Categories
MARKO

MARKO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Marko

likuyamba ndi mau akuti ichi ndi “chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu”. Yesu akumuonetsa monga munthu amene akuchita zinthu zambiri komanso waulamuliro. Ulamuliro wake ukuoneka mu chiphunzitso chake, mu mphamvu yake pa ziwanda ndi kuwakhululukira anthu machimo ao. Yesu akudzitchula kuti ndi Mwana wa Munthu, amene anabwera kudzapereka moyo wake kuti awapulumutse anthu ku machimo ao.

Marko

akulemba mbiri ya Yesu mwachimvekere, mwachangu ndi motsindika kwambiri pa zimene Yesu anachita, osati pa mau ake kapena pa chiphunzitso chake. Atanena mwachidule za Yohane Mbatizi ndi za ubatizo wa Yesu, wolembayo akuthamangira kulemba za utumiki wa Yesu wa kuchiritsa ndi kuphunzitsa. Kenaka akutionetsa kuti omutsatira a Yesu anali kumumvetsetsa pamene adani ake anapitirira kudana naye. Mitu yomaliza imakamba zimene Yesu anachita mu sabata yake yomaliza ya utumiki wake pansi pano, makamaka kupachikidwa pamtanda ndi kuukanso kwake.

Za mkatimu

Chiyambi cha Uthenga Wabwino

1.1-13

Utumiki wa Yesu ku Galileya

1.14—9.50

Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu

10.1-52

Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira

11.1—15.47

Kuukanso kwa Yesu

16.1-8

Ambuye woukitsidwayo aonekera nakwera kumwamba

16.9-20

Categories
MARKO

MARKO 1

Yohane Mbatizi

1 Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa YesuKhristu, Mwana wa Mulungu.

2 Monga mwalembedwa mu Yesayamneneri,

Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,

amene adzakonza njira yanu.

3 Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

4 Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.

5 Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a kuYerusalemuonse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.

6 Ndipo Yohane anavala ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo.

7 Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula zingwe za nsapato zake.

8 Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.

Kubatizidwa ndi kuyesedwa kwa Yesu

9 Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.

10 Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m’madzi, anaona Iye thambo litang’ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:

11 ndipo mau anatuluka m’thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

12 Ndipo pomwepo Mzimu anamkakamiza kunka kuchipululu.

13 Ndipo anakhala m’chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndiSatana; nakhala ndi zilombo, ndipoangeloanamtumikira.

Yesu aitana ophunzira ake oyamba

14 Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,

15 nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino.

16 Ndipo pakuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m’nyanja; pakuti anali asodzi.

17 Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.

18 Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.

19 Ndipo atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m’chombo nakonza makoka ao.

20 Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m’chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.

Achiritsidwa wogwidwa ndi chiwanda ku Kapernao

21 Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku laSabataiye analowa m’sunagogenaphunzitsa.

22 Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.

23 Ndipo pomwepo panali munthu m’sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye.

24 Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.

25 Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye.

26 Ndipo mzimu wonyansa, pomng’amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.

27 Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.

28 Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.

Achiritsidwa mpongozi wa Petro ndi odwala ena

29 Ndipo pomwepo, potuluka m’sunagoge, iwo analowa m’nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.

30 Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:

31 ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.

32 Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.

33 Ndipo mzinda wonse unasonkhana pakhomo.

34 Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.

35 Ndipo m’mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.

36 Ndipo Simoni ndi anzake anali naye anamtsata,

37 nampeza, nanena naye, Akufunani Inu anthu onse.

38 Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imeneyi.

39 Ndipo analowa m’masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Yesu achiritsa wakhate

40 Ndipo anadza kwa Iye wodwalakhate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.

41 Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.

42 Ndipo pomwepo khate linamchoka, ndipo anakonzedwa.

43 Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo,

44 nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.

45 Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m’mudzi, koma anakhala padera m’mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/1-cf352c2d6b715dfd62ddd3f707f6522f.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 2

Achiritsa wodwala manjenje

1 Ndipo polowanso Iye mu Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m’nyumba.

2 Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.

3 Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai.

