Categories
MASALIMO

MASALIMO 140

Davide apempha Mulungu amlanditse kwa mdani woipa wamphamvu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide.

1 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;

ndisungeni kwa munthu wachiwawa;

2 amene adzipanga zoipa mumtima mwao;

masiku onse amemeza nkhondo.

3 Anola lilime lao ngati njoka;

pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m’manja mwa woipa;

ndisungeni kwa munthu wachiwawa;

kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.

5 Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe;

anatcha ukonde m’mphepete mwa njira;

ananditchera makwekwe.

6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;

munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.

7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa,

munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.

8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;

musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.

9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,

choipa cha milomo yao chiwaphimbe.

10 Makala amoto awagwere;

aponyedwe kumoto;

m’maenje ozama, kuti asaukenso.

11 Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi;

choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.

12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,

ndi kuweruzira aumphawi.

13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;

oongoka mtima adzakhala pamaso panu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/140-f00ee044309bcb1491e964d9efe48d2e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 141

Davide apempha Mulungu amthandize poyesedwa ndi zoipa

Salimo la Davide.

1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;

munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

2 Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu;

kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.

3 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;

sungani pakhomo pa milomo yanga.

4 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa,

kuchita ntchito zoipa

ndi anthu akuchita zopanda pake;

ndipo ndisadye zankhuli zao.

5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo:

akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;

mutu wanga usakane:

Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;

nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.

7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,

monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.

8 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;

ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga.

9 Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo,

ndisakodwe m’makwekwe a iwo ochita zopanda pake.

10 Oipa agwe pamodzi m’maukonde ao,

kufikira nditapitirira ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/141-36576f5f05d631c1d64279db9e575199.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 142

Pemphero pakuopsedwa kwakukulu

Chilangizo cha Davide, muja anakhala m’phanga; Pemphero.

1 Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova;

ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.

2 Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake;

ndionetsa msauko wanga pamaso pake.

3 Pamene mzimu wanga unakomoka m’kati mwanga, munadziwa njira yanga.

M’njira ndiyendamo ananditchera msampha.

4 Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;

pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.

5 Ndinafuulira kwa inu, Yehova;

ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga,

gawo langa m’dziko la amoyo.

6 Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri;

ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana.

7 Tulutsani moyo wanga m’ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;

olungama adzandizinga;

pakuti mudzandichitira zokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/142-4d4719bacbb778eb570fed3078acd2bf.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 143

Davide apempha Mulungu amlanditse msanga kwa adani ake

Salimo la Davide.

1 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga;

ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.

2 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;

pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.

3 Pakuti mdani alondola moyo wanga;

apondereza pansi moyo wanga;

andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.

4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;

mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga.

5 Ndikumbukira masiku a kale lomwe;

zija mudazichita ndilingirirapo;

ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.

6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:

Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.

7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.

Musandibisire nkhope yanu;

ndingafanane nao akutsikira kudzenje.

8 Mundimvetse chifundo chanu mamawa;

popeza ndikhulupirira Inu:

Mundidziwitse njira ndiyendemo;

popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.

9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;

ndibisala mwa Inu.

10 Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;

Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.

11 Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu;

mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m’sautso.

12 Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga,

ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;

pakuti ine ndine mtumiki wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/143-c4534d5452662442eac4ab35bfdad210.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 144

Davide ayamika Mulungu kuti anamtchinjiriza, napempha ampulumutse kuti anthu adalenso

Salimo la Davide.

1 Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,

wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo,

zala zanga zigwirane nao:

2 Ndiye chifundo changa, ndi linga langa,

msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga;

chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama;

amene andigonjetsera anthu anga.

3 Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?

Mwana wa munthu kuti mumsamalira?

4 Munthu akunga mpweya;

masiku ake akunga mthunzi wopitirira.

5 Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:

Khudzani mapiri ndipo adzafuka.

6 Ng’animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa;

tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.

7 Tulutsani manja anu kuchokera m’mwamba;

ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu,

kudzanja la alendo;

8 amene pakamwa pao alankhula zachabe,

ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.

9 Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;

pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.

10 Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso:

Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.

11 Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo,

amene pakamwa pao alankhula zachabe,

ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.

12 Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime;

ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya,

zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

13 Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu;

ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.

14 Kuti ng’ombe zathu zikhale zosenza katundu;

ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo,

pasakhalenso kufuula m’makwalala athu.

15 Odala anthu akuona zotere;

odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/144-9253b4113173caad0bef2b5147452584.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 145

Ukulu ndi ukoma wa Mulungu

Salimo lolemekeza; la Davide.

1 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;

ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

2 Masiku onse ndidzakuyamikani;

ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

3 Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ndi ukulu wake ngwosasanthulika.

4 Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake,

ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

5 Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu,

ndi ntchito zanu zodabwitsa.

6 Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa;

ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7 Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu,

nadzaimbira chilungamo chanu.

8 Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo;

osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.

9 Yehova achitira chokoma onse;

ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

10 Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;

ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11 Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,

adzalankhulira mphamvu yanu.

12 Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake,

ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.

