Categories
MASALIMO

MASALIMO 90

Mulungu ndiye wachikhalire, munthu ndiye wakutha msanga

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

1 Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo

m’mibadwomibadwo.

2 Asanabadwe mapiri,

kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,

inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,

Inu ndinu Mulungu.

3 Mubweza munthu akhale fumbi;

nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.

4 Pakuti pamaso panu zaka zikwi

zikhala ngati dzulo, litapita,

ndi monga ulonda wa usiku.

5 Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo;

mamawa akhala ngati msipu wophuka.

6 Mamawa uphuka bwino;

madzulo ausenga, nuuma.

7 Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu;

ndipo m’kuzaza kwanu tiopsedwa.

8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,

ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.

9 Pakuti masiku athu onse apitirira mu ukali wanu;

titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.

10 Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri,

kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu;

koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake;

pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.

11 Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,

ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

12 Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,

kuti tikhale nao mtima wanzeru.

13 Bwerani, Yehova; kufikira liti?

Ndipo alekeni atumiki anu.

14 Mutikhutitse nacho chifundo chanu m’mawa;

ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.

15 Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa,

ndi zaka tidaona choipa.

16 Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu,

ndi ulemerero wanu pa ana ao.

17 Ndipo chisomo chake cha Ambuye Mulungu wathu chikhalire pa ife;

ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu;

inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/90-f23d46ae4557ce62afa33168355e0332.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 91

Mulungu asungadi wodzipereka kwa Iye

1 Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba

adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

2 Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;

Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

3 Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi,

kumliri wosakaza.

4 Adzakufungatira ndi nthenga zake,

ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake;

choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

5 Sudzaopa choopsa cha usiku,

kapena muvi wopita usana;

6 kapena mliri woyenda mumdima,

kapena chionongeko chakuthera usana.

7 Pambali pako padzagwa chikwi,

ndi zikwi khumi padzanja lamanja lako;

sichidzakuyandikiza iwe.

8 Koma udzapenya ndi maso ako,

nudzaona kubwezera chilango oipa.

9 Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga!

Udaika Wam’mwambamwamba chokhalamo chako;

10 palibe choipa chidzakugwera,

ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

11 Pakuti adzalamuliraangeloake za iwe,

akusunge m’njira zako zonse.

12 Adzakunyamula pa manja ao,

ungagunde phazi lako pamwala.

13 Udzaponda mkango ndi mphiri;

udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

14 Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;

ndidzamkweza m’mwamba, popeza adziwa dzina langa.

15 Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha;

kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;

ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

16 Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,

ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/91-f6c6a65bedf2646c3fe08f32811e404e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 92

Anthu onse ayamike Mulungu chifukwa cha ntchito zake, chilungamo chake, ndi chifundo chake

Salimo, Nyimbo ya pa Sabata.

1 Nkokoma kuyamika Yehova,

ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu.

2 Kuonetsera chifundo chanu mamawa,

ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.

3 Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa;

pazeze ndi kulira kwake.

4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu,

ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.

5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova,

zolingalira zanu nzozama ndithu.

6 Munthu wopulukira sachidziwa;

ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;

7 chakuti pophuka oipa ngati msipu,

ndi popindula ochita zopanda pake;

chitero kuti adzaonongeke kosatha.

8 Koma Inu, Yehova, muli m’mwamba kunthawi yonse.

9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,

pakuti, taonani, adani anu adzatayika;

ochita zopanda pake onse adzamwazika.

10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;

anandidzoza mafuta atsopano.

11 Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira,

m’makutu mwanga ndamva chokhumba ine

pa iwo akuchita zoipa akundiukira.

12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;

adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

13 Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova,

adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu.

14 Atakalamba adzapatsanso zipatso;

adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,

15 kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;

Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/92-932cff6c0bcd754f622cfa753d8f06fc.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 93

Ufumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi chiyero

1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu;

wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m’chuuno;

dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.

2 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;

Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.

3 Mitsinje ikweza, Yehova,

mitsinje ikweza mkokomo wao;

mitsinje ikweza mafunde ao.

4 Yehova Wam’mwamba ndiye wamphamvu,

wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,

ndi mafunde olimba a nyanja.

5 Mboni zanu zivomerezeka ndithu;

chiyero chiyenera nyumba yanu,

Yehova, kunthawi za muyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/93-31e10020bca2d40d7747c9da21afd644.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 94

Mulungu wolungama adzaweruza oipa

1 Mulungu wakubwezera chilango,

Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.

2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:

Bwezerani odzikuza choyenera iwo.

3 Oipa adzatumpha ndi chimwemwe kufikira liti, Yehova?

Oipa adzatero kufikira liti?

4 Anena mau, alankhula zowawa;

adzitamandira onse ochita zopanda pake.

5 Aphwanya anthu anu, Yehova,

nazunza cholowa chanu.

6 Amapha wamasiye ndi mlendo,

nawapha ana amasiye.

