Categories
GENESIS

GENESIS 20

Abrahamu kwa mfumu Abimeleki

1 Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.

2 Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleki mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara

3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m’kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.

4 Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?

5 Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.

6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m’kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.

7 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.

8 Ndipo Abimeleki analawira m’mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m’makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri

9 Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.

10 Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Unaona chiyani iwe kuti wachita ichi?

11 Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.

12 Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.

13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.

14 Ndipo Abimeleki anatenga nkhosa ndi ng’ombe ndi akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake.

15 Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.

16 Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasilivamazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.

17 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.

18 Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m’nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/20-27796640a9bf389abc70fd76a250db1b.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 21

Kubadwa kwa Isaki

1 Ndipo Yehova anayang’anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena.

2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu mu ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

3 Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isaki.

4 Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isaki pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye.

5 Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake.

6 Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.

7 Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna mu ukalamba wake.

Abrahamu achotsa Hagara

8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.

9 Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.

10 Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m’nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki.

11 Ndipo mauwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake.

12 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.

13 Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako.

14 Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m’chipululu cha Beereseba.

15 Ndipo anatha madzi a m’thumba ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba.

16 Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira.

17 Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.

18 Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m’dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.

19 Ndipo Mulungu anamtsegula m’maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza thumba ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.

20 Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m’chipululu, nakhala wauta.

21 Ndipo anakhala m’chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.

Abrahamu apangana ndi Abimeleki

22 Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m’zonse uzichita iwe;

23 tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.

24 Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira.

25 Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.

26 Ndipo anati Abimeleki, Sindinadziwe amene anachita icho; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.

27 Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng’ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.

28 Ndipo Abrahamu anapatula anaankhosa aakazi asanu ndi awiri pa okha.

29 Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Nanga anaankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?

30 Ndipo anati, Anaankhosa aakazi asanu ndi awiriwa uwalandire padzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.

31 Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.

32 Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.

33 Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.

34 Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m’dziko la Afilisti.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/21-a2c8fee2a2eb1c1bd6e7a21ade0eae6c.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 22

Isaki aperekedwa nsembe

1 Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.

2 Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.

3 Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.

4 Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake naona malowo patali.

5 Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.

6 Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m’dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri.

7 Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; komamwanawankhosawa nsembe yopsereza ali kuti?

8 Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.

9 Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.

10 Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lake, natenga mpeni kuti amuphe mwana wake.

11 Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.

12 Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.

13 Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang’ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m’chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake.

14 Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M’phiri la Yehova chidzaoneka.

15 Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kachiwiri,

16 nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,

17 kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;

18 m’mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.

19 Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.

20 Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;

21 Uzi woyamba ndi Buzi mphwake, ndi Kemuwele atate wake wa Aramu;

22 ndi Kesedi, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele.

23 Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu.

24 Ndipo mkazi wake wamng’ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/22-7ae30558c82c32669ac7380bb801c947.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 23

Imfa ndi kuikidwa kwa Sara

1 Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara.

2 Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.

3 Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati,

4 Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.

5 Ndipo ana a Hiti anayankha Abrahamu nati kwa iye,

6 Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m’manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu.

7 Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m’dzikomo, ana a Hiti.

8 Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari,

9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pamunda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

10 Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti, ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake, kuti,

11 Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m’menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.

12 Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m’dzikomo.

13 Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m’dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m’menemo.

14 Ndipo Efuroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye,

15 Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli asilivamazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu.

16 Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.

17 Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m’mundamo, yokhala m’malire monse mozungulira momwemo,

18 inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake.

19 Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m’phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani.

20 Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m’menemo, likhale lake lamanda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/23-14572c4b955c58837c431f5a8996ed45.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 24

Rebeka apalidwa ubwenzi ndi Isaki

1 Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.

2 Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:

3 ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.

4 Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isaki mkazi.

5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu?

6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.

7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.

9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho.

10 Ndipo mnyamatayo anatengangamirakhumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m’dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.

11 Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mzinda, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.

12 Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu.

13 Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mzinda atuluka kudzatunga madzi;

14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.

15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.

16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m’maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.

17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako.

18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m’manja mwake namwetsa iye.

19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamira zako, mpaka zitamwa zonse.

