Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 10

Kuchimwa ndi kuphedwa kwa Nadabu ndi Abihu

1 Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yake ya zofukiza, naikamo moto, naikapo chofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wachilendo, umene sanawauze.

2 Ndipo panatuluka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso ya Yehova.

3 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.

4 Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.

5 Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawavula malaya ao a m’kati, kunka nao kunja kwa chigono, monga Mose adauza.

6 Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang’amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.

7 Ndipo musatuluka pakhomo pachihema chokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anachita monga mwa mau a Mose.

8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,

9 Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m’mene mulowa m’chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

10 ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera;

11 ndi kuti muphunzitse ana a Israele malemba onse amene Yehova analankhula nao ndi dzanja la Mose.

12 Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;

13 ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero.

14 Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.

15 Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nao pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako aamuna, mwa lemba losatha; monga Yehova analamula.

16 Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yauchimo, ndipo taonani, adaitentha. Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati,

17 Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m’malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova?

18 Taonani, sanalowe nao mwazi wake m’malo opatulika m’katimo; mukadaidyera ndithu m’malo opatulika, monga ndinakuuzani.

19 Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yauchimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yauchimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova?

20 Pamene Mose adamva ichi chidamkomera pamaso pake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/10-2192967e650a071c25b548795e1ece6b.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 11

Za nyama zodyeka ndi zosadyeka ndi zakufa zodetsa munthu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,

2 Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.

3 Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.

4 Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda;ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.

5 Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika chiboda, muiyese yodetsedwa.

6 Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika chiboda, mumuyese wodetsedwa.

7 Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.

8 Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.

9 Mwa zonse zili m’madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m’madzi, m’nyanja, ndi m’mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.

10 Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m’nyanja, ndi m’mitsinje, mwa zonse zokwawa za m’madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m’madzi, muziziyesa zonyansa;

11 inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.

12 Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m’madzimo muziyese zonyansa.

13 Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;

14 ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wake;

15 khwangwala mwa mtundu wake;

16 ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi mwa mtundu wake;

17 ndi nkhutukutu ndi nswankhono ndi manchichi;

18 tsekwe, vuwo, ndi dembo;

19 indwa, ndi chimeza monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.

20 Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa.

21 Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kutumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:

22 dzombe mwa mtundu wake, ndi chirimamine mwa mitundu yake, ndi njenjete mwa mtundu wake ndi tsokonombwe mwa mitundu yake.

23 Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.

24 Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;

25 ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

26 Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.

27 Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28 Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.

29 Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake;

30 ndi gondwa, ndi mng’azi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi birimankhwe.

31 Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; aliyense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

32 Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m’madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.

33 Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m’chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m’mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe.

34 Chakudya chilichonse chokhala m’mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m’chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa.

35 Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.

36 Koma kasupe kapena chitsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.

37 Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera.

38 Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wake kakagwapo, muiyese yodetsedwa.

39 Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

40 Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

41 Ndipo zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya.

42 Zonse zoyenda chafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.

43 Musamadzinyansitsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.

44 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.

45 Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.

46 Ichi ndi chilamulo cha nyama, ndi cha mbalame, ndi cha zamoyo zonse zakuyenda m’madzi, ndi cha zamoyo zonse zakukwawa pansi;

47 kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/11-6e4506ab2854ab0d65409bb9ca4d34fa.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 12

Za kuyeretsedwa kwa mkazi

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.

3 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.

4 Ndipo akhale m’mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m’malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake.

5 Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m’mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.

6 Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze nayemwanawankhosawa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo lachihema chokomanako, kwa wansembe;

7 ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake.

8 Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/12-9edf57504e7b74c73d7216a1e80de2c5.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 13

Malamulo a pa nthenda yakhate

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhatepa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;

3 ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbuu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa.

4 Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;

5 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirire pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

6 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;

7 koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsa kwa wansembe kuti atchedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;

8 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa, ndilo khate.

9 Pamene nthenda yakhate ili mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe;

10 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira,

11 ndilo khate lakale pa khungu la thupi lake, ndipo wansembe amutche wodetsedwa; asambindikiretse popeza ali wodetsedwa.

12 Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;

13 pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lake, amutche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera.

14 Koma tsiku lililonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa.

15 Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namutche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.

16 Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,

17 ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amutche woyera wanthendayo; ndiye woyera.

18 Ndipo pamene thupi lili ndi chilonda pakhungu pake, ndipo chapola,

19 ndipo padali chilonda pali chotupa choyera, kapena chikanga chotuuluka, pamenepo achionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,

20 ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m’chilondamo.

