Categories
LUKA

LUKA 10

Yesu atuma ophunzira makumi asanu ndi awiri

1 Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

2 Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.

3 Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati anaankhosa pakati pa mimbulu.

4 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.

5 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowamo muyambe mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.

6 Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.

7 Ndipo m’nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m’nyumba.

8 Ndipo m’mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;

9 ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako,

10 ndipo salandira inu, m’mene mwatuluka kumakwalala ake nenani,

11 Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

12 Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo.

13 Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.

14 Koma ku Tiro ndi Sidoni kudzapiririka m’chiweruziro, koposa inu.

15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa.

16 Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.

17 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.

18 Ndipo anati kwa iwo, NdinaonaSatanaalinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.

19 Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.

Yesu akondwera

21 Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

22 Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.

23 Ndipo m’mene anapotolokera kwaophunziraake, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona.

24 Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimve.

Fanizo la Msamariya wachifundo

25 Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?

26 Ndipo anati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?

27 Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.

28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.

29 Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?

30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera kuYerusalemukunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.

31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.

32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina.

33 KomaMsamariyawina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,

34 nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

35 Ndipo m’mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

36 Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?

37 Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.

Marita ndi Maria

38 Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m’mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake.

39 Ndipo anali ndi mbale wake wotchedwa Maria, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ake.

40 Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.

41 Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;

42 koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/10-267ea5208d698f9d5dec155e7c29b820.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 11

Pemphero la Ambuye

1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m’mene analeka, wina waophunziraake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.

2 Ndipo anati kwa iwo, M’mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze;

3 tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.

4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.

Fanizo la bwenzi laliuma

5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;

6 popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndilibe chompatsa;

7 ndipo iyeyu wa m’katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?

8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.

9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.

10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m’malo mwa nsomba?

12 Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

13 Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Za Yesu ndi Belezebulu

14 Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15 Koma ena mwa iwo anati, NdiBelezebulumkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

16 Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.

17 Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m’kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m’kati mwake igwa.

18 Ndiponso ngatiSatanaagawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.

19 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

20 Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

21 Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;

22 koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.

23 Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

24 Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;

25 ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.

26 Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

27 Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.

28 Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.

Chizindikiro cha Yona

29 Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona.

30 Pakuti monga ngati Yona anali chizindikiro kwa Aninive, chotero adzakhalansoMwana wa Munthukwa mbadwo uno.

31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.

32 Amuna a ku Ninive adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.

Za nyali ya thupi

33 Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m’chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.

34 Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe lili la mdima wokhawokha.

35 Potero yang’anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima.

36 Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.

Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi

37 Ndipo pakulankhula Iye, anamuitanaMfarisikuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.

38 Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.

39 Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.

40 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m’kati mwake?

41 Koma patsani mphatso yachifundo za m’katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.

42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.

43 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m’masunagoge, ndi kupatsidwa moni m’misika.

44 Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.

45 Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

46 Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

47 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.

48 Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndiatumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

50 kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

51 kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

52 Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.

53 Ndipo pamene Iye anatuluka m’menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;

54 namlindira akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/11-2845763e9c31457eda97cf907371e2fd.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 12

Yesu awachenjeza za chinyengo

1 Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwaophunziraake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate chaAfarisi, chimene chili chinyengo.

2 Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

3 Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m’khutu, m’zipinda za m’kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.

Awatchulira amene ayenera kumuopa

4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita.

5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kuGehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.

6 Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

7 komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.

8 Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde,Mwana wa Munthuadzamvomereza iye pamaso paangeloa Mulungu;

9 Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.

10 Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

11 Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m’sunagogendi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;

12 pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

Fanizo la mwini chuma wopusa

13 Ndipo munthu wa m’khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.

14 Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15 Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

16 Ndipo Iye ananena naofanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino.

17 Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga?

18 Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa.

19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20 Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21 Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Nkhawa za moyo wathu

22 Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.

23 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.

24 Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake?

26 Kotero ngati simungathe ngakhale chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

27 Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa.

28 Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wakuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang’ono?

29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a padziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31 Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani.

32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Fanizo la kapolo wochezera

35 Khalani odzimangira m’chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37 Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m’chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38 Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39 Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.

40 Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza.

41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42 Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?

43 Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.

44 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

45 Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

46 mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

47 Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

48 Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang’ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

Yesu aponya moto padziko lapansi

49 Ine ndinadzera kuponya moto padziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati unatha kuyatsidwa?

50 Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51 Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere padziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52 pakuti kuyambira tsopano adzakhala m’nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53 Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.

Zizindikiro za nyengo yake

54 Koma Iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene paliponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.

55 Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

58 Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m’nyumba yandende.

59 Ine ndinena kwa iwe, Sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri kukumaliza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/12-23493812a929ede4ee5f12ee3c0fe5f3.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 13

Maphedwe a Agalileya, nsanja ya Siloamu

1 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.

2 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi?

3 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.

4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?

5 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.

