Categories
MASALIMO

MASALIMO 40

Alemekeza chipulumutso cha Mulungu, alalikira poyera chilungamo cha Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;

ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

2 Ndipo anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko,

ndi m’thope la pachithaphwi;

nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

3 Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,

chilemekezo cha kwa Mulungu wanga;

ambiri adzachiona, nadzaopa,

ndipo adzakhulupirira Yehova.

4 Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;

wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.

5 Inu, Yehova, Mulungu wanga,

zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri,

ndipo zolingirira zanu za pa ife;

palibe wina wozifotokozera Inu;

ndikazisimba ndi kuzitchula,

zindichulukira kuziwerenga.

6 Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo;

mwanditsegula makutu.

Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.

7 Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;

m’buku mwalembedwa za Ine,

8 kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga;

ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.

9 Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu;

onani, sindidzaletsa milomo yanga,

mudziwa ndinu Yehova.

10 Chilungamo chanu sindinachibise m’kati mwamtima mwanga;

chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena;

chifundo chanu ndi choonadi chanu

sindinachibisire msonkhano waukulu.

11 Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu,

chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

Pemphero lopempha chithandizo

12 Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,

zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;

ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.

13 Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni;

fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14 Achite manyazi nadodome

iwo akulondola moyo wanga kuti auononge.

Abwerere m’mbuyo, nachite manyazi

iwo okondwera kundichitira choipa.

15 Apululuke, mobwezera manyazi ao

amene anena nane, Hede, hede.

16 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;

iwo akukonda chipulumutso chanu

asaleke kunena, Abuke Yehova.

17 Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;

koma Ambuye andikumbukira ine.

Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga,

musamachedwa, Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/40-d3f26f2ab09029c80757c98a1bc7ef02.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 41

Mulungu adalitsa wosamalira osauka. Adani ndi mabwenzi amchitira Davide zoipa, Mulungu amlanditse

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Wodala iye amene asamalira wosauka!

Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo,

ndipo adzadalitsika padziko lapansi,

ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.

3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;

podwala iye mukonza pogona pake.

4 Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova;

Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu.

5 Adani anga andinenera choipa, ndi kuti,

adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?

6 Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;

mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake,

akanka nayenda namakanena.

7 Onse akudana nane andinong’onezerana;

apangana chondiipsa ine.

8 Chamgwera chinthu choopsa, ati;

popeza ali gonire sadzaukanso.

9 Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira,

ndiye amene adadyako mkate wanga,

anandikwezera chidendene chake.

10 Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse,

kuti ndiwabwezere.

11 Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,

popeza mdani wanga sandiseka.

12 Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga,

ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.

13 Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele,

kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.

Amen, ndi Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/41-537b08f0cc93ae7eeaae58059123a735.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 42

Mtima wolira kuyanjana ndi Mulungu mu Kachisi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.

1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;

motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu,

la kwa Mulungu wamoyo.

Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?

3 Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa,

usana ndi usiku;

pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,

Mulungu wako ali kuti?

4 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m’kati mwa ine,

pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu,

ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu,

ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika,

ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso

chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

6 Mulungu wanga, moyo wanga

udziweramira m’kati mwanga;

chifukwa chake ndikumbukira Inu m’dziko la Yordani,

ndi mu Aheremoni, m’kaphiri ka Mizara.

7 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,

pa mkokomo wa matiti anu;

mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.

8 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake,

ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine.

Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.

9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa,

mwandiiwala chifukwa ninji?

Ndimayenderanji wakulira

chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?

10 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga;

pakunena ndine dzuwa lonse,

Mulungu wako ali kuti?

11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,

ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/42-ae42dc50afb061e3a3a74ad4c3630ce9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 43

Davide alira akhale ku Kachisi

1 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo.

Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?

Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?

3 Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere;

zindifikitse kuphiri lanu loyera,

kumene mukhala Inuko.

