Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 20

Ziletsedwa chipembedzo cha Moleke ndi zoipa zina

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala mu Israele, amene apereka mbeu zake kwaMoleki, azimupha ndithu; anthu a m’dziko amponye miyala.

3 Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.

4 Ndipo ngati anthu a m’dzikomo akambisa munthuyo pang’ono ponse, pamene apereka a mbeu zake kwa Moleki, kuti asamuphe;

5 pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.

6 Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.

7 Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8 Ndipo musunge malemba anga ndi kuwachita; Ine ndine Yehova wakupatula inu.

9 Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.

10 Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.

11 Munthu akagona naye mkazi wa atate wake, wavula atate wake; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamutu pao.

12 Munthu akagona ndi mpongozi wake, awaphe onse awiri; achita chisokonezo; mwazi wao ukhale pamutu pao.

13 Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.

14 Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu.

15 Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi.

16 Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.

17 Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.

18 Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.

19 Usamavula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anavula abale ake; asenze mphulupulu yao.

20 Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wake, navula mbale wa atate wake; asenze kuchimwa kwao; adzafa osaona ana.

21 Munthu akatenga mkazi wa mbale wake, chodetsa ichi; wavula mbale wake; adzakhala osaona ana.

22 Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m’mwemo.

23 Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.

24 Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.

25 Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.

26 Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.

27 Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/20-02a435d2c1519b534d4d79f2a8478a25.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 21

Za kupatulika kwa ansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;

2 koma chifukwa cha abale ake enieni ndiwo, mai wake, ndi atate wake, ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi, ndi mbale wake;

3 ndi chifukwa cha mlongo wake weniweni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse chifukwa cha iwowa.

4 Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wake, asadzidetse, ndi kudziipsa.

5 Asamete tsitsi la pamutu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.

6 Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.

7 Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake.

8 Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.

9 Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto.

10 Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung’amba zovala zake.

11 Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.

12 Asatuluke m’malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.

13 Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.

14 Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.

15 Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.

Ansembe akhale opanda chilema pathupi

16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

17 Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake.

18 Pakuti munthu aliyense wokhala nacho chilema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mphuno, kapena wamkulu chiwalo,

19 kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja,

20 kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wachipere, kapena wopunduka kumoto.

21 Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala nacho chilema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali nacho chilema asayandikize kupereka chakudya cha Mulungu wake.

22 Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;

23 koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.

24 Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, ndi ana onse a Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/21-6765c66192a9bd7d389afcb35b03c097.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 22

Ansembe ayere pakudya zopatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.

3 Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.

4 Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndikhate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;

5 ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse;

6 munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.

7 Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.

8 Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.

9 Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m’mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.

10 Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.

11 Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m’nyumba yake, adyeko mkate wake.

12 Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.

13 Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.

14 Ndipo munthu akadyako chinthu chopatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi chopatulikacho.

15 Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova;

16 ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

Za nsembe zaufulu

17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

18 Nena ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali mu Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;

19 kuti mulandiridwe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema, ya ng’ombe, kapena nkhosa kapena mbuzi.

20 Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.

21 Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng’ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.

22 Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto paguwa la nsembe.

23 Ng’ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.

24 Nyama yofula, kapena chophwanya kapena chosansantha, kapena chotudzula, kapena chodula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamachita ichi m’dziko mwanu.

25 Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.

26 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27 Zikamabadwa ng’ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m’tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.

28 Koma musamaipha ng’ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzimodzi.

29 Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.

30 Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m’mawa; Ine ndine Yehova.

31 Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.

32 Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israele; Ine ndine Yehova wakukupatulani,

33 amene ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/22-53b5903e8d2edea58c557fda651d22ae.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 23

Za nyengo zoikika za Yehova

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.

3 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndiloSabatalakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m’nyumba zanu zonse.

Paska

4 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, misonkhano yopatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.

5 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, paliPaskawa Yehova.

6 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilochikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsaa Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.

7 Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.

8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Zipatso zoyamba

9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m’dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

11 ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.

12 Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonzemwanawankhosawopanda chilema, wa chaka chimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.

13 Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.

14 Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m’nyumba zanu zonse.

15 Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;

16 muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.

17 Mutuluke nayo m’zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.

18 Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, anaankhosa asanu ndi awiri, opanda chilema a chaka chimodzi, ndi ng’ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

19 Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika.

20 Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi anaankhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.

