Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 10

Kenturiyo Kornelio

1 Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio,kenturiyowa gulu lotchedwa la Italiya,

2 ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.

3 Iye anapenya m’masomphenya poyera,mngelowa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.

4 Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.

5 Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, aitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro;

6 acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m’mbali mwa nyanja.

7 Ndipo m’mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;

8 ndipo m’mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa.

9 Koma m’mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m’mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;

10 koma m’mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka;

11 ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi chotengera chilinkutsika, chonga ngati chinsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinai, ndi kutsikira padziko pansi;

12 m’menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m’mlengalenga.

13 Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye.

14 Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

15 Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba.

16 Ndipo chinachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chinatengedwa kunka kumwamba.

17 Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,

18 ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wotchedwanso Petro, acherezedwako.

19 Ndipo m’mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

20 Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine.

21 Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; chifukwa chake mwadzera nchiyani?

22 Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.

23 Pamenepo anawalowetsa nawachereza.

Ndipo m’mawa mwake ananyamuka natuluka nao, ndi ena a abale a ku Yopa anamperekeza iye.

24 Ndipo m’mawa mwake analowa mu Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.

25 Ndipo panali pakulowa Petro, Kornelio anakomana naye, nagwa pa mapazi ake, namlambira.

26 Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.

27 Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;

28 ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;

29 chifukwa chakenso ndinadza wosakana, m’mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji?

30 Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m’nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira,

31 nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.

32 Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m’mbali mwa nyanja.

33 Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.

34 Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;

35 koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.

36 Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa YesuKhristu(ndiye Ambuye wa onse)

37 mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira;

38 za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

39 Ndipo ife ndife mboni za zonse adazichita m’dziko la Ayuda ndi muYerusalemu; amenenso anamupha, nampachika pamtengo.

40 Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti aonetsedwe,

41 si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.

42 Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.

43 Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.

44 Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.

45 Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidweonse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

46 Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

47 Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

48 Ndipo analamulira iwo abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/10-cff5f78829404878e1d33b680f02ccc5.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 11

Petro adziwerengera pamaso pa Mpingo kuti anabatiza Korneliyo

1 Komaatumwindi abale akukhala mu Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.

2 Ndipo pamene Petro adakwera kudza kuYerusalemu, iwo akumdulidweanatsutsana naye,

3 nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.

4 Koma Petro anayamba kuwafotokozera chilongosolere, nanena,

5 Ndinali ine m’mzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m’kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;

6 chimenecho ndidachipenyetsetsa ndinachilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zilombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga.

7 Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.

8 Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m’kamwa mwanga ndi kale lonse.

9 Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m’mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba.

10 Ndipo ichi chinachitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.

11 Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m’mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.

12 Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m’nyumba ya munthuyo;

13 ndipo anatiuza ife kuti adaonamngelowakuimirira m’nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;

14 amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.

15 Ndipo m’mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.

16 Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

17 Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye YesuKhristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

18 Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.

Uthenga Wabwino ulalikidwa kwa amitundu a ku Antiokeya

19 Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.

20 Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m’mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.

21 Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupirira unatembenukira kwa Ambuye.

22 Ndipo mbiri yao inamveka m’makutu aMpingowakukhala mu Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;

23 ameneyo, m’mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;

24 chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye.

25 Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;

26 ndipo m’mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipoophunziraanayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.

27 Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.

28 Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu padziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.

29 Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala mu Yudeya;

30 ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/11-3025d1899bac86e65b24e908cc1ec26d.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 12

Herode azunza Mpingo; amupha Yakobo, naponya Petro kundende. Petro apulumuka m’ndende. Imfa ya Herode

1 Koma nyengo imeneyoHerodemfumu anathira manja ena a muMpingokuwachitira zoipa.

2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.

3 Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa.

4 Ndipo m’mene adamgwira, anamuika m’ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapitaPaska.

5 Pamenepo ndipo Petro anasungika m’ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

6 Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende.

7 Ndipo taonani,mngelowa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m’nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m’manja mwake.

