Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Machitidwe a Atumwi

likungopitiriza nkhani yomwe idayamba kale mu

Luka

. Cholinga chenicheni cha bukuli ndicho kunena za m’mene otsatira a Yesu, motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, anafalitsira Uthenga Wabwino wonena za Iye kuyambira “mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya lonse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko”. (1.8) Imeneyi ndi mbiri ya chiyambi cha Chikhristu pakati pa Ayuda mpaka pamene chinafalikira pakati pa anthu a m’dziko lonse lapansi. Wolembayo amafunitsitsa kuwatsimikizira awerengi kuti Akhristu sali ogalukira ulamuliro wa Aroma, koma kuti Chikhristu chikungokwaniritsa za m’chipembedzo cha Chiyuda.

Buku la

Machitidwe

lingathe kugawidwa m’magawo atatu akuluakulu, pofuna kuonetsa kulikonse kumene Uthenga Wabwino wa Yesu umalalikidwa ndipo mipingo imayamba, Chikhristu chimanka chikulirakulira: (1) Yesu akwera kunka kumwamba ndipo Chikhristu chiyamba ku Yerusalemu; (2) Mpingo ufalikira kumadera ozungulira Palestina; (3) Mpingo ukulabe, kufika ku Nyanja ya Meditereniyani mpaka ku Roma.

Chinthu chofunika kwambiri mu buku la

Machitidwe

ndicho ntchito ya Mzimu Woyera, amene anabwera ndi mphamvu pa okhulupirira ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste ndipo akupitiriza kutsogolera ndi kulimbikitsa mpingo ndi atsogoleri ake kudzera mu zochitika zimene zalembedwa mu bukuli. Mauthenga a mpingo woyamba akulembedwa mwachidule mu maulaliki osiyanasiyana, ndipo zinthu zimene zalembedwa mu buku la

Machitidwe

zikuonetsa mphamvu ya uthengawu m’moyo wa okhulupirira ndi mu Mpingo.

Za mkatimu

Kukonzekera mboni 1.1-26

a. Lamulo ndi lonjezo lomaliza la Yesu 1.1-14

b. Asankha wolowa m’malo mwa Yudasi 1.15-26

Mboni za mu Yerusalemu 2.1—8.3

Mboni za mu Yudeya ndi mu Samariya 8.4—12.25

Utumiki wa Paulo 13.1—28.31

a. Ulendo woyamba 13.1—14.28

b. Msonkhano wa ku Yerusalemu 15.1-35

c. Ulendo wachiwiri 15.36—18.22

d. Ulendo wachitatu 18.23—21.16

e. Paulo aponyedwa m’ndende ku Yerusalemu, ku Kesareya ndi ku Roma 21.17—28.31

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 1

Yesu akwera kunka Kumwamba

1 Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,

2 kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyeraatumwiamene adawasankha;

3 kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;

4 ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke kuYerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;

5 pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

6 Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi ino mubwezera ufumu kwa Israele?

7 Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.

8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

9 Ndipo m’mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.

10 Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;

11 amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Asankha mlowammalo wa Yudasi

12 Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku laSabata.

13 Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi SimoniZelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.

14 Iwo onse analikukangalika m’kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.

15 Ndipo m’masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),

16 Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m’kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.

17 Chifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lake la utumiki uwu.

18 (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;

19 ndipo chinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m’manenedwe ao kadzikoka kanatchedwa Akeledama, ndiko, kadziko ka mwazi.)

20 Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalimo,

Pogonera pake pakhale bwinja,

ndipo pasakhale munthu wogonapo;

ndipo uyang’aniro wake autenge wina.

21 Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa natuluka mwa ife,

22 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.

23 Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi.

24 Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,

25 alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.

26 Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/1-efff22e641f1f1523c69ab3ddd472107.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 2

Tsiku la Pentekoste

1 Ndipo pakufika tsiku laPentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.

2 Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.

3 Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha.

4 Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

5 Koma anali muYerusalemuokhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo.

6 Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m’chilankhulidwe chake cha iye yekha.

7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?

8 Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m’chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?

9 Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;

10 mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma,

11 ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m’malilime athu zazikulu za Mulungu.

12 Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?

13 Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.

Chodzikanira cha Petro

14 Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga.

