Categories
MASALIMO

MASALIMO 110

Ufumu wa Ambuye

Salimo la Davide.

1 Yehova ananena kwa Ambuye wanga,

Khalani padzanja lamanja langa,

kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.

2 Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera kuZiyoni;

chitani ufumu pakati pa adani anu.

3 Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu:

M’moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha,

muli nao mame a ubwana wanu.

4 Yehova walumbira, ndipo sadzasintha,

Inu ndinu wansembe kosatha

monga mwa chilongosoko chaMelkizedeki.

5 Ambuye padzanja lamanja lako

adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.

6 Adzaweruza mwaamitundu,

adzadzaza dziko ndi mitembo;

adzaphwanya mitu m’maiko ambiri.

7 Adzamwa kumtsinje wa panjira;

chifukwa chake adzaweramutsa mutu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/110-cb1ea9992b1b11c76287ea4ef90ccbb9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 111

Alemekeza Mulungu pa ntchito zao zazikulu zokoma

1 Aleluya.

Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,

mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.

2 Ntchito za Yehova nzazikulu,

zofunika ndi onse akukondwera nazo.

3 Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu:

Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha.

4 Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake;

Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.

5 Anapatsa akumuopa Iye chakudya;

adzakumbukirachipanganochake kosatha.

6 Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake,

pakuwapatsa cholowa chaamitundu.

7 Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo;

malangizo ake onse ndiwo okhulupirika.

8 Achirikizika kunthawi za nthawi,

achitika m’choonadi ndi chilunjiko.

9 Anatumizira anthu ake chipulumutso;

analamulira chipangano chake kosatha;

dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.

10 Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru;

onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma;

chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/111-48a698421ca28f8091fe9ff011fd8829.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 112

Adalitsidwa akuopa Mulungu

1 Aleluya.

Wodala munthu wakuopa Yehova,

wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

2 Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi;

mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

3 M’nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma:

Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.

4 Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima;

Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.

5 Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa;

adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.

6 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse;

wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.

7 Sadzaopa mbiri yoipa;

mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.

8 Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha,

kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi;

chilungamo chake chikhalitsa kosatha;

nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.

10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;

adzakukuta mano, nadzasungunuka;

chokhumba oipa chidzatayika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/112-54499c8107a4ce09f7f943fb8a67cffa.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 113

Anthu onse alemekeze dzina la Mulungu wothandiza aumphawi

1 Aleluya;

Lemekezani, inu atumiki a Yehova;

lemekezani dzina la Yehova.

2 Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha.

3 Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake

lilemekezedwe dzina la Yehova.

4 Yehova akwezeka pamwamba paamitunduonse,

ulemerero wake pamwambamwamba.

5 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?

Amene akhala pamwamba patali,

6 nadzichepetsa apenye

zam’mwamba ndi za padziko lapansi.

7 Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi,

nakweza waumphawi kumchotsa kudzala.

8 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu,

pamodzi ndi akulu a anthu ake.

9 Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana,

akhale mai wokondwera ndi ana.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/113-80e0287586e593a9476072f8b40eebd9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 114

Alemekeze Mulungu pa chipulumutso chija cha mu Ejipito

1 M’mene Israele anatuluka ku Ejipito,

nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;

2 Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.

3 Nyanjayo inaona, nithawa;

Yordani anabwerera m’mbuyo.

4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,

timapiri ngati anaankhosa.

5 Unathawanji nawe, nyanja iwe?

Unabwereranji m’mbuyo, Yordani iwe?

6 Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu?

Ngati anaankhosa, zitunda inu?

7 Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye,

pamaso pa Mulungu wa Yakobo;

8 amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi,

nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/114-5ab6e84572c010674e158936ab27822a.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 115

Mulungu ndi wa ulemerero, mafano ndiwo achabe

1 Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai,

koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,

chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.

2 Aneneranjiamitundu,

Ali kuti Mulungu wao?

3 Koma Mulungu wathu ndiye ali m’mwamba;

achita chilichonse chimkonda.

