Categories
MASALIMO

MASALIMO 60

Madandaulo ndi pempho la Davide

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri.

1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;

mwakwiya; tibwezereni.

2 Mwagwedeza dziko, mwaling’amba.

Konzani ming’alu yake; pakuti ligwedezeka.

3 Mwaonetsa anthu anu zowawa,

mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.

4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,

aikweze chifukwa cha choonadi.

5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,

pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.

6 Mulungu walankhula m’chiyero chake; ndidzakondwerera,

ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.

7 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;

ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga;

Yuda ndiye wolamulira wanga.

8 Mowabu ndiye mkhate wanga;

pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga.

Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.

9 Adzandifikitsa ndani m’mzinda wa m’linga?

Adzanditsogolera ndani ku Edomu?

10 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya?

Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.

11 Tithandizeni kunsautso;

kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.

12 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima,

ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/60-396c9720e403cdadaf93d7346d326fac.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 61

Poopsedwa Davide athamangira Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.

1 Imvani mfuu wanga, Mulungu;

mverani pemphero langa.

2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu,

pomizika mtima wanga.

Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m’kutalika kwake.

3 Pakuti munakhala pothawirapo panga;

nsanja yolimba pothawa mdani ine.

4 Ndidzagoneragonerabe m’chihema mwanu;

ndidzathawira mobisalamo m’mapiko anu.

5 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;

munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.

6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.

Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo.

7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;

mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.

8 Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse,

kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/61-1e56a0cd41ef1a4cbbcc64d8486c8292.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 62

Posautsidwa Davide athamangira Mulungu yekha

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Yedutuni. Salimo la Davide.

1 Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha;

chipulumutso changa chifuma kwa Iye.

2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;

msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

3 Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti,

kumupha iye, nonsenu,

monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?

4 Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake;

akondwera nao mabodza;

adalitsa ndi m’kamwa mwao,

koma atemberera mumtima.

5 Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha;

pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.

6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa,

msanje wanga, sindidzagwedezeka.

7 Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga.

Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.

8 Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu,

tsanulirani mitima yanu pamaso pake.

Mulungu ndiye pothawirapo ife.

9 Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza,

pakuwayesa apepuka;

onse pamodzi apepuka koposa mpweya.

10 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba;

chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

11 Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri,

kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu.

12 Chifundonso ndi chanu, Ambuye,

Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense

monga mwa ntchito yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/62-1668ff3568829050b8ae71291efba225.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 63

Mtima woliralira kuyanjana ndi Mulungu

Salimo la Davide; muja anakhala m’chipululu cha Yuda.

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga;

ndidzakufunani m’matanda kucha.

Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu,

thupi langa lilirira Inu,

m’dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,

monga ndinakuonani m’malo oyera.

3 Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake;

milomo yanga idzakulemekezani.

4 Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga;

ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;

ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani

ndi milomo yakufuula mokondwera.

6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,

ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;

ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8 Moyo wanga uumirira Inu.

Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,

adzalowa m’munsi mwake mwa dziko.

10 Adzawapereka kumphamvu ya lupanga;

iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

yense wakulumbirira iye adzatamandira;

pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/63-dd5022b579c322c447c9f170e2fa695e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 64

Davide apempha Mulungu amtchinjirize pa omlalira

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Imvani Mulungu, mau anga, m’kudandaula kwanga;

sungani moyo wanga angandiopse mdani.

2 Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa;

pa phokoso la ochita zopanda pake.

3 Amene anola lilime lao ngati lupanga,

napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;

4 kuponyera wangwiro mobisika:

Amponyera modzidzimutsa, osaopa.

5 Alimbikitsana m’chinthu choipa;

apangana za kutchera misampha mobisika;

akuti, Adzaiona ndani?

6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha;

chingakhale cha m’kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.

7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi;

adzalaswa modzidzimutsa.

8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;

onse akuwaona adzawathawa.

9 Ndipo anthu onse adzachita mantha;

nadzabukitsa chochita Mulungu,

nadzasamalira ntchito yake.

10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova,

nadzakhulupirira Iye;

ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/64-f8cb3fc909cb65eb3e048846840dd693.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 65

Davide alemekeza Mulungu pa madalitso ochuluka

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide. Nyimbo.

1 MuZiyoniakulemekezani Inu mwachete, Mulungu,

adzakuchitirani Inu chowindachi.

2 Wakumva pemphero Inu,

zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.

3 Mphulupulu zinandipambana;

koma mudzafafaniza zolakwa zathu.

4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,

akhale m’mabwalo anu.

Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu,

za m’malo oyera a Kachisi wanu.

5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m’chilungamo,

Mulungu wa chipulumutso chathu;

ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi,

ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.

6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;

pozingidwa nacho chilimbiko.

7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja,

kukuntha kwa mafunde ake,

ndi phokoso la mitundu ya anthu.

8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha

chifukwa cha zizindikiro zanu;

mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.

9 Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira,

mulilemeretsa kwambiri;

mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi,

muwameretsera tirigu m’mene munakonzera nthaka.

10 Mukhutitsa nthaka yake yolima;

mufafaniza nthumbira zake;

muiolowetsa ndi mvumbi;

mudalitsa mmera wake.

11 Muveka chakachi ndi ukoma wanu;

ndipo mabande anu akukha zakucha.

12 Akukha pa mabusa a m’chipululu;

ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.

13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;

ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;

zifuula mokondwera, inde ziimbira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/65-b7355099f446294b6dd7e354ffe4751b.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 66

Achenjeza onse alemekeze Mulungu pa ntchito zake zodabwitsa

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Nyimbo, Salimo.

1 Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.

2 Imbirani ulemerero wa dzina lake;

pomlemekeza mumchitire ulemerero.

3 Nenani kwa Mulungu, Ha,

ntchito zanu nzoopsa nanga!

Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.

4 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,

ndipo lidzakuimbirani;

ndzaimbira dzina lanu.

5 Idzani, muone ntchito za Mulungu;

zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.

6 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda.

Anaoloka mtsinje choponda pansi,

apo tinakondwera mwa Iye.

7 Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha;

maso ake ayang’aniraamitundu;

opikisana ndi Iye asadzikuze.

8 Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,

ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.

9 Iye amene asunga moyo wathu tingafe,

osalola phazi lathu literereke.

10 Pakuti munatiyesera, Mulungu,

munatiyenga monga ayengasiliva.

11 Munapita nafe kuukonde;

munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.

12 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;

tinapyola moto ndi madzi;

koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

13 Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,

ndidzakuchitirani zowinda zanga,

14 zimene inazitchula milomo yanga,

ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.

15 Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona,

pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa;

ndidzakonza ng’ombe pamodzi ndi mbuzi.

16 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,

ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.

17 Ndinamfuulira Iye pakamwa panga,

ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.

18 Ndikadasekera zopanda pake m’mtima mwanga,

Ambuye sakadamvera.

19 Koma Mulungu anamvadi;

anamvera mau a pemphero langa.

20 Wolemekezeka Mulungu,

amene sanandipatutsire ine pemphero langa,

kapena chifundo chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/66-cd2c9e7202df993c36a1484f8905c376.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 67

Amitundu alemekeze Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Neginoto. Salimo. Nyimbo.

1 Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,

atiwalitsire nkhope yake;

2 kuti njira yanu idziwike padziko lapansi,

chipulumutso chanu mwaamitunduonse.

3 Anthu akuyamikeni, Mulungu;

anthu onse akuyamikeni.

4 Anthu akondwere, nafuule mokondwera;

pakuti mudzaweruza anthu molunjika,

ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.

5 Anthu akuyamikeni, Mulungu;

anthu onse akuyamikeni.

6 Dziko lapansi lapereka zipatso zake,

Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.

7 Mulungu adzatidalitsa;

ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/67-029d8e9e029b86de068d98b51bdff7f7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 68

Mau akuyamikira Mulungu wa chipulumutso chonse

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo.

1 Auke Mulungu, abalalike adani ake;

iwonso akumuda athawe pamaso pake.

2 Muwachotse monga utsi uchotseka;

monga phula lisungunuka pamoto,

aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.

3 Koma olungama akondwere;

atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu;

ndipo asekere nacho chikondwerero.

4 Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake;

undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha;

dzina lake ndiye Yehova;

ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.

5 Mulungu, mokhala mwake moyera,

ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

6 Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha;

atulutsa am’ndende alemerere;

koma opikisana naye akhala m’dziko lopanda madzi.

7 Pakutuluka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu,

pakuyenda paja Inu m’chipululu.

8 Dziko lapansi linagwedezeka,

inde thambo linakha pamaso pa Mulungu;

Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu,

Mulungu wa Israele.

9 Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula,

munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.

10 Gulu lanu linakhala m’dziko muja.

Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.

11 Ambuye anapatsa mau,

akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.

12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa,

ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

13 Pogona inu m’makola a zoweta,

mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndisiliva,

ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.

14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m’dzikomo,

munayera ngati matalala mu Zalimoni.

