Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 20

Paulo apitanso ku Masedoniya, ndi Grisi, ndi Asiya

1 Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitanaophunzirawo, ndipo m’mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.

2 Ndipo m’mene atapitapita m’mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi.

3 Ndipo m’mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.

4 Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.

5 Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Troasi.

6 Ndipo tinapita m’ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.

7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m’mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.

8 Ndipo munali nyali zambiri m’chipinda chapamwamba m’mene tinasonkhanamo.

9 Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.

10 Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.

11 Ndipo m’mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kucha, anachokapo.

12 Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.

13 Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha.

14 Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene.

15 Ndipo m’mene tidachokerapo, m’mawa mwake tinafika pandunji pa Kiyo; ndi m’mawa mwake tinangokocheza ku Samo, ndi m’mawa mwake tinafika ku Mileto.

16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi mu Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale kuYerusalemutsiku laPentekoste.

Mau a Paulo kwa akulu a ku Efeso

17 Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu aMpingo.

18 Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,

19 wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;

20 kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba zanu,

21 ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu YesuKhristu.

22 Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko;

23 koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m’mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

24 Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.

25 Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.

26 Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.

27 Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.

28 Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.

29 Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;

30 ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.

31 Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleke usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.

32 Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa.

33 Sindinasirirasiliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.

34 Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.

35 M’zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

36 Ndipo m’mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

37 Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona,

38 nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/20-0b9aab20dc0015ed822a847e95a3403e.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 21

Paulo atabwera ku Yerusalemu amgwira mu Kachisi

1 Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m’mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara;

2 ndipo m’mene tinapeza ngalawa yakuoloka kunka ku Fenisiya, tinalowamo, ndi kupita nayo.

3 Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.

4 Ndipo m’mene tinapezaophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere kuYerusalemu.

5 Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m’mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,

6 ndi kulawirana; ndipo tinalowa m’ngalawa, koma iwo anabwera kwao.

7 Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wochokera ku Tiro, tinafika ku Ptolemaisi; ndipo m’mene tidalonjera abale, tinakhala nao tsiku limodzi.

8 Ndipo m’mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m’mene tinalowa m’nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.

9 Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.

10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeyamneneri, dzina lake Agabu.

11 Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m’manja aamitundu.

12 Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.

13 Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.

14 Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.

15 Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.

16 Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.

17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.

18 Ndipo m’mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.

19 Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.

20 Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;

21 ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.

22 Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika.

23 Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda;

24 amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.

25 Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.

26 Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m’mawa mwake m’mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.

27 Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,

28 nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.

29 Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi.

30 Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.

31 Ndipo m’mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti mu Yerusalemu monse muli piringupiringu.

32 Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo.

33 Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?

34 Koma wina anafuula kena, wina kena, m’khamumo; ndipo m’mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

35 Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo;

36 pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.

37 Ndipo poti alowe naye m’linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?

38 Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?

39 Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mu Silisiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.

40 Ndipo m’mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m’chinenedwe cha Chihebri, nanena:

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/21-511529252834baaf16f306f15a2d6882.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 22

Paulo achita chodzikanira chake kwa anthu

1 Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.

2 Ndipo pakumva kuti analankhula nao m’chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati,

3 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m’mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;

4 ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa kuYerusalemu, kuti alangidwe.

6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.

7 Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine?

8 Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.

9 Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamve mau akulankhula nane.

10 Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.

11 Ndipo popeza sindinapenye, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

12 Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,

13 anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.

14 Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m’kamwa mwake.

15 Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.

16 Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.

17 Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,

18 ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga mu Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.

19 Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m’ndende ndi kuwapanda m’masunagogeonse iwo akukhulupirira Inu;

20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.

21 Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwaamitundu.

22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

23 Ndipo pakufuula iwo, ndi kutaya zovala zao, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga,

24 kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.

25 Ndipo m’mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwakenturiyowakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?

26 Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.

27 Ndipo kapitao wamkuluyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.

28 Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.

29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

Paulo pa bwalo la akulu

30 Koma m’mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/22-704f7465cd64b43aa563953d43cc3a5b.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 23

1 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m’bwalo la akulu a milanduanati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.

2 Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake.

3 Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?

4 Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?

5 Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.

6 Koma pozindikira Paulo kuti ena ndiAsaduki, ndi enaAfarisi, anafuula m’bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.

7 Ndipo pamene adatero, kunakhala chilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.

8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapenamngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.

9 Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?

10 Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m’linga.

11 Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni kuYerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.

