Categories
MASALIMO

MASALIMO 20

Kupempherera mfumu potulukira iye kunkhondo

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso;

dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;

2 likutumizire thandizo lotuluka m’malo oyera,

ndipo likugwirizize kuchokera muZiyoni;

3 likumbukire zopereka zako zonse,

lilandire nsembe yako yopsereza;

4 likupatse cha mtima wako,

ndipo likwaniritse upo wako wonse.

5 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu,

ndipo m’dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera;

Yehova akwaniritse mapempho ako onse.

6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake;

adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera

ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.

7 Ena atama magaleta, ndi ena akavalo;

koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.

8 Iwowa anagonjeka, nagwa;

koma ife tauka, ndipo takhala chilili.

9 Yehova, pulumutsani,

mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/20-17416fa199165412977454d9dde10c18.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 21

Davide ayamika Mulungu pa kugonjetsa adani

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;

adzakondwera kwakukulu m’chipulumutso chanu!

2 Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake,

ndipo simunakane pempho la milomo yake.

3 Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma;

muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.

4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;

mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.

5 Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu;

mumchitira iye ulemu ndi ukulu.

6 Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse;

mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.

7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,

ndipo mwa chifundo cha Wam’mwambamwamba sadzagwedezeka iye.

8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse,

dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.

9 Mudzawaika ngati ng’anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.

Yehova adzawatha m’kukwiya kwake,

ndipo moto udzawanyeketsa.

10 Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa padziko lapansi,

ndi mbeu zao mwa ana a anthu.

11 Pakuti anakupangirani choipa,

anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.

12 Pakuti mudzawabweza m’mbuyo,

popiringidza m’nsinga zanu pankhope pao.

13 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu;

potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/21-3b1823598324ec263045853364f077b7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 22

Posautsidwa Davide adandaulira, apemphera, ayamika Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Ajelet Hasakara. Salimo la Davide.

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?

Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa,

ndi kwa mau a kubuula kwanga?

2 Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza;

ndipo usiku, sindikhala chete.

3 Koma Inu ndinu woyera,

wakukhala m’malemekezo a Israele.

4 Makolo athu anakhulupirira Inu;

anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.

5 Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa;

anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi.

6 Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai,

chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.

7 Onse akundipenya andiseka;

akwenzula, apukusa mutu, nati,

8 Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,

amlanditse tsopano popeza akondwera naye.

9 Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa;

wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.

10 Chibadwire ine anandisiyira Inu,

kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.

11 Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi,

pakuti palibe mthandizi.

12 Ng’ombe zamphongo zambiri zandizinga;

mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.

13 Andiyasamira m’kamwa mwao,

ngati mkango wozomola ndi wobangula.

14 Ndathiridwa pansi monga madzi,

ndipo mafupa anga onse anaguluka.

Mtima wanga ukunga sera;

wasungunuka m’kati mwa matumbo anga.

15 Mphamvu yanga yauma ngati phale;

ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga;

ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.

16 Pakuti andizinga agalu,

msonkhano wa oipa wanditsekereza;

andiboola m’manja anga ndi m’mapazi anga.

17 Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse;

iwo ayang’ana nandipenyetsetsa ine.

18 Agawana zovala zanga,

nachita maere pa malaya anga.

19 Koma Inu, Yehova, musakhale kutali;

mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.

20 Landitsani moyo wanga kulupanga;

wokondedwa wanga kumphamvu ya galu,

21 ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango;

inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati.

22 Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,

pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.

23 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;

inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu;

ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.

24 Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe

ndi zunzo la wozunzika;

ndipo sanambisire nkhope yake;

koma pomfuulira Iye, anamva.

25 Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu,

zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.

26 Ozunzika adzadya nadzakhuta,

adzayamika Yehova iwo amene amfuna,

ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.

27 Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira

nadzatembenukira kwa Yehova,

ndipo mafuko onse aamitunduadzagwadira pamaso panu.

28 Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;

Iye achita ufumu mwa amitundu.

29 Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira;

onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake,

ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.

30 Mbumba ya anthu idzamtumikira;

kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.

31 Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake

kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/22-be2bc28b2bd260d5d7142d35176ffe14.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 23

Amwai amene Yehova akhala Mbusa wao

Salimo la Davide.

1 Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

2 Andigonetsa kubusa lamsipu,

anditsogolera kumadzi odikha.

3 Atsitsimutsa moyo wanga;

anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

4 Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa,

sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine;

chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.

5 Mundiyalikira gome pamaso panga m’kuona kwa adani anga;

mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.

6 Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata

masiku onse a moyo wanga,

ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/23-87d6e75eac2f73168f547c4625dcb6ed.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 24

Ulemerero wa Yehova

Salimo la Davide.

1 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe,

dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo.

2 Pakuti Iye analimanga pazinyanja,

nalikhazika pamadzi.

3 Adzakwera ndani m’phiri la Yehova?

Nadzaima m’malo ake oyera ndani?

4 Woyera m’manja, ndi woona m’mtima, ndiye;

iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe,

ndipo salumbira monyenga.

5 Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,

ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.

6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,

iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.

7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;

ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha,

kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

8 Mfumu imene ya ulemerero ndani?

Yehova wamphamvu ndi wolimba,

Yehova wolimba kunkhondo.

