Categories
MASALIMO

MASALIMO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Ili ndi buku la nyimbo ndi mapemphero. Mau ake adalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa nthawi yaitali, ndipo Aisraele ankagwiritsa ntchito mauwo popembedza Yehova. Masalimowo alipo amitundumitundu: ena ndi nyimbo zotamanda Mulungu, zopembedza, kapena zothokoza; ena ndi mau opempha chithandizo ndi chitetezo pa nthawi ya mavuto, ena ndi mau olapa ndi opepesera machimo, mau opempha chikhululukiro, mwinanso mau opempha Mulungu kuti alange adani. Masalimowo ngothandiza anthu pakupemphera, aliyense molingana ndi zimene zadzaza mumtima wake, komanso moganizira zosowa za anthu onse a Mulungu ndi ubwino wao. Yesu nayenso ankagwiritsa ntchito Masalimowo popemphera; ndipo kuyambira pa chiyambi cha Mpingo, Akhristu akhala akugwiritsa ntchito buku lomwelo pamwambo wachipembedzo.

Za mkatimu

Bukuli lili ndi zigawo zisanu:

Masalimo 1 mpaka 41

Masalimo 42 mpaka 72

Masalimo 73 mpaka 89

Masalimo 90 mpaka 106

Masalimo 107 mpaka 150

Categories
MASALIMO

MASALIMO 1

Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa

1 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,

kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa,

kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2 Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake;

ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.

3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;

wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake,

tsamba lake lomwe losafota;

ndipo zonse azichita apindula nazo.

4 Oipa satero ai;

koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5 Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo,

kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.

6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;

koma mayendedwe a oipa adzatayika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/1-7cc95113bd363644c1c5933efc45eb76.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 2

Ufumu wa wodzozedwa wa Yehova

1 Aphokoseranjiamitundu,

nalingiriranji anthu zopanda pake?

2 Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi,

nachita upo akulu pamodzi,

Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,

3 Tidule zomangira zao,

titaye nsinga zao.

4 Wokhala m’mwambayo adzaseka;

Ambuye adzawanyoza.

5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake,

nadzawaopsa mu ukali wake.

6 Koma Ine ndadzoza mfumu yanga

PaZiyoni, phiri langa loyera.

7 Ndidzauza za chitsimikizo:

Yehova ananena ndi Ine,

Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.

8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu

akhale cholowa chako,

ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.

9 Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo;

udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.

10 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru;

langikani, oweruza inu a dziko lapansi.

11 Tumikirani Yehova ndi mantha,

ndipo kondwerani ndi chinthenthe.

12 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye,

ndipo mungatayike m’njira

ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake.

Odala onse akumkhulupirira Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/2-0cb4e5951d6c2f03d6a79956f669cf45.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 3

Kukhulupirika kwa Mulungu

Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wake.

1 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine!

Akundiukira ine ndi ambiri.

2 Ambiri amati kwa moyo wanga,

alibe chipulumutso mwa Mulungu.

3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa;

ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga,

ndipo andiyankha m’phiri lake loyera.

5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;

ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.

6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.

7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!

Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;

mwawathyola mano oipawo.

8 Chipulumutso ncha Yehova;

dalitso lanu likhale pa anthu anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/3-60f1eca1f3eec23e92384018de71d6bc.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 4

Pemphero posautsidwa

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.

1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa;

pondichepera mwandikulitsira malo.

Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.

2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?

Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?

3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo,

adzamva Yehova m’mene ndimfuulira Iye.

4 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.

Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.

5 Iphani nsembe za chilungamo,

ndipo mumkhulupirire Yehova.

6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani?

Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

7 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga,

chakuposa chao m’nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.

8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;

chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/4-41ebdc08e25d9ab62ee6ed79d53b14ad.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 5

Matsoka a oipa, madalitso a olungama

Kwa Mkulu wa Nyimbo: aimbire zitoliro. Salimo la Davide.

1 Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.

2 Tamvetsani mau a kufuula kwanga,

Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga;

pakuti kwa Inu ndimapemphera.

3 M’mawa, Yehova, mudzamva mau anga;

m’mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.

4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa

mphulupulu siikhala ndi Inu.

5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu,

mudana nao onse akuchita zopanda pake.

6 Mudzaononga iwo akunena bodza;

munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo,

Yehova anyansidwa naye.

7 Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu

ndidzalowa m’nyumba yanu;

ndidzagwada kuyang’ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.

8 Yehova, munditsogolere m’chilungamo chanu,

chifukwa cha akundizondawo;

mulungamitse njira yanu pamaso panga.

9 Pakuti m’kamwa mwao mulibe mau okhazikika;

m’kati mwao m’mosakaza;

m’mero mwao ndi manda apululu;

lilime lao asyasyalika nalo.