4 Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula tsindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m’mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo.

5 Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.

6 Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,

7 Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?

8 Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m’mitima yanu?

9 Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?

10 Koma kuti mudziwe kutiMwana wa Munthuali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo padziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),

11 Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.

12 Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.

Yesu aitana Levi

13 Ndipo anatulukanso kunka m’mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa.

14 Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.

15 Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m’nyumba mwake, ndipoamisonkhondi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndiophunziraake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.

16 Ndipo alembi a kwaAfarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.

17 Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing’anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.

Kudzikana kudya

18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?

19 Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sangathe kusala.

20 Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.

21 Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo.

22 Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m’matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m’matumba atsopano.

Yesu mwini Sabata

23 Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku laSabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu.

24 Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata?

25 Ndipo ananena nao, Simunawerenge konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?

26 Kuti analowa m’nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

27 Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata;

28 motero Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata lomwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/2-ffab84990ed7d75525d03ade6d2850d2.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 3

Yesu achiritsa wa dzanja lopuwala

1 Ndipo analowanso m’sunagoge; ndipo munali munthu m’menemo ali ndi dzanja lake lopuwala.

2 Ndipo anamuyang’anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku laSabata; kuti ammange mlandu.

3 Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.

4 Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.

5 Ndipo m’mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.

6 NdipoAfarisianatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.

7 Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndiophunziraake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,

8 ndi a kuYerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.

9 Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye,

10 pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.

11 Ndipo mizimu yonyansa, m’mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

12 Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.

Apatula ophunzira khumi ndi awiri

13 Ndipo anakwera m’phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.

14 Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,

15 ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda.

16 Ndipo Simoni anamutcha Petro;

17 ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu;

18 ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,

19 ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye.

Za Yesu ndi Belezebulu

Ndipo analowa m’nyumba.

20 Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.

21 Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.

22 Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali nayeBelezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.

23 Ndipo m’mene adawaitana iwo, ananena nao m’mafanizo,Satanaangathe bwanji kutulutsa Satana?

24 Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sungathe kukhazikika.

25 Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, singathe kukhazikika nyumbayo.

26 Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sangathe kukhazikika, koma atsirizika.

27 Komatu palibe munthu akhoza kulowa m’nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma ayambe wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m’nyumba mwake.

28 Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;

29 koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;

30 pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

Abale ake a Yesu

31 Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.

32 Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.

33 Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?

34 Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.

35 Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/3-7c22451e30212b0d8e077d5bb546ab21.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 4

Fanizo la wofesa

1 Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m’nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m’mbali mwa nyanja.

2 Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m’mafanizo, nanena nao m’chiphunzitso chake,

3 Mverani: taonani, wofesa anatuluka kukafesa;

4 ndipo kunali, m’kufesa kwake, zina zinagwa m’mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya.

5 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya;

6 ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.

7 Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.

8 Ndipo zina zinagwa m’nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

9 Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.

10 Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.

11 Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m’mafanizo;

12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.

13 Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?

Kumasulira kwa fanizo la wofesa

14 Wofesa afesa mau.

15 Ndipo iwo ndiwo a m’mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudzaSatananachotsa mau ofesedwa mwa iwo.

16 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;

17 ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa.

18 Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,

19 ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.

20 Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

Fanizo la nyali

21 Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake?

22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam’tseri, koma kuti kakaululidwe.

23 Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.

24 Ndipo ananena nao, Yang’anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.

25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako.

Fanizo la mbeu

26 Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;

27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.

28 Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m’ngalamo.

29 Pakucha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.

Fanizo la mbeu yampiru

30 Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?

31 Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko,

32 koma pamene ifesedwa, imera nkukula koposa zitsamba zonse, nkukhala ndi nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m’mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.

33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;

34 ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m’tseri anatanthauzira zonse kwaophunziraake.

Yesu aletsa namondwe

35 Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina.

36 Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.

37 Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.

38 Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?

39 Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.

40 Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?

41 Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/4-3e8b40ea9cc6590ef53e50c37c8f2678.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 5

Yesu achiritsa wogwidwa ndi mzimu wonyansa ku Gerasa

1 Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa.

2 Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa,

3 amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;

4 pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.

