Categories
MASALIMO

MASALIMO 120

Apempha Mulungu amlanditse pa omnamiza

Nyimbo yokwerera.

1 Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga,

ndipo anandivomereza.

2 Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza,

ndi kulilime lonyenga.

3 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji,

lilime lonyenga iwe?

4 Mivi yakuthwa ya chiphona,

ndi makala tsanya.

5 Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki,

kuti ndigonera m’mahema a Kedara!

6 Moyo wanga unakhalitsa nthawi

pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.

7 Ine ndikuti, Mtendere;

koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/120-9446c9b8452065a4e6d585a5fdd35301.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 121

Mulungu Msungi wokhulupirika wa anthu ake

Nyimbo yokwerera.

1 Ndikweza maso anga kumapiri:

Thandizo langa lidzera kuti?

2 Thandizo langa lidzera kwa Yehova,

wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

3 Sadzalola phazi lako literereke:

Iye amene akusunga sadzaodzera.

4 Taonani, wakusunga Israele

sadzaodzera kapena kugona.

5 Yehova ndiye wakukusunga;

Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.

6 Dzuwa silidzawamba usana,

mwezi sudzakupanda usiku.

7 Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse;

adzasunga moyo wako.

8 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako,

kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/121-fa95c6d1f2abdc05f916ba5667688051.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 122

Apempherera mtendere wa Yerusalemu

Nyimbo yokwerera; ya Davide.

1 Ndinakondwera m’mene ananena nane,

Tiyeni kunyumba ya Yehova.

2 Mapazi athu alinkuima

m’zipata zanu,Yerusalemu

3 Yerusalemu anamangidwa

ngati mzinda woundana bwino:

4 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;

akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.

5 Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo,

mipando ya nyumba ya Davide.

6 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;

akukonda inu adzaona phindu.

7 M’linga mwako mukhale mtendere,

m’nyumba za mafumu mukhale phindu.

8 Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga,

ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.

9 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu

ndidzakufunira zokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/122-04dd1aec5107e11f98773d32fe0bf372.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 123

Pemphero la wonyozedwa

Nyimbo yokwerera.

1 Ndikweza maso anga kwa Inu,

kwa Inu wakukhala kumwamba.

2 Taonani, monga maso a anyamata

ayang’anira dzanja la ambuye wao,

monga maso a adzakazi

ayang’anira dzanja la mbuye wao wamkazi:

Momwemo maso athu ayang’anira Yehova Mulungu wathu,

kufikira atichitira chifundo.

3 Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo;

pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.

4 Moyo wathu wakhuta ndithu

ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,

ndi mnyozo wa odzikuza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/123-3cf70daca6d6cb1ca6b207ff6ebd2c65.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 124

Mulungu yekha walanditsa anthu ake

Nyimbo yokwerera; ya Davide.

1 Akadapanda kukhala nafe Yehova,

anene tsono Israele;

2 Akadapanda kukhala nafe Yehova,

pakutiukira anthu:

3 Akadatimeza amoyo,

potipsera mtima wao.

4 Akadatimiza madziwo,

mtsinje ukadapita pa moyo wathu;

5 madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.

6 Alemekezedwe Yehova,

amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao.

7 Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;

msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka.

8 Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova,

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/124-2ff8b83e597e46994d314767b3d637d9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 125

Okhulupirira Yehova akhazikika mtima

Nyimbo yokwerera.

1 Iwo akukhulupirira Yehova

akunga phiri laZiyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.

2 Monga mapiri azingaYerusalemu,

momwemo Yehova azinga anthu ake,

kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

3 Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama;

kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.

4 Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma;

iwo okhala oongoka mumtima mwao.

5 Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota,

Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake.

Mtendere ukhale pa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/125-eebef3497cf7bba78426c82c1869b5f7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 126

Ayamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo wao

Nyimbo yokwerera.

1 Pobweza Yehova ukapolo waZiyoni,

tinakhala ngati anthu akulota.

2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,

ndi lilime lathu linafuula mokondwera;

pamenepo anati kwaamitundu,

Yehova anawachitira iwo zazikulu.

3 Yehova anatichitira ife zazikulu;

potero tikhala okondwera.

4 Bwezani ukapolo wathu, Yehova,

ngati mitsinje ya kumwera.

5 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

6 Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;

adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera,

alikunyamula mitolo yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/126-3263cbbe85cce41a2b4edb42773efe99.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 127

Madalitso onse, a m’banja omwe, achokera kwa Mulungu

Nyimbo yokwerera; ya Solomoni.

1 Akapanda kumanga nyumba Yehova,

akuimanga agwiritsa ntchito chabe;

akapanda kusunga mzinda Yehova,

mlonda adikira chabe.

2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,

kudya mkate wosautsa kuupeza;

kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m’tulo.

3 Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova;

chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.

4 Ana a ubwana wake wa munthu

akunga mivi m’dzanja lake la chiphona.

5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake:

sadzachita manyazi iwo,

pakulankhula nao adani kuchipata.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/127-eeeab4dcd9f3f75aeebe2f4be6f88302.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 128

Wakuopa Yehova adalitsidwa m’banja mwake

Nyimbo yokwerera.

1 Wodala yense wakuopa Yehova,

wakuyenda m’njira zake.

2 Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako;

wodala iwe, ndipo kudzakukomera.

3 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m’mbali za nyumba yako;

ana ako adzanga timitengo taazitonapozinga podyera pako.

4 Taonani, m’mwemo adzadalitsika

munthu wakuopa Yehova.

5 Yehova adzakudalitsa ali muZiyoni;

ndipo udzaona zokoma zaYerusalemumasiku onse a moyo wako.

6 Inde, udzaona zidzukulu zako.

Mtendere ukhale ndi Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/128-8627e2c90ea4f24759ec93550f80d408.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 129

Israele asautsidwa koma osafafanizidwa

Nyimbo yokwerera.

1 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga,

anene tsono Israele;

2 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga;

koma sanandilake.

3 Olima analima pamsana panga;

anatalikitsa mipere yao.

4 Yehova ndiye wolungama;

anadulatu zingwe za oipa.

5 Achite manyazi nabwerere m’mbuyo.

Onse akudana nayeZiyoni.

6 Akhale ngati udzu womera patsindwi,

wakufota asanauzule;

7 umene womweta sadzaza nao dzanja lake,

kapena womanga mitolo sakupatira manja.

8 Angakhale opitirirapo sanena,

Dalitso la Mulungu likhale pa inu;

tikudalitsani m’dzina la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/129-93250a4a1c17089c758d1fec58b2d20a.mp3?version_id=1068—