Categories
LUKA

LUKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Luka

likunena za Yesu monga Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Aisraele komanso Mpulumutsi wa anthu onse. Luka akunena kuti Yesu anaitanidwa ndi Mzimu wa Ambuye kuti, “awuze anthu osauka Uthenga Wabwino” (4.18), ndipo uthengawo ukuonetsa kuti Yesu anali wokhudzidwa ndi anthu amene ali ndi zosowa zosiyanasiyana. Nkhani inanso imene ikuonekera kwambiri mu buku la

Luka

ndiyo ya chimwemwe. Makamaka izi zikupezeka mu mitu yoyambirira ya bukuli pamene akunena za kubwera kwa Yesu, komanso kumapeto pamene Yesu akukwera kunka kumwamba. Luka analembanso mbiri ya chiyambi ndi kukula kwa mpingo wa Chikhristu Yesu atakwera mu buku lija la

Machitidwe

.

Bukuli lili ndi magawo awiri (mutu 1—2 ndi 9—19) m’mene muli nkhani zimene zikupezeka mu

Luka

yekha, nkhanizi ndi monga nyimbo ya angelo ndi ulendo wa abusa kukaona Yesu ali kakhanda, mwana Yesu ali mu Kachisi, ndiponso fanizo la Msamariya wachifundo ndi la Mwana wolowerera. Mu buku lonseli, nkhani yaikulu yagona pa pemphero, Mzimu Woyera, udindo wa azimai pa utumiki wa Yesu komanso kuti Mulungu amakhululukira machimo.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-4

Kubadwa ndi ubwana wa Yohane Mbatizi komanso Yesu 1.5—2.52

Utumiki wa Yohane Mbatizi 3.1-20

Ubatizo ndi kuyesedwa kwa Yesu 3.21—4.13

Utumiki wa Yesu ku Galileya 4.14—9.50

Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 9.51—19.27

Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 19.28—23.56

Kuukanso, kuonekera ndi kukwera kumwamba kwa Ambuye 24.1-53

Categories
LUKA

LUKA 1

1 Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife,

2 monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,

3 kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

4 kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira.

Aneneratu za kubadwa kwa Yohane

5 Masiku aHerode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.

6 Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.

7 Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.

8 Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu,

9 monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye mu Kachisi wa Ambuye.

10 Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

11 Ndipo anamuonekera iyemngelowa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.

12 Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.

13 Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.

14 Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.

15 Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

16 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.

17 Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

18 Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.

19 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.

20 Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirire mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.

21 Ndipo anthu analikulindira Zekariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake mu Kachisimo.

22 Koma m’mene iye anatulukamo, sanathe kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya mu Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

23 Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake.

24 Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

25 Ambuye wandichitira chotero m’masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Aneneratu za kubadwa kwa Yesu

26 Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete,

27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.

28 Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.

29 Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani.

30 Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu.

31 Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.

32 Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:

33 ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.

34 Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?

35 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.

36 Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37 Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

38 Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.

Maria acheza kwa Elizabeti

39 Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda;

40 nalowa m’nyumba ya Zekariya, nalonjera Elizabeti.

41 Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m’mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;

42 nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako.

43 Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga?

44 Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m’makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga.

45 Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.

Nyimbo ya Maria

46 Ndipo Maria anati,

Moyo wanga ulemekeza Ambuye,

47 ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

48 chifukwa Iye anayang’anira umphawi wa mdzakazi wake;

pakuti taonani, kuyambira tsopano,

anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.

49 Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu;

ndipo dzina lake lili loyera.

50 Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo

pa iwo amene amuopa Iye.

51 Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake;

Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao.

52 Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu,

ndipo anakweza aumphawi.

53 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,

ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu.

54 Anathangatira Israele mnyamata wake,

kuti akakumbukire chifundo,

55 (Monga analankhula kwa makolo athu)

kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.