8 Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m’chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine.

9 Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwe kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

10 Ndipo m’mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang’ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera.

11 Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m’dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.

12 Ndipo m’mene adalingirirapo, anadza kunyumba ya Maria amake wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera.

13 Ndipo m’mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda.

14 Ndipo pozindikira mau ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sanatsegule pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.

15 Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wake.

16 Koma Petro anakhala chigogodere; ndipo m’mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.

17 Koma m’mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m’ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.

18 Koma kutacha, panali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti.

19 Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.

20 Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m’mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.

21 Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.

22 Ndipo anthu osonkhanidwawo anafuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.

23 Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.

24 Koma mau a Mulungu anakula, nachulukitsa.

25 Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera kuYerusalemum’mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/12-2e81b23a94deeabe05ff9ceefbec99c4.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 13

Ulendo woyamba wa Paulo. Mpingo wa ku Antiokeya utuma Paulo ndi Barnabasi amuke kwa amitundu. Alalikira pa Kipro. Elimasi watsenga

1 Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya muMpingowa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndiHerodechiwangacho, ndi Saulo.

2 Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.

3 Pamenepo, m’mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.

4 Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m’ngalawa ku Kipro.

5 Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m’masunagogea Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.

6 Ndipo m’mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga,mneneriwonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu;

7 ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

8 Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire.

9 Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,

10 nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?

11 Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.

12 Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.

Mau a Paulo m’sunagoge wa Antiokeya wa mu Pisidiya

13 Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka kuYerusalemu.

14 Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m’sunagoge tsiku laSabata, nakhala pansi.

15 Ndipo m’mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

16 Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.

17 Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m’dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m’menemo.

18 Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m’chipululu.

19 Ndipo m’mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri mu Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;

20 ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo.

21 Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai.

22 Ndipo m’mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.

23 Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;

24 Yohane atalalikiratu, asanafike Iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israele.

25 Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake.

26 Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.

27 Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.

28 Ndipo ngakhale sanapeze chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.

29 Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m’manda.

30 Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa;

31 ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.

32 Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo;

33 kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.

34 Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide.

35 Chifukwa anenanso mu Salimo lina, Simudzapereka Woyera wanu aone chivundi.

36 Pakutitu, Davide, m’mene adautumikira uphungu wa Mulungu m’mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;

37 koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaone chivundi.

38 Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo;

39 ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.

40 Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:

41 Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;

kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu,

ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.

42 Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.

43 Ndipo m’mene anthu a m’sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m’chisomo cha Mulungu.

44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kumva mau a Mulungu.

45 Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.

46 Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwaamitundu.

47 Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti,

Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu,

kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.

48 Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.

49 Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m’dziko lonse.

50 Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m’malire ao.

51 Koma iwo, m’mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio.

52 Ndipoophunziraanadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/13-cf553d947e36e623913694e7382b1a75.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 14

Uthenga Wabwino ulalikidwa ku Ikonio, Listara, ndi Deribe

1 Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m’sunagogewa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.

2 Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu.

3 Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.

4 Ndipo khamu la mzindawo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndiatumwi.

5 Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala,

6 iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:

7 kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.

8 Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m’mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.

9 Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang’anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,

10 anati ndi mau aakulu, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.

11 Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m’chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.

12 Ndipo anamutcha Barnabasi, Zeusi; ndi Paulo, Heremesi, chifukwa anali wotsogola kunena.

13 Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mzinda, anadza nazo ng’ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.

14 Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang’amba zofunda zao, natumphira m’khamu,

15 nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:

16 m’mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m’njira mwao.

17 Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.

18 Pakunena izo, anavutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

19 Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.

20 Koma pamene anamzingaophunzirawo, anauka iye, nalowa m’mzinda; m’mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe.

21 Pamene analalikira Uthenga Wabwino mumzindamo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya,

22 nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

23 Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha muMpingouliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndikusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

24 Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfiliya.

25 Ndipo atalankhula mau mu Perga, anatsikira ku Ataliya;

26 komweko anachoka m’ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo.

27 Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.

