Categories
GENESIS

GENESIS 40

Yosefe m’kaidi amasulira maloto

1 Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.

2 NdipoFaraoanakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate.

3 Ndipo anaika iwo asungidwe m’nyumba ya kazembe wa alonda, m’kaidi, umo anamangidwa Yosefe.

4 Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo.

5 Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m’kaidi.

6 Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m’mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya.

7 Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m’nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?

8 Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.

9 Ndipo wopereka chikho wamkulu anafotokozera Yosefe loto lake, nati kwa iye, M’kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga:

10 ndipo m’mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha;

11 ndipo chikho cha Farao chinali m’dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m’chikho cha Farao ndi kupereka chikho m’dzanja la Farao.

12 Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;

13 akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m’dzanja lake, monga kale lomwe m’mene unali wopereka chikho chake.

14 Koma undikumbukire ine m’mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m’nyumbamu:

15 chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m’dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m’dzenjemu.

16 Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamutu panga;

17 m’lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m’lichero la pamutu panga.

18 Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu;

19 akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

20 Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake.

21 Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m’manja a Farao.

22 Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira.

23 Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/40-93356015cc8e6505d637146485f77e89.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 41

Yosefe ammasulira Farao maloto ake

1 Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu,Faraoanalota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.

2 Ndipo, taonani, zinatuluka m’mtsinjemo ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.

3 Ndipo, taonani ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m’mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng’ombe zinazo m’mphepete mwa mtsinje.

4 Ndipo ng’ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka.

5 Ndipo anagona nalotanso kachiwiri; ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino.

6 Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum’mawa, zinamera pambuyo pao.

7 Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota.

8 Ndipo panali m’mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.

9 Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero.

10 Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m’nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu:

11 ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lake.

12 Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.

13 Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika.

14 Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m’dzenjemo: ndipo iye anameta, nasintha malaya ake, nalowa kwa Farao.

15 Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.

16 Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.

17 Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M’loto langa taona, ndinaima m’mphepete mwa mtsinje;

18 ndipo taona, zinatuluka m’mtsinjemo ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m’mabango;

19 ndipo taona, ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m’dziko la Ejipito;

20 ndipo ng’ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa.

21 Ndipo pamene zinadya sizinadziwike kuti zinadya; koma zinaipabe m’maonekedwe ao monga poyamba.

22 Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m’kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;

23 ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum’mawa, zinamera pambuyo pao;

24 ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.

25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam’masulira Farao.

26 Ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto lili limodzi.

27 Ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum’mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

28 Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao.

29 Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka chakudya m’dziko lonse la Ejipito;

30 ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m’dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;

31 ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m’mbuyoyo, pakuti idzavuta.

32 Ndipo lotolo linabwerezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.

33 Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang’anire dziko la Ejipito.

34 Farao achite chotere, alembe woyang’anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m’zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu.

35 Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m’manja a Farao akhale chakudya m’mizinda, namsunge.

36 Ndipo chakudyacho chidzakhala m’dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m’dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.

Yosefe wolamulira dziko la Ejipito

37 Ndipo chinthucho chinali chabwino m’maso mwa Farao, ndi m’maso mwa anyamata ake.

38 Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m’mtima mwake?

39 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.

40 Uziyang’anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.

41 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Ejipito.

42 Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;

43 ndipo anamkweza iye m’galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.

44 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m’dziko lonse la Ejipito.

45 Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m’dziko la Ejipito.

46 Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita padziko lonse la Ejipito.

47 Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri.

48 Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m’dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m’mizinda; chakudya cha m’minda, yozinga mizinda yonse, anachisunga m’menemo.

49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.

50 Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana aamuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

51 Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.

52 Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m’dziko la kusauka kwanga.

53 Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m’dziko la Ejipito, zinatha.

54 Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m’maiko monse; koma m’dziko lonse la Ejipito munali chakudya.

55 Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.

56 Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m’dziko la Ejipito.