56 Ndipo Maria anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake.

Kubadwa kwa Yohane Mbatizi

57 Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna.

58 Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.

59 Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.

60 Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane.

61 Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili.

62 Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti?

63 Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.

64 Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.

65 Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m’dziko lonse la mapiri a Yudeya.

66 Ndipo onse amene anazimva anazisunga m’mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.

Nyimbo ya Zekariya

67 Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,

68 Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele;

chifukwa Iye anayang’ana, nachitira anthu ake chiombolo.

69 Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso,

mwa fuko la Davide mwana wake.

70 Monga Iye analankhula ndi m’kamwa

mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,

71 chipulumutso cha adani athu,

ndi padzanja la anthu onse amene atida ife.

72 Kuchitira atate athu chifundo,

ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;

73 chilumbiro chimene Iye anachilumbira

kwa Abrahamu atate wathu.

74 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu,

tidzamtumikira Iye, opanda mantha,

75 m’chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse.

76 Eya, ndipo iwetu kamwanawe,

udzanenedwamneneriwa Wamkulukulu;

pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.

77 Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso,

ndi makhululukidwe a machimo ao,

78 chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu.

M’menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.

79 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;

kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

80 Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m’mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/1-fdb33d2e143fa4e8486eef00956e02c1.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 2

Kubadwa kwa Yesu Khristu

1 Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwaKaisaraAugusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;

2 ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya.

3 Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake.

4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;

5 kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.

6 Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira.

7 Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m’nsalu, namgoneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti anasowa malo m’nyumba ya alendo.

Abusa a ku Betelehemu

8 Ndipo panali abusa m’dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang’anira zoweta zao usiku.

9 Ndipomngelowa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha aakulu.

10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse;

11 pakuti wakubadwirani inu lero, m’mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene aliKhristuAmbuye.

12 Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.

13 Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,

14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,

ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

15 Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.

16 Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.

17 Ndipo iwo, m’mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

18 Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.

19 Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.

20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.

Kudulidwa ndi kuperekedwa kwa Yesu

21 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m’mimba.

22 Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka kuYerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye,

23 (monga mwalembedwa m’chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)

24 ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m’chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.

Za Simeoni ndi za Anna

25 Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.

26 Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye.

27 Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo,

28 pomwepo iye anamlandira Iye m’manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,

29 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,

lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere;

30 chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu,

31 chimene munakonza pamaso pa anthu onse,

32 kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu,

ndi ulemerero wa anthu anu Israele.

33 Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye.

34 Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;

35 eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m’mitima yambiri akaululidwe.

36 Ndipo panali Anna,mneneriwamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,

37 zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndikusala kudyandi kupemphera usiku ndi usana.

38 Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.

39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.

40 Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mnyamata Yesu pakati pa aphunzitsi

41 Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu kuPaska.

42 Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero;

43 ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m’mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe;

44 koma iwo anayesa kuti Iye ali m’chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;

45 ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye.

46 Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

47 Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.

48 Ndipo m’mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.

49 Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?

50 Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao.

51 Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.

52 Ndipo Yesu anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/2-013093f3a1226e51e733da965eae0be0.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 3

Kulalikira kwa Yohane Mbatizi

1 Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa TiberioKaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndiHerodechiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;

2 pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m’chipululu.

3 Ndipo iye anadza kudziko lonse la m’mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;

4 monga mwalembedwa m’buku la Yesayamneneri, kuti,

Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa,

ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa;

ndipo zokhota zidzakhala zolungama,

ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

6 ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.

7 Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8 Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.

9 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

10 Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani?

11 Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.

12 Ndipoamisonkhoomwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?

13 Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa chimene anakulamulirani.

14 Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

15 Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m’mitima yao za Yohane, ngati kapena iye aliKhristu;

16 Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

17 amene chouluzira chake chili m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m’nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m’moto wosazima.

18 Choteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri.

19 KomaHerodemfumu ija, m’mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita,

20 anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m’nyumba yandende.