Ayuda apangana chiwembu cha kupha Paulo. Apulumukira ku Kesareya

12 Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;

13 ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi anali oposa makumi anai.

14 Amenewo anadza kwa ansembe aakulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.

15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m’linga, namfotokozera Paulo.

17 Ndipo Paulo anadziitanirakenturiyowina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.

18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam’nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

19 Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m’tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?

20 Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la akulu a milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

21 Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang’anira lonjezano lanu.

22 Pamenepo ndipo kapitao wamkulu anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi.

23 Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;

24 ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.

25 Ndipo analembera kalata yakuti,

26 Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni.

27 Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

28 Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye kubwalo lao la akulu a milandu.

29 Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.

30 Ndipo m’mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.

31 Pamenepo ndipo asilikali, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.

32 Koma m’mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;

33 iwowo, m’mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.

34 Ndipo m’mene adawerenga anafunsa achokera m’dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Silisiya,

35 anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m’nyumba ya milandu yaHerode.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/23-568074d4eaa1e3d0ebcd7ef8fa118d2c.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 24

Felikisi amva mlandu wa Paulo

1 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

2 Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,

3 tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu.

4 Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu.

5 Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;

6 amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira.

8 Ndipo kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.

9 Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.

10 Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

11 popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine kuYerusalemukukalambira;

12 ndipo sanandipeze mu Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m’sunagogekapena m’mzinda.

13 Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.

14 Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;

15 ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.

16 M’menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.

17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;

18 popereka izi anandipeza woyeretsedwa mu Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;

19 koma panali Ayuda ena a ku Asiya, ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20 Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pabwalo la akulu a milandu,

21 koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

22 Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

23 Ndipo analamulirakenturiyoamsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.

24 Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro chaKhristuYesu.

25 Ndipo m’mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.

26 Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye.

27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m’malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m’nsinga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/24-10fce9817b34fbdfb4df072bb1525c7f.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 25

Paulo pa bwalo la milandu la Fesito. Anena akatulukira kwa Kaisara

1 Pamenepo Fesito m’mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka kuYerusalemukuchokera ku Kesareya.

2 Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira,

3 nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.

4 Pamenepo Fesito anayankha, kuti Paulo asungike ku Kesareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa.

5 Chifukwa chake, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.

6 Ndipo m’mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m’mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.

7 Ndipo m’mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanathe kuzitsimikiza;

8 koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwe kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena paKaisara.

9 Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?

10 Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitire kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.

11 Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.

12 Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.

Paulo adzinenera kwa Agripa

13 Ndipo atapita masiku ena,Agripamfumuyo, ndi Berenise anafika ku Kesareya, nalankhula Fesito.

14 Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Fesito anafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m’ndende Felikisi,

15 amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake.

16 Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.

17 Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwe, koma m’mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.

18 Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamtchulire konse chifukwa cha zoipa zonga ndinazilingirira ine;

19 koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.

20 Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi.

21 Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara.

22 Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.

23 M’mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao aakulu, ndi amuna omveka a mzindawo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo.

24 Ndipo Fesito anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.

25 Koma ndinapeza ine kuti sanachite kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.

26 Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.

27 Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam’nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/25-ac58dba654869ce8e04f71c924864329.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 26

1 NdipoAgripaanati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:

2 Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;

3 makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

4 Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene anakhala chiyambire mwa mtundu wanga muYerusalemu, awadziwa Ayuda onse;

5 andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhalaMfarisimonga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu.

6 Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu analichita kwa makolo athu;

7 kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.

8 Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa?

9 Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

10 Chimenenso ndinachita mu Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m’ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.

11 Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m’masunagogeonse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.

12 M’menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe aakulu,

13 dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m’chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.

15 Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.

16 Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe;

17 ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwaamitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo,

18 kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro waSatanakulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.

19 Potero, Mfumu Agripa, sindinakhale ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;

20 komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m’dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.

21 Chifukwa cha izi Ayuda anandigwira mu Kachisi, nayesa kundipha.

22 Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang’ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;

23 kutiKhristuakamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.

24 Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.

25 Koma Paulo anati, Ndilibe misala, Fesito womvekatu; koma nditulutsa mau a choonadi ndi odziletsa.

26 Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m’tseri.

27 Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa kuti muwakhulupirira.

28 Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkhristu.

29 Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang’ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.

30 Ndipo ananyamuka mfumu, ndi kazembe, ndi Berenise, ndi iwo akukhala nao;

31 ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzake, nanena, Munthu uyu sanachite kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.

