Categories
GENESIS

GENESIS 30

1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

2 Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m’malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?

3 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.

4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye.

5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.

6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.

7 Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.

8 Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali.

9 Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.

10 Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna.

11 Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi.

12 Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.

13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.

14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m’thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.

16 Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.

17 Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu.

18 Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.

19 Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi.

20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.

21 Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina.

22 Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m’mimba mwake.

23 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga;

24 namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.

Labani apangana ndi Yakobo

25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.

26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.

27 Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.

28 Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.

29 Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine.

30 Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

31 Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.

32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m’menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33 Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m’tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34 Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang’ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m’dzanja la ana ake aamuna.

36 Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wauwisi wa libne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m’menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m’nthyolemo.

38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m’michera yakumwera, m’mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

39 Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.

40 Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang’anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m’zoweta za Labani.

41 Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m’micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.

42 Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziike zimenezo: ndipo zofooka, zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo.

43 Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndingamira, ndi abulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/30-e6e40d35f373542b400321411c9183aa.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 31

Yakobo afuna kwao nathawa nazo zake

1 Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m’zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.

2 Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekere iye monga kale.

3 Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.

4 Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake,

5 ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.

6 Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.

7 Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.

8 Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo.

9 Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.

10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m’kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.

11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m’kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.

12 Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.

13 Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m’dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

14 Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m’nyumba ya atate wathu?

15 Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

16 Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite.

17 Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pangamira;

18 ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona mu Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.

19 Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anabaaterafia atate wake.

20 Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Mwaramu mobisika, m’mene sanamuuze iye kuti analinkuthawa.

21 Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang’anire kuphiri la Giliyadi.

Labani alondola wothawayo

22 Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa.

23 Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.

24 Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

25 Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m’phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m’phiri la Giliyadi.

26 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.

27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?

28 Ndipo sunandiloleze ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero.

29 M’dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

30 Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?

31 Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi.

32 Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang’anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

33 Ndipo Labani analowa m’hema wa Yakobo, ndi m’hema wa Leya, ndi m’mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m’hema wa Leya nalowa m’hema wa Rakele.

34 Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamira, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m’hema monse, koma sanawapeze.

35 Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi zili pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.

36 Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?

37 Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m’nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.

38 Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.

39 Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.

40 Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m’maso mwanga.

41 Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m’nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.

42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m’manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.

Labani apangana ndi Yakobo

43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga aakazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?

44 Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.

45 Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.

46 Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo.

47 Ndipo Labani anatcha pamenepo Yegara-Sahaduta; koma Yakobo anatcha Galedi.

48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;

49 ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang’anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake.

50 Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.

51 Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona choimiritsachi, ndachiimiritsa pakati pathu.

52 Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa.

53 Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.

54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

55 M’mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/31-04a38507240ece77257e0133469f7fed.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 32

1 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye.

2 Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu.

Yakobo akonzekeratu kukomana ndi Esau

3 Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.

4 Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:

5 ndipo ndili nazo ng’ombe ndi abulu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.

6 Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.

7 Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndingamira, zikhale makamu awiri;

8 ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka.

9 Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:

10 sindiyenera zazing’ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.

11 Mundipulumutsetu ine m’dzanja la mkulu wanga, m’dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.

12 Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mchenga wa pa nyanja, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake.

13 Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkulu wake:

14 mbuzi zazikazi mazana awiri, atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi mazana awiri, ndi zazimuna makumi awiri,

15 ngamira zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng’ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, abulu aakazi makumi awiri ndi ana khumi.

16 Ndipo anazipereka zimenezo m’manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina.

17 Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako?

18 Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.

19 Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye:

20 ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.

21 Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono.

Yakobo alimbana ndi mngelo nalandira dzina latsopano

22 Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki.

23 Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonse anali nazo.

24 Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha.

25 Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetse, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.

26 Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.

27 Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo.

28 Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.

29 Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.

30 Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.

31 Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake.

32 Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/32-bcca3bec1ef1fd14960c7ab0a885612f.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 33

Yakobo ayanjanitsidwa ndi Esau

1 Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja.

2 Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.

3 Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.

4 Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.

5 Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.

6 Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi.

7 Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi.

8 Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga.

9 Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.

10 Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.

11 Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.

12 Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine.

13 Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.

14 Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang’onopang’ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri.

15 Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.

16 Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.

17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.

Yakobo afika ku Sekemu

18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m’dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.

19 Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu.

20 Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/33-b31b30b9f8e4ef2aae55ca926d7415a0.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 34

Dina ndi a Sekemu

1 Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

2 Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.

