Categories
MASALIMO

MASALIMO 130

Pemphero lakuti akhululukidwe

Nyimbo yokwerera.

1 M’mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.

2 Ambuye, imvani liu langa;

makutu anu akhale chimverere

mau a kupemba kwanga.

3 Mukasunga mphulupulu, Yehova,

adzakhala chilili ndani, Ambuye?

4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro,

kuti akuopeni.

5 Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira,

ndiyembekeza mau ake.

6 Moyo wanga uyang’anira Ambuye,

koposa alonda matanda kucha;

inde koposa alonda matanda kucha.

7 Israele, uyembekezere Yehova;

chifukwa kwa Yehova kuli chifundo,

kwaonso kuchulukira chiombolo.

8 Ndipo adzaombola Israele

ku mphulupulu zake zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/130-08ede17c17095cb89fbacd5a4d727f95.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 131

Kudzichepetsa kwa Davide pakupemphera

Nyimbo yokwerera; ya Davide.

1 Yehova, mtima wanga sunadzikuze

ndi maso anga sanakwezeke;

ndipo sindinatsate zazikulu,

kapena zodabwitsa zondiposa.

2 Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga;

ngati mwana womletsa kuyamwa amake,

moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.

3 Israele, uyembekezere Yehova,

kuyambira tsopano kufikira kosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/131-4a5e96ec1785b548b0bd2c780c328f05.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 132

Davide asamalira Kachisi ndi likasa. Lonjezano la Mulungu

Nyimbo yokwerera.

1 Yehova, kumbukirani Davide

kuzunzika kwake konse.

2 Kuti analumbira Yehova,

nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,

3 Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,

ngati ndidzakwera pa kama logonapo;

4 ngati ndidzalola maso anga agone,

kapena zikope zanga ziodzere;

5 kufikira nditapezera Yehova malo,

chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

6 Taonani, tinachimva mu Efurata;

tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.

7 Tidzalowa mokhalamo Iye;

tidzagwadira kumpando wa mapazi ake.

8 Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;

Inu ndi hema wa mphamvu yanu.

9 Ansembe anu avale chilungamo;

ndi okondedwa anu afuule mokondwera.

10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu

musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

11 Yehova analumbira Davide zoona;

sadzalibweza; ndi kuti,

Wa iwo okhala zipatso za thupi lako

ndidzaika pa mpando wachifumu wako.

12 Ana ako akasungachipanganochanga

ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa,

ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,

13 pakuti Yehova anasankhaZiyoni;

analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,

14 Pampumulo panga mpano posatha,

Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.

15 Ndidzadalitsatu chakudya chake;

aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.

16 Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso:

Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.

17 Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga;

ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali.

18 Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi;

koma pa iyeyu korona wake adzamveka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/132-1a766d8dc23c1a98cb39b86003c887b4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 133

Chikondano cha abale ndi chokoma

Nyimbo yokwerera; ya Davide.

1 Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu

kuti abale akhale pamodzi!

2 Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu,

akutsikira kundevu,

inde kundevu za Aroni;

akutsikira kumkawo wa zovala zake.

3 Ngati mame a ku Heremoni,

akutsikira pa mapiri aZiyoni.

Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo,

ndilo moyo womka muyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/133-de1654ae8ff13fcab0f2dd7436667ef5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 134

Afulumizidwa anthu kulemekeza Yehova

Nyimbo yokwerera.

1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse,

akuimirira m’nyumba ya Yehova usiku.

2 Kwezani manja anu kumalo oyera,

nimulemekeze Yehova.

3 Yehova, ali muZiyoni, akudalitseni;

ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/134-c0ab6cf3799896400acd612283803b61.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 135

Mulungu alemekezedwa pa ukulu wake. Mafano ndi achabe

1 Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova!

Lemekezani inu atumiki a Yehova.

2 Inu akuimirira m’nyumba ya Yehova,

m’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

3 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;

muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.

4 Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,

Israele, akhale chuma chake chenicheni.

5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu,

ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

6 Chilichonse chimkonda Yehova achichita,

kumwamba ndi padziko lapansi, m’nyanja ndi mozama monse.

7 Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi;

ang’animitsa mphezi zidzetse mvula;

atulutsa mphepo mosungira mwake.

8 Anapanda oyamba a Ejipito,

kuyambira munthu kufikira zoweta.

9 Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe,

paFaraondi pa omtumikira onse.

10 Ndiye amene anapandaamitunduambiri,

napha mafumu amphamvu;

11 Sihoni mfumu ya Aamori,

ndi Ogi mfumu ya Basani,

ndi maufumu onse a Kanani:

12 Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa,

cholowa cha kwa Israele anthu ake.

13 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;

chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo.

14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,

koma adzaleka atumiki ake.

15 Mafano a amitundu ndiwosilivandi golide,

ntchito ya manja a anthu.

16 Pakamwa ali napo koma osalankhula;

maso ali nao, koma osapenya;

17 makutu ali nao, koma osamva;

inde, pakamwa pao palibe mpweya.

18 Akuwapanga adzafanana nao;

inde, onse akuwakhulupirira.

19 A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova:

A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:

20 A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:

Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.

21 Alemekezedwe Yehova kuchokera muZiyoni,

amene akhala muYerusalemu.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/135-17e07ebb8041dcceaa116f59e06f9179.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 136

Mulungu alemekezedwe pa chifundo chake

1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

2 Yamikani Mulungu wa milungu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

3 Yamikani Mbuye wa ambuye;

pakuti chifundo chake nchosatha.

