Categories
MASALIMO

MASALIMO 10

Athamangira Mulungu pothawa adani omtsata

1 Muimiranji patali, Yehova?

Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;

agwe m’chiwembu anapanganacho.

3 Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake,

adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

4 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira.

Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.

5 Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse;

maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;

adani ake onse awanyodola.

6 Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine;

ku mibadwomibadwo osagwa m’tsoka ine.

7 M’kamwa mwake mwadzala kutemberera

ndi manyengo ndi kuchenjerera;

pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

8 Akhala m’molalira midzi;

mobisalamo akupha munthu wosachimwa.

Ambisira waumphawi nkhope yake.

9 Alalira monga mkango m’ngaka mwake;

alalira kugwira wozunzika,

agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.

10 Aunthama, nawerama,

ndipo aumphawi agwa m’zala zake.

11 Anena m’mtima mwake, Mulungu waiwala;

wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;

musaiwale ozunzika.

13 Woipa anyozeranji Mulungu,

anena m’mtima mwake, Simudzafunsira?

14 Mwapenya; pakuti mumayang’anira chivutitso

ndi chisoni kuti achipereke m’manja mwanu;

waumphawi adzipereka kwa Inu;

wamasiye mumakhala mthandizi wake.

15 Thyolani mkono wa woipa;

ndipo wochimwa, mutsate choipa chake

kufikira simuchipezanso china.

16 Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya;

aonongekaamitundum’dziko lake.

17 Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika,

mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;

18 kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,

kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/10-4363149da873ad6239f11877cd226247.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 11

Yehova asunga anthu ake nalanga oipa

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Ndakhulupirira Yehova,

mutani nkunena kwa moyo wanga,

Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?

2 Pakuti, onani, oipa akoka uta,

apiringidza muvi wao pansinga,

kuwaponyera mumdima oongoka mtima.

3 Akapasuka maziko,

wolungama angachitenji?

4 Yehova ali mu Kachisi wake woyera,

Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba;

apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.

5 Yehova ayesa wolungama mtima,

koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.

6 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa;

moto ndi miyala yasulufure,

ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m’chikho chao.

7 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama;

woongoka mtima adzapenya nkhope yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/11-6a0cc3d8a7d5d581b3105676a8e68595.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 12

Anthu ndi amabodza, Mulungu ndiye woona

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Seminiti. Salimo la Davide.

1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;

pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.

2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake,

amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.

3 Yehova adzadula milomo yonse yothyasika,

lilime lakudzitamandira;

4 amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;

milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?

5 Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika,

chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi,

ndiuka tsopano, ati Yehova;

ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.

6 Mau a Yehova ndi mau oona;

ngatisilivawoyenga m’ng’anjo yadothi,

yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.

7 Mudzawasunga, Yehova,

mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse.

8 Oipa amayenda mozungulirazungulira,

potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/12-7c5bb2f4a31918aa5895fc65a425fe52.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 13

Munkhawa athawira Mulungu namkhulupirira

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti?

Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?

2 Ndidzachita uphungu m’moyo mwanga kufikira liti,

pokhala ndi chisoni m’mtima mwanga tsiku lonse?

Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?

3 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga.

Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;

4 kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa;

ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.

5 Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu;

mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.

6 Ndidzaimbira Yehova,

pakuti anandichitira zokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/13-9cde76954810ab1f67a49fbbdcdf3261.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 14

Anthu oipadi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.

Achita zovunda, achita ntchito zonyansa;

kulibe wakuchita bwino.

2 Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu,

kuti aone ngati aliko wanzeru,

wakufuna Mulungu.

3 Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima;

palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.

4 Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu?

Pakudya anthu anga monga akudya mkate,

ndipo saitana pa Yehova.

5 Pamenepa anaopaopatu,

pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.

6 Munyazitsa uphungu wa wozunzika,

koma Yehova ndiye pothawira pake.