13 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,

ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.

14 Yehova agwiriziza onse akugwa,

naongoletsa onse owerama.

15 Maso a onse ayembekeza Inu;

ndipo muwapatsa chakudya chao m’nyengo zao.

16 Muolowetsa dzanja lanu,

nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

17 Yehova ali wolungama m’njira zake zonse,

ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.

18 Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,

onse akuitanira kwa Iye m’choonadi.

19 Adzachita chokhumba iwo akumuopa;

nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

20 Yehova asunga onse akukondana naye;

koma oipa onse adzawaononga.

21 Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova;

ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera

kunthawi za nthawi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/145-1717429a59961e0a42ee09b207785c43.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 146

Chifooko cha munthu, chikhulupiriko cha Mulungu

1 Aleluya;

Ulemekeze Yehova, moyo wanga.

2 Ndidzalemekeza Yehova m’moyo mwanga;

ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.

3 Musamakhulupirira zinduna,

kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.

4 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake;

tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.

5 Wodala munthu amene akhala naye

Mulungu wa Yakobo kuti amthandize,

chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.

6 Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi,

nyanja ndi zonse zili m’mwemo.

Ndiye wakusunga choonadi kosatha,

7 ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika;

ndiye wakupatsa anjala chakudya;

Yehova amasula akaidi.

8 Yehova apenyetsa osaona;

Yehova aongoletsa onse owerama;

Yehova akonda olungama.

9 Yehova asunga alendo;

agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye;

koma akhotetsa njira ya oipa.

10 Yehova adzachita ufumu kosatha,

Mulungu wako,Ziyoni, ku mibadwomibadwo.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/146-682faa55b24b87d18539b47852aa329c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 147

Alemekeze dzina la Mulungu chifukwa cha zokoma amachitira anthu ake

1 Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;

pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.

2 Yehova amangaYerusalemu;

asokolotsa otayika a Israele.

3 Achiritsa osweka mtima,

namanga mabala ao.

4 Awerenga nyenyezi momwe zili;

azitcha maina zonsezi.

5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri;

nzeru yake njosatha.

6 Yehova agwiriziza ofatsa;

atsitsira oipa pansi.

7 Yamikani Yehova ndi kuthira mang’ombe;

muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:

8 Amene aphimba thambo ndi mitambo,

amene akonzera mvula nthaka,

amene aphukitsa msipu pamapiri.

9 Amene apatsa zoweta chakudya chao,

ana a khwangwala alikulira.

10 Mphamvu ya kavalo siimkonda:

Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye,

iwo akuyembekeza chifundo chake.

12 Yerusalemu, lemekezani Yehova;

Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.

13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:

Anadalitsa ana anu m’kati mwanu.

14 Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere;

akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.

15 Atumiza lamulo lake kudziko lapansi;

mau ake athamanga liwiro.

16 Apatsa chipale chofewa ngati ubweya;

awaza chisanu ngati phulusa.

17 Aponya matalala ake ngati zidutsu:

Adzaima ndani pa kuzizira kwake?

18 Atumiza mau ake nazisungunula;

aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.

19 Aonetsa mau ake kwa Yakobo;

malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.

20 Sanatero nao anthu a mtundu wina;

ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/147-908d9874eb731e84402030f8fb68f978.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 148

Zolengedwa zonse zilemekeze Mulungu

1 Aleluya.

Lemekezani Yehova kochokera kumwamba;

mlemekezeni m’misanje.

2 Mlemekezeni,angeloake onse;

mlemekezeni, makamu ake onse.

3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;

mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.

4 Mlemekezeni, m’mwambamwamba,

ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.

5 Alemekeze dzina la Yehova;

popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.

6 Anazikhazikanso kunthawi za nthawi;

anazipatsa chilamulo chosatumphika.

7 Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi,

zinsomba inu, ndi malo ozama onse;

8 moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu;

mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;

9 mapiri ndi zitunda zonse;

mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:

10 Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse;

zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.

11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;

zinduna ndi oweruza onse a padziko.

12 Anyamata ndiponso anamwali;

okalamba pamodzi ndi ana.

13 Alemekeze dzina la Yehova;

pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka;

ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.

14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake,

chilemekezo cha okondedwa ake onse;

ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/148-c66f417a2811e794129a4da622dd16f6.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 149

Okhulupirira onse alemekeze Mulungu wao

1 Aleluya,

Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano,

ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

2 Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga;

ana aZiyoniasekere mwa mfumu yao.

3 Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang’ombe;

amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

4 Popeza Yehova akondwera nao anthu ake;

adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.

5 Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu:

Afuule mokondwera pamakama pao.

6 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,

ndi lupanga lakuthwa konsekonse m’dzanja lao;

7 kubwezera chilango akunja,

ndi kulanga mitundu ya anthu;

8 kumanga mafumu ao ndi maunyolo,

ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo,

9 kuwachitira chiweruzo cholembedwacho.

Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/149-b1b2c40a110f35b6860b2e347ecb0dc0.mp3?version_id=1068—