10 Muwayese otsutsika Mulungu;

agwe nao uphungu wao.

M’kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse;

pakuti anapikisana ndi Inu.

11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,

afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;

nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

12 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;

mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/5-7ac8e9291abfdad07ec8a74c1b4764ae.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 6

Davide apempha chifundo kwa Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto, pa Seminiti. Salimo la Davide.

1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,

ndipo musandilange muukali wanu.

2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine.

Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.

3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu;

ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?

4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;

ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.

5 Pakuti muimfa m’mosakumbukira Inu;

m’mandamo adzakuyamikani ndani?

6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga;

ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;

mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

7 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni;

lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.

8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake;

pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.

9 Wamva Yehova kupemba kwanga;

Yehova adzalandira pemphero langa.

10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu

adani anga onse;

adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/6-12e6ac2c0a2d65440fbb65d805f91b7a.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 7

Adani amzinga, Davide adziponya kwa Mulungu

Syigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini.

1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu;

mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

2 kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,

ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.

3 Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi;

ngati m’manja anga muli chosalungama;

4 ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine;

(inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);

5 mdani alondole moyo wanga, naupeze;

naupondereze pansi moyo wanga,

naukhalitse ulemu wanga m’fumbi.

6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,

nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa;

ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.

7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;

ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba.

8 Yehova aweruza anthu mlandu;

mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa,

ndi ungwiro wanga uli mwa ine.

9 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani,

koma wolungamayo mumkhazikitse.

Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.

10 Chikopa changa chili ndi Mulungu,

wopulumutsa oongoka mtima.

11 Mulungu ndiye Woweruza wolungama,

ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

12 Akapanda kutembenuka munthu,

iye adzanola lupanga lake;

wakoka uta wake, naupiringidza.

13 Ndipo anamkonzera zida za imfa;

mivi yake aipanga ikhale yansakali.

14 Taonani, ali m’chikuta cha zopanda pake;

anaima ndi chovuta, nabala bodza.

15 Anachita dzenje, nalikumba,

nagwa m’mbuna yomwe anaikumba.

16 Chovuta chake chidzambwerera mwini,

ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.

17 Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake;

ndipo ndidzaimbira Yehova Wam’mwambamwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/7-a085905e3182f7625fd62b99645e6371.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 8

Davide aimbira ulemerero wa Mulungu, ndi ulemu umene Mulungu achitira mtundu wa anthu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi. Salimo la Davide.

1 Yehova, Ambuye wathu,

dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!

Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.

2 M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu,

chifukwa cha otsutsana ndi Inu,

kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.

3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu,

mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,

4 munthu ndani kuti mumkumbukira?

Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?

5 Pakuti munamchepsa pang’ono ndi Mulungu,

munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

6 Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu;

mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;

7 nkhosa ndi ng’ombe, zonsezo,

ndi nyama zakuthengo zomwe;

8 mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja.

Zopita m’njira za m’nyanja.

9 Yehova, Ambuye wathu,

dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/8-827fd393f5e57445a7dc0fb268d8e7a4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 9

Ayamikira chipulumutso chachikulu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Muti-Labeni. Salimo la Davide.

1 Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse;

ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse.

2 Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu;

ndidzaimbira dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu.

3 Pobwerera m’mbuyo adani anga,

akhumudwa naonongeka pankhope panu.

4 Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga;

mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.

5 Mwadzudzulaamitundu, mwaononga woipayo,

mwafafaniza dzina lao kunthawi yonka muyaya.

6 Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse;

ndipo mizindayo mwaipasula,

chikumbukiro chao pamodzi chatha.

7 Koma Yehova akhala chikhalire,

anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze.

8 Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m’chilungamo,

nadzaweruza anthu molunjika.

9 Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi.

Msanje m’nyengo za nsautso;

10 ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu;

pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.

11 Imbirani zoyamika Yehova, wokhala kuZiyoni;

lalikirani mwa anthu ntchito zake.

12 Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira;

saiwala kulira kwa ozunzika.

13 Ndichitireni chifundo, Yehova;

penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo,

inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.

14 Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;

pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,

ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.

15 Amitundu anagwa m’mbuna imene anaikumba,

lakodwa phazi lao muukonde anautchera.

16 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza,

woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

17 Oipawo adzabwerera kumanda,

inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

18 Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi,

kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.

19 Ukani, Yehova, asalimbike munthu;

amitundu aweruzidwe pankhope panu.

20 Muwachititse mantha, Yehova;

adziwe amitundu kuti ali anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/9-fffea0a1edf8ea5da8db738c323b4b66.mp3?version_id=1068—