21 Koma wansembe akachiona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sichinakumbe kubzola khungu, koma chazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

22 ndipo ngati chapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndilo khate.

23 Koma ngati chikanga chaima pomwepo, chosakula, ndicho chipsera cha chilonda; ndipo wansembe amutche woyera.

24 Kapena pamene thupi lidapsa ndi moto pakhungu pake, ndipo mnofu wofiira wakupsawo usanduka chikanga chotuuluka, kapena chotuwa;

25 pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m’kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

26 Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m’chikangamo, ndipo sichikumba kubzola khungu, koma chazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

27 ndipo wansembe amuone tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati chakula pakhungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate.

28 Ndipo ngati chikanga chiima pomwepo, chosakula pakhungu koma chazimba; ndicho chotupa chakupsa; ndipo wansembe amutche woyera; pakuti ndicho chipsera chakupsa.

29 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandevu,

30 wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu.

31 Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;

32 ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,

33 pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;

34 ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amutche woyera, ndipo iye atsuke zovala zake, nakhala woyera.

35 Koma ngati mfundu ikula pakhungu atatchedwa woyera;

36 pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa.

37 Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amutche woyera.

38 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lake, zikanga zoyerayera;

39 wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga zili pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.

40 Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.

41 Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pake ndiye wa masweswe, koma woyera.

42 Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lilikubuka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi.

43 Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pamutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;

44 ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amutchetu wodetsedwa; nthenda yake ili pamutu pake.

45 Ndipo azing’amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m’mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!

46 Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono.

47 Ndiponso ngati nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya, kapena chathonje;

48 ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;

49 ngati nthenda ili yobiriwira, kapena yofiira pachovala, kapena pachikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;

50 ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse chija cha nthenda masiku asanu ndi awiri;

51 naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.

52 Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.

53 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa;

54 pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke chija pali khate, nachibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55 ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulike maonekedwe ake, yosakulanso nthenda, ndicho chodetsedwa; uchitenthe ndi moto; ndilo funka, kungakhale kuyera kwake kuli patsogolo kapena kumbuyo.

56 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa chovala, kapena chikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;

57 ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda.

58 Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera.

59 Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/13-2b30359154b7c3a72df02d2519f25819.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 14

Malamulo a pa kumyeretsa wakhate

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2 Chilamulo cha wakhatetsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe;

3 ndipo wansembe atuluke kunka kunja kwa chigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda yakhate yapola pa wakhateyo;

4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndihisope;

5 ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m’mbale yadothi pamwamba pamadzi oyenda;

6 natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m’mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pamadzi oyenda;

7 nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lake, namutche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.

8 Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.

9 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera.

10 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndimwanawankhosammodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.

11 Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo lachihema chokomanako;

12 ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

13 Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pamalo opatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.

14 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;

15 ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini;

16 ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m’mafuta ali m’dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;

17 ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m’dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula;

18 natsitsitize mafuta otsala m’dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.

19 Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;

20 ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa paguwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.

21 Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;

22 ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.

23 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe.

24 Ndipo wansembe atenge mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndi muyeso uja wa mafuta, ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

25 naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;

26 ndipo wansembe athireko mafuta aja m’chikhato chake chamanzere cha iye mwini;

27 ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m’dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;

28 ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m’dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pamalo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;

29 ndipo mafuta otsala m’dzanja la wansembe atsitsitize pamutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova.

30 Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,

31 limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.

32 Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake.

33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

34 Mutakafika m’dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m’nyumba ya dziko lanulanu;

35 pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m’nyumba.

36 Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m’nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m’nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;

37 naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m’makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ake yakumba kubzola khoma;

38 pamenepo wansembe azituluka ku khomo la nyumba, natseka nyumbayo masiku asanu ndi awiri;

39 ndipo wansembe abwerenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m’makoma a nyumba;

40 pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mzinda;

41 napalitse nyumba m’kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mzinda dothi adapalako;

42 natenge miyala ina, naikhazike m’malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.

43 Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m’nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m’nyumba namatanso;

44 pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m’nyumba, ndiyo khate lonyeka m’nyumba; ndiyo yodetsedwa.

45 Ndipo apasule nyumbayo, miyala yake, ndi mitengo yake, ndi dothi lake lonse kumzinda kuzitaya ku malo akuda.

46 Ndiponso iye wakulowa m’nyumba masiku ake ili yotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

47 Ndipo iye wakugona m’nyumbayo atsuke zovala zake; ndi iye wakudya m’nyumbayo atsuke zovala zake.

48 Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakule m’nyumba, ataimata nyumba; wansembe aitche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.