Yesu abatizidwa

21 Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,

22 ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m’thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Makolo a Yesu

23 Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli,

24 mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,

25 mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai,

26 mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda,

27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, mwana wa Neri,

28 mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Eri,

29 mwana wa Yose, mwana wa Eliyezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,

30 mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,

31 mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide,

32 mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni,

33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,

34 mwana wa Yakobo, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahori,

35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela,

36 mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,

38 mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana waAdamu, mwana wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/3-1e8865de12b328f436ba6493d1c9c9ea.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 4

Kuyesedwa kwa Yesu

1 Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu

2 kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

5 Ndipo m’mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono.

6 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7 Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,

ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.

9 Ndipo anamtsogolera Iye kuYerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

10 pakuti kwalembedwa kuti,

Adzalamulaangeloake za iwe, kuti akutchinjirize.

11 Ndipo,

Pa manja ao adzakunyamula iwe,

kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.

12 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,

Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

13 Ndipo mdierekezi, m’mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina.

Yesu aphunzitsa ku Nazarete nachotsedwako

14 Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15 Ndipo Iye anaphunzitsa m’masunagogemwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m’sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m’kalata.

17 Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesayamneneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18 Mzimu wa Ambuye uli pa Ine,

chifukwa chake Iye anandidzoza Ine

ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:

anandituma Ine kulalikira am’nsinga mamasulidwe,

ndi akhungu kuti apenyanso,

kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

19 kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.

20 Ndipo m’mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m’sunagogemo anamyang’anitsa Iye.

21 Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.

22 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m’kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

24 Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.

25 Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;

26 ndipo Eliya sanatumidwe kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye.

27 Ndipo munali akhateambiri mu Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.

28 Ndipo onse a m’sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;

29 nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, nanka naye pamutu paphiri pamene panamangidwa mzinda wao, kuti akamponye Iye pansi.

30 Koma Iye anapyola pakati pao, nachokapo.

Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi chiwanda

31 Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;

32 chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro.

33 Ndipo m’sunagoge munali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti,

34 Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m’mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.

36 Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

37 Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.

Yesu achiritsa mpongozi wa Simoni

38 Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m’sunagoge, nalowa m’nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

39 Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.

40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.

41 Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiyeKhristu.

Yesu alalikira m’masunagoge

42 Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere.

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44 Ndipo Iye analikulalikira m’masunagoge a ku Yudeya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/4-1264bf56b62a6c7b943fffc488829b55.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 5

Asodzi athandizidwa ndi Yesu, namtsata

1 Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete;

2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m’menemo, nalikutsuka makoka ao.

3 Ndipo Iye analowa m’ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono. Ndipo anakhala pansi m’menemo, naphunzitsa m’ngalawa makamuwo a anthu.

4 Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.

5 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

6 Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka ao analinkung’ambika;

7 ndipo anakodola anzao a m’ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.

8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.

9 Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10 ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11 Ndipo m’mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.

Wakhate achiritsidwa

12 Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

13 Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.

14 Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.

15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.

16 Koma Iye anazemba, nanka m’mapululu, nakapemphera.

Yesu achiritsa munthu wamanjenje

17 Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapoAfarisindiaphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndiYerusalemu:ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.

18 Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye.

19 Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

20 Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.

21 Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?

22 Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m’mitima yanu?

23 Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?

24 Koma kuti mudziwe kutiMwana wa Munthuali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.

26 Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.

Kuitanidwa kwa Levi

27 Ndipo zitatha izi Iye anatuluka, naona munthuwamsonkho, dzina lake Levi, alikukhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.

28 Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye.

29 Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.

30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang’ung’udza kwaophunziraake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?

31 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing’anga; koma akudwala ndiwo.

32 Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.

Za kudzikana kudya

33 Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.

34 Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?

35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.