4 Mafano ao ndiwo asilivandi golide,

ntchito za manja a anthu.

5 Pakamwa ali napo, koma osalankhula;

maso ali nao, koma osapenya;

6 makutu ali nao, koma osamva;

mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;

7 manja ali nao, koma osagwira;

mapazi ali nao, koma osayenda;

kapena sanena pammero pao.

8 Adzafanana nao iwo akuwapanga;

ndi onse akuwakhulupirira.

9 Israele, khulupirira Yehova:

Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.

10 Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:

Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao.

11 Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;

ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.

12 Yehova watikumbukira; adzatidalitsa:

adzadalitsa nyumba ya Israele;

adzadalitsa nyumba ya Aroni.

13 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,

aang’ono ndi aakulu.

14 Yehova akuonjezereni dalitso,

inu ndi ana anu.

15 Odalitsika inu a kwa Yehova,

wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;

koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.

17 Akufa salemekeza Yehova,

kapena aliyense wakutsikira kuli chete:

18 Koma ife tidzalemekeza Yehova

kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/115-0d615b1f7103a4c1fa3eacfa1fef0728.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 116

Chikondi ndi chiyamiko cha pa Mulungu chifukwa cha chipulumutso chake

1 Ndimkonda, popeza Yehova amamva

mau anga ndi kupemba kwanga.

2 Popeza amanditcherera khutu lake,

chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.

3 Zingwe za imfa zinandizinga,

ndi zowawa za manda zinandigwira:

ndinapeza nsautso ndi chisoni.

4 Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova;

ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.

5 Yehova ngwa chifundo ndi wolungama;

ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.

6 Yehova asunga opusa;

ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.

7 Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;

pakuti Yehova anakuchitira chokoma.

8 Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,

maso anga kumisozi,

mapazi anga, ndingagwe.

9 Ndidzayenda pamaso pa Yehova

m’dziko la amoyo.

10 Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula;

ndinazunzika kwambiri.

11 Pofulumizidwa mtima ndinati ine,

anthu onse nga mabodza.

12 Ndidzabwezera Yehova chiyani

chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?

13 Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso,

ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

14 Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,

tsopano, pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya okondedwa ake

nja mtengo wake pamaso pa Yehova.

16 Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu;

ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;

mwandimasulira zondimanga.

17 Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko,

ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

18 Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,

tsopano, pamaso pa anthu ake onse.

19 M’mabwalo a nyumba ya Yehova,

pakati pa inu,Yerusalemu.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/116-3178daf74cb0be201f61ae679bf87313.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 117

Alemekezedwe Mulungu pa chifundo chake

1 Lemekezani Yehova,amitunduonse;

muimbireni, anthu onse.

2 Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu;

ndi choonadi cha Yehova nchosatha.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/117-dd33831ee49cc4e0997665d126bdbd45.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 118

Wa Salimo alemekeza Mulungu womlanditsa m’manja mwa adani

1 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

2 Anene tsono Israele,

kuti chifundo chake nchosatha.

3 Anene tsono nyumba ya Aroni,

kuti chifundo chake nchosatha.

4 Anene tsono iwo akuopa Yehova,

kuti chifundo chake nchosatha.

5 M’mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;

anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.

6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;

adzandichitanji munthu?

7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;

m’mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.

8 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

koposa kukhulupirira munthu.

9 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

koposa kukhulupirira akulu.

10 Amitunduonse adandizinga,

zedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

11 Adandizinga, inde, adandizinga:

Indedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

12 Adandizinga ngati njuchi;

anazima ngati moto waminga;

indedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

13 Kundikankha anandikankha ndikadagwa;

koma Yehova anandithandiza.

14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

ndipo anakhala chipulumutso changa.

15 M’mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera

Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:

16 Dzanja lamanja la Yehova likwezeka,

Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,

ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.

18 Kulanga anandilangadi Yehova:

koma sanandipereke kuimfa ai.

19 Nditsegulireni zipata za chilungamo;

ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.