4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,

kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni,

ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,

ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/43-8197488d3ef56fba8d833b7567548e6e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 44

Anthu a Mulungu akumbuke zithandizo zakale popempha chipulumutso m’tsoka lao

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.

1 Mulungu, tidamva m’makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,

za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.

2 Inu munapirikitsaamitundundi dzanja lanu,

koma iwowa munawaoka;

munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.

3 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao,

ndipo mkono wao sunawapulumutse.

Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu,

ndi kuunika kwa nkhope yanu.

Popeza munakondwera nao,

4 Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu;

lamulirani chipulumutso cha Yakobo.

5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe,

m’dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

6 Pakuti uta wanga,

ndipo lupanga langa silingandipulumutse.

7 Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,

ndipo akudana nafe, mudawachititsa manyazi.

8 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,

ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.

9 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;

ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.

10 Mutibwereretsa kuthawa otisautsa,

ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.

11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;

ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.

12 Mugulitsa anthu anu kwachabe,

ndipo mtengo wake simupindula nao.

13 Mutisandutsa chotonza kwa anzathu,

ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.

14 Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,

ndi kuti anthu atipukusire mitu.

15 Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga,

ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.

16 Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano;

chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.

17 Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,

ndipo sitinachite monyenga m’pangano lanu.

18 Mtima wathu sunabwerere m’mbuyo,

ndipo m’mayendedwe athu sitinapatuke m’njira yanu;

19 mungakhale munatithyola mokhala zilombo,

ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.

20 Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,

ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;

21 Mulungu sakadasanthula ichi kodi?

Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.

22 Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse;

tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.

23 Galamukani, mugoneranji, Ambuye?

Ukani, musatitaye chitayire.

24 Mubisiranji nkhope yanu,

ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?

25 Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi,

pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.

26 Ukani, tithandizeni,

tiomboleni mwa chifundo chanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/44-de9af6db6f1f40d0e02f99000a4b2758.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 45

Nyimbo yoimbira ukwati wa mfumu

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi.

1 Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma.

Ndinena zopeka ine za mfumu,

lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.

2 Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu;

anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu,

chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.

3 Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu,

wamphamvu inu,

ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.

4 Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani,

kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo;

ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.

5 Mivi yanu njakuthwa;

mitundu ya anthu igwa pansi pa inu;

iwalasa mumtima adani a mfumu.

6 Mpando wachifumu wanu,

Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya.

Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.

7 Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa,

chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu

ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.

8 Zovala zanu zonse nzamure, ndi khonje, ndi kasiya;

m’zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu

mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.

9 Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu;

ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu

wovala golide wa ku Ofiri.

10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako;

uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

11 potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako,

pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.

12 Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso;

achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.

13 Mwana wamkazi wa mfumu

ngwa ulemerero wonse m’kati mwa nyumba,

zovala zake nza malukidwe agolide.

14 Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga,

anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.

15 Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera,

adzalowa m’nyumba ya mfumu.

16 M’malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,

udzawaika akhale mafumu m’dziko lonse lapansi.

17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m’mibadwomibadwo;

chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu

kunthawi za nthawi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/45-ceb1eb564497f56d68a77058a8f45072.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 46

Mulungu ndiye pothawirapo anthu ake

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Pa Alamot. Nyimbo.

1 Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,

thandizo lopezekeratu m’masautso.

2 Chifukwa chake sitidzachita mantha,

lingakhale lisandulika dziko lapansi,

angakhale mapiri asunthika, nakhala m’kati mwa nyanja.

3 Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu,

nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

4 Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu.

Malo oyera okhalamo Wam’mwambamwamba.

5 Mulungu ali m’kati mwake, sudzasunthika,

Mulungu adzauthandiza mbandakucha.

6 Amitunduanapokosera, maufumu anagwedezeka,

ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.

7 Yehova wa makamu ali ndi ife;

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

8 Idzani, penyani ntchito za Yehova,

amene achita zopululutsa padziko lapansi.

9 Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;

athyola uta, nadula nthungo;

atentha magaleta ndi moto.