Fanizo la mkuyu wosabala

6 Ndipo Iye ananenafanizoili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m’munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

7 Ndipo anati kwa wosungira munda wampesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake?

8 Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;

9 ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

Achiritsa mkazi wopeteka

10 Ndipo analikuphunzitsa m’sunagogemwina, tsiku laSabata.

11 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

12 Ndipo Yesu m’mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.

13 Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.

14 Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m’menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, ameneSatanaanammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?

17 Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m’khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye.

Fanizo la mpiru ndi la chotupitsa

18 Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?

19 Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m’munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m’mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.

20 Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani?

21 Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.

Khomo lopapatiza

22 Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.

23 Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo,

24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

25 Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;

26 pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m’makwalala a kwathu;

27 ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.

28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.

29 Ndipo anthu adzachokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu.

30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.

Amchenjeza Yesu za Herode. Yesu alirira Yerusalemu

31 Nthawi yomweyo anadzapoAfarisiena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwaHerodeafuna kupha Inu.

32 Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.

33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kutimneneriaonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.

34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simunafunai!

35 Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/13-9528ed474be52e402ab33dfd17d49421.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 14

Yesu achiritsa munthu wambulu

1 Ndipo panali pamene Iye analowa m’nyumba ya mmodzi wa akulu aAfarisitsiku laSabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.

2 Ndipo onani, panali pamaso pake munthu wambulu.

3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?

4 Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite.

5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?

6 Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.

Fanizo la mipando ya ulemu

7 Ndipo Iye ananenafanizokwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,

8 Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,

9 ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.

10 Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe.

11 Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.

12 Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

13 Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;

14 ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.

Fanizo la phwando lalikulu

15 Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

16 Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikulu; naitana anthu ambiri;

17 ndipo anatumiza kapolo wake pa nthawi ya phwando kukanena kwa oitanidwawo, Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano.

18 Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika.

19 Ndipo anati wina, Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika.

20 Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.

21 Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.

22 Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo.

23 Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.

24 Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.

Womtsata Ambuye adzayesedwa

25 Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo,

26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzirawanga.

27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.

28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?

29 Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye,

30 ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.

Fanizo la mfumu yanzeru

31 Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sayamba wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?

32 Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.

33 Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.

34 Kotero mchere uli wokoma; koma ngati mchere utasukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani?

35 Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/14-dc3e05e0d7d0eea440279880ea6b7e76.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 15

Fanizo la nkhosa yosokera

1 Komaamisonkhoonse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye.

2 NdipoAfarisindi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao.

3 Koma anati kwa iwofanizoili, nanena,

4 Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

5 Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera.

6 Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Fanizo la ndalama yotayika

8 Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasilivakhumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza?

9 Ndipo m’mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.

10 Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso paangeloa Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Fanizo la mwana wolowerera

11 Ndipo Iye anati, Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri;

12 ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake.

13 Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng’onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.

14 Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.

15 Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfumu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba.

16 Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.

17 Koma m’mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

18 Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu;

19 sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu.

20 Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.

21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.

22 Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;

23 ndipo idzani naye mwanawang’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;

24 chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.

25 Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina.

26 Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?

27 Ndipo uyu anati kwa iye, Mng’ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang’ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo.

28 Koma anakwiya, ndipo sanafune kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira.

29 Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwire lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatse ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.

30 Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang’ombe wonenepa.

31 Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse zili zako.

32 Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/15-cafb9bb996ae86a039e1e01d7119cb3a.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 16

Fanizo la kapitao wonyenga

1 Ndipo Iye ananenanso kwaophunziraake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.

2 Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.

3 Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi.

4 Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene ananditulutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao.

5 Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wake, nanena kwa woyamba, Unakongola chiyani kwa mbuye wanga?

6 Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata yako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.

7 Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata yako nulembere makumi asanu ndi atatu.

8 Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m’mbadwo wao koposa ana a kuunika.

9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.

10 Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chachikulu.

11 Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m’chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona?

12 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

13 Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Za mphamvu ya chilamulo

14 KomaAfarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.

15 Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.

16 Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo.

17 Kuti thambo ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang’ono kachilamulo kagwe nkwapatali.

18 Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.

Fanizo la mwini chuma ndi Lazaro waumphawi

19 Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;

20 ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda,

21 ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake.

22 Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndiangelokunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m’manda.

23 Ndipo m’dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifuwa mwake.

24 Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m’lawi ili la moto.

25 Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.

26 Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.

27 Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga;

28 pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo.

29 Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.

30 Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima.

31 Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/16-a025e8f9dafb364a80bbb8e7b5343d27.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 17

Za zolakwitsa, ndi makhululukidwe, ndi mphamvu ya chikhulupiriro ndi kutumikira kwathu

1 Ndipo anati kwaophunziraake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.

2 Kukolowekedwa mwala wamphero m’khosi mwake ndi kuponyedwa iye m’nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang’ono awa nkwapatali.

3 Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire.

4 Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.