21 Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m’nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22 Ndipo pakukolola dzinthu za m’dziko mwanu, usamakololetsa m’mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25 Musamagwira ntchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

Tsiku la chitetezero

26 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27 Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.

28 Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29 Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.

30 Ndi munthu aliyense wakugwira ntchito iliyonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wake.

31 Musamagwira ntchito iliyonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m’nyumba zanu zonse.

32 Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.

Chikondwerero cha Misasa

33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

34 Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri palichikondwerero cha Misasaya Yehova, masiku asanu ndi awiri.

35 Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira ntchito ya masiku ena.

36 Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.

37 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake;

38 pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.

39 Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m’dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule.

40 Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yovalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.

41 Ndipo musunge chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri m’chaka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wachisanu ndi chiwiri.

42 Mukhale m’misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m’dziko la Israele akhale m’misasa;

43 kuti mibadwo yanu ikadziwe kuti ndinakhalitsa ana a Israele m’misasa, pamene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

44 Ndipo Mose anafotokozera ana a Israele nyengo zoikika za Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/23-03d2b1e86ffff569a7652348a628cd3f.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 24

Za mafuta a nyalizo ndi mkate woonekera

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Uza ana a Israele, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.

3 Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m’chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m’mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.

4 Akonze nyalizo pa choikaponyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.

5 Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi.

6 Ndipo utiike m’mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

7 Nuikelubaniloona ku mzere uliwonse, kuti likhale kumkate ngati chokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.

8 Nthawi zonse tsiku laSabataaukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha.

9 Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.

Kulangidwa kwa wotemberera Mulungu ndi ochimwira zina

10 Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele, atate wake ndiye Mwejipito, anatuluka mwa ana a Israele; ndi mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraeleyo analimbana naye munthu Mwisraele kuchigono;

11 ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.

12 Ndipo anamsunga m’kaidi, kuti awafotokozere m’mene anenere Yehova.

13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

14 Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.

15 Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Aliyense wotemberera Mulungu wake azisenza kuchimwa kwake.

16 Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m’dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.

17 Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu.

18 Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere ina; moyo kulipa moyo.

19 Munthu akachititsa mnansi wake chilema, monga umo anachitira momwemo amchitire iye;

20 kuthyola kulipa kuthyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anachitira munthu chilema, momwemo amchitire iye.

21 Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere ina; iye wakupha munthu, amuphe.

22 Chiweruzo chanu chifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m’dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

23 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/24-f940e6a0670f7ca70e7ce95233c9ed00.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 25

Za chaka chopumula dziko

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’phiri la Sinai, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m’dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira YehovaSabata.

3 Zaka zisanu ndi chimodzi ubzale m’munda mwako, ndi zaka zisanu ndi chimodzi udzombole mpesa zako, ndi kucheka zipatso zake;

4 koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m’munda mwako, usamadzombola mipesa yako.

5 Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

6 Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

7 ndi ng’ombe zako, ndi nyama zili m’dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao.

Za chaka choliza lipenga

8 Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.

9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m’mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m’dziko lanu lonse.

10 Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m’dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.

11 Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m’mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.

12 Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda.

13 Chaka choliza lipenga ichi mubwerere nonse ku zakezake.

14 Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;

15 monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.

16 Monga mwa kuchuluka kwa zaka zake uonjeze mtengo wake, ndi monga mwa kuchepa kwa zaka zake uchepetse mtengo wake; pakuti akugulitsa powerenga masiku ake.

17 Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18 M’mwemo muchite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo mudzakhala m’dzikomo okhazikika.

19 Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika.

20 Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21 pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22 Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe.

Za kuombola dziko ndi nyumba

23 Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24 Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

25 Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.

26 Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lake lachionetsa, nachipeza chofikira kuchiombola;

27 pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwake, nabwezere wogulayo zotsalirapo nabwerere iye ku dziko lake.

28 Koma dzanja lake likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo chogulitsacho chikhale m’dzanja lake la iye adachigulayo, kufikira chaka choliza lipenga; koma chaka choliza lipenga chituluke, nabwerere iye ku dziko lake.

29 Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m’mzinda wa m’linga, aiombole chisanathe chaka choigulitsa; kufikira kutha chaka akhoza kuombola.

30 Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwake kwa chaka champhumphu, nyumba ili m’mzinda wa m’lingayi idzakhala yake ya iye adaigula yosamchokeranso mwa mibadwo yake; siidzatuluka chaka choliza lipenga.

