Asasiyane mwamuna ndi mkazi wake
1 Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.
2 Ndipo anadza kwa IyeAfarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye.
3 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani?
4 Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa.
5 Koma Yesu anati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili.
6 Koma kuyambira pa chiyambi cha malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi.
7 Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amai wake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake;
8 ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi.
9 Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu.
10 Ndipo m’nyumbaophunziraanamfunsanso za chinthu ichi.
11 Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo;
12 ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.
Yesu adalitsa tiana
13 Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula.
14 Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.
15 Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.
16 Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.
Mnyamata mwini chuma chambiri
17 Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
18 Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.
19 Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
20 Ndipo iye anati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mwana.
21 Ndipo Yesu anamyang’ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.
22 Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri.
23 Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!
24 Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!
25 Nkwa pafupi kutingamiraipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.
26 Ndipo anadabwa, nanena kwa Iye, Ndipo angathe kupulumuka ndani?
27 Yesu anawayang’ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
28 Petro anayamba kunena naye, Onani, ife tinasiya zonse, ndipo tinakutsatani Inu.
29 Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo,
30 amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha.
31 Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.
Ali panjira kukwera ku Yerusalemu
32 Ndipo iwo anali m’njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,
33 nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipoMwana wa Munthuadzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;
34 ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.
Ana a Zebedeo apempha ulemu
35 Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chilichonse tidzapempha kwa Inu.
36 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani?
37 Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ulemerero wanu.
38 Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?
39 Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;
40 koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu.
41 Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane.
42 Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo.
43 Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;
44 ndipo aliyense amene afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse.
45 Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.
Baratimeo wakhungu wa ku Yeriko
46 Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m’mene Iye analikutuluka mu Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m’mbali mwa njira.
47 Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kufuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo.
48 Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo.
49 Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.
50 Ndipo iye anataya chofunda chake, nazunzuka, nadza kwa Yesu.
51 Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.
52 Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/10-a5891fb89c35a2ecb07d1b3d2cd846cf.mp3?version_id=1068—