57 Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m’dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/41-21583131850d3c27433a9cb9de2da4f7.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 42

Abale a Yosefe afika ku Ejipito

1 Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang’anana?

2 Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.

3 Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu mu Ejipito.

4 Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam’gwere iye.

5 Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m’dziko la Kanani munali njala.

6 Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m’dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.

7 Ndipo Yosefe anaona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? Nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya.

8 Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikire iye.

9 Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.

10 Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya.

11 Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.

12 Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.

13 Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m’dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng’ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

14 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.

15 Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo waFarao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

16 Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.

17 Ndipo anaika onse m’kaidi masiku atatu.

18 Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;

19 ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m’kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;

20 koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho.

21 Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.

22 Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.

23 Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira.

24 Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.

25 Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m’thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.

Abale a Yosefe apita kwao

26 Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo.

27 Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.

28 Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife?

29 Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;

30 kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko.

31 Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda;

32 tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng’ono ali ndi atate wathu m’dziko la Kanani.

33 Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;

34 idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m’dziko muno.

35 Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m’thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.

36 Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.

37 Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m’manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.

38 Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m’njira m’mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/42-9d3d1a8f0ae5c3fafd2608e20deac2fa.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 43

Abale a Yosefe atsikiranso ku Ejipito

1 Ndipo njala inakula m’dzikomo.

2 Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang’ono.

3 Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.

4 Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya.

5 Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.

6 Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?

7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

8 Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang’ono.

9 Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse:

10 pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.

11 Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m’dziko muno m’zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang’ono, ndi uchi pang’ono, zonunkhira ndimure, ndi mfula, ndi katungurume;

12 nimutenge ndalama zowirikiza m’manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m’manja mwanu; kapena sanachite dala;

13 mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja:

14 Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.

Abalewo m’nyumba ya Yosefe

15 Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m’manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.

16 Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m’nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

17 Munthuyo anachita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m’nyumba ya Yosefe.

18 Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m’nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m’matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.

19 Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,

20 Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya:

21 ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m’manja mwathu.

22 Ndalama zina tatenga m’manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m’matumba athu.

23 Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m’matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni.

24 Ndipo munthuyo analowetsa anthu m’nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.

25 Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo.

26 Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m’nyumba mphatso zinali m’manja mwao, namweramira iye pansi.

27 Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?

28 Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.

29 Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng’ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.

30 Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m’chipinda chake naliramo.

31 Ndipo anasamba nkhope yake, natuluka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani chakudya.

32 Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.

33 Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng’ono monga ung’ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.

34 Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/43-6be6eff2cb068be2374f7f8442d3cbab.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 44

Abalewo ayesedwa ndi Yosefe

1 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.

2 Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng’ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mau ananena Yosefe.

3 Pamene kudacha, anamukitsa anthu iwo ndi abulu ao.

4 Atatuluka m’mzinda asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m’malo mwa zabwino?

5 Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero.

6 Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo.

7 Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu achite chotero?

8 Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m’dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m’nyumba ya mbuyanga kapenasilivakapena golide?

9 Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.

10 Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa.

11 Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake.

12 Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng’ono nachipeza chikho m’thumba la Benjamini:

13 ndipo anang’amba zovala zao, nasenzetsa yense bulu wake, nabwera kumzinda.

14 Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.

15 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu?

Yuda apembedzera Benjamini kwa Yosefe

16 Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m’dzanja lake.

17 Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m’dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.

18 Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m’makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngatiFarao.

19 Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?

20 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng’ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.

21 Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m’maso mwanga.

22 Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa.

23 Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga.

24 Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanu atate wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.

25 Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife chakudya pang’ono.

26 Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng’ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng’ono akapanda kukhala ndi ife.

27 Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana aamuna awiri;

28 wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;

29 ndipo ngati mukandichotsera ameneyonso, ndipo ngati chimgwera choipa, mudzanditsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.

30 Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;

31 kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.

32 Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.

33 Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m’malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake.