20 Ndipo anafulumira nathira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamira zake zonse.

21 Munthuyo ndipo anamyang’anira iye, nakhala chete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.

22 Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m’manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.

23 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi kunyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife?

24 Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.

25 Natinso kwa iye, Tili nao udzu ndi zakudya zambiri ndi malo ogona.

26 Munthuyo ndipo anawerama mutu namyamika Yehova.

27 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m’njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.

28 Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo kunyumba ya amake.

29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.

31 Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.

32 Munthuyo ndipo analowa m’nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.

33 Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.

34 Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.

35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng’ombe, ndisilivandi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.

36 Ndipo Sara mkazi wake wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo.

37 Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana aakazi a Kanani, m’dziko mwao m’mene ndikhala ine;

38 koma udzanke kunyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi.

39 Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanditsata ine.

40 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m’njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;

41 ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako.

42 Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m’mene ndinkamo ine;

43 taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi ndimwe pang’ono m’mtsuko mwako;

44 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.

45 Ndisanathe kunena m’mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.

46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lake, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamira.

47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.

48 Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m’njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.

49 Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.

50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.

51 Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.

52 Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi.

53 Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.

54 Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m’mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

55 Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka.

56 Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m’njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

57 Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pake.

58 Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka.

59 Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.

60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.

61 Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamira natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.

62 Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m’dziko la kumwera.

63 Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m’munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, taona, ngamira zinalinkudza.

64 Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anaona Isaki anatsika pa ngamira.

65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m’munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.

66 Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita.

67 Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m’hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/24-006b0bf6dce6bba173f56f7d6772eead.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 25

Kumwalira kwa Abrahamu

1 Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura.

2 Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa.

3 Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.

4 Ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.

5 Ndipo Abrahamu anampatsa Isaki zonse anali nazo.

6 Koma kwa ana a akazi ake aang’ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum’mawa, ku dziko la kum’mawa.

7 Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.

8 Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.

9 Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m’phanga la Makipela, m’munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;

10 munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.

11 Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi.

Mbumba ya Ismaele

12 Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:

13 ndipo maina a ana a Ismaele, maina ao m’mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismaele ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Adibeele, ndi Mibisamu,

14 ndi Misima, ndi Duma, ndi Masa;

15 ndi Hadadi, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;

16 ana a Ismaele ndi awa: maina ao m’midzi yao, m’misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m’mitundu yao.

17 Zaka za moyo wa Ismaele ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake.

18 Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum’mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.

Esau ndi Yakobo

19 Mibadwo ya Isaki mwana wake wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isaki:

20 ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.

21 Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.

22 Ndipo ana analimbana m’kati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? Ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.

23 Yehova ndipo anati kwa iye,

Mitundu iwiri ili m’mimba mwako,

magulu awiri a anthu adzatuluka m’mimba mwako;

gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake;

wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.

24 Atatha masiku ake akubala, taonani, amapasa anali m’mimba mwake.

25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.

26 Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.

Esau agulitsa ukulu wake

27 Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m’thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m’mahema.

28 Ndipo Isaki anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m’thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo.

29 Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka:

30 ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.

31 Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.

32 Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanji nao?

33 Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake.

34 Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/25-68aca786c7b683b1480297a1b776566c.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 26

Isaki akhala kwa Afilisti

1 Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.

2 Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m’dziko m’mene ndidzakuuza iwe;

3 khala mlendo m’dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;

4 ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m’mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;

5 chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.

6 Ndipo Isaki anakhala mu Gerari;

7 ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.

8 Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang’ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.

9 Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye.

10 Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang’ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife.

11 Ndipo Abimeleki anauza anthu ake, nati, Aliyense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zoonatu adzaphedwa.

12 Ndipo Isaki anabzala m’dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.

13 Ndipo analemera munthuyo, nalemera ndithu kufikira kuti anakhala wolemera kwambiri:

14 ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje.

15 Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.

16 Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife.

17 Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m’chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko.

18 Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.

19 Ndipo anyamata a Isaki anakumba m’chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka.

20 Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye.

21 Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina.

22 Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m’dziko muno.

23 Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba.

24 Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga.

25 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.

Isaki apangana ndi Abimeleki

26 Ndipo ananka kwa iye Abimeleki kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake.

27 Ndipo Isaki anati kwa iwo, Mwandidzera chifukwa chiyani, inu akundida ine, ndi kundichotsa kwanu?

28 Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;

29 kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudze iwe, sitidakuchitire kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.

