuti afune dzina lanu, Yehova.

17 Achite manyazi, naopsedwe kosatha;

ndipo asokonezeke, naonongeke.

18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,

ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/83-d2cdb0eba6aa3310d96e8863b2c3cdf6.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 84

Okhala m’nyumba ya Yehova ndiwo amwai

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi; Salimo la ana a Kora.

1 Pokhala Inu mpotikonda ndithu,

Yehova wa makamu!

2 Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;

mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.

3 Mbawanso inapeza nyumba,

ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake,

pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,

mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

4 Odala iwo akugonera m’nyumba mwanu;

akulemekezani chilemekezere.

5 Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu;

mumtima mwake muli makwalala a kuZiyoni.

6 Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe;

inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso.

7 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,

aoneka pamaso pa Mulungu muZiyoni.

8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa.

Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.

9 Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu;

ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.

10 Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma

koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.

Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga,

kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.

11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa;

Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero;

sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

12 Yehova wa makamu,

wodala munthu wakukhulupirira Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/84-e7d9f9ab67bd1354cd497363362f5251.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 85

Akumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la ana a Kora.

1 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;

munabweza ukapolo wa Yakobo.

2 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,

munafotsera zolakwa zao zonse.

3 Munabweza kuzaza kwanu konse;

munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.

4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,

nimuletse udani wanu wa pa ife.

5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?

Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?

6 Kodi simudzatipatsanso moyo,

kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?

7 Tionetseni chifundo chanu, Yehova,

tipatseni chipulumutso chanu.

8 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;

pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,

ndi okondedwa ake;

koma asabwererenso kuchita zopusa.

9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi

ndi iwo akumuopa Iye;

kuti m’dziko mwathu mukhale ulemu.

10 Chifundo ndi choonadi zakomanizana;

chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.

11 Choonadi chiphukira m’dziko;

ndi chilungamo chasuzumira chili m’mwamba.

12 Inde Yehova adzapereka zokoma;

ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.

13 Chilungamo chidzamtsogolera;

ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/85-c4c844fc1b8f723f7281b828236e7378.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 86

Davide apempha Mulungu kolimba amlanditse

Pemphero la Davide.

1 Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;

pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.

2 Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;

Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.

3 Mundichitire chifundo, Ambuye;

pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.

4 Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;

pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.

5 Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,

ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.

6 Tcherani khutu pemphero langa, Yehova;

nimumvere mau a kupemba kwanga.

7 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;

popeza mudzandivomereza.

8 Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;

ndipo palibe ntchito zonga zanu.

9 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye;

nadzalemekeza dzina lanu.

10 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa;

Inu ndinu Mulungu, nokhanu.

11 Mundionetse njira yanu, Yehova;

ndidzayenda m’choonadi chanu,

muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

12 Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga,

ndi mtima wanga wonse;

ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.

13 Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu;

ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

14 Mulungu, odzikuza andiukira,

ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,

ndipo sanaike Inu pamaso pao.

15 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo,

wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.

16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo;

mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,

ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17 Mundichitire chizindikiro choti chabwino;

kuti ondida achione, nachite manyazi,

popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/86-c3329e477997094a5e689f1421a56f9d.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 87

Yehova akonda Ziyoni

Salimo la ana a Kora. Nyimbo.

1 Maziko ake ali m’mapiri oyera.

2 Yehova akonda zipata zaZiyoni

koposa zokhalamo zonse za Yakobo.

3 Mzinda wa Mulungu, inu,

akunenerani zakukulemekezani.

4 Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine;

taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi;

uyu anabadwa komweko.

5 Ndipo adzanena za Ziyoni,

uyu ndi uyo anabadwa m’mwemo;

ndipo Wam’mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.

6 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu,

uyu anabadwa komweko.

7 Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati,

akasupe anga onse ali mwa inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/87-8028e33da24193bb61a5791c0db3b52c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 88

Wa Salimo atchula masautso ake, napempha Mulungu amdalitse kuimfa

Nyimbo, Salimo la ana a Kora. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Mahalati Leanoti. Chilangizo cha Hemani Mwezara.

1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,

ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.

2 Pemphero langa lidze pamaso panu;

munditcherere khutu kukuwa kwanga.

