Israele anapikisana ndi Yehova kwambiri, Iye nawalanga nawalanditsanso. Amlemekezepo
1 Aleluya.
Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino:
Pakuti chifundo chake nchosatha.
2 Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova,
adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?
3 Odala iwo amene asunga chiweruzo,
iye amene achita chilungamo nthawi zonse.
4 Mundikumbukire, Yehova,
monga momwe muvomerezana ndi anthu anu;
mundionetsa chipulumutso chanu:
5 Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu,
kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu,
kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.
6 Talakwa pamodzi ndi makolo athu;
tachita mphulupulu, tachita choipa.
7 Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito;
sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji;
koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
8 Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
kuti adziwitse chimphamvu chake.
9 Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa:
Potero anawayendetsa mozama ngati m’chipululu.
10 Ndipo anawapulumutsa m’dzanja la iye amene anawada,
nawaombola kudzanja la mdani.
11 Ndipo madziwo anamiza owasautsa;
sanatsale mmodzi yense.
12 Pamenepo anavomereza mau ake;
anaimbira chomlemekeza.
13 Koma anaiwala ntchito zake msanga;
sanalindire uphungu wake:
14 Popeza analakalakatu kuchidikhako,
nayesa Mulungu m’chipululu.
15 Ndipo anawapatsa chopempha iwo;
koma anaondetsa mitima yao.
16 Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose
ndi Aroni woyerayo wa Yehova.
17 Dziko lidayasama nilidameza Datani,
ndipo linafotsera gulu la Abiramu.
18 Ndipo m’gulu mwao mudayaka moto;
lawi lake lidapsereza oipawo.
19 Anapanga mwanawang’ombe ku Horebu,
nagwadira fano loyenga.
20 M’mwemo anasintha ulemerero wao
ndi fanizo la ng’ombe yakudya msipu.
21 Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao,
amene anachita zazikulu mu Ejipito;
22 zodabwitsa m’dziko la Hamu,
zoopsa ku Nyanja Yofiira.
23 Potero Iye adati awaononge,
pakadapanda Mose wosankhika wake,
kuima pamaso pake pogamukapo,
kubweza ukali wake ungawaononge.
24 Anapeputsanso dziko lofunika,
osavomereza mau ake;
25 koma anadandaula m’mahema mwao,
osamvera mau a Yehova.
26 Potero anawasamulira dzanja lake,
kuti awagwetse m’chipululu:
27 Kugwetsanso mbeu zao mwaamitundu,
ndi kuwabalalitsa m’maiko maiko.
28 Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori,
nadyanso nsembe za akufa.
29 Ndipo anamkwiyitsa nazo zochita zao;
kotero kuti mliri unawagwera.
30 Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango:
Ndi mliriwo unaletseka.
31 Ndipo adamuyesa iye wachilungamo,
ku mibadwomibadwo kunthawi zonse.
32 Anautsanso mkwiyo wake kumadzi a Meriba,
ndipo kudaipira Mose chifukwa cha iwowa:
33 Pakuti anawawitsa mzimu wake,
ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yake.
34 Sanaononga mitunduyo ya anthu,
imene Yehova adawauza;
35 koma anasokonekerana nao amitundu,
naphunzira ntchito zao:
36 Ndipo anatumikira mafano ao,
amene anawakhalira msampha:
37 Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,
38 nakhetsa mwazi wosachimwa,
ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi,
amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani;
m’mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.
39 Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao,
nachita chigololo nao machitidwe ao.
40 Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake,
nanyansidwa Iye ndi cholowa chake.
41 Ndipo anawapereka m’manja a amitundu;
ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.
42 Adani ao anawasautsanso,
nawagonjetsa agwire mwendo wao.
43 Iye anawalanditsa kawirikawiri;
koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao,
ndi mphulupulu zao zinawafoketsa.
44 Koma anapenya nsautso yao,
pakumva kufuula kwao:
45 Ndipo anawakumbukirachipanganochake,
naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.
46 Ndipo anawachitira kuti apeze nsoni
pamaso pa onse amene adawamanga ndende.
47 Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu,
ndi kutisokolotsa kwa amitundu,
kuti tiyamike dzina lanu loyera,
ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.
48 Wodala Yehova, Mulungu wa Israele,
kuyambira kosayamba kufikira kosatha.
Ndi anthu onse anene,Amen.
Aleluya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/106-38135923c8802db246d8450c9533e008.mp3?version_id=1068—