Categories
MALAKI

MALAKI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneri Malaki adalalikira nthawi imene Ayuda anali atamanganso Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Iye analangiza ansembe ndi anthu ao, kuti adziperekenso kwa Yehova ndi kumamutumikira mokhulupirika, ndi kuti apewe ziphuphu, zachiphamaso ndi kunyenga kulikonse, ndipo asamale za chipembedzo.

Ansembe ndi anthu ena amachita chinyengo pa zopereka zao kwa Mulungu, ndipo samatsana chiphunzitso cha Mulungu.

Mneneriyo anawauzanso kuti lidzafika tsiku limene Yehova adzabwera kudzazenga mlandu ndi kuyeretsa anthu ake, ndipo adachita izi potumiza wamthenga wake kuti akakonze njira ndi kunenera za chipangano chake.

Za mkatimu

Kuchimwa kwa Aisraele pa zinthu zina ndi zina

1.1—2.16

Yehova akubwera kudzaweruza ndi kuyeretsa anthu ake

2.17—4.6

Categories
MALAKI

MALAKI 1

Kusayamika kwa Israele pa chikondi cha Mulungu

1 Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.

2 Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;

3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m’chipululu.

4 Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.

5 Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.

6 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

7 Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M’menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

8 Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.

9 Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.

10 Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu.

11 Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwaamitundu; ndipo m’malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.

13 Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.

14 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m’gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/1-5411abd1b38cae2bed800f0e3693a448.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 2

Mau akutsutsa ansembe

1 Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

2 Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.

3 Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.

4 Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kutichipanganochanga chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.

5 Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.

6 Chilamulo cha zoona chinali m’kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m’milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.

7 Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.

8 Koma inu mwapatuka m’njira; mwakhumudwitsa ambiri m’chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.

9 Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.

Za kukwatira akazi achilendo. Za kuleka mkazi kosayenera

10 Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu?

11 Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi muYerusalemumwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.

12 Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi, wogalamutsa ndi wovomereza m’mahema a Yakobo, ndi iye wopereka chopereka kwa Yehova wa makamu.

13 Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m’dzanja lanu.

14 Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.

15 Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.

16 Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.

17 Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/2-f56e10ee099421a823118c4582ffae26.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 3

Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye

1 Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wachipanganoamene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2 Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3 ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsasiliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndiYerusalemuchidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

6 Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.

Za kusalanda za Mulungu ndi madalitso atsatapo

7 Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

8 Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.

9 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

10 Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m’munda, ati Yehova wa makamu.

12 Ndipoamitunduonse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

13 Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani?

14 Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?

15 Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.

16 Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.

17 Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.

18 Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/3-789b8f3961efcb83707bd67ef5b71b72.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 4

Oipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale chilamulo; adzafika Eliya

1 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.

2 Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m’mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang’ombe onenepa otuluka m’khola.

3 Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.

4 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.

5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliyamnenerilisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

6 Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/4-2b57f622ee755e75b295c6e1107275a1.mp3?version_id=1068—