3 Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto,

ndi moyo wanga wayandikira kumanda.

4 Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;

ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.

5 Wotayika pakati pa akufa,

ngati ophedwa akugona m’manda,

amene simuwakumbukiranso;

ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

6 Munandiika kunsi kwa dzenje,

kuli mdima, kozama.

7 Mkwiyo wanu utsamira pa ine,

ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.

8 Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;

munandiika ndiwakhalire chonyansa.

Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.

9 Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga:

Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;

nditambalitsira manja anga kwa Inu.

10 Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa?

Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?

11 Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi,

chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?

12 Zodabwitsa zanu zidzadziwika mumdima kodi,

ndi chilungamo chanu m’dziko la chiiwaliko?

13 Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova,

ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.

14 Yehova mutayiranji moyo wanga?

Ndi kundibisira nkhope yanu?

15 Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;

posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.

16 Kuzaza kwanu kwandimiza;

zoopsa zanu zinandiononga.

17 Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;

zinandizinga pamodzi.

18 Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,

odziwana nane akhala kumdima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/88-c65f8280cc82f24316af7a4b441cf06d.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 89

Pangano la Mulungu ndi Davide Mulungu adzapulumutsa anthu ake

Chilangizo cha Etani Mwezara.

1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse,

pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu

ku mibadwomibadwo.

2 Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka;

mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.

3 Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga,

ndinalumbirira Davide mtumiki wanga.

4 Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse,

ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.

5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova;

chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.

6 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?

Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?

7 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima,

ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.

8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?

Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.

9 Inu ndinu wakuchita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;

pakuuka mafunde ake muwachititsa bata.

10 Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;

munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;

munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.

12 Munalenga kumpoto ndi kumwera;

Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m’dzina lanu.

13 Muli nao mkono wanu wolimba;

m’dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.

14 Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu;

chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.

15 Odala anthu odziwa liu la lipenga;

ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

16 Akondwera m’dzina lanu tsiku lonse;

ndipo akwezeka m’chilungamo chanu.

17 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;

ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.

18 Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova;

ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.

19 Pamenepo munalankhula m’masomphenya ndi okondedwa anu,

ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona;

ndakweza wina wosankhika mwa anthu.

20 Ndapeza Davide mtumiki wanga;

ndamdzoza mafuta anga oyera.

21 Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;

inde mkono wanga udzalimbitsa.

22 Mdani sadzamuumira mtima;

ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.

23 Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake;

ndidzapandanso odana naye.

24 Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa

zidzakhala naye;

ndipo nyanga yake idzakwezeka m’dzina langa.

25 Ndipo ndidzaika dzanja lake panyanja,

ndi dzanja lamanja lake pamitsinje.

26 Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,

Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.

27 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,

womveka wa mafumu a padziko lapansi.

28 Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse,

ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.

29 Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire,

ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba.

30 Ana ake akataya chilamulo changa,

osayenda m’maweruzo anga,

31 nakaipsa malembo anga;

osasunga malamulo anga.

32 Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,

ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

33 Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse,

ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.

34 Sindidzaipsa chipangano changa,

kapena kusintha mau otuluka m’milomo yanga.

35 Ndinalumbira kamodzi m’chiyero changa;

sindidzanamizira Davide.

36 Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse,

ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.

37 Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse,

ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.

38 Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,

munakwiya naye wodzozedwa wanu.

39 Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu;

munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.

40 Munapasula makoma ake onse;

munagumula malinga ake.

41 Onse opita panjirapa amfunkhira,

akhala chotonza cha anansi ake.

42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;

munakondweretsa adani ake onse.

43 Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake,

osamuimika kunkhondo.

44 Munaleketsa kuwala kwake,

ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake.

45 Munafupikitsa masiku a mnyamata wake;

munamkuta nao manyazi.

46 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;

ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?

47 Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi;

munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?

48 Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?

Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?

49 Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye,

munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?

50 Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu;

ndichisenza m’chifuwa mwanga

chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu.

51 Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho;

chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.

52 Wodalitsika Yehova kunthawi yonse.

Amen ndi Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/89-440e7f8cad219e8890e8f4ad568878c7.mp3?version_id=1068—