49 Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;

50 naphe mbalame imodzi m’mbale yadothi, pamwamba pamadzi oyenda;

51 natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, naziviike m’mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m’madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m’nyumba;

52 nayeretse nyumba ndi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.

53 Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mzinda kuthengo koyera; motero aichitire choitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.

54 Ichi ndi chilamulo cha nthenda iliyonse yakhate, ndi yamfundu;

55 ndi ya khate la chovala, ndi la nyumba;

56 ndi yachotupa, ndi yankhanambo, ndi yachikanga;

57 kulangiza tsiku loti chikhala chodetsa, ndi tsiku loti chikhala choyera; ichi ndi chilamulo cha khate.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/14-589d035c54e453a0377984828e45462a.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 15

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Nenani nao ana a Israele, nimuti nao, Pamene mwamuna aliyense ali ndi nthenda yakukha m’thupi mwake, akhale wodetsedwa, chifukwa cha kukha kwake.

3 Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m’thupi mwake, ngakhale chaleka m’thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake.

4 Kama aliyense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi chinthu chilichonse achikhalira chili chodetsedwa.

5 Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

6 Ndipo iye wakukhalira chinthu chilichonse adachikhalira wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

7 Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8 Ndipo wakukhayo akalavulira wina woyera; pamenepo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9 Ndipo mbereko iliyonse akwerapo wakukhayo ili yodetsedwa.

10 Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

11 Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m’manja m’madzi, atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

12 Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.

13 Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwake, natsuke zovala zake; nasambe thupi lake ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.

14 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo lachihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;

15 ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake.

16 Ndipo munthu aliyense akagona uipa, azisamba thupi lake lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

17 Ndipo chovala chilichonse, ndi chikopa chilichonse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, zidzakhalabe zodetsedwa kufikira madzulo.

18 Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.

19 Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwake nkwa mwazi m’thupi mwake, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo aliyense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

20 Ndipo chinthu chilichonse agonapo pokhala ali padera nchodetsedwa; ndi chinthu chilichonse akhalapo nchodetsa.

21 Ndipo aliyense akhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

22 Ndipo aliyense akhudza chinthu chilichonse akhalapo iye, atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

23 Ndipo chikakhala pakama, kapena pa chinthu chilichonse akhalapo iye, atachikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

24 Ndipo ngati mwamuna aliyense agona naye, ndi kudetsa kwake kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama aliyense agonapo ali wodetsedwa.

25 Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwake, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwake; masiku onse chilinkukha chomdetsa chake, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwake.

26 Kama aliyense agonapo masiku a kukha kwake akhale ngati kama wa kuoloka kwake; ndi chinthu chilichonse akhalapo chili chodetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwake.

27 Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28 Koma akayeretsedwa kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa.

29 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.

30 Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yauchimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake komdetsa.

31 Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m’kudetsedwa kwao, pamene adetsa chihema changa ali pakati pao.

32 Ichi ndi chilamulo cha wakukha, ndi cha iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;

33 ndi cha mkazi alinkudwala ndi kudetsedwa kwake, ndi cha iye alikukha kapena mwamuna, kapena mkazi, ndi cha iye agona ndi mkazi wodetsedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/15-a8b6a22b5fa003f56e9dcb565ce18614.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 16

Za tsiku lotetezera chaka ndi chaka

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana aamuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;

2 ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m’malo opatulika m’tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.

3 Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng’ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.

4 Avale malaya a m’kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m’chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.

5 Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.

6 Ndipo Aroni abwere nayo ng’ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.

7 Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pachihema chokomanako.

8 Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazele.

9 Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yauchimo.

10 Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazele, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti achite nayo chotetezera, kuitumiza kuchipululu ikhale ya Azazele.

11 Ndipo Aroni abwere nayo ng’ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng’ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;

12 natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa paguwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m’tseri mwa nsalu yotchinga;

13 naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.

14 Ndipo atengeko mwazi wa ng’ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum’mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri.

15 Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m’tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng’ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;

16 nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.

17 Ndipo musakhale munthu m’chihema chokomanako pakulowa iye kuchita chotetezera m’malo opatulika, kufikira atuluka, atachita chotetezera yekha, ndi mbumba yake, ndi msonkhano wonse wa Israele.