28 Ndipo anakhala pamenepo ndi ophunzira nthawi yaikulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/14-b6662dbb75d75c7ba755c121a5a41c96.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 15

Ku Yerusalemu atumwi ndi akulu aweruza za mdulidwe ndi Malamulo a Mose

1 Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapandakudulidwamonga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.

2 Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka kuYerusalemukwaatumwindi akulu kukanena za funsolo.

3 Ndipo iwo anaperekezedwa ndiMpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko chaamitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.

4 Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.

5 Koma anauka ena a mpatuko waAfarisiokhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.

6 Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.

7 Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m’kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.

8 Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

9 ndipo sanalekanitse ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m’chikhulupiriro.

10 Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi laophunziragoli, limene sanathe kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

11 Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye YesuKhristu, monga iwo omwe.

12 Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.

13 Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine:

14 Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.

15 Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa,

16 Zikatha izo ndidzabwera,

ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa;

ndidzamanganso zopasuka zake,

ndipo ndidzachiimikanso:

17 Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,

ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo,

18 ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo

chiyambire dziko lapansi.

19 Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,

20 koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

21 Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m’mizinda yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m’masunagogemasabata onse.

22 Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m’gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

23 Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:

24 Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulire;

25 chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,

26 anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.

27 Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.

28 Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;

29 kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

30 Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

31 Pamene anawerenga, anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake.

32 Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.

33 Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.

35 Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.

Paulo ndi Barnabasi alekana

36 Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m’mizinda yonse m’mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.

37 Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko

38 Koma sikunamkomere Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.

39 Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m’ngalawa, nanka ku Kipro.

Ulendo wachiwiri wa Paulo

40 Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.

41 Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/15-83ee5dd69ebe51144522b3b168a38dbb.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 16

1 Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzirawina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki.

2 Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio.

3 Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m’maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki.

4 Pamene anapita kupyola pamizinda, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamuliraatumwindi akulu a paYerusalemu.

5 KoteroMipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiwerengo chao tsiku ndi tsiku.

6 Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;

7 pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleze;

8 ndipo pamene anapita pambali pa Misiya, anatsikira ku Troasi.

Masomphenya a ku Troasi. Paulo aoloka nalalikira ku Filipi. Za Lidia wogulitsa chibakuwa. Mdindo wa ku Filipi

9 Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.

10 Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.

11 Chotero tinachokera ku Troasi m’ngalawa, m’mene tinalunjikitsa ku Samotrase, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli;

12 pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m’dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.

13 Tsiku laSabatatinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.

14 Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.

15 Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo anatiumiriza ife.

16 Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.

17 Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.

18 Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m’dzina la YesuKhristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

19 Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu,

20 ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa avuta kwambiri mzinda wathu, ndiwo Ayuda,

21 ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma.

22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang’ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.

23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m’ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

24 Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m’chipinda cha m’kati, namangitsa mapazi ao m’zigologolo.

25 Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo analinkuwamva;

26 ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

27 Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am’ndende adathawa.

28 Koma Paulo anafuula ndi mau aakulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.

29 Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m’kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi,

30 nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?

31 Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.

32 Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake.

33 Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.

34 Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.

35 Kutacha, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.

36 Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.

37 Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m’tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.

38 Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.

39 Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawatulutsa, anawapempha kuti achoke pamzinda.

40 Ndipo anatuluka m’ndendemo, nalowa m’nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/16-d2fa865f2ae959b430bc4da3b5da4d7f.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 17

Paulo ku Tesalonika ndi Berea

1 Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunalisunagogewa Ayuda.

2 Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira,

3 natsimikiza, kuti kunayeneraKhristukumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.

4 Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi aakulu osati owerengeka.

5 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m’mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.

6 Pamene sanawapeze anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mzinda, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

7 amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo aKaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.

8 Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mzinda, pamene anamva zimenezi.

9 Ndipo pamene analandira chikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.

10 Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m’sunagoge wa Ayuda.

11 Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

12 Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira; ndi akazi a Chigriki omveka, ndi amuna, osati owerengeka.

13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu.