34 Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/44-0aea1cd6be0adedd04f1eaab7eff9996.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 45

Yosefe adziulula kwa abale ake

1 Ndipo Yosefe sanakhoze kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake.

2 Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m’nyumba yaFarao.

3 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.

4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe mu Ejipito.

5 Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.

6 Zaka ziwirizi muli njala m’dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga.

7 Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m’dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu.

8 Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.

9 Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe.

10 Ndipo mudzakhala m’dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;

11 ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.

12 Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m’kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu.

13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.

14 Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake.

15 Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.

16 Ndipo mbiri yake inamveka m’nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.

17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;

18 katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.

19 Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m’dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.

20 Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu.

21 Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.

22 Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli asilivamazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.

23 Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za mu Ejipito, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.

24 Ndipo anamukitsa abale ake, ndipo anachoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira.

25 Ndipo anakwera kutuluka mu Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao.

26 Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m’dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.

27 Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

28 ndipo Israele anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/45-f4cb83decd2d54067677f7d441d37780.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 46

Yakobo atsikira ku Ejipito

1 Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.

2 Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m’masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.

3 Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;

4 Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako.

5 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao aang’ono, ndi akazi ao, m’magaleta ameneFaraoanatumiza kuti amnyamule iye.

6 Ndipo anatenga ng’ombe zao ndi chuma chao anachipeza m’dziko la Kanani, nadza ku Ejipito, Yakobo ndi mbeu zake zonse pamodzi ndi iye;

7 ana ake aamuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana aakazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo mu Ejipito.

8 Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

9 Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi.

10 Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.

11 Ndi ana aamuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.

12 Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m’dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.

13 Ndi ana aamuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi.

14 Ndi ana aamuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele.

15 Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

16 Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.

17 Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.

18 Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi.

19 Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini.

20 Kwa Yosefe kunabadwa m’dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

21 Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.

22 Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai.

23 Ndi ana aamuna a Dani: Husimu.

24 Ndi ana aamuna a Nafutali: Yazeele, ndi Guni, ndi Yezere ndi Silemu.

25 Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.

26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m’chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

27 ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye mu Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa mu Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.

Yakobo akomana ndi Yosefe

28 Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pake kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yonka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni.

29 Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake.

30 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo.

31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m’dziko la Kanani, afika kwa ine;

32 ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng’ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng’ombe zao ndi zonse ali nazo.

33 Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani?

34 Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng’ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m’dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/46-6ca9879d206aae064fa8211a3d54fd7e.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 47

Yakobo aonetsedwa kwa Farao

1 Ndipo Yosefe analowa nauzaFaraonati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng’ombe zao, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m’dziko la Goseni.

2 Ndipo mwa abale ake anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao.

3 Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.

4 Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m’dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m’dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m’dziko la Goseni.

5 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe;

6 dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m’dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang’anire ng’ombe zanga.

7 Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.

8 Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati?

9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m’masiku a ulendo wao.

10 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao.

11 Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m’dziko la Ejipito, m’dera lokometsetsa la m’dziko, m’dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao.

12 Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.

Yosefe agulira Farao dziko la Ejipito

13 Ndipo munalibe chakudya m’dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo.

14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m’dziko la Ejipito ndi m’dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao.

15 Ndipo zitatha ndalama zonse m’dziko la Ejipito ndi m’dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama.

16 Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng’ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng’ombe zanu ngati ndalama zatsirizika.

17 Ndipo anadza nazo ng’ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng’ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.

18 Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng’ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;

19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.

20 Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.

21 Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake.

22 Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao.

23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu siizi, mubzale m’dziko.

24 Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.

25 Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.

26 Ndipo Yosefe analamulira lamulo la padziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhale la Farao.

27 Ndipo Israele anakhala m’dziko la Ejipito, m’dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m’menemo, nabalana nachuluka kwambiri.

28 Ndipo Yakobo anakhala m’dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.

29 Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;

30 koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m’dziko la Ejipito, ukandiike ine m’manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.