15 Pakuti awa sanaledzere monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku;

16 komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndimneneriYowele,

17 Ndipo kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu,

ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse,

ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera,

ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,

ndi akulu anu adzalota maloto;

18 ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa

ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m’thambo la kumwamba,

ndi zizindikiro padziko lapansi;

mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;

20 dzuwa lidzasanduka mdima,

ndi mwezi udzasanduka mwazi,

lisanadze tsiku la Ambuye,

lalikulu ndi loonekera.

21 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana

pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

22 Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;

23 ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;

24 yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.

25 Pakuti Davide anena za Iye,

Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;

chifukwa ali padzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;

26 mwa ichi unakondwera mtima wanga,

ndipo linasangalala lilime langa;

ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo.

27 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa,

kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,

28 munandidziwitsa ine njira za moyo;

mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.

30 Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m’chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;

31 iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwaKhristu, kuti sanasiyidwe m’dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.

32 Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.

33 Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.

34 Pakuti Davide sanakwere Kumwamba ai; koma anena yekha,

Ambuye anati kwa Mbuye wanga,

khalani kudzanja lamanja langa,

35 kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.

36 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.

Otembenuka mtima oyamba

37 Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndiatumwienawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?

38 Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

39 Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

40 Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.

41 Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

42 Ndipo anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano, m’kunyema mkate ndi mapemphero.

43 Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.

44 Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana.

45 Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

46 Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

47 nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/2-17a32e370ecf310f60447aa5b70a4ee1.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 3

Wopunduka chibadwire achiritsidwa. Chonenera Petro mu Kachisi

1 Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai.

2 Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;

3 ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe mu Kachisi, anapempha alandire chaulere.

4 Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang’ane ife.

5 Ndipo iye anavomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.

6 Koma Petro anati,Silivandi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M’dzina la YesuKhristuMnazarayo, yenda.

7 Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.

8 Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao mu Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.

9 Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;

10 namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Chipata Chokongola cha Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.

11 Koma m’mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.

12 Koma m’mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?

13 Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.

14 Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,

15 ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.

16 Ndipo pa chikhulupiriro cha m’dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

17 Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munachichita mosadziwa, monganso akulu anu.

18 Koma zimene Mulungu analalikiratu m’kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.

19 Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;

20 ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu;

21 amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.

22 Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inumnenerimwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m’zinthu zilizonse akalankhule nanu.

23 Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.

24 Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuele ndi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.

25 Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.

26 Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/3-88753cdfda64a6c347786148f32cce71.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 4

Petro ndi Yohane ku bwalo la akulu

1 Koma m’mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndiAsadukianadzako,

2 ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.

3 Ndipo anawathira manja, nawaika m’ndende kufikira m’mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo.

4 Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.

5 Koma panali m’mawa mwake, anasonkhana pamodzi muYerusalemuoweruza, ndi akulu, ndi alembi;

6 ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe.

7 Ndipo m’mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m’dzina lanji, mwachita ichi inu?

8 Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,

9 ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi machiritsidwe ake,

10 zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m’dzina la YesuKhristuMnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya.

12 Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.

13 Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.

14 Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

15 Koma pamene anawalamulira iwo achoke m’bwalo la akulu a milandu, ananena wina ndi mnzake,

16 kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala mu Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

17 Komatu tiwaopse asalankhulenso m’dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu.

18 Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu.

19 Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;

20 pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.

21 Koma m’mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.

22 Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.

Okhulupirira athamangira kupemphera

23 Ndipo m’mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao.

24 Ndipo m’mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m’menemo;

25 amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati,

Amitunduanasokosera chifukwa chiyani?

Nalingirira zopanda pake anthu?

26 Anadzindandalitsa mafumu a dziko,

ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi,

kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake.

27 Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m’mzinda munoHerode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;

28 kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.

29 Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,

30 m’mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

31 Ndipo m’mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

Madyerano a Akhristu oyamba

32 Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

33 Ndipoatumwianachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.

34 Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa,

35 nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.

36 Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro,

37 pokhala nao munda, anaugulitsa, nabwera nazo ndalama zake, naziika pa mapazi a atumwi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/4-ed5119da8347e112edb9418b5abc49ff.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 5

Za Ananiya ndi Safira

1 Koma munthu wina dzina lake Ananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake,

2 anagulitsa chao, napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe anadziwa, natenga chotsala, nachiika pa mapazi aatumwi.