3 Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

4 Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.

5 Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake aamuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.

6 Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.

7 Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.

8 Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake.

9 Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi.

10 Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m’menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m’menemo.

11 Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.

12 Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

13 Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

14 nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.

15 Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndikudulidwaamuna onse;

16 pamenepo tidzakupatsani inu ana athu aakazi, ndipo tidzadzitengera ana anu aakazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.

17 Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.

18 Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori.

19 Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.

20 Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mzinda wao, nalankhulana ndi anthu a mzinda wao, kuti,

21 Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m’dzikomo, achite malonda m’menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi.

22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23 Kodi ng’ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24 Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mzinda wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mzinda wao.

25 Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m’mzinda napha amuna onse.

26 Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m’nyumba ya Sekemu nachoka naye.

27 Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mzinda chifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28 Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m’mzinda, ndi za m’munda;

29 ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m’nyumba.

30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

31 Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/34-712269c133e20d1605ac1c6913eb0126.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 35

Yakobo amanga ku Betele

1 Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.

2 Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:

3 tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m’njira m’mene ndinapitamo.

4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m’manja mwao, ndi mphete zinali m’makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.

5 Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.

6 Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Betele), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye.

7 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake.

8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.

9 Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye.

10 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israele: ndipo anamutcha dzina lake Israele.

11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m’chuuno mwako;

12 ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isaki ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.

13 Ndipo Mulungu anakwera kumchokera iye kumene ananena naye.

14 Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.

15 Ndipo Yakobo anatcha dzina lake la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Betele.

Rakele amwalira pobadwa Benjamini

16 Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.

17 Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.

18 Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.

19 Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).

20 Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero.

21 Ndipo Israele anapita namanga hema wake paseri pa nsanja ya Edere.

Ana a Yakobo

22 Ndipo panali pamene Israele anakhala m’dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng’ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:

23 ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;

24 ana aamuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini;

25 ana aamuna a Biliha mdzakazi wake wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafutali;

26 ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.

Imfa ya Isaki

27 Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki.

28 Ndipo masiku a Isaki anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.

29 Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/35-b8a36f1bec22f27e56faf6e4cdbee401.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 36

Mbumba ya Esau

1 Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi:

2 Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi;

3 ndi Basemati mwana wamkazi wa Ismaele, mlongo wake wa Nebayoti.

4 Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele;

5 ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m’dziko la Kanani.

6 Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m’banja mwake, ndi ng’ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m’dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake.

7 Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng’ombe zao.

8 Ndipo Esau anakhala m’phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.

9 Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m’phiri la Seiri ndi iyi:

10 amenewa ndi maina a ana aamuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wake wa Esau, Reuwele mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wake wa Esau.

11 Ndipo ana aamuna a Elifazi ndiwo Temani, Omara, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi.

12 Ndipo Timna anali mkazi wake wamng’ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau.

13 Ndi ana aamuna a Reuwele: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wake wa Esau.

14 Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.

15 Amenewa ndi mafumu a ana aamuna a Esau: ana aamuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omara, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,

16 mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m’dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Ada.

17 Amenewa ndi ana aamuna a Reuwele mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reuwele m’dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Basemati mkazi wake wa Esau.

18 Amenewa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.

19 Amenewa ndi ana aamuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.

20 Amenewa ndi ana aamuna a Seiri Muhori, okhala m’dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibiyoni, ndi Ana,

21 ndi Disoni ndi Ezere ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m’dziko la Edomu.

22 Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemani: mlongo wake wa Lotani anali Timna.

23 Ana a Sobala ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebala, Sefo ndi Onamu.

24 Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m’chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake.

25 Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26 Ana a Disoni ndi awa: Hemudani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerani.

27 Ana a Ezere ndi awa: Bilihani, ndi Zaavani, ndi Akani.

28 Ana a Disani ndi awa: Uzi ndi Arani.

29 Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobala, mfumu Zibiyoni, mfumu Ana,

30 mfumu Disoni, mfumu Ezere, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m’dziko la Seiri.

31 Amenewa ndi mafumu analamulira m’dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israele mfumu aliyense.

32 Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira mu Edomu, ndipo dzina la mzinda wake ndilo Dinihaba.

33 Ndipo Bela anamwalira, ndipo Yobabu mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozira analamulira m’malo mwake.