10 Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu,

Ndidzabuka mwa amitundu,

ndidzabuka padziko lapansi.

11 Yehova wa makamu ali ndi ife,

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/46-bca78a4e765d1c318275c4da76140e29.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 47

Mau a kulemekeza Mulungu mwini dziko lonse lapansi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Ombani m’manja, mitundu yonse ya anthu;

fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.

2 Pakuti Yehova Wam’mwambamwamba ndiye woopsa;

ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.

3 Atigonjetsera anthu,

naikaamitundupansi pa mapazi athu.

4 Atisankhira cholowa chathu,

chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.

5 Mulungu wakwera ndi mfuu,

Yehova ndi liu la lipenga.

6 Imbirani Mulungu, imbirani;

imbirani mfumu yathu, imbirani.

7 Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi;

imbirani ndi chilangizo.

8 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu,

Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.

9 Akulu a anthu asonkhana

akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu,

pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;

akwezeka kwakukulu Iyeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/47-3f699d23b0b2fdb809c608e8b2a6d8f4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 48

Ukoma ndi ulemerero wa Ziyoni

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,

m’mzinda wa Mulungu wathu, m’phiri lake loyera.

2 Phiri laZiyoni, chikhalidwe chake nchokoma

kumbali zake za kumpoto,

ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi,

mzinda wa mfumu yaikulu.

3 Mulungu adziwika m’zinyumba zake ngati msanje.

4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,

anapitira pamodzi.

5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;

anaopsedwa, nathawako.

6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;

anamva chowawa, ngati wam’chikuta.

7 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum’mawa.

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya

m’mzinda wa Yehova wa makamu, m’mzinda wa Mulungu wathu,

Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

9 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu,

m’kati mwa Kachisi wanu.

10 Monga dzina lanu, Mulungu,

momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi;

m’dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.

11 Likondwere phiri la Ziyoni,

asekere ana aakazi a Yuda,

chifukwa cha maweruzo anu.

12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge,

werengani nsanja zake.

13 Penyetsetsani malinga ake,

yesetsani zinyumba zake;

kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m’mbuyo.

14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu

kunthawi za nthawi,

adzatitsogolera kufikira imfa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/48-ba5befffea5b0683b72b66ebb5cb961c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 49

Za pansi pano nza chabe

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Dzamveni kuno, anthu inu nonse;

tcherani khutu, inu nonse amakono,

2 awamba ndi omveka omwe,

achuma ndi aumphawi omwe.

3 Pakamwa panga padzanena zanzeru;

ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.

4 Ndidzatchera khutu kufanizo,

ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.

5 Ndidzaoperanji masiku oipa,

pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?

6 Iwo akutama kulemera kwao;

nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;

7 kuombola mbale sangadzamuombole,

kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.

8 Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali,

ndipo chilekeke nthawi zonse.

9 Kuti akhale ndi moyo osafa,

osaona chivundi.

10 Pakuti aona anzeru amafa,

monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,

nasiyira ena chuma chao.

11 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire,

ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo;

atchapo dzina lao padziko pao.

12 Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa,

afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.

13 Njira yao ino ndiyo kupusa kwao,

koma akudza m’mbuyo avomereza mau ao.

14 Aikidwa m’manda ngati nkhosa;

mbusa wao ndi imfa.

Ndipo m’mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao;

ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda,

kuti pokhala pake padzasowa.

15 Koma Mulungu adzaombola moyo wanga

kumphamvu ya manda.

Pakuti adzandilandira ine.

16 Usaope polemezedwa munthu,

pochuluka ulemu wa nyumba yake;

17 pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse;

ulemu wake sutsika naye kumtsata m’mbuyo.

18 Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo,

ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.

19 Adzamuka kumbadwo wa makolo ake;

sadzaona kuunika nthawi zonse.

20 Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,

afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/49-63177fae33b2620218f9b42ce5891658.mp3?version_id=1068—