18 Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng’ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

19 Ndipo awazepo mwazi wina ndi chala chake kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulichotsera zodetsa za ana a Israele.

20 Ndipo atatha kuchitira chotetezera malo opatulika, ndi chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;

21 ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,

22 ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kunka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m’chipululu.

23 Pamenepo Aroni alowe m’chihema chokomanako, navule zovala zabafuta zimene anazivala polowa m’malo opatulika, nazisiye komweko.

24 Ndipo asambe thupi lake ndi madzi kumalo kopatulika, navale zovala zake, natuluke, napereke nsembe yopsereza yake, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nachite chodzitetezera yekha ndi anthu.

25 Ndipo atenthe mafuta a nsembe yauchimo paguwa la nsembe.

26 Ndipo iye amene anachotsa mbuzi ipite kwa Azazele atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.

27 Koma ng’ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m’malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.

28 Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.

29 Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m’dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;

30 popeza tsikuli adzachitira inu chotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukuchotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.

31 Likhale kwa inuSabatalakupumula, kuti mudzichepetse; ndilo lemba losatha.

32 Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lake achite ntchito ya nsembe m’malo mwa atate wake, achite chotetezera, atavala zovala zabafuta, zovala zopatulikazo.

33 Ndipo achite chotetezera malo opatulikatu, natetezere chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo.

34 Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/16-596f49fbd12f9baf6cfa7c496b07a8e4.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 17

Popereka nsembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, ndi ana a Israele onse, nuti nao, Ichi ndi chimene Yehova wauza, ndi kuti,

3 Munthu aliyense wa mbumba ya Israele akapha ng’ombe, kapenamwanawankhosa, kapena mbuzi, m’chigono, kapena akaipha kunja kwa chigono,

4 osadza nayo ku khomo lachihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;

5 kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.

6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo paguwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.

7 Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.

8 Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,

9 osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

Aletsedwa kudya mwazi

10 Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

11 Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.

12 Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi.

13 Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.

14 Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzachotsedwa.

15 Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m’dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.

16 Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lake, adzasenza mphulupulu yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/17-ffa03bba4158ccf6aea2c54bc7e4aad3.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 18

Malamulo a pa ulemu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

3 Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m’malemba ao.

4 Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m’mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.

7 Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula.

8 Usamavula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

9 Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.

10 Usamavula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.

11 Usamavula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.

12 Usamavula mlongo wa atate wako; ndiye wa chibale cha atate wako.

13 Usamavula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.

14 Usamavula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wake; ndiye mai wako.

15 Usamavula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamamvula.

16 Usamavula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.

17 Usamavula mkazi ndi mwana wamkazi wake; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wake, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wake kumvula; ndiwo abale; chochititsa manyazi ichi.

18 Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wake, kumvula, kumvula pamodzi ndi mnzake, akali ndi moyo mnzakeyo.

19 Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake.

20 Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

21 Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa chaMoleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

22 Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.

23 Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.

24 Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakutiamitunduamene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25 dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m’mwemo.

26 Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m’dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu.

27 (Pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

28 lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.

29 Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao.

30 Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/18-e8b4ea68235ca78f2defb92a03425d3d.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 19

Malamulo ena osiyanasiyana

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.

3 Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

4 Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.

6 Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m’mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto.

7 Akakadya konse tsiku lachitatu kali chonyansa, kosavomerezeka:

8 koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

9 Pakukolola dzinthu za m’dziko mwanu, usamakololetsa m’mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.

10 Usamakunkha khunkha la m’munda wako wampesa, usamazitola zidagwazi za m’munda wako wampesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

11 Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.

12 Musamalumbira monama ndi kutchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

13 Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m’mawa.

14 Usamatemberera wogontha; usamaika chokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

15 Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.

16 Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

17 Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.

18 Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.

19 Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m’munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.

20 Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.

21 Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ku khomo lachihema chokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopalamula.

22 Ndipo wansembe achite chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula pamaso pa Yehova, chifukwa cha kuchimwa adachimwaku; ndipo adzakhululukidwa chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwaku.

23 Ndipo mukadzalowa m’dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.

24 Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova.

25 Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26 Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.

27 Musamameta mduliro, kapena kumeta m’mphepete mwa ndevu zanu.

28 Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova.

29 Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi.

30 Muzisunga masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

31 Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32 Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

33 Ndipo mlendo akagonera m’dziko mwanu, musamamsautsa.

34 Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

35 Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake.

36 Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito.

37 Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/19-3e6e19165a48c740c73db2aaef4c8a47.mp3?version_id=1068—