Amfunsa Yesu za ulamuliro
1 Ndipo kunali lina la masiku ao m’mene Iye analikuphunzitsa anthu mu Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;
2 ndipo anati, nanena naye, Mutiuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene?
3 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze:
4 Ubatizo wa Yohane unachokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?
5 Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena uchokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirire chifukwa ninji?
6 Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane alimneneri.
7 Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene uchokera.
8 Ndipo Yesu anati kwa iwo Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu izi.
Fanizo la olima munda wampesa
9 Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthufanizoili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.
10 Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.
11 Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu.
12 Ndipo anatumizanso wina wachitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja.
13 Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzachita chiyani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamchitira iye ulemu.
14 Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.
15 Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wampesawo adzawachitira chiyani?
16 Iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iai!
17 Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa,
Mwala umene anaukana omanga nyumba,
womwewu unakhala mutu wa pangodya.
18 Munthu yense wakugwa pamwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.
Za msonkho
19 Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.
20 Ndipo anamyang’anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
21 Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;
22 kodi kuloledwa kupereka msonkho kwaKaisara, kapena iai?
23 Koma Iye anazindikira chinyengo chao, nati kwa iwo,
24 Tandionetsani Ine rupiya latheka. Chithunzithunzi ndi cholemba chake ncha yani? Anati iwo, Cha Kaisara.
25 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.
26 Ndipo sanakhoze kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete.
Yesu ayankha Asaduki za kuuka kwa akufa
27 Ndipo anadza kwa IyeAsadukiena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye,
28 nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.
29 Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana;
30 ndipo wachiwiri,
31 ndi wachitatu anamtenga mkaziyo; ndipo choteronso asanu ndi awiri onse, sanasiye mwana, namwalira.
32 Pomalizira anamwaliranso mkaziyo.
33 Potero m’kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.
34 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:
35 koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.
36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndiangelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.
37 Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.
38 Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.
39 Ndipo alembi ena anayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino.
40 Pakuti sanalimbenso mtima kumfunsa Iye kanthu kena.
Khristu mwana wa Davide
41 Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kutiKhristuyo ndiye mwana wa Davide?
42 Pakuti Davide yekha anena m’buku la Masalimo,
Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,
ukhale padzanja langa lamanja,
43 kufikira Ine ndikaika adani ako pansi pa mapazi ako.
44 Chotero Davide anamtchula Iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji?
Ophunzira achenjere nao alembi
45 Ndipo pamene anthu onse analinkumva Iye, anati kwaophunzira,
46 Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m’misika, ndi mipando yaulemu m’sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;
47 amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/20-c020f66e808b62ebc37855793f1b500a.mp3?version_id=1068—