9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;

inde weramutsani, zitseko zosatha inu,

kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

10 Mfumu imene ya ulemerero ndani?

Yehova wa makamumakamu,

ndiye Mfumu ya ulemerero.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/24-0f47e0f7343c5bc9f37210a8a529040a.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 25

Davide apempha Mulungu amlanditse kwa adani

Salimo la Davide.

1 Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova.

2 Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu,

ndisachite manyazi;

adani anga asandiseke ine.

3 Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi;

adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.

4 Mundidziwitse njira zanu,

Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

5 Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse;

pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;

Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

6 Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu;

pakuti izi nza kale lonse.

7 Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga

kapena zopikisana nanu.

Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu,

chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

8 Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima,

chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira.

9 Adzawatsogolera ofatsa m’chiweruzo;

ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

10 Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi,

kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.

11 Chifukwa cha dzina lanu, Yehova,

ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.

12 Munthuyo wakuopa Yehova ndani?

Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.

13 Moyo wake udzakhala mokoma;

ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.

14 Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye;

ndipo adzawadziwitsa pangano lake.

15 Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka;

pakuti Iye adzaonjola mapazi anga mu ukonde.

16 Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo;

pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika.

17 Masautso a mtima wanga akula,

munditulutse m’zondipsinja.

18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga;

ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.

19 Penyani adani anga, popeza achuluka;

ndipo andida ndi udani wachiwawa.

20 Sungani moyo wanga, ndilanditseni,

ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.

21 Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,

pakuti ndayembekezera Inu.

22 Ombolani Israele, Mulungu,

m’masautso ake onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/25-6c03c4b9e544cdd9107e6f76a782fa68.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 26

Davide popempha Mulungu amweruze, atchula zokoma zake

Salimo la Davide.

1 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga,

ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.

2 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;

yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.

3 Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga;

ndipo ndayenda m’choona chanu.

4 Sindinakhala pansi ndi anthu achabe;

kapena kutsagana nao anthu othyasika.

5 Ndidana nao msonkhano wa ochimwa,

ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa.

6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;

kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;

7 kuti ndimveketse mau a chiyamiko,

ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.

8 Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu,

ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.

9 Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,

kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;

10 amene m’manja mwao muli mphulupulu,

ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.

11 Koma ine, ndidzayenda mu ungwiro wanga;

mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.

12 Phazi langa liponda pachidikha,

m’misonkhano ndidzalemekeza Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/26-98dd20ba10f08be410bb9361a3194952.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 27

Davide atamadi Yehova, naliradi kuyanjana ndi Mulungu

Salimo la Davide.

1 Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

2 Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga,

inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.

3 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,

mtima wanga sungachite mantha;

ingakhale nkhondo ikandiukira,

inde pomweponso ndidzakhulupirira.

4 Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,

ndidzachilondola ichi,

Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,

kupenya kukongola kwake kwa Yehova

ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.

5 Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake,

adzandibisa mkati mwa chihema chake;

pathanthwe adzandikweza.

6 Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka

pamwamba pa adani anga akundizinga;

ndipo ndidzapereka m’chihema mwake

nsembe za kufuula mokondwera;

ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.

7 Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine;

mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze.

8 Pamene munati, Funani nkhope yanga;

mtima wanga unati kwa Inu.

Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.

9 Musandibisire ine nkhope yanu;

musachotse kapolo wanu ndi kukwiya.

Inu munakhala thandizo langa;

musanditaye, ndipo musandisiye

Mulungu wa chipulumutso changa.

10 Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,

koma Yehova anditola.

11 Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,

munditsogolere panjira yachidikha,

chifukwa cha adani anga.

12 Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa,

chifukwa zinandiukira mboni zonama

ndi iwo akupumira zachiwawa.

13 Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova

m’dziko la amoyo, ndikadatani!

14 Yembekeza Yehova,

limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako;

inde, yembekeza Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/27-def2c9f5a95c37697f91c2701787cbe3.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 28

Apempha chipulumutso, ayamika populumutsidwa

Salimo la Davide.

1 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira;

thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva;

pakuti ngati munditontholera ine,

ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.

2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,

pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.

3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa,

ndi ochita zopanda pake;

amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,

koma mumtima mwao muli choipa.

4 Muwapatse monga mwa ntchito zao,

ndi monga mwa choipa chochita iwo;

muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao;

muwabwezere zoyenera iwo.

5 Pakuti sasamala ntchito za Yehova,

kapena machitidwe a manja ake,

adzawapasula, osawamanganso.

6 Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.

7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa;

mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza,

chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu;

ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

8 Yehova ndiye mphamvu yao,

inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.

9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu;

muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/28-18f7c07f0c5a257e43abf9589f958ea2.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 29

Achenjeza akulu alemekeze Mulungu

Salimo la Davide.

1 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2 Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake,

gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

3 Liu la Yehova lili pamadzi;

Mulungu wa ulemerero agunda,

ndiye Yehova pamadzi ambiri.

4 Liu la Yehova ndi lamphamvu;

liu la Yehova ndi lalikulukulu.

5 Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;

inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.

6 Aitumphitsa monga mwanawang’ombe;

Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.

7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.

8 Liu la Yehova ligwedeza chipululu;

Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.

9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,

ndipo lipulula nkhalango;

ndipo mu Kachisi mwake zonse zili m’mwemo zimati, Ulemerero.

10 Yehova anakhala pa chigumula,

inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.

11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu,

Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/29-11d4e31f4df43387d25d187297c4fd77.mp3?version_id=1068—