Categories
LEVITIKO

LEVITIKO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Levitiko

likukamba za malamulo a chipembedzo ndi miyambo yosiyanasiyana mu Israele wakale, komanso za malamulo okhudza ansembe amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti malamulowo akutsatidwa bwino lomwe.

Mutu waukulu mu bukuli ndiwakuti Yehova ndi Woyera ndipo anthu ake ayenera kukhala oyera mtima pa kupembedza kwao ndiponso moyo wao onse kuti ubale wao ndi Mulungu usasokonezeke.

Mau amene amadziwika bwino kuchokera mu bukuli ndi omwe Yesu adawanena kuti ndilo lamulo lachiwiri lalikulu: “Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (19.18)

Za mkatimu

Malamulo onena za zopereka ndi nsembe

1.1—7.38

Aroni ndi ana ake awadzoza kukhala ansembe

8.1—10.20

Malamulo onena za mwambo wa kuyeretsedwa ndi kudetsedwa

11.1—15.33

Za tsiku lotetezera

16.1-34

Malamulo onena za chiyero pa moyo ndi pa chipembedzo

17.1—27.34

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 1

Za nsembe yopsereza

1 Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m’chihema chokomanakoIye, nati,

2 Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng’ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.

3 Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.

4 Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwake, imtetezere.

5 Pamenepo aiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.

6 Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zake.

7 Ndipo ana a Aroni wansembeyo asonkhe moto paguwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;

8 ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni zili pa moto wa paguwa la nsembe;

9 koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

10 Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.

11 Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

12 Ndipo aikadzule ziwalo zake, pamodzi ndi mutu wake ndi mafuta ake; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni zili pa moto wa paguwa la nsembe.

13 Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

14 Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.

15 Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe paguwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,

16 nachotse chitsokomero, ndi chipwidza chake, nazitaye kufupi kwa guwa la nsembe, kum’mawa, kudzala;

17 nang’ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/1-0d295e4ee536a35d97a46eb6f48a7b53.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 2

Za nsembe yaufa ndi ya zipatso zoyamba

1 Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapolubani.

2 Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

3 Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.

4 Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta.

5 Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m’chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosakaniza ndi mafuta.

6 Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.

7 Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta.

8 Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe.

9 Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.

10 Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.

11 Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.

12 Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize paguwa la nsembe zichite fungo lokoma.

13 Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wachipanganocha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.

14 Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola.

15 Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo lubani; ndiyo nsembe yaufa.

16 Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/2-162d45fc8e2fcdd233876d61636b8e6d.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 3

Za nsembe yoyamika

1 Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng’ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.

2 Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata chachihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

3 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

4 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.

5 Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

6 Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;

7 akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova;

8 naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

9 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

10 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.

11 Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.

12 Ndipo chopereka chake chikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova;

13 naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

14 Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

15 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.

16 Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.

17 Likhale lemba losatha m’mibadwo yanu m’nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/3-71dd31a1ca0c0ac9186cc3e776eb3866.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 4

Za nsembe yauchimo pochimwa wansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;

3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng’ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.

4 Ndipo adze nayo ng’ombeyo ku khomo lachihema chokomanakopamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng’ombeyo, naiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova.

5 Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng’ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;

6 ndipo wansembeyo aviike chala chake m’mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.

7 Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m’chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng’ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

8 Ndipo achotse mafuta onse a ng’ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

9 ndi impso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso,

10 umo azikachotsera pa ng’ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe yopsereza.

11 Natulutse chikopa cha ng’ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,

12 inde ng’ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.

Za nsembe yauchimo pochimwa mtundu wonse wa Israele

13 Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;

14 kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng’ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako.

15 Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng’ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova.

16 Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng’ombeyo ku chihema chokomanako;

17 naviike chala chake m’mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, chakuno cha nsalu yotchinga.

18 Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m’chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

19 Ndipo achotse mafuta ake onse, nawatenthe paguwa la nsembe.

20 Atero nayo ng’ombeyo; monga umo anachitira ng’ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21 Ndipo atulutse ng’ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng’ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.

Za nsembe yauchimo pochimwa mkulu

22 Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;

23 akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;

24 naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.

25 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.

26 Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

Za nsembe yauchimo pochimwa munthu yekha

27 Ndipo akachimwa wina wa anthu a m’dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;

28 akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.

29 Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.

30 Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.

31 Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

32 Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema.

33 Naike dzanja lake pamutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.

34 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;

35 nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/4-bba5afa812842cfceb4b415d57aac9c1.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 5

Za nsembe yopalamula

1 Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;

2 kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.

3 Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:

4 kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:

5 ndipo kudzali, atapalamula chimodzi cha izi, aziwulula chimene adachimwa nacho;

6 nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.

7 Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.

8 Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yauchimo, napotole mutu wake pakhosi pake, osauchotsa;

9 nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.

10 Ndipo aikonze inzake ikhale nsembe yopsereza, monga mwa lemba lake; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa adachimwira, ndipo adzakhululukidwa.

11 Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapolubaniai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.

12 Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.

13 Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.

14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

15 Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m’gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli asiliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;

16 ndipo abwezere cholakwira chopatulikacho, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amchitire chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula; ndipo adzakhululukidwa.

17 Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.

18 Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m’khola lake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera chifukwa cha kusachimwa dala kwake, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.

19 Iyo ndiyo nsembe yopalamula; munthuyu anapalamula ndithu pamaso pa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/5-2698f851e9ab2cd7165051da9d7c2fd4.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 6

Za nsembe yopalamula pochimwa dala munthu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;

3 kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;

4 pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;

5 kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.

6 Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m’khola mwake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula, adze nayo kwa wansembe;

7 ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena zilizonse akazichita ndi kupalamula nazo.