20 Chipata cha Yehova ndi ichi;

olungama adzalowamo.

21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,

ndipo munakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene omangawo anaukana

wakhala mutu wa pangodya.

23 Ichi chidzera kwa Yehova;

nchodabwitsa ichi pamaso pathu.

24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;

tidzasekera ndi kukondwera m’mwemo.

25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;

tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.

26 Wodala wakudzayo m’dzina la Yehova;

takudalitsani kochokera m’nyumba ya Yehova.

27 Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;

mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;

ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,

pakuti chifundo chake nchosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/118-ea1f8e4aa14fcd99c2b772e2e0d4c19c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 119

Chilamulo cha Mulungu ndi chokometsetsa. Adalitsidwa akuchisunga

1 Odala angwiro m’mayendedwe ao,

akuyenda m’chilamulo cha Yehova.

2 Odala iwo akusunga mboni zake,

akumfuna ndi mtima wonse;

3 inde, sachita chosalungama;

ayenda m’njira zake.

4 Inu munatilamulira,

tisamalire malangizo anu ndi changu.

5 Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga

kuti ndisamalire malemba anu.

6 Pamenepo sindidzachita manyazi,

pakupenyerera malamulo anu onse.

7 Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka,

pakuphunzira maweruzo anu olungama.

8 Ndidzasamalira malemba anu:

Musandisiye ndithu.

9 Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?

Akawasamalira monga mwa mau anu.

10 Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;

ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.

11 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,

kuti ndisalakwire Inu.

12 Inu ndinu wodala Yehova;

ndiphunzitseni malemba anu.

13 Ndinafotokozera ndi milomo yanga

maweruzo onse a pakamwa panu.

14 Ndinakondwera m’njira ya mboni zanu,

koposa ndi chuma chonse.

15 Ndidzalingirira pa malangizo anu,

ndi kupenyerera mayendedwe anu.

16 Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;

sindidzaiwala mau anu.

17 Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;

ndipo ndidzasamalira mau anu.

18 Munditsegulire maso, kuti ndipenye

zodabwitsa za m’chilamulo chanu.

19 Ine ndine mlendo padziko lapansi;

musandibisire malamulo anu.

20 Mtima wanga wasweka ndi kukhumba

maweruzo anu nyengo zonse.

21 Munadzudzula odzikuza otembereredwa,

iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.

22 Mundichotsere chotonza, ndi chimpepulo;

pakuti ndinasunga mboni zanu.

23 Nduna zomwe zinakhala zondineneza;

koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.

24 Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa,

ndizo zondipangira nzeru.

25 Moyo wanga umamatika ndi fumbi;

mundipatse moyo monga mwa mau anu.

26 Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:

Mundiphunzitse malemba anu.

27 Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;

kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.

28 Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni:

Mundilimbitse monga mwa mau anu.

29 Mundichotsere njira ya chinyengo;

nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu.

30 Ndinasankha njira yokhulupirika;

ndinaika maweruzo anu pamaso panga.

31 Ndimamatika nazo mboni zanu;

musandichititse manyazi, Yehova.

32 Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,

mutakulitsa mtima wanga.

33 Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;

ndidzaisunga kufikira kutha kwake.

34 Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;

ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.

35 Mundiyendetse mopita malamulo anu;

pakuti ndikondwera m’menemo.

36 Lingitsani mtima wanga kumboni zanu,

si ku chisiriro ai.

37 Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe,

mundipatse moyo mu njira yanu.

38 Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,

ndiye wodzipereka kukuopani.

39 Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho;

popeza maweruzo anu ndi okoma.

40 Taonani, ndinalira malangizo anu;

mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.

41 Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova,

ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu.

42 Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;

popeza ndikhulupirira mau anu.

43 Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga;

pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.

44 Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalire

kunthawi za nthawi.

45 Ndipo ndidzayenda mwaufulu;

popeza ndinafuna malangizo anu.

46 Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,

osachitapo manyazi.

47 Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,

amene ndiwakonda.

48 Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;

ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.