5 Ndipoatumwianati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro.

6 Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m’nyanja; ndipo ukadamvera inu.

7 Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;

8 wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?

9 Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa?

10 Chotero inunso m’mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.

Yesu achiritsa akhate khumi

11 Ndipo kunali, pakumuka kuYerusalemuIye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.

12 Ndipo m’mene analowa Iye m’mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;

13 ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.

14 Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m’kumuka kwao, anakonzedwa.

15 Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m’mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau aakulu;

16 ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo analiMsamariyaameneyo.

17 Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja?

18 Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeke mmodzi kodi, koma mlendo uyu?

19 Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.

Za kufikanso kwa Ambuye

20 Ndipo pameneAfarisianamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;

21 ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m’kati mwa inu.

22 Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku aMwana wa Munthu, koma simudzaliona.

23 Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! Taonani ili? Musachoka kapena kuwatsata;

24 pakuti monga mphezi ing’anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m’tsiku lake.

25 Koma ayenera ayambe wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno.

26 Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu.

27 Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m’chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.

28 Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;

29 koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu udavumba moto ndisulufurezochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;

30 momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu.

31 Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa tsindwi, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m’munda modzimodzi asabwere ku zake za m’mbuyo.

32 Kumbukirani mkazi wa Loti.

33 Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.

34 Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

35 Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

37 Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/17-8aaea162cdb9799223cee29e0895bfe8.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 18

Fanizo la woweruza wosalungama

1 Ndipo anawanenerafanizolakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;

2 nanena, M’mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.

3 Ndipo m’mzinda momwemo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane.

4 Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;

5 koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake.

6 Ndipo Ambuye anati, Tamverani chonena woweruza wosalungama.

7 Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?

8 Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. KomaMwana wa Munthupakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?

Fanizo la Mfarisi ndi wamsonkho

9 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

10 Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayoMfarisindi mnzakewamsonkho.

11 Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha,Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;

12 ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo.

13 Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.

14 Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.

Yesu adalitsa ana

15 Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pameneophunziraanaona anawadzudzula.

16 Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.

17 Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

Mkulu mwini chuma

18 Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha?

19 Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.

20 Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako.

21 Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.

22 Koma m’mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

23 Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri.

24 Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

25 Pakuti nkwapafupi kwangamiraipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.

26 Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa?

27 Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

28 Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.

29 Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum’bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu,

30 koma adzalandira zobwezedwa koposatu m’nthawi ino; ndipo m’nthawi ilinkudza moyo wosatha.

Yesu aneneratu za mazunzo ake

31 Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka kuYerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.

32 Pakuti adzampereka kwaamitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu;

33 ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka.

34 Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo.

Msaona wa ku Yeriko

35 Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m’mbali mwa njira, napemphapempha;

36 ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, Ichi nchiyani?

37 Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.

38 Ndipo anafuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.

39 Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.

40 Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m’mene adafika pafupi, anamfunsa iye,

41 Ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso.

42 Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.

43 Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/18-177d6c72454fe99c76e4209c6b65fd18.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 19

Zakeyo asandulika mtima

1 Ndipo analowa, napyola pa Yeriko.

2 Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu waamisonkho, nali wachuma.

3 Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sanathe, chifukwa cha khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.

4 Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi.

5 Ndipo m’mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako.

6 Ndipo anafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera.

7 Ndipo m’mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.

8 Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.

9 Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.

10 PakutiMwana wa Munthuanadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.

Fanizo la ndalama khumi za mina

11 Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanenafanizo, chifukwa anali Iye pafupi paYerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.

12 Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.

13 Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.

14 Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m’mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.

15 Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda.

16 Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi.

17 Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m’chaching’onong’ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi.

18 Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu.

19 Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza mizinda isanu.

20 Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m’kansalu;

21 pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiike pansi, mututa chimene simunachifese.

22 Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;

23 ndipo sunapereke bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake?

24 Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi.

25 Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi.

26 Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.

27 Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.

28 Ndipo m’mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.

Yesu alowa mu Yerusalemu

29 Ndipo kunali, m’mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, paphiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri aophunzira,

30 nati, Mukani kumudzi uli pandunji panu; m’menemo, polowa, mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iliyonse; mummasule iye nimumtenge.

31 Ndipo munthu akati kwa inu, Mummasuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye.

32 Ndipo anachoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo.

33 Ndipo pamene anamasula mwana wa bulu, eni ake anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa bulu?

34 Ndipo anati, Ambuye amfuna iye.

35 Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu.

36 Ndipo pakupita Iye, anayala zovala zao m’njira.

37 Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;

38 nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba.

39 NdipoAfarisiena a m’khamu la anthu anati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.

40 Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.

Yesu alirira Yerusalemu

41 Ndipo m’mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,

42 nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.

43 Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;

44 ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang’aniridwe ako.

Ayeretsa Kachisi kachiwiri

45 Ndipo analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao,

46 Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

47 Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;

48 ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/19-8a7e45abc844a3dc5a178076f8bd17a8.mp3?version_id=1068—