Chilamulo cha nsembe yopsereza

8 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

9 Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m’mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

10 Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m’mphepete mwa guwa la nsembe.

11 Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.

12 Ndipo moto wa paguwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m’mawa ndi m’mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

13 Moto uziyakabe paguwa la nsembe, wosazima.

Chilamulo cha nsembe yaufa

14 Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.

15 Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndilubanilonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe paguwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.

16 Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m’malo opatulika; pa bwalo lachihema chokomanakoachidye.

17 Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.

18 Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.

Nsembe ya ansembe podzozedwa iwo

19 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

20 Chopereka cha Aroni ndi ana ake, chimene azibwera nacho kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ichi: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale chopereka chaufa kosalekeza, nusu lake m’mawa, nusu lake madzulo.

21 Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova.

22 Ndipo wansembe wodzozedwa m’malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova.

23 Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.

Chilamulo cha nsembe yauchimo

24 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

25 Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri.

26 Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m’malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.

27 Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m’malo opatulika.

28 Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi.

29 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.

30 Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m’malo opatulika; aitenthe ndi moto.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/6-ae8dc593c6f88e91662651c97fe1fbbe.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 7

Chilamulo cha nsembe yopalamula

1 Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri.

2 Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yopalamula; nawaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

3 Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,

4 ndi impso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso;

5 ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yopalamula.

6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m’malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.

7 Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera.

8 Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense.

9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.

10 Ndipo nsembe zonse zaufa zosakaniza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.

Chilamulo cha nsembe yoyamika

11 Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi:

12 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.

13 Abwere nacho chopereka chake pamodzi ndi timitanda ta mkate wachotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zake.

14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

15 Kunena za nyama ya nsembe yolemekeza ya nsembe zoyamika zake, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m’mawa.

16 Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m’mawa adye chotsalirapo;

17 koma chotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lachitatu, achitenthe.

18 Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.

19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.

20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

21 Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Aletsedwa asadye mafuta ndi mwazi

22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

23 Lankhula ndi ana a Israele ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng’ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.

24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.

25 Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

26 Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m’nyumba zanu zonse.

27 Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Za gawo la ansembe

28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

29 Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yake kwa Yehova, azidza nacho chopereka chake kwa Yehova chochokera ku nsembe yoyamika yake;

30 adze nazo m’manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

31 Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo paguwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.

32 Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe ukhale nsembe yokweza yochokera ku nsembe zoyamika zanu.

33 Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.

34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.

35 Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;

36 limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

37 Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika;

38 chimene Yehova analamulira Mose m’phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israele abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m’chipululu cha Sinai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/7-81e0e3a7e70e5f00fd75b9a529f818b8.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 8

Kupatulidwa kwa ansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng’ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

3 nusonkhanitse khamu lonse ku khomo lachihema chokomanako.

4 Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako.

5 Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ichi ndi chimene Yehova adauza kuti chichitike.

6 Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.

7 Ndipo anamveka ndi malaya a m’kati, nammanga m’chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndiefodi, nammanga m’chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.

8 Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m’chapachifuwaUrimu ndi Tumimu.

9 Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10 Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza chihema, ndi zonse zili m’mwemo, nazipatula.

11 Ndipo anawazako paguwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.

12 Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.

13 Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m’kati, nawamanga m’chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.

14 Ndipo anabwera nayo ng’ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng’ombe ya nsembe yauchimo.

15 Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.

16 Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha paguwa la nsembe.

17 Koma ng’ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose.

18 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19 Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

20 Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zake; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Kupatulidwa kwa Aroni ndi ana ake

22 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa mphongoyo.

23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.

24 Pamenepo anabwera nao ana aamuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo paguwa la nsembe pozungulira.

25 Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26 ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27 anaika zonsezi m’manja mwa Aroni, ndi m’manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28 Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29 Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.

31 Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.

32 Koma chotsalira cha nyama ndi mkate muchitenthe ndi moto.

33 Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.

34 Monga anachita lero lino, momwemo Yehova analamula kuchita, kukuchitirani chotetezera.

35 Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.

36 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anachita zonse zimene Yehova analamula padzanja la Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/8-a03376c1aa1f275964a32ff735d993af.mp3?version_id=1068—

Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 9

Aroni adziperekera yekha ndi anthu nsembe, ndizo nsembe zoyamba

1 Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake aamuna, ndi akulu a Israele;

2 ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwanawang’ombe wamwamuna, akhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda chilema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.

3 Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang’ombe, ndimwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;

4 ndi ng’ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosakaniza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

5 Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pachihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova.

6 Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

7 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova analamula.

8 Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwanawang’ombe wa nsembe yauchimo, ndiyo ya kwa iye yekha.

9 Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m’mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;

10 koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha paguwa la nsembe; monga Yehova analamula Mose.

11 Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi chikopa kunja kwa chigono.

12 Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira.

13 Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, chiwalochiwalo, ndi mutu wake; ndipo anazitentha paguwa la nsembe.

14 Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza paguwa la nsembe.

15 Ndipo anabwera nacho chopereka cha anthu, natenga mbuzi ya nsembe yauchimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yauchimo, monga yoyamba ija.

16 Ndipo anabwera nayo nsembe yopsereza naipereka monga mwa lemba lake.

17 Ndipo anabwera nayo nsembe yaufa, natengako wodzala dzanja, nautentha paguwa la nsembe, angakhale adatentha nsembe yopsereza ya m’mawa.

18 Anaphanso ng’ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira,

19 ndi mafuta a ng’ombe; ndi a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira wamafuta, ndi chophimba matumbo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa;

20 ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo paguwa la nsembe.

21 Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.

22 Ndipo Aroni anakweza dzanja lake kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.

23 Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.

24 Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/9-8cd74e175cda4789d4371d005b1999fc.mp3?version_id=1068—