31 Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israele anawerama kumutu kwa kama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/47-233fa038282c36393b77d3718be1592e.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 48

Yakobo adalitsa ana a Yosefe

1 Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.

2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama.

3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m’dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

4 Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.

5 Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m’dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.

6 Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m’cholowa chao.

7 Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m’dziko la Kanani m’njira, itatsala nthawi yaing’ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).

8 Ndipo Israele anayang’ana ana aamuna a Yosefe, nati, Ndani awa?

9 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.

10 Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

11 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.

12 Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi.

13 Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m’dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m’dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye.

14 Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng’ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.

15 Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,

16 mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.

17 Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pamutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pamutu wa Efuremu ndi kuliika pamutu wa Manase.

18 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.

19 Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.

20 Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.

21 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.

22 Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m’dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/48-2cf7bc2e7173c11ad315fc043dd9323d.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 49

Yakobo adalitsa ana ake namwalira

1 Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.

2 Sonkhanani, tamvani, ana aamuna a Yakobo;

tamverani Israele atate wanu.

3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga,

mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga;

ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.

4 Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;

chifukwa unakwera pa kama wa atate wako;

pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.

5 Simeoni ndi Levi ndiwo abale;

zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.

6 Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao;

ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao;

chifukwa m’kukwiya kwao anapha munthu.

M’kufuna kwao anapundula ng’ombe.

7 Kutembereredwe kukwiya kwao,

chifukwa kunali koopsa;

ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe.

Ndidzawagawanitsa mu Yakobo.

Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.

8 Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;

dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;

ana aamuna a atate wako adzakuweramira.

9 Yuda ndi mwana wa mkango,

kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera;

anawerama pansi, anabwatama ngati mkango,

ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?

10 Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda,

kapena wolamulira pakati pa mapazi ake,

kufikira atadza Silo;

ndipo anthu adzamvera iye.

11 Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa,

ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika;

natsuka malaya ake m’vinyo,

ndi chofunda chake m’mwazi wa mphesa.

12 Maso ake adzafiira ndi vinyo,

ndipo mano ake adzayera ndi mkaka.

13 Zebuloni adzakhala m’mphepete mwa nyanja;

ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa;

ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.

14 Isakara ndiye bulu wolimba,

alinkugona pakati pa makola.

15 Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,

ndi dziko kuti linali lokondweretsa;

ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule,

nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.

16 Dani adzaweruza anthu ake,

monga limodzi la mafuko a Israele.

17 Dani adzakhala njoka m’khwalala,

songo panjira,

imene iluma zitendene za kavalo,

kuti womkwera wake agwe chambuyo.

18 Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.

19 Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye;

koma iye adzapsinja pa chitendeni chao.

20 Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta,

ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu.

21 Nafutali ndi mbawala yomasuka;

apatsa mau abwino.

22 Yosefe ndi nthambi yobala,

nthambi yobala pambali pa kasupe;

nthambi zake ziyangayanga palinga.

23 Eni uta anavutitsa iye kwambiri,

namponyera iye, namzunza.

24 Koma uta wake unakhala wamphamvu,

ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa.

Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo.

(Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele.)

25 Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,

ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe.

Ndi madalitso a Kumwamba,

madalitso a madzi akuya akukhala pansi,

madalitso a mawere, ndi a mimba.

26 Madalitso a atate wako

apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,

kufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire.

Adzakhala pamutu wa Yosefe,

ndi pakati pamutu wa iye amene ali wolekanitsidwa

ndi abale ake.

27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;

m’mamawa adzadya chomotola,

madzulo adzagawa zofunkha.

28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.

29 Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m’phanga lili m’munda wa Efuroni Muhiti,

30 m’phanga lili m’munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m’dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake:

31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya:

32 munda ndi phanga lili m’menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti

33 Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake aamuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/49-098659bc775f80dce959efb58601b9df.mp3?version_id=1068—