14 Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko.

Paulo ku Atene

15 Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.

16 Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano.

17 Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m’sunagoge, ndi m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.

18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.

19 Ndipo anamgwira, nanka naye kuAreopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe?

20 Pakuti ufika nazo kumakutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?

21 (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.)

22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

23 Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.

24 Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo ndiye Ambuye, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja;

25 satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

26 ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;

27 kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife;

28 pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.

29 Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapenasiliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

30 Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;

31 chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.

32 Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.

33 Choncho Paulo anatuluka pakati pao.

34 Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/17-466a46e1480558cd878479aeeea7f039.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 18

Paulo ku Korinto ndi ku Efeso. Abwera ku Yerusalemu

1 Zitapita izi anachoka ku Atene, nadza ku Korinto.

2 Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke mu Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo:

3 ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.

4 Ndipo anafotokozera m’sunagogemasabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.

5 Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiyeKhristu.

6 Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwaamitundu.

7 Ndipo anachoka kumeneko, nalowa m’nyumba ya munthu, dzina lake Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yake inayandikizana ndi sunagoge.

8 Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.

9 Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m’masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete;

10 chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m’mzinda muno.

11 Ndipo anakhala komwe chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mau a Mulungu mwa iwo.

12 Tsono pamene Galio anali chiwanga chaAkaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,

13 kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo.

14 Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pake, Galio anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;

15 koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang’ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.

16 Ndipo anawapirikitsa pa mpando wachiweruziro.

17 Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalire zimenezi.

18 Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m’ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.

19 Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m’sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.

20 Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi ina yoenjezerapo, sanavomereze;

21 koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m’ngalawa.

22 Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjeraMpingo, natsikira ku Antiokeya.

23 Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsaophunziraonse.

Apolo ku Efeso ndi Korinto

24 Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m’malembo.

25 Iyeyo anaphunzitsidwa m’njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;

26 ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m’sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

27 Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera makalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;

28 pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/18-c8dc85f4ca22a08cc9e1b020505eca76.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 19

Ulendo wachitatu wa Paulo. Demetrio autsa phokoso

1 Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napezaophunziraena;

2 ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamve konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.

3 Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m’chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane.

4 Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.

5 Pamene anamva ichi, anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.

6 Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

7 Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.

8 Ndipo iye analowa m’sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

9 Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m’sukulu ya Tirano.

10 Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.

11 Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pazokha ndi manja a Paulo;

12 kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.

13 Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.

14 Ndipo panali ana aamuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene anachita ichi.

15 Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?

16 Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawagonjetsa onsewo, kotero kuti anathawa m’nyumba amaliseche ndi olasidwa.

17 Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.

18 Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao.

19 Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasilivazikwi makumi asanu.

20 Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu napambana.

21 Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndiAkaya, kunka kuYerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.

22 Pamene anatuma ku Masedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi mu Asiya.

23 Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.

24 Pakuti munthu wina dzina lake Demetrio wosula siliva, amene anapanga tiakachisi tasiliva, ta Aritemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri;

25 amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza chuma chathu.

26 Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:

27 ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a mu Asiya onse, ndi onse a m’dziko lokhalamo anthu, ampembedza.

28 Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, nafuula, nati, Wamkulu ndi Aritemi wa ku Efeso.

29 Ndipo m’mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.

30 Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, ophunzira ake sanamloleze.

31 Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ake, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye kubwalo lakusewera.

32 Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwe chifukwa chake cha kusonkhana.

33 Ndipo anatulutsa Aleksandro m’khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Aleksandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.

34 Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akufuula monga maora awiri, Wamkulu ndi Aritemi wa Aefeso.

35 Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi?

36 Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu kaliuma.

37 Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za mu Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano.

38 Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane.

39 Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m’msonkhano wolamulidwa.

40 Pakutinso palipo potiopsa kuti adzatineneza za chipolowe chalero; popeza palibe chifukwa cha kufotokozera za chipiringu chimene.

41 Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/19-733a1e868c0c157ff2d7618d22c6b455.mp3?version_id=1068—