31 Koma nyumba za m’midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m’dziko; ziomboledwe, zituluke m’chaka choliza lipenga.

32 Kunena za mizinda ya Alevi, nyumba za m’mizinda yaoyao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.

33 Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m’mzinda wakewake, ituluke m’chaka choliza lipenga, popeza nyumba za m’mizinda ya Alevi ndizo zaozao mwa ana a Israele.

34 Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo laolao kosatha.

35 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.

36 Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.

37 Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera.

38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.

Za mbale wodzigulitsa akhale kapolo

39 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa ntchito monga kapolo;

40 azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga.

41 Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake.

42 Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.

43 Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.

44 Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala aamitunduakuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi.

45 Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m’dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu.

46 Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m’mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza.

47 Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo;

48 atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole;

49 kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha.

50 Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.

51 Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndalama zakumuombola zochokera ku ndalama zomgulazo.

52 Ndipo zikamtsalira zaka pang’ono kufikira chaka choliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zake abwezere mtengo wake wakumuombola.

53 Akhale naye monga wolipidwa chaka ndi chaka; asamamlamulira momzunza pamaso pako.

54 Ndipo akapanda kumuombola motero, azituluka chaka choliza lipenga, iye ndi ana ake omwe.

55 Pakuti ana a Israele ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/25-e056d396e53fb7fe0389a3bf17133017.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 26

Malamulo, malonjezo, ndi machenjezo

1 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m’dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

2 Musunge masabataanga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

3 Mukamayenda m’malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;

4 ndidzakupatsani mvula m’nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m’minda idzabala zipatso zake.

5 Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m’dziko mwanu okhazikika.

6 Ndipo ndidzapatsa mtendere m’dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m’dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m’dziko mwanu.

7 Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

8 Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

9 Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazikachipanganochanga ndinapangana nanucho.

10 Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kutulutsa zakale chifukwa cha zatsopano.

11 Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.

12 Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.

13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.

14 Koma mukapanda kundimvera Ine, osachita malamulo awa onse;

15 ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa;

16 ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m’chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.

17 Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.

18 Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.

19 Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;

20 ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m’dziko siidzabala zobala zake.

21 Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.

22 Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang’ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

23 Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;

24 Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.

25 Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m’mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m’manja mwa mdani.

26 Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27 Ndipo mukapanda kundimvera Ine, chingakhale ichi, ndi kuyenda motsutsana nane;

28 Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.

29 Ndipo mudzadya nyama ya ana anu aamuna; inde nyama ya ana anu aakazi mudzaidya.

30 Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31 Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.

32 Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m’mwemo adzadabwa nako.

33 Ndipo ndidzabalalitsa inu mwaamitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.

34 Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m’dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake.

35 Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m’masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36 Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m’maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37 Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

38 Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.

39 Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m’moyo ndi mphulupulu zao m’maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m’moyo.

40 Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

41 Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

42 pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.

43 Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

44 Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m’dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.

45 Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.

46 Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m’phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/26-2cddbc1f50ce0c90d8a7ecf0463bbd34.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 27

Chowinda ndi chiombolo chake

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene munthu achita chowinda cha padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.

3 Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu asiliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

4 Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu.

5 Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi.

6 Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.

7 Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.

8 Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

9 Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

10 Asaisinthe, yokoma m’malo mwa yoipa, kapena yoipa m’malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m’malo mwa inzake, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.

11 Ndipo chikakhala cha nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe;

12 ndipo wansembeyo aiyese mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo.

13 Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake.

14 Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.

15 Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yake, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yake.

16 Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.

17 Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.

18 Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.

19 Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.

20 Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

21 koma potuluka m’chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe.

22 Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wakewake;

23 pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wake wa kuyesa kwako kufikira chaka choliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, chikhale chinthu chopatulikira Yehova.

24 Chaka choliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lakelake.

25 Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri.

26 Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng’ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27 Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

Za choperekedwa chiperekere, ndi lakhumi la za nthaka ndi za m’khola

28 Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.

29 Asamuombole munthu woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.

30 Limodzi mwa magawo khumi la zonse m’dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.

31 Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu.

32 Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng’ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.

33 Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola.

34 Awa ndi malamulo, amene Yehova analamula Mose, awauze ana a Israele, m’phiri la Sinai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/27-a285716b27d48e26454d0e64634e00c4.mp3?version_id=1068—