5 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m’manda ndi m’mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala.

6 Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;

7 ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.

8 Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.

9 Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri.

10 Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko.

11 Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri.

12 Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.

13 Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m’nyanja.

14 Ndipo akuziweta anathawa, nauza m’mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho.

15 Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.

16 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.

17 Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m’malire ao.

18 Ndipo m’mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.

19 Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.

20 Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

Mwana wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu

21 Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.

22 Ndipo anadzako mmodzi wa akulu asunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,

23 nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.

24 Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.

25 Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri,

26 ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing’anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang’ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,

27 m’mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m’khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake.

28 Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.

29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m’thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake.

30 Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m’khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga?

31 Ndipoophunziraake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani?

32 Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi.

33 Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse.

34 Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.

35 M’mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?

36 Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.

37 Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.

38 Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri.

39 Ndipo m’mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m’tulo.

40 Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m’mene munali mwanayo.

41 Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye,Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.

42 Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.

43 Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/5-b1dbb167811aa64b74cb4b84357b645d.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 6

Apeputsa Yesu ku Nazarete

1 Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipoophunziraake anamtsata.

2 Ndipo pofika tsiku laSabata, anayamba kuphunzitsa m’sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?

3 Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

4 Ndipo Yesu ananena kwa iwo,Mnenerisakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake.

5 Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa.

6 Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m’midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

Yesu atuma khumi ndi awiriwo

7 Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

8 ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m’lamba lao;

9 koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri.

10 Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m’nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako.

11 Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.

12 Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.

13 Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa.

Kuphedwa kwa Yohane Mbatizi

14 Ndipo mfumuHerodeanamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.

15 Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo.

16 Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.

17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m’nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.

18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.

19 Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze;

20 pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye.

21 Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya;

22 ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.

23 Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.

24 Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi.

25 Ndipo pomwepo analowa m’mangum’mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.

26 Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.

27 Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m’nyumba yandende;

28 natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake.

29 Ndipo m’mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m’manda.

Yesu achulukitsa mikate

30 Ndipoatumwianasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.

31 Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

32 Ndipo anachokera m’ngalawa kunka kumalo achipululu padera.

33 Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m’midzi monse, nawapitirira.

34 Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35 Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;

36 muwauze kuti amuke, alowe kuminda ndi kumidzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.

37 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?

38 Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani, mukaone. Ndipo m’mene anadziwa ananena, Isanu, ndi nsomba ziwiri.

39 Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu.

40 Ndipo anakhala pansi mabungwemabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.

41 Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang’ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.

42 Ndipo anadya iwo onse, nakhuta.

43 Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.

44 Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.

Yesu ayenda pa nyanja

45 Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m’ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m’mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.

46 Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m’phiri kukapemphera.

47 Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.

48 Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

49 koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula:

50 pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope.

51 Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m’ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukulu mwa iwo okha;

52 pakuti sanazindikire za mikateyo, koma mitima yao inauma.

53 Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padooko.

54 Ndipo pamene anatuluka m’ngalawa anamzindikira pomwepo,

55 nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.

56 Ndipo kumene konse adalowa Iye m’midzi, kapena m’mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/6-44e056abd7acf338f477d9993ae47538.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 7

Miyambo ya makolo ao

1 Ndipo anasonkhana kwa IyeAfarisi, ndi alembi ena, akuchokera kuYerusalemu,

2 ndipo anaona kutiophunziraake ena anadya mkate ndi m’manja mwakuda, ndiwo osasamba.

3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m’manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;

4 ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m’thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

5 Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m’manja mwakuda?

6 Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa,

Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao,

koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.

7 Koma andilambira Ine kwachabe,

ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

8 Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.

9 Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.

10 Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;

11 koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake,Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine,

12 simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake;

13 muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.

14 Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:

15 kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.

17 Ndipo m’mene Iye adalowa m’nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iyefanizolo.

18 Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;

19 chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m’mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.

20 Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu.

21 Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere,

22 zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

23 zoipa izi zonse zituluka m’kati, nkudetsa munthu.

Mkazi wa Siro-Fenisiya

24 Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m’nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.

25 Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.

26 Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m’mwana wake.