15 Phiri la Basani ndilo phiri la Mulungu;

Phiri la Basani ndilo phiri la mitumitu.

16 Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu,

ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?

Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

17 Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri,

inde zikwi zowirikizawirikiza,

Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m’malo opatulika.

18 Munakwera kunka kumwamba,

munapita nao undende kuuyesa ndende;

munalandira zaufulu mwa anthu,

ngakhale mwa opikisana nanu,

kuti Yehova Mulungu akakhale nao.

19 Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu,

ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.

20 Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso;

ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.

21 Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake,

pakati pamutu pa iye woyendabe m’kutsutsika kwake.

22 Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basani,

ndidzawatenganso kozama kwa nyanja,

23 kuti uviike phazi lako m’mwazi,

kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.

24 Anapenya mayendedwe anu, Mulungu,

mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m’malo oyera.

25 Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m’mbuyo,

pakatipo anamwali oimba mangaka.

26 Lemekezani Mulungu m’misonkhano,

ndiye Yehova, inu a gwero la Israele.

27 Apo pali Benjamini wamng’ono, wakuwachita ufumu,

akulu a Yuda, ndi a upo wao,

akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.

28 Mulungu wako analamulira mphamvu yako,

Limbitsani, Mulungu, chimene munatichitira.

29 Chifukwa cha Kachisi wanu wa muYerusalemu

mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.

30 Dzudzulani chilombo cha m’bango,

khamu la mphongo ndi ng’ombe za anthu,

yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva;

anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

31 Akulu adzafumira ku Ejipito;

Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.

32 Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;

imbirani Ambuye zomlemekeza.

33 Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba,

oyambira kale lomwe;

taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.

34 Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;

ukulu wake uli pa Israele,

ndi mphamvu yake m’mitambo.

35 Inu Mulungu, ndinu woopsa m’malo oyera anu;

Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake

mphamvu ndi chilimbiko.

Alemekezeke Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/68-1abf2ff8650099a7f9c68dc73b8fe592.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 69

Davide adandaulira kwa Mulungu chifukwa cha zowawa azimva

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Pa Syosyanimu. Salimo la Davide.

1 Ndipulumutseni Mulungu;

pakuti madzi afikira moyo wanga.

2 Ndamira m’thope lozama, lopanda poponderapo;

ndalowa m’madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.

3 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum’mero kwauma gwaa!

M’maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

4 Ondida kopanda chifukwa achuluka

koposa tsitsi la pamutu panga;

ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu.

Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.

5 Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;

ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.

6 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye, Yehova wa makamu,

asachite manyazi chifukwa cha ine,

iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele,

asapepulidwe chifukwa cha ine.

7 Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu,

chimpepulo chakuta nkhope yanga.

8 Abale anga andiyesa mlendo,

ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9 Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya;

ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10 Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,

koma uku kunandikhalira chotonza.

11 Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli,

koma amandiphera mwambi.

12 Okhala pachipata akamba za ine;

ndipo oledzera andiimba.

13 Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu,

Yehova, m’nyengo yolandirika;

Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu,

mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.

14 Mundilanditse kuthope, ndisamiremo,

ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.

15 Chigumula chisandifotsere,

ndipo chakuya chisandimize;

ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.

16 Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma;

munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.

17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;

pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.

18 Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;

ndipulumutseni chifukwa cha adani anga.

19 Mudziwa chotonza changa, ndi manyazi anga,

ndi chimpepulo changa.

Akundisautsa ali pamaso panu.

20 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine;

ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe;

ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.

21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa;

nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.

22 Gome lao likhale msampha pamaso pao;

pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.

23 M’maso mwao mude, kuti asapenye;

ndipo munjenjemeretse m’chuuno mwao kosalekeza.

24 Muwatsanulire mkwiyo wanu,

ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.

25 Pokhala pao pakhale bwinja;

m’mahema mwao musakhale munthu.

26 Pakuti alondola amene Inu munampanda;

ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.

27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;

ndipo asafikire chilungamo chanu.

28 Afafanizidwe m’buku lamoyo,

ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29 Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;

chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.

30 Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira,

ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.

31 Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng’ombe,

inde mphongo za nyanga ndi ziboda.

32 Ofatsa anachiona, nakondwera,

ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.

33 Pakuti Yehova amvera aumphawi,

ndipo sapeputsa am’ndende ake.

34 Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,

nyanja ndi zonse zoyenda m’mwemo.

35 Pakuti Mulungu adzapulumutsaZiyoni,

nadzamanga mizinda ya Yuda;

ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.

36 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira;

ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m’mwemo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/69-f68152a569022f718108a6f7b543097b.mp3?version_id=1068—