49 Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu,

amene munandiyembekezetsa nao.

50 Chitonthozo changa m’kuzunzika kwanga ndi ichi;

pakuti mau anu anandipatsa moyo.

51 Odzikuza anandinyoza kwambiri:

koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.

52 Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,

ndipo ndinadzitonthoza.

53 Ndinasumwa kwakukulu,

chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.

54 Malemba anu anakhala nyimbo zanga

m’nyumba ya ulendo wanga.

55 Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova,

ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.

56 Ichi ndinali nacho,

popeza ndinasunga malangizo anu.

57 Yehova ndiye gawo langa:

Ndinati ndidzasunga mau anu.

58 Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:

Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.

59 Ndinaganizira njira zanga,

ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.

60 Ndinafulumira, osachedwa,

kusamalira malamulo anu.

61 Anandikulunga nazo zingwe za oipa;

koma sindinaiwale chilamulo chanu.

62 Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani

chifukwa cha maweruzo anu olungama.

63 Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,

ndi iwo akusamalira malangizo anu.

64 Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, Yehova;

mundiphunzitse malemba anu.

65 Munachitira mtumiki wanu chokoma, Yehova,

monga mwa mau anu.

66 Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru;

pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.

67 Ndisanazunzidwe ndinasokera;

koma tsopano ndisamalira mau anu.

68 Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino;

mundiphunzitse malemba anu.

69 Odzikuza anandipangira bodza:

Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

70 Mtima wao unona ngati mafuta;

koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.

71 Kundikomera kuti ndinazunzidwa;

kuti ndiphunzire malemba anu.

72 Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera

koposa golide ndisilivazikwizikwi.

73 Manja anu anandilenga nandiumba;

mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.

74 Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;

popeza ndayembekezera mau anu.

75 Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,

ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

76 Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani,

monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.

77 Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo;

popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.

78 Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza:

Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.

79 Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,

ndipo adzadziwa mboni zanu.

80 Mtima wanga ukhale wangwiro m’malemba anu;

kuti ndisachite manyazi.

81 Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu:

Ndinayembekezera mau anu.

82 Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,

ndikuti, Mudzanditonthoza liti?

83 Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;

koma sindiiwala malemba anu.

84 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?

Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?

85 Odzikuza anandikumbira mbuna,

ndiwo osasamalira chilamulo chanu.

86 Malamulo anu onse ngokhulupirika;

andilondola nalo bodza; ndithandizeni.

87 Akadandithera padziko lapansi;

koma ine sindinasiye malangizo anu.

88 Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu;

ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.

89 Mau anu aikika kumwamba,

kosatha, Yehova.

90 Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo;

munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.

91 Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero;

pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.

92 Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa,

ndikadatayika m’kuzunzika kwanga.

93 Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;

popeza munandipatsa nao moyo.

94 Ine ndine wanu, ndipulumutseni

pakuti ndinafuna malangizo anu.

95 Oipa anandilalira kundiononga;

koma ndizindikira mboni zanu.

96 Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse;

koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.

97 Ha! Ndikondadi chilamulo chanu;

ndilingiriramo ine tsiku lonse.

98 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;

pakuti akhala nane chikhalire.

99 Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;

pakuti ndilingalira mboni zanu.

100 Ndizindikira koposa okalamba

popeza ndinasunga malangizo anu.

101 Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa,

kuti ndisamalire mau anu.

102 Sindinapatukane nao maweruzo anu;

pakuti Inu munandiphunzitsa.

103 Mau anu azunadi powalawa ine!

Koposa uchi m’kamwa mwanga.

104 Malangizo anu andizindikiritsa;

chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.

105 Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,

ndi kuunika kwa panjira panga.

106 Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,

kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.

107 Ndazunzika kwambiri:

Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.

108 Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,

ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.

109 Moyo wanga ukhala m’dzanja langa chikhalire;

koma sindiiwala chilamulo chanu.

110 Oipa ananditchera msampha;

koma sindinasokere m’malangizo anu.

111 Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha;

pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.