3 Koma Petro anati, Ananiya,Satanaanadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?

4 Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m’manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.

5 Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.

6 Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika.

7 Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, analowa.

8 Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti.

9 Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.

10 Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.

11 Ndipo anadza mantha aakulu paMpingowonse, ndi pa onse akumva izi.

12 Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m’khonde la Solomoni.

13 Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;

14 ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;

15 kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.

16 Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozunguliraYerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.

Atumwi apulumutsidwa m’ndende, natengedwanso kupita nao kubwalo la akulu

17 Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko chaAsaduki, nadukidwa,

18 nathira manja atumwi, nawaika m’ndende ya anthu wamba.

19 Komamngelowa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,

20 Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.

21 Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa abwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.

22 Koma anyamata amene adafikako sanawapeze m’ndende, ndipo pobwera anafotokoza,

23 nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.

24 Koma m’mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.

25 Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m’ndende ali mu Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.

26 Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

27 Ndipo m’mene adadza nao, anawaika pabwalo la akulu a milandu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,

28 nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

29 Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo.

31 Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.

32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.

33 Koma m’mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.

34 Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiyeMfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang’ono.

35 Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.

36 Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.

37 Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.

38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka;

39 koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.

40 Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m’mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

41 Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.

42 Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m’nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikiraKhristuYesu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/5-66f69414f814cb0f3eebc1e508cbb28c.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 6

Asankha atumiki asanu ndi awiri

1 Koma masiku awo, pakuchulukitsaophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.

2 Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.

3 Chifukwa chake, abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.

4 Koma ife tidzalimbika m’kupemphera, ndi kutumikira mau.

5 Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:

6 amenewo anawaika pamaso paatumwi; ndipo m’mene adapemphera, anaika manja pa iwo.

7 Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu kuYerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.

Stefano woyamba wophedwa chifukwa cha Khristu

8 Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.

9 Koma anauka ena a iwo ochokera m’sunagogewa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.

10 Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.

11 Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.

12 Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,

13 naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;

14 pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.

15 Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m’bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope yamngelo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/6-e007e06b172b12613c28467f8679e022.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 7

1 Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?

2 Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;

3 nati kwa iye, Tuluka kudziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe.

4 Pamenepo anatuluka m’dziko la Akaldeya namanga mu Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m’dziko lino, m’mene mukhalamo tsopano;

5 ndipo sanampatse cholowa chake m’menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

6 Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai.

7 Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m’malo muno.

8 Ndipo anampatsa iyechipanganochamdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.

9 Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,

10 namlanditsa iye m’zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso paFaraomfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.

11 Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani yense, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeze chakudya makolo athu.

12 Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu mu Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba.

13 Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.

14 Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

15 Ndipo Yakobo anatsikira ku Ejipito; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;

16 ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m’manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.

17 Koma m’mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka mu Ejipito,

18 kufikira inauka mfumu ina pa Ejipito, imene siinamdziwe Yosefe.

19 Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.

20 Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m’nyumba ya atate wake:

21 ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wake.

22 Ndipo Mose anaphunzira nzeru zonse za Aejipito; nali wamphamvu m’mau ake ndi m’ntchito zake.

23 Koma pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israele.

24 Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamtchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwejipito.

25 Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikire.

26 Ndipo m’mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?

27 Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?

28 Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha Mwejipito dzulo?

29 Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m’dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana aamuna awiri.

30 Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekeramngelom’chipululu cha Sinai, m’lawi la moto wa m’chitsamba.

31 Koma Mose pakuona, anazizwa pa choonekacho; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye,

32 akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.

33 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato kumapazi ako; pakuti pamalo amene upondapo mpopatulika.

34 Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.

35 Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.

36 Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m’chipululu zaka makumi anai.

37 Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsiraniMneneriwa mwa abale anu, monga ine.

38 Uyu ndiye amene anali muMpingom’chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m’phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;

39 amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m’mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,

40 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa mu Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

41 Ndipo anapanga mwanawang’ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao.

42 Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m’buku la aneneri,

Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe

zaka makumi anai m’chipululu, nyumba ya Israele inu?