4 Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

5 Amene analenga zakumwamba mwanzeru;

pakuti chifundo chake nchosatha.

6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi;

pakuti chifundo chake nchosatha.

7 Amene analenga miuni yaikulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

8 Dzuwa liweruze usana;

pakuti chifundo chake nchosatha.

9 Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;

pakuti chifundo chake nchosatha.

10 Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba;

pakuti chifundo chake nchosatha.

11 Natulutsa Israele pakati pao;

pakuti chifundo chake nchosatha.

12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka;

pakuti chifundo chake nchosatha.

13 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira;

pakuti chifundo chake nchosatha.

14 Napititsa Israele pakati pake;

pakuti chifundo chake nchosatha.

15 NakhuthulaFaraondi khamu lake mu Nyanja Yofiira:

pakuti chifundo chake nchosatha.

16 Amene anatsogolera anthu ake m’chipululu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

17 Amene anapanda mafumu aakulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

18 Ndipo anawapha mafumu omveka;

pakuti chifundo chake nchosatha.

19 Sihoni mfumu ya Aamori;

pakuti chifundo chake nchosatha.

20 Ndi Ogi mfumu ya Basani;

pakuti chifundo chake nchosatha.

21 Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa;

pakuti chifundo chake nchosatha.

22 Cholowa cha kwa Israele mtumiki wake;

pakuti chifundo chake nchosatha.

23 Amene anatikumbukira popepuka ife;

pakuti chifundo chake nchosatha.

24 Natikwatula kwa otisautsa;

pakuti chifundo chake nchosatha.

25 Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya;

pakuti chifundo chake nchosatha.

26 Yamikani Mulungu wa Kumwamba,

pakuti chifundo chake nchosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/136-3ce0d50841b7431da42362b695c5d946.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 137

Kudandaula kwa Ayuda ku Babiloni

1 Ku mitsinje ya ku Babiloni,

kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira,

pokumbukiraZiyoni.

2 Pa msondodzi uli m’mwemo

tinapachika mazeze athu.

3 Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo

ndipo akutizunza anafuna tisekere,

ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.

4 Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova

m’dziko lachilendo?

5 Ndikakuiwalani, Yerusalemu,

dzanja lamanja langa liiwale luso lake.

6 Lilime langa limamatike kunsaya zanga,

ndikapanda kukumbukira inu;

ndikapanda kusankha Yerusalemu

koposa chimwemwe changa chopambana.

7 Yehova, kumbukirani ana a Edomu

tsiku la Yerusalemu;

amene adati, Gamulani, gamulani,

kufikira maziko ake.

8 Mwana wamkazi wa ku Babiloni,

iwe amene udzapasulidwa;

wodala iye amene adzakubwezera chilango

monga umo unatichitira ife.

9 Wodala iye amene adzagwira makanda ako,

ndi kuwaphwanya pathanthwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/137-ebdfdfe95ab47203bfc2919fabb5e2db.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 138

Davide ayamika Mulungu pa kukhulupirika kwake, naneneratu kuti mafumu onse adzatero

Salimo la Davide.

1 Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse;

ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.

2 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera,

ndi kuyamika dzina lanu,

chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu;

popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

3 Tsiku loitana ine, munandiyankha,

munandilimbitsa ndi mphamvu m’moyo mwanga.

4 Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani,

Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.

5 Ndipo adzaimbira njira za Yehova;

pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;

koma wodzikuza amdziwira kutali.

7 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;

mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,

ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

8 Yehova adzanditsirizira za kwa ine:

Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse:

Musasiye ntchito za manja anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/138-baf99d1c1610bf2b5dde57b52d513be1.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 139

Mulungu ali ponseponse, adziwa zonse

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide.

1 Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.

2 Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga,

muzindikira lingaliro langa muli kutali.

3 Muyesa popita ine ndi pogona ine,

ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.

4 Pakuti asanafike mau pa lilime langa,

taonani, Yehova, muwadziwa onse.

5 Munandizinga kumbuyo ndi kumaso,

nimunaika dzanja lanu pa ine.

6 Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa:

Kundikhalira patali, sindifikirako.

7 Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?

Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?

8 Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko;

kapena ndikadziyalira kuGehena, taonani, muli komweko.

9 Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha,

ndi kukhala ku malekezero a nyanja;

10 kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera,

nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

11 Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe,

ndi kuunika kondizinga kukhale usiku.

12 Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu,

koma usiku uwala ngati usana;

mdima ukunga kuunika.

13 Pakuti Inu munalenga impso zanga;

munandiumba ndisanabadwe ine.

14 Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa

nchoopsa ndi chodabwitsa;

ntchito zanu nzodabwitsa;

moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

15 Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika,

poombedwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi.

16 Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya,

ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu,

masiku akuti ziumbidwe,

pakalibe chimodzi cha izo.

17 Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu!

Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!

18 Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga:

Ndikauka ndikhalanso nanu.

19 Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu:

Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine.

20 Popeza anena za Inu moipa,

ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.

21 Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova?

Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?

22 Ndidana nao ndi udani weniweni,

ndiwayesa adani.

23 Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;

mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.

24 Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa,

nimunditsogolere panjira yosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/139-1027ada5dc3d0158a17f5a9160443273.mp3?version_id=1068—