32 Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwaKaisara.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/26-70b689c39d51cfea0d689c3eb85aba48.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 27

Amtumiza Paulo ku Roma. Tsoka panyanja

1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m’ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwakenturiyodzina lake Julio, wa gulu la Augusto.

2 Ndipo m’mene tidalowa m’ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.

3 Ndipo m’mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.

4 Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kuseri kwa Kipro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe.

5 Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Silisiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mira wa Likiya.

6 Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Aleksandriya, ilikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo.

7 Ndipo m’mene tidapita pang’onopang’ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m’tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;

8 ndipo popazapazapo movutika, tinafika kumalo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo panali mzinda wa Lasea.

9 Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza,

10 nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.

11 Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.

12 Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.

13 Ndipo poomba pang’ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m’mbali mwa Krete.

14 Koma patapita pang’ono idaombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Yurakulo;

15 ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.

16 Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching’ono dzina lake Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma movutika;

17 ndipo m’mene adaukweza, anachita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Siriti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.

18 Ndipo povutika kwakukulu ndi namondweyo, m’mawa mwake anayamba kutaya akatundu;

19 ndipo tsiku lachitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.

20 Ndipo m’mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalire masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng’ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo.

21 Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.

22 Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.

23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku waleromngelowa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,

24 nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso paKaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.

25 Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.

26 Koma tiyenera kutayika pa chisumbu chakuti.

27 Koma pofika usiku wakhumi ndi chinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m’nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda;

28 ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.

29 Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuche.

30 Ndipo m’mene amalinyero anafuna kuthawa m’ngalawa, natsitsira bwato m’nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikulu,

31 Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m’ngalawa inu simukhoza kupulumuka.

32 Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwato, naligwetsa.

33 Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu.

34 Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.

35 Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m’mene adaunyema anayamba kudya.

36 Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga chakudya iwo omwe.

37 Ndipo ife tonse tili m’ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi.

38 Ndipo m’mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m’nyanja.

39 Ndipo kutacha sanazindikire dzikolo; koma anaona pali bondo la mchenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.

40 Ndipo m’mene anataya anangula anawasiya m’nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga.

41 Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.

42 Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa.

43 Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m’nyanja, nafike pamtunda,

44 ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m’ngalawa. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/27-64a25c3e84ce4b1a1a497f8d1fd31670.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 28

Paulo pa Melita

1 Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinatchedwa Melita.

2 Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.

3 Koma pamene Paulo adaola chisakata cha nkhuni, nachiika pamoto, inatulukamo njoka, chifukwa cha kutenthaku, niluma dzanja lake.

4 Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m’nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.

5 Koma anakutumulira chilombocho kumoto, osamva kupweteka.

6 Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m’mene adalindira nthawitu, naona kuti sanapweteke konse, anasintha maganizo, nati, Ndiye Mulungu.

7 Koma pafupi pamenepo panali minda, mwini wake ndiye mkulu chisumbucho, dzina lake Publio; amene anatilandira ife, natichereza okoma masiku atatu.

8 Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.

9 Ndipo patachitika ichi, enanso a m’chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa;

10 amenenso anatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife anatiikira zotisowa.

Paulo afika ku Roma, nakhala wandende m’nyumba ya iye yekha zaka ziwiri

11 Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m’ngalawa ya ku Aleksandriya, idagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, Ana Amapasa.

12 Ndipo pamene tinakocheza ku Sirakusa, tinatsotsako masiku atatu.

13 Ndipo pochokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwera, ndipo m’mawa mwake tinafika ku Puteoli:

14 pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma.

15 Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.

16 Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.

17 Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam’nsinga kuchokera kuYerusalemuku manja a Aroma;

18 ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe chifukwa cha kundiphera.

19 Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kutulukira kwaKaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.

20 Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu.

21 Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandire makalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadze kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.

22 Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.

23 Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.

24 Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere.

25 Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa YesayaMnenerikwa makolo anu,

26 ndi kuti,

Pita kwa anthu awa, nuti,

Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;

ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;

27 pakuti mtima wa anthu awa watupatu,

ndipo m’makutu mwao mmolema kumva,

ndipo maso ao anawatseka;

kuti angaone ndi maso,

nangamve ndi makutu,

nangazindikire ndi mtima,

nangatembenuke,

ndipo Ine ndingawachiritse.

28 Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwaamitundu; iwonso adzamva.

30 Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m’nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,

31 ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye YesuKhristundi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/28-3811151ec2daa4795f028ad84138f818.mp3?version_id=1068—