30 Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.

31 Ndipo analawira m’mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m’mtendere.

32 Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.

33 Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.

34 Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti.

35 Ndipo iwo anapweteka mtima wa Isaki ndi wa Rebeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/26-3365e9c525c0539f1ec2a5fb7d287d5a.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 27

Yakobo adalitsidwa m’malo mwa Esau

1 Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.

2 Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga:

3 Tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama:

4 nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.

5 Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo.

6 Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Taona ndinamva atate wako alimkunena ndi Esau mkulu wako kuti,

7 Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe.

8 Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe.

9 Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino tambuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda:

10 ndipo udzapita nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe.

11 Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala.

12 Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.

13 Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.

14 Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.

15 Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m’nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng’ono;

16 ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala;

17 ndipo anapereka m’dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga.

18 Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?

19 Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.

20 Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.

21 Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.

22 Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.

23 Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.

24 Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene.

25 Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.

26 Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.

27 Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati,

Taona, kununkhira kwa mwana wanga,

kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;

28 Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba,

ndi zonenepa za dziko lapansi,

ndi tirigu wambiri ndi vinyo.

29 Anthu akutumikire iwe,

mitundu ikuweramire iwe;

uchite ufumu pa abale ako,

ana a amai ako akuweramire iwe.

Wotemberereka aliyense akutemberera iwe,

wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.

30 Ndipo panali atatha Isaki kumdalitsa Yakobo, atatuluka Yakobo pamaso pa Isaki atate wake, Esau mkulu wake analowa kuchokera kuthengo.

31 Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine.

32 Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau.

33 Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.

34 Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.

35 Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.

36 Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?

37 Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?

38 Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.

39 Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye,

Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi,

pa mame a kumwamba akudzera komwe.

40 Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako,

nudzakhala kapolo wa mphwako.

Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka,

udzachotsa goli lake pakhosi pako.

41 Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m’mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.

42 Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng’ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.

43 Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;

44 ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka utamchokera ukali mkulu wako;

45 mpaka utamchokera mkwiyo mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?

46 Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/27-7e474b920497f45b7c188b0cefe944de.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 28

1 Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.

2 Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.

3 Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:

4 akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m’dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.

5 Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.

Yakobo apita ku Padanaramu

6 Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani;

7 ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu;

8 ndipo Esau anaona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretse Isaki atate wake:

9 ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake.

Loto la Yakobo ku Betele

10 Ndipo Yakobo anachoka mu Beereseba, nanka ku Harani.

11 Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pamutu wake, nagona tulo kumeneko.

12 Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.

13 Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;

14 mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum’mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

15 Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.

16 Ndipo Yakobo anauka m’tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

17 Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba.

18 Yakobo ndipo anauka m’mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.

19 Ndipo anatcha dzina la pamenepo Betele; pakuyamba dzina lake la mzindawo ndi Luzi.

20 Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m’njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala,

21 kuti ndibwerenso kunyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga,

22 ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/28-a67b2319495cc1b0fc7360ec21bfa727.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 29

Yakobo akomana ndi Rakele

1 Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum’mawa.

2 Ndipo anayang’ana, taonani, chitsime m’dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.

3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.

4 Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani.

5 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa.

6 Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.

7 Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.

8 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.

9 Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta.

10 Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.

11 Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ake, nalira.

12 Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake.

Labani alandira Yakobo

13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m’nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.

14 Ndipo Labani anati kwa iye, Eetu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.

15 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?

16 Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng’ono ndi Rakele.

17 Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.

18 Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng’ono.

19 Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine.

20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.

Leya ndi Rakele

21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

22 Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.

23 Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wake wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.

24 Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya.

25 Ndipo panali m’mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?

26 Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng’ono asanapatse wamkulu.

27 Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.

28 Yakobo ndipo anachita chotero namaliza sabata lake; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wake wamkazi kuti akwatire iyenso.

29 Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Rakele.

30 Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.

Ana a Yakobo

31 Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m’mimba mwake; koma Rakele anali wouma.

32 Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.

33 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.

34 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana aamuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi.

35 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/29-8b8f5419f6e18bbb450f12683846f397.mp3?version_id=1068—