Categories
HABAKUKU

HABAKUKU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneriyu adalalika mau ake pamene Ababiloni adaononga ufumu wa Aasiriya (610-600 BC.). Habakuku akhumudwa poona kuti nawonso ndi anthu ankhanza. Iye anavutika mumtima ndipo anadandaula kwa Mulungu nati, “mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini” (1.13). Yankho la Mulungu ndi lakuti iye adzachitapo kanthu nthawi itakwana, koma pakadali pano, “wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake” (2.4).

Kwinako bukuli likumaliza ndi ndakatulo yotamanda ukulu wa Mulungu ndi kuonetsa chikhulupiriro chosagwedezeka cha mlakatuliyo.

Za mkatimu

Kudandaula kwa Habakuku

1.1—2.4

Tsoka kwa anthu osalungama

2.5-20

Pemphero la Habakuku

3.1-19

Categories
HABAKUKU

HABAKUKU 1

Chisalungamo cha Ayuda. Ababiloni adzawadzera ndi kuononga zonse. Mneneri apempherera Ayuda

1 Katundu adamuonamneneriHabakuku

2 Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa.

3 Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani.

4 Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.

5 Penyani mwaamitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.

6 Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m’malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.

7 Ali oopsa, achititsa mantha, chiweruzo chao ndi ukulu wao zituluka kwa iwo eni.

8 Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya.

9 Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m’tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga.

10 Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.

11 Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.

12 Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.

13 Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;

14 ndi kuyesa anthu ngati nsomba za m’nyanja, ngati zokwawa zopanda wakuzilamulira.

15 Aziwedza zonse ndi mbedza, azigwira mu ukonde wake, nazisonkhanitsa m’khoka mwake; chifukwa chake asekera nakondwerera.

16 Chifukwa chake aphera nsembe ukonde wake, nafukizira khoka lake, pakuti mwa izi gawo lake lilemera, ndi chakudya chake chichuluka.

17 Kodi m’mwemo adzakhuthula mu ukonde mwake osaleka kuphabe amitundu?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAB/1-db82ab5beb63c7e08ff3f5ffd53ba4b0.mp3?version_id=1068—

Categories
HABAKUKU

HABAKUKU 2

Ababiloni omwe adzalangidwa

1 Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang’anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha chiyani pa choneneza changa.

2 Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.

3 Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

4 Taonani, moyo wake udzikuza, wosaongoka m’kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.

5 Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa chikhumbo chake ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsiraamitunduonse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu.

6 Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.

7 Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?

8 Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.

9 Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m’dzanja la choipa!

10 Wapangira nyumba yako chamanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wachimwira moyo wako.

11 Pakuti mwala wa m’khoma ufuula, ndi mtanda wa kuphaso udzauvomereza.

12 Tsoka iye wakumanga mzinda ndi mwazi, nakhazikitsa mzinda ndi chisalungamo!

13 Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?

14 Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja.

15 Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!

16 Udzazidwa nao manyazi m’malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.

17 Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.

18 Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?

19 Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndisiliva, ndi m’kati mwake mulibe mpweya konse.

20 Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAB/2-a7456691eb67bc77a4a5c326a52c01ea.mp3?version_id=1068—

Categories
HABAKUKU

HABAKUKU 3

Pemphero la Habakuku

1 Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti.

2 Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;

Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka,

pakati pa zaka mudziwitse;

pa mkwiyo mukumbukire chifundo.

3 Mulungu anafuma ku Temani,

ndi Woyerayo kuphiri la Parani.

Ulemerero wake unaphimba miyamba,

ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.

4 Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika;

anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m’dzanja lake,

ndi komweko kunabisika mphamvu yake.

5 Patsogolo pake panapita mliri,

ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.

6 Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;

anapenya, nanjenjemeretsaamitundu;

ndi mapiri achikhalire anamwazika,

zitunda za kale lomwe zinawerama;

mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.

7 Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;

nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.

8 Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?

Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,

kapena ukali wanu panyanja,

kuti munayenda pa akavalo anu,

pa magaleta anu a chipulumutso?

9 Munapombosola uta wanu;

malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.

Munang’amba dziko lapansi ndi mitsinje.

10 Mapiri anakuonani, namva zowawa;

chigumula cha madzi chinapita;

madzi akuya anamveketsa mau ake,

nakweza manja ake m’mwamba.

11 Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;

pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo.

Pa kung’anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.

12 Munaponda dziko ndi kulunda,

munapuntha amitundu ndi mkwiyo.

13 Munatulukira chipulumutso cha anthu anu,

chipulumutso cha odzozedwa anu;

munakantha mutu wa nyumba ya woipa,

ndi kufukula maziko kufikira m’khosi.

14 Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake;

anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza;

kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.

15 Munaponda panyanja ndi akavalo anu,

madzi amphamvu anaunjikana mulu.

16 Ndinamva, ndi m’mimba mwanga munabwadamuka,

milomo yanga inanthunthumira pamau,

m’mafupa mwanga mudalowa chivundi,

ndipo ndinanjenjemera m’malo mwanga;

kuti ndipumule tsiku lamsauko,

pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.

17 Chinkana mkuyu suphuka,

kungakhale kulibe zipatso kumpesa;

yalephera ntchito yaazitona,

ndi m’minda m’mosapatsa chakudya;

ndi zoweta zachotsedwa kukhola,

palibenso ng’ombe m’makola mwao;

18 koma ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.

19 Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga,

asanduliza mapazi anga ngati a mbawala,

nadzandipondetsa pa misanje yanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAB/3-d60f571ace2388a1506eb2489361e3af.mp3?version_id=1068—