43 Ndipo munatenga chihema chaMoleki,

ndi nyenyezi ya mulungu Refani,

zithunzizo mudazipanga kuzilambira;

ndipo ndidzakutengani kunka nanu m’tsogolo mwake mwa Babiloni.

44 Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m’chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.

45 Chimenenso makolo athu akudza m’mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao zaamitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;

46 amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.

47 Koma Solomoni anammangira nyumba.

48 Komatu Wamwambamwambayo sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,

49 Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga,

ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga.

Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye,

kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

50 Silinapange dzanja langa zinthu izi zonse kodi?

51 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.

52 Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;

53 inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunge.

54 Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.

55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,

56 nati, Taonani, ndipenya mu Mwamba motseguka, ndiMwana wa Munthualikuimirira padzanja lamanja la Mulungu.

57 Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m’makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;

58 ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.

59 Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.

60 Ndipo m’mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m’mene adanena ichi, anagona tulo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/7-35d833e0e0d81de5414a6e3244110e39.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 8

Uthenga Wabwino pa Samariya. Simoni wanyanga

1 Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu paMpingounali muYerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m’maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osatiatumwiai.

2 Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.

3 Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m’ndende.

4 Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.

5 Ndipo Filipo anatsikira kumzinda wa ku Samariya, nawalalikira iwoKhristu.

6 Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikiro zimene anazichita.

7 Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau aakulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa.

8 Ndipo panakhala chimwemwe chachikulu m’mzindamo.

9 Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m’mzindamo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu;

10 ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu.

11 Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake.

12 Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

13 Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m’mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.

14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;

15 amenewo, m’mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:

16 pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.

17 Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18 Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,

19 nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti aliyense amene ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.

20 Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.

21 Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.

22 Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako.

23 Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama.

24 Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

25 Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri yaAsamariya.

Filipo ndi mdindo wa ku Etiopiya

26 Komamngelowa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.

27 Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;

28 ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa galeta wake, nawerengamneneriYesaya.

29 Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu.

30 Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?

31 Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

32 Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo:

Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa,

ndi mongamwanawankhosaali duu pamaso pa womsenga,

kotero sanatsegule pakamwa pake.

33 M’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa;

mbadwo wake adzaubukitsa ndani?

Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.

34 Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina?

35 Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

36 Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?

38 Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye.

39 Ndipo pamene anakwera kutuluka m’madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonenso, pakuti anapita njira yake wokondwera.

40 Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m’midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/8-fd3842d197227cd51ea532457f22b8e3.mp3?version_id=1068—

Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 9

Kusandulika mtima kwa Saulo panjira ya ku Damasiko

1 Koma Saulo, wosaleka kupumira paophunziraa Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,

2 napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa kuYerusalemu.

3 Ndipo poyenda ulendo wake, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kochokera kumwamba;

4 ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?

5 Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;

6 komatu, uka, nulowe m’mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.

7 Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu.

8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenye kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye mu Damasiko.

9 Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadye kapena kumwa.

10 Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m’masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,

11 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m’nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera

12 ndipo anaona mwamuna dzina lake Ananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.

13 Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu mu Yerusalemu;

14 ndi kuti pano ali nao ulamuliro wa kwa ansembe aakulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.

15 Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso paamitundundi mafumu ndi ana a Israele;

16 pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.

17 Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m’nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

18 Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m’maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;

19 ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu.

Azunzika mzunziyo

Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.

20 Ndipo pomwepo m’masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.

21 Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.

22 Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndiKhristu.

23 Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;

24 koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;

25 koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.

26 Koma m’mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.

27 Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwaatumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m’njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m’dzina la Yesu.

28 Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu, nanena molimbika mtima m’dzina la Ambuye;

29 ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.

30 Koma m’mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.

31 Pamenepo ndipoMpingowa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m’kuopa kwa Ambuye ndi m’chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.

Achiritsidwa Eneya; aukitsidwa Tabita

32 Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida.

33 Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.

34 Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.

35 Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Lida ndi ku Saroni, natembenukira kwa Ambuye amenewa.

36 Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.

37 Ndipo kunali m’masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m’chipinda chapamwamba.

38 Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m’mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.

39 Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M’mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

40 Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

41 Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m’mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

42 Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.

43 Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/9-2039bced8cb78d90f6f7ac6664f28c82.mp3?version_id=1068—