36 Ndipo Iye ananenansofanizokwa iwo, kuti, Palibe munthu ang’amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.

37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.

38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m’matumba atsopano.

39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/5-8c13c28ffeb75c80b5816d67601277f7.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 6

Yesu Mbuye wa tsiku la Sabata

1 Ndipo kunali tsiku laSabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipoophunziraake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m’manja mwao, nadya.

2 KomaAfarisiena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata?

3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi;

4 kuti analowa m’nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?

5 Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti,Mwana wa Munthuali Mbuye wa tsiku la Sabata.

Achiritsa munthu wa dzanja lopuwala

6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m’sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala.

7 Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.

8 Koma Iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lake lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.

9 Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?

10 Ndipo pamene anaunguzaunguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako. Ndipo iye anatero, ndi dzanja lake linabwerera momwe.

11 Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.

Yesu asankha ophunzira khumi ndi awiri

12 Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m’kupemphera kwa Mulungu.

13 Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina laoatumwi:

14 Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo,

15 ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwaZelote,

16 ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye.

Chiphunzitso cha paphiri

17 Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndiYerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;

18 ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa,

19 ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.

20 Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

21 Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.

22 Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.

23 Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo.

24 Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu.

25 Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.

26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.

27 Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu,

28 dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.

29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako.

30 Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

32 Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nao.

33 Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho.

34 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.

35 Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

36 Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

37 Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.

38 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

39 Ndipo Iye ananenanso naofanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m’mbuna?

40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m’mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.

41 Ndipo uyang’aniranji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda wa m’diso la iwe mwini suuzindikira?

42 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m’diso lako, wosayang’anira iwe mwini mtanda uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m’diso lako, ndipo pomwepo udzayang’anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m’diso la mbale wako.

43 Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino.

44 Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa.

45 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’choipa chake: pakuti m’kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

46 Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?

47 Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.

48 Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunathe kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino.

49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/6-95fca2c57f68424ae8ae883c4645b1b8.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 7

Kenturiyo wa ku Kapernao

1 Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m’makutu a anthu, analowa mu Kapernao.

2 Ndipo kapolo wakenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.

3 Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake.

4 Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;

5 pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ifesunagoge.

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;

7 chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.

8 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita.

9 Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.

10 Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu.

Aukitsa mnyamata ku Naini

11 Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumzinda, dzina lake Naini; ndipoophunziraake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye.

12 Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.

13 Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.

14 Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

15 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.

16 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti,Mneneriwamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.

17 Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Amithenga a Yohane Mbatizi

18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.

19 Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

20 Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

21 Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

22 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhateakonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

25 Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m’nyumba za mafumu.

26 Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.

27 Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,

Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,

amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng’ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

29 Ndipo anthu onse ndiamisonkhoomwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

30 KomaAfarisindi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.

31 Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani?

32 Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.

33 Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.

34 Mwana wa Munthuwafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

35 Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.

Mkazi adzoza mapazi a Yesu

36 Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m’nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.

37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m’mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,

38 naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.

39 Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.

40 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.

41 Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu.

42 Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

43 Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa.

44 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m’mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.

45 Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.

46 Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.

47 Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.

48 Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa.

49 Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?

50 Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/7-543b8d72ae78bbff60c8e929963b6646.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 8

Akazi otumikira Yesu ndi chuma chao

1 Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,

2 ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

3 ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao waHerode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.

Fanizo la Wofesa

4 Ndipo pamene khamu lalikulu la anthu linasonkhana, ndi anthu a kumidzi yonse anafika kwa Iye, anati mwafanizo:

5 Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m’kufesa kwake zina zinagwa m’mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m’mlengalenga zinatha kuzidya.

6 Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho.

7 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nkuzitsamwitsa.

8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.

9 Ndipoophunziraake anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili lili lotani?

10 Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.

11 Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.

12 Ndipo za m’mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m’mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

13 Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.

14 Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m’kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

15 Ndipo zija za m’nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Fanizo la nyali

16 Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17 Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala choonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kuvumbuluka.