27 Ndipo ananena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.

28 Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

29 Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m’mwana wako wamkazi.

30 Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.

Yesu achiritsa munthu wogontha ndi wosalankhula

31 Ndipo anatulukanso m’maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.

32 Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.

33 Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m’makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake:

34 nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye,Efata, ndiko, Tatseguka.

35 Ndipo makutu ake anatseguka, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire.

36 Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.

37 Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/7-a4e70fae1048b45600f04b6543e6c177.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 8

Yesu achulukitsa mikate kachiwiri

1 Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Iye anadziitaniraophunziraake, nanena nao,

2 Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya:

3 ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.

4 Ndipo ophunzira ake anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m’chipululu muno?

5 Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri.

6 Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.

7 Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.

8 Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri.

9 Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.

10 Ndipo pomwepo analowa m’ngalawa ndi ophunzira ake, nafika ku mbali ya ku Dalamanuta.

Afarisi afuna chizindikiro

11 NdipoAfarisianatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye.

12 Ndipo anausitsa moyo m’mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!

13 Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m’ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.

Chotupitsa mkate cha Afarisi

14 Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m’ngalawa koma umodzi wokha.

15 Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang’anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate chaHerode.

16 Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate.

17 Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma?

18 Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi?

19 Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.

20 Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri.

21 Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?

Yesu achiritsa munthu wakhungu ku Betsaida

22 Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.

23 Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m’maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?

24 Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.

25 Pamenepo anaikanso manja m’maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.

26 Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m’mudzi.

Petro avomereza Khristu

27 Ndipo anatuluka Yesu, ndi ophunzira ake, nalowa kumidzi ya ku Kesareya-Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ake, nanena nao, Kodi anthu ananena kuti Ine ndine yani?

28 Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.

29 Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, NdinuKhristu.

30 Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye.

Yesu aneneratu za mazunzo ndi imfa yake

31 Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kutiMwana wa Munthuakamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.

32 Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.

33 Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga,Satanaiwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.

Kunyamula mtanda

34 Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.

35 Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.

36 Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?

37 Pakuti munthu akapereka chiyani chosintha nacho moyo wake?

38 Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika naoangeloake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/8-e87776aaabbc902cb1ecd2ba35a96ccc.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 9

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

1 Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.

2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao paphiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:

3 ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbuu; monga ngati muomba wotsuka nsalu padziko lapansi sangathe kuziyeretsai.

4 Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.

5 Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu,Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

6 Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu.

7 Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m’mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.

8 Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.

9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pameneMwana wa Munthuakadzauka kwa akufa.

10 Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani?

11 Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya?

12 Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?

13 Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.

Achiritsidwa mwana wogwidwa ndi mzimu wosalankhula

14 Ndipo pamene anadza kwaophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.

15 Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlonjera.

16 Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsana nao chiyani?

17 Ndipo wina wa m’khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;

18 ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze.

19 Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.

20 Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng’amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.

21 Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.

22 Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.

23 Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

24 Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.

25 Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

26 Ndipo pamene unafuula, numng’ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

27 Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

28 Ndipo pamene Iye adalowa m’nyumba, ophunzira ake anamfunsa m’tseri, kuti, Nanga bwanji sitinathe ife kuutulutsa?

29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sungathe kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

Yesu anena kachiwiri za imfa yake

30 Ndipo anachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafune kuti munthu adziwe.

31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m’manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

32 Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.

Wamkulu ndani mu Ufumu wa Mulungu?

33 Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m’nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?

34 Koma iwo anakhala chete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzake panjira, kuti, wamkulu ndani?

35 Ndipo m’mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.

36 Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao,

37 Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.

Osatsutsana nafe athandizana nafe

38 Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife.

39 Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.

40 Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe.

41 Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake aKhristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.

Malakwitso

42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m’khosi mwake, naponyedwe iye m’nyanja.

43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa muGehena, m’moto wosazima.

45 Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m’moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa mu Gehena.

47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu Gehena;

48 kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi moto suzimidwa.

49 Pakuti onse adzathiridwa mchere wamoto.

50 Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/9-14eae60b02e6bfe589c82130bbb6d20a.mp3?version_id=1068—