7 Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera kuZiyoni!

Pakubweretsa Yehova anthu ake a m’nsinga,

pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/14-077b876ad14e0f22bfb7d2de2c9b5075.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 15

Chikhalidwe cha munthu woona wa Mulungu

Salimo la Davide.

1 Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu?

Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?

2 Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo,

nanena zoonadi mumtima mwake.

3 Amene sasinjirira ndi lilime lake,

nachitira mnzake choipa,

ndipo satola miseche pa mnansi wake.

4 M’maso mwake munthu woonongeka anyozeka;

koma awachitira ulemu akuopa Yehova.

Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.

5 Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu,

ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa.

Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/15-b5acfb14ce5ab7bfc019521093f17172.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 16

Munthu wokhulupirira Mulungu akhazikika mtima, osaopa kutayika

Mikitamu wa Davide.

1 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.

2 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga,

ndilibe chabwino china choposa Inu.

3 Za oyera mtima okhala padziko lapansi,

iwo ndiwo omveka mbiri,

mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.

4 Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina.

Sindidzathira nsembe zao zamwazi,

ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.

5 Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa,

ndinu wondigwirira cholandira changa.

6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa;

inde cholowa chokoma ndili nacho.

7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu,

usikunso impso zanga zindilangiza.

8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse;

popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

9 Chifukwa chake wasekera mtima wanga,

nukondwera ulemu wanga;

mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.

10 Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;

simudzalola wokondedwa wanu avunde.

11 Mudzandidziwitsa njira ya moyo,

pankhope panu pali chimwemwe chokwanira;

m’dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/16-f9ecd68e0862fca5c3c92330c486c3b5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 17

Davide apempha Mulungu amsunge pa ofuna kumuononga

Pemphero la Davide.

1 Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga;

tcherani khutu ku pemphero langa

losatuluka m’milomo ya chinyengo.

2 Pankhope panu patuluke chiweruzo changa;

maso anu apenyerere zolunjika.

3 Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;

mwandisuntha, simupeza kanthu;

mwatsimikiza mtima kuti m’kamwa mwanga simudzalakwa.

4 Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu

ndingalowe njira za woononga.

5 M’mayendedwe anga ndasunga mabande anu,

mapazi anga sanaterereke.

6 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu;

tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.

7 Onetsani chifundo chanu chodabwitsa,

Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu

kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.

8 Ndisungeni monga kamwana ka m’diso,

ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,

9 kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,

adani a pa moyo wanga amene andizinga.

10 Mafuta ao awatsekereza;

m’kamwa mwao alankhula modzikuza.

11 Tsopano anatizinga m’mayendedwe athu,

apenyetsetsa m’maso kuti atigwetse pansi.

12 Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,

ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.

13 Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse,

landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;

14 kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,

kwa anthu a dziko lapansi pano

amene cholowa chao chili m’moyo uno,

ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika;

akhuta mtima ndi ana,

nasiyira ana amakanda zochuluka zao.

15 Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m’chilungamo,

ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/17-9d8ddf7ef741f74133cbdf9abe033de3.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 18

Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova, amene ananena kwa Yehova mau a nyimbo iyi m’mene Yehova anamlanditsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Saulo: ndipo anati,

1 Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.

2 Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa,

ndi Mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye;

chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

3 Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika,

ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.

4 Zingwe za imfa zinandizinga,

ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa.

5 Zingwe za manda zindizinga,

misampha ya imfa inandifikira ine.

6 M’kusauka kwanga ndinaitana Yehova,

ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;

mau anga anawamva mu Kachisi mwake,

ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m’makutu mwake.

7 Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi,

ndi maziko a mapiri ananjenjemera

nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.

8 Unakwera utsi wotuluka m’mphuno mwake,

ndi moto wa m’kamwa mwake unanyeka

nuyakitsa makala.