18 Chifukwa chake yang’anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.

Amake ndi abale a Yesu

19 Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu.

20 Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.

21 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.

Yesu atontholetsa namondwe

22 Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m’ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.

23 Ndipo m’mene iwo anali kupita pamadzi, Iye anagona tulo. Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

24 Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.

25 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m’kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?

Munthu wa ku Gerasa wogwidwa ndi ziwanda

26 Ndipo iwo anakocheza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya.

27 Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m’nyumba, koma m’manda.

28 Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.

29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.

30 Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

31 Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.

32 Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m’phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.

33 Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanjamo, nilitsamwa.

34 Ndipo akuwetawo m’mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza okhala mumzinda ndi kuminda.

35 Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.

36 Ndipo amene anaona anawauza iwo machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo.

37 Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m’ngalawa, nabwerera.

38 Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena,

39 Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Mwana wamkazi wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu

40 Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.

41 Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wasunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;

42 chifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu a mipingo anakanikizana naye.

43 Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing’anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,

44 anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chovala chake; ndipo pomwepo nthenda yake inaleka.

45 Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.

46 Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine.

47 Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo.

48 Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

49 M’mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.

50 Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupirira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.

51 Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake.

52 Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.

53 Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa.

54 Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka.

55 Ndipo mzimu wake unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo Iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.

56 Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/8-aaf6e03713788729cc74446afa83cf79.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 9

Yesu atuma ophunzira ake kukalalikira mau

1 Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.

2 Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.

3 Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.

4 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.

5 Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m’mene mutuluka m’mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

6 Ndipo iwo anatuluka, napita m’midzi yonse, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse.

Herode ndi Yohane Mbatizi

7 NdipoHerodechiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

8 koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kutimneneriwina wa akale aja anauka.

9 Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye.

Yesu achulukitsa mikate

10 Ndipo atabweraatumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.

11 Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.

12 Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.

13 Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

14 Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwaophunziraake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.

15 Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

16 Ndipo Iye, m’mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang’ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.

17 Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri.

Petro avomereza Khristu

18 Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?

19 Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.

20 Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati,Khristuwa Mulungu.

21 Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense;

22 nati, Kuyenera kutiMwana wa Munthuamve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.

Za kusenza mtanda

23 Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

24 Pakuti aliyense amene akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma aliyense amene akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu.

25 Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?

26 Pakuti aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi waangelooyera.

27 Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

28 Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m’phiri kukapemphera.

29 Ndipo m’kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.

30 Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;

31 amene anaonekera mu ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza kuYerusalemu.

32 Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m’mene anayera m’maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.

33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.

34 Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo.

35 Ndipo munatuluka mau mumtambo, nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye.

36 Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.

Achiritsa mwana wodwala khunyu

37 Ndipo panali, m’mawa mwake, atatsika m’phiri, khamu lalikulu la anthu linakomana naye.

38 Ndipo onani, anafuula munthu wa m’khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang’anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:

39 ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng’amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.

40 Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe.

41 Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.

42 Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng’ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.

43 Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,

44 Alowe mau amenewa m’makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m’manja a anthu.

45 Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.

Wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba

46 Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani.

47 Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo,

48 Amene aliyense akalandire kamwana aka m’dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.

Osatsutsana nafe athandizana nafe

49 Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.

50 Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

Asamariya amkaniza Yesu

51 Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,

52 natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m’mudzi waAsamariya, kukamkonzera Iye malo.

53 Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.

54 Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?

55 Koma Iye anapotoloka nawadzudzula.

56 Ndipo anapita kumudzi kwina.

Matsatidwe a Yesu

57 Ndipo m’mene iwo analikuyenda m’njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako.

58 Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu.

59 Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndiyambe ndamuka kuika maliro a atate wanga.

60 Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.

61 Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga.

62 Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/9-99296c912029fd5fc8bb7bc77ff750ff.mp3?version_id=1068—