7 Ndipo amati, Yehova sachipenya,

ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira.

8 Zindikirani, opulukira inu mwa anthu;

ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?

9 Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?

Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

10 Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?

Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?

11 Yehova adziwa zolingalira za munthu,

kuti zili zachabe.

12 Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;

ndi kumphunzitsa m’chilamulo chanu;

13 kuti mumpumitse masiku oipa;

kufikira atakumbira woipa mbuna.

14 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake,

ndipo sadzataya cholowa chake.

15 Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo,

ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.

16 Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa?

Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?

17 Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,

moyo wanga ukadakhala kuli chete.

18 Pamene ndinati, Literereka phazi langa,

chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.

19 Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga,

zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

20 Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza,

wakupanga chovuta chikhale lamulo?

21 Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama,

namtsutsa wa mwazi wosachimwa.

22 Koma Yehova wakhala msanje wanga;

ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

23 Ndipo anawabwezera zopanda pake zao,

nadzawaononga m’choipa chao;

Yehova Mulungu wathu adzawaononga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/94-5b364ab52b3af2c250190f9d84302da4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 95

Adandaulira anthu alemekeze namvere Mulungu wao wamkulu

1 Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera;

tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.

2 Tidze nacho chiyamiko pamaso pake,

timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.

3 Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu;

ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.

4 Malo ozama a dziko lapansi ali m’dzanja lake;

chuma cha m’mapiri chomwe ndi chake.

5 Nyanja ndi yake, anailenga;

ndipo manja ake anaumba dziko louma.

6 Tiyeni, tipembedze tiwerame;

tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.

7 Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,

ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,

ndi nkhosa za m’dzanja mwake.

Lero, mukamva mau ake!

8 Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,

ngati tsiku la ku Masa m’chipululu.

9 Pamene makolo anu anandisuntha,

anandiyesa, anapenyanso chochita Ine.

10 Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni,

ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima,

ndipo sadziwa njira zanga.

11 Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga,

ngati adzalowa mpumulo wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/95-34c60166f30781937b950777181dfa92.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 96

Onse a pansi pano ndi am’mwamba omwe alemekeze Mulungu

1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;

muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.

2 Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake;

lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

3 Fotokozerani ulemerero wake mwaamitundu;

zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.

4 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ayenera amuope koposa milungu yonse.

5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano,

koma Yehova analenga zakumwamba.

6 Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu.

M’malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.

7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,

mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

8 Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake;

bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.

9 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa,

njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.

10 Nenani mwaamitundu, Yehova achita ufumu;

dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;

adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.

11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;

nyanja ibume mwa kudzala kwake.

12 Munda ukondwerere ndi zonse zili m’mwemo;

pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera.

13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;

pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi

Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,

ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/96-3de72cfe218307b222ad2e70bf7c0450.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 97

Ulemerero wa ufumu wa Mulungu

1 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;

zisumbu zambiri zikondwerere.

2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;

chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa

mpando wake wachifumu.

3 Moto umtsogolera,

nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.

4 Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;

dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.

5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,

pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6 Kumwamba kulalikira chilungamo chake,

ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.

7 Onse akutumikira fano losema,

akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:

Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

8 Ziyonianamva nakondwera,

nasekerera ana aakazi a Yuda;

chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.

9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi,

ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.

10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:

Iye asunga moyo wa okondedwa ake;

awalanditsa m’manja mwa oipa.

11 Kuunika kufesekera wolungama,

ndi chikondwerero oongoka mtima.

12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;

ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/97-6c65878c73f9e757113cb19d347e9fb8.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 98

Alemekeze Mulungu pa chifundo ndi choonadi chao

Salimo.

1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;

popeza anachita zodabwitsa:

Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera,

zinamchitira chipulumutso.

2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake;

anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.

3 Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake

kunyumba ya Israele;

malekezero onse a dziko lapansi

anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

4 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;

kuwitsani ndi kufuulira mokondwera;

inde, imbirani zomlemekeza.

5 Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze;

ndi zeze ndi mau a salimo.

6 Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova,

ndi mbetete ndi liu la lipenga.

7 Nyanja ifuule ndi kudzala kwake;

dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;

8 mitsinje iombe m’manja;

mapiri afuule pamodzi mokondwera.

9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;

adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,

ndipo mitundu ya anthu molunjika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/98-ac8f04ab9533726087f9e969fcb70cf5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 99

Mulungu wamkulu wachifundo alemekezedwe

1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;

Iye akhala pakati paakerubi; dziko lapansi ligwedezeke.

2 Yehova ndiye wamkulu muZiyoni;

ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.

Ili ndilo loyera.

4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;

Inu mukhazikitsa zolunjika,

muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.

5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:

Iye ndiye Woyera.

6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,

ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;

anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

7 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:

Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.

8 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:

munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,

mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.

9 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani paphiri lake loyera;

pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/99-77e66ae4cdf6bfda694f115ffc645d1e.mp3?version_id=1068—