9 Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;

ndipo pansi pa mapazi ake panali mdima bii.

10 Ndipo anaberekeka pakerubi, nauluka;

nauluka msanga pa mapiko a mphepo.

11 Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga;

mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.

12 Mwa kuchezemira kunali pamaso pake makongwa anakanganuka,

matalala ndi makala amoto.

13 Ndipo anagunda m’mwamba Yehova,

ndipo Wam’mwambamwamba anamvetsa liu lake;

matalala ndi makala amoto.

14 Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa;

inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

15 Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,

nafukuka maziko a dziko lapansi,

mwa kudzudzula kwanu, Yehova,

mwa mpumo wa mpweya wa m’mphuno mwanu.

16 Anatuma kuchokera m’mwamba, ananditenga;

anandivuula m’madzi ambiri.

17 Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,

ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18 Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;

koma Yehova anali mchirikizo wanga.

19 Ananditulutsanso andifikitse motakasuka;

anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20 Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa;

anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,

ndipo sindinachitire choipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga,

ndipo malemba ake sindinawachotse kwa ine.

23 Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye,

ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa.

24 Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa chilungamo changa,

monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pake.

25 Pa wachifundo mukhala wachifundo;

pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.

26 Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;

pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27 Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;

koma maso okweza muwatsitsa.

28 Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;

Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29 Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;

ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30 Mulungu ndiye wangwiro m’njira zake;

mau a Yehova ngoyengeka;

ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.

31 Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?

Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32 Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m’chuuno,

nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

33 Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala,

nandiimitsa pamsanje panga.

34 Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo;

kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

35 Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;

ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,

ndipo chifatso chanu chandikuza ine.

36 Mwandipondetsa patalipatali,

sanaterereke mapazi anga.

37 Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza,

ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.

38 Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka,

adzagwa pansi pa mapazi anga.

39 Pakuti mwandizingiza mphamvu m’chuuno ku nkhondoyo;

mwandigonjetsera amene andiukira.

40 Ndipo adani anga mwawalozetsa m’mbuyo kwa ine,

kuti ndipasule ondidawo.

41 Anafuula, koma panalibe wopulumutsa;

ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze.

42 Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo;

ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

43 Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;

mwandiika mutu waamitundu;

mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.

44 Pakumva m’khutu za ine adzandimvera,

alendo adzandigonjera monyenga.

45 Alendo adzafota,

nadzatuluka monjenjemera m’ngaka mwao.

46 Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;

nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.

47 Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango,

nandigonjetsera mitundu ya anthu.

48 Andipulumutsa kwa adani anga.

Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine,

mundikwatula kwa munthu wachiwawa.

49 Chifukwa chake Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu,

ndipo dzina lanu ndidzaliimbira.

50 Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu;

nachitira chifundo wodzozedwa wake,

Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/18-941b51d1b23796a989b54e0b72f4dd8b.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 19

Davide alemekeza zolengedwa ndi Mulungu, ndi malamulo ao omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;

ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.

2 Usana ndi usana uchulukitsa mau,

ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.

3 Palibe chilankhulidwe, palibe mau;

liu lao silimveka.

4 Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi,

ndipo mau ao ku malekezero a m’dziko muli anthu.

Iye anaika hema la dzuwa m’menemo,

5 ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake,

likondwera ngati chiphona kuthamanga m’njira.

6 Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo,

ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake;

ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.

7 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;

mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.

8 Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima;

malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.

9 Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse;

maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.

10 Ndizo zifunika koposa golide,

inde, golide wambiri woyengetsa;

zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.

11 Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo,

m’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.

12 Adziwitsa zolowereza zake ndani?

Mundimasule kwa zolakwa zobisika.

13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;

zisachite ufumu pa ine.

Pamenepo ndidzakhala wangwiro,

ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.

14 Mau a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga

avomerezeke pamaso panu,

Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/19-dbb1b75cff85c5c4a164cc3805ea20cf.mp3?version_id=1068—