34 Ndipo Yobabu anamwalira, ndipo Husamu wa ku dziko la Atemani analamulira m’malo mwake.

35 Ndipo Husamu anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midiyani m’dambo la Mowabu, analamulira m’malo mwake: dzina la mzinda wake ndi Aviti.

36 Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masireka analamulira m’malo mwake.

37 Ndipo Samila anamwalira, ndipo Shaulo wa ku Rehoboti pambali pa nyanja analamulira m’malo mwake.

38 Ndipo Shaulo anamwalira, ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m’malo mwake.

39 Ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m’malo mwake; dzina la mzinda wake ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wake ndi Mehetabele, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu.

40 Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja ao, monga malo ao, monga maina ao ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Yeteti,

41 mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni,

42 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibizara,

43 mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m’dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/36-2129d4261016b3bbf222e1d37019403c.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 37

Yosefe agulitsidwa ndi abale ake

1 Ndipo Yakobo anakhala m’dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m’dziko la Kanani.

2 Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.

3 Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.

4 Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.

5 Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa.

6 Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota:

7 pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m’munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.

8 Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.

9 Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.

10 Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?

11 Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m’mtima mwake.

12 Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wao mu Sekemu.

13 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.

14 Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m’chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

15 Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m’thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani?

16 Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta.

17 Munthuyo ndipo anati, Anachoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotani. Yosefe ndipo anatsata abale ake, nawapeza ali ku Dotani.

18 Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.

19 Ndipo anati wina ndi mnzake, Taonani, alinkudza mwini maloto uja.

20 Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m’dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake.

21 Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m’manja mwao; nati, Tisamuphe iye.

22 Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m’dzenjemo m’chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m’manja mwao, ambwezenso kwa atate wake.

23 Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye;

24 ndipo anamtenga iye, namponya m’dzenjemo; m’dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m’menemo.

25 Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang’ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndingamirazao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndimurealinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.

26 Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake?

27 Tiyeni timgulitse iye kwa Aismaele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake.

28 Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m’dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli asilivamakumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.

29 Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m’dzenjemo: ndipo iye anang’amba nsalu yake.

30 Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?

31 Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m’mwazi wake:

32 natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.

33 Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.

34 Yakobo ndipo anang’amba malaya ake, na vala chiguduli m’chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.

35 Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.

36 Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna yaFarao, kazembe wa alonda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/37-3b270ffe47ca8aa108e99e21d2dcc680.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 38

Yuda ndi Tamara

1 Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.

2 Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Suwa: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye.

3 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri.

4 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani.

5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.

6 Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara.

7 Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.

8 Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu.

9 Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake.

10 Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso.

11 Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m’nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m’nyumba ya atate wake.

12 Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.

13 Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake.

14 Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.

15 Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake.

16 Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.

17 Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m’ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza?

18 Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m’dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

19 Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chofunda chake, navala zovala zamasiye zake.

20 Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.

21 Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.

22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye.

24 Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.

25 Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang’anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo?

26 Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.

27 Ndipo panali nthawi ya kubala kwake, taonani, amapasa anali m’mimba mwake.

28 Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga padzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa.

29 Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziphothyolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.

30 Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/38-5c3d37c0d60dba834cde2ff20e75a688.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 39

Yosefe ayesedwa ndi mkazi wa Potifara

1 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna yaFarao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m’manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.

2 Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m’nyumba ya mbuyake Mwejipito.

3 Ndipo mbuyake anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m’dzanja lake zonse anazichita.

4 Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yake, naika m’manja mwake zonse anali nazo.

5 Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m’nyumba ndi m’munda.

6 Ndipo iye anasiya zake zonse m’manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.

7 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang’anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.

8 Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m’nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m’manja anga;

9 mulibe wina m’nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?

10 Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye.

11 Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m’nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m’nyumba m’katimo.

12 Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m’dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo.

13 Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya chofunda chake m’dzanja lake, nathawira kubwalo,

14 anaitana aamuna a m’nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau aakulu:

15 ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo.

16 Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake.

17 Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:

18 ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja.

19 Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima.

20 Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m’kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m’mwemo m’kaidimo.

21 Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang’anira kaidi.

22 Ndipo woyang’anira kaidi anapereka m’manja a Yosefe akaidi onse okhala m’kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m’menemo, iye ndiye wozichita.

23 Woyang’anira m’kaidi sanayang’anire kanthu kalikonse kamene kanali m’manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/39-2d1bab61017fc54aa1b6d2b602a24850.mp3?version_id=1068—