112 Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu,

kosatha, kufikira chimaliziro.

113 Ndidana nao a mitima iwiri;

koma ndikonda chilamulo chanu.

114 Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa;

ndiyembekezera mau anu.

115 Mundichokere ochita zoipa inu;

kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.

116 Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;

ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa.

117 Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,

ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire.

118 Mupepula onse akusokera m’malemba anu;

popeza chinyengo chao ndi bodza.

119 Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala:

Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.

120 Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;

ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.

121 Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo;

musandisiyira akundisautsa.

122 Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere;

odzikuza asandisautse.

123 Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu,

ndi mau a chilungamo chanu.

124 Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu,

ndipo ndiphunzitseni malemba anu.

125 Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;

kuti ndidziwe mboni zanu.

126 Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu;

pakuti anaswa chilamulo chanu.

127 Chifukwa chake ndikonda malamulo anu

koposa golide, inde golide woyengeka.

128 Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika

malangizo anu onse akunena zonse;

koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.

129 Mboni zanu nzodabwitsa;

chifukwa chake moyo wanga uzisunga.

130 Potsegulira mau anu paunikira;

kuzindikiritsa opusa.

131 Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu;

popeza ndinakhumba malamulo anu.

132 Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo,

monga mumatero nao akukonda dzina lanu.

133 Khazikitsani mapazi anga m’mau anu;

ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.

134 Mundiombole kunsautso ya munthu:

Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.

135 Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;

ndipo mundiphunzitse malemba anu.

136 Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi,

popeza sasamalira chilamulo chanu.

137 Inu ndinu wolungama, Yehova,

ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

138 Mboni zanuzo mudazilamulira

zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.

139 Changu changa chinandithera,

popeza akundisautsa anaiwala mau anu.

140 Mau anu ngoyera ndithu;

ndi mtumiki wanu awakonda.

141 Wamng’ono ine, ndi wopepulidwa;

koma sindiiwala malemba anu.

142 Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha;

ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

143 Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;

koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

144 Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;

mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.

145 Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;

ndidzasunga malemba anu.

146 Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,

ndipo ndidzasamalira mboni zanu.

147 Ndinafuula kusanake:

ndinayembekezera mau anu.

148 Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku,

kuti ndilingirire mau anu.

149 Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu;

mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

150 Otsata zachiwembu andiyandikira;

akhala kutali ndi chilamulo chanu.

151 Inu muli pafupi, Yehova;

ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.

152 Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,

kuti munazikhazika kosatha.

153 Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;

pakuti sindiiwala chilamulo chanu.

154 Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;

mundipatse moyo monga mwa mau anu.

155 Chipulumutso chitalikira oipa;

popeza safuna malemba anu.

156 Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova;

mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.

157 Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri;

koma sindinapatukane nazo mboni zanu.

158 Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;

popeza sasamalira mau anu.

159 Penyani kuti ndikonda malangizo anu;

mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu.

160 Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi;

ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.

161 Nduna zinandilondola kopanda chifukwa;

koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu.

162 Ndikondwera nao mau anu,

ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.

163 Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;

koma ndikonda chilamulo chanu.

164 Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,

chifukwa cha maweruzo anu olungama.

165 Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri;

ndipo alibe chokhumudwitsa.

166 Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova,

ndipo ndinachita malamulo anu.

167 Moyo wanga unasamalira mboni zanu;

ndipo ndizikonda kwambiri.

168 Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;

popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.

169 Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova;

mundizindikiritse monga mwa mau anu.

170 Kupemba kwanga kudze pamaso panu;

mundilanditse monga mwa mau anu.

171 Milomo yanga itulutse chilemekezo;

popeza mundiphunzitsa malemba anu.

172 Lilime langa liimbire mau anu;

pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.

173 Dzanja lanu likhale lakundithandiza;

popeza ndinasankha malangizo anu.

174 Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova;

ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.

175 Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;

ndipo maweruzo anu andithandize.

176 Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu;

pakuti sindiiwala malamulo anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/119-58c604d3573d228e8e4d87bb21504897.mp3?version_id=1068—