Categories
GENESIS

GENESIS Mau Oyamba

Mau Oyamba

Dzina lakuti

Genesis

litanthauza “chiyambi”. Bukuli likukamba za kulengedwa kwa dziko, chiyambi cha mtundu wa anthu, gwero la uchimo komanso mavuto m’dzikoli, komanso zimene Mulungu anachita pofuna kuwathandiza anthu. Buku la

Genesis

likhoza kugawidwa m’magawo awiri: Gawo loyamba ndilo kulengedwa kwa dziko ndi mbiri ya anthu oyamba. M’menemu timvamo za Adamu ndi Heva, Kaini ndi Abele, Nowa ndi nkhani ya chigumula komanso nsanja ya ku Babele (mutu 1—11). Gawo lachiwiri ndilo mbiri ya makolo oyamba a Aisraele. Oyambirira wa iwo ndiye Abrahamu, amene adziwika bwino chifukwa cha chikhulupiriro chake ndi kumvera kwake. Kenaka timva za mwana wake Isake, komanso mdzukulu wake Yakobo (amene adziwikanso ndi dzina loti Israele), ndiponso za ana 12 a Yakobo amene pa iwo mafuko 12 a Israele amangikapo. Pa nkhaniyi wolembayo akukhazikika kwambiri pa mmodzi mwa ana a Yakobo, dzina lake Yosefe. Akukamba za zonse zimene zinachitika kufikira pamene Yakobo ndi ana ake anapita kukakhala ku Ejipito pamodzi ndi mabanja ao (mutu 12—50).

Ngakhale bukuli likukamba za anthu, komabe mfundo yaikulu imene bukuli likunena ndi zomwe Mulungu anachita. Likuyamba ndi kutsimikiza kuti Mulungu ndi amene analenga dziko lapansi, ndipo likumaliza ndi lonjezo lakuti Mulungu adzapitirizabe kusamalira anthu ake. Mulungu ndiye mwininkhani m’buku lonseli, ndipo Iye ndi amene amaweruza ndi kulanga onse amene achita zoipa, amatsogolera ndi kuthandiza anthu ake, nawongolera zochitika zonse. Wolemba Bukuli amafuna kuti Aisraele azidzakumbukira za m’mene makolo ao ankakhulupirira Mulungu, ndi kuti nawonso moyo wao udzakhazikike pa chikhulupiriro chomwecho.

Za mkatimu

Kulengedwa kwa kumwamba ndi dziko lapansi komanso kwa munthu

1.1—2.25

Gwero la uchimo ndi masautso

3.1-24

Mibadwo kuchokera pa Adamu kufika pa Nowa

4.1—5.32

Mbiri ya Nowa ndi chigumula

6.1—10.32

Nsanja ya Babele

11.1-9

Mibadwo kuchokera pa Semu kufika pa Abramu

11.10-32

Mbiri ya makolo akale: Abrahamu, Isake ndi Yakobo

12.1—35.29

Mbumba ya Esau

36.1-43

Mbiri ya Yosefe ndi abale ake

37.1—45.28

Aisraele ku Ejipito

46.1—50.26

Categories
GENESIS

GENESIS 1

Kulengedwa kwa kumwamba ndi dziko lapansi

1 Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

2 Dziko lapansi ndipo linali lopasuka ndi losoweka; ndipo mdima unali pamwamba panyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pamadzi.

3 Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

5 Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku loyamba.

6 Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi.

7 Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.

8 Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachiwiri.

9 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.

10 Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

11 Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, padziko lapansi: ndipo kunatero.

12 Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

13 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachitatu.

14 Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

15 Zikhale zounikira m’thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero.

16 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching’ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

17 Mulungu ndipo adaika zimenezo m’thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi,

18 zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

19 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachinai.

20 Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga.

21 Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m’madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

22 Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m’nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi.

23 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachisanu.

24 Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng’ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

25 Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng’ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

Kulengedwa kwa munthu

26 Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m’nyanja, ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pang’ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.

27 Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

28 Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m’nyanja, ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.

29 Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m’mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

30 ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m’mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.

31 Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/1-f70439bf5cabe22929920ce09b2720af.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 2

1 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.

2 Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.

3 Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.

4 Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.

5 Ndi zomera zonse za m’munda zisanakhale m’dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m’munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;

6 koma inakwera nkhungu yotuluka padziko lapansi, nkuthirira ponse pamwamba panthaka.

7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.

Pokhala pake pamunthu

8 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edeni chakum’mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.

9 Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.

10 Ndipo unatuluka mu Edeni mtsinje wakuthirira m’mundamo, m’menemo ndipo unalekana nuchita miyendo inai.

11 Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m’mene muli golide;

12 golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu.

13 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi.

14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum’mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.

15 Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edeni kuti aulime nauyang’anire.

16 Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko;

17 koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.

18 Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.

19 Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m’thengo, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga; ndipo anapita nazo kwaAdamukuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.

20 Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m’mlengalenga ndi zamoyo zonse za m’thengo: koma kwa Adamu sanapezeke womthangatira iye.

21 Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake.

22 Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.

23 Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna.

24 Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.

25 Onse awiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/2-d8d6f33eaf8c51a8d97df43b382b23b2.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 3

Kuchimwa kwa Adamu ndi Heva

1 Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?

2 Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye.

3 Koma zipatso za mtengo umene uli m’kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

4 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5 chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.

6 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.

7 Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.

8 Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m’munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisalaAdamundi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pamitengo ya m’munda.

9 Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10 Ndipo anati, Ndinamva mau anu m’mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.

11 Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?

12 Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.

13 Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.

14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

15 ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.

16 Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.

17 Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:

18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo:

19 m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.

20 Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Heva; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse.

21 Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo.

22 Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,

23 Yehova Mulungu anamtulutsa iye m’munda wa Edeni, kuti alime nthaka m’mene anamtenga iye.

24 Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazikaakerubicha kum’mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/3-ac803b5dee7ff3dcff0de60934d699fb.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 4

Kaini ndi Abele. Kuphedwa koyamba

1 Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

2 Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.

3 Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.

4 Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang’anira Abele ndi nsembe yake:

5 koma sanayang’anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.

6 Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?

7 Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.

8 Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.

9 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang’anira mphwanga?

10 Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka.

11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:

12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.

13 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka.

14 Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.

15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.

Mbumba ya Kaini

16 Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m’dziko la Nodi, kum’mawa kwake kwa Edeni.

17 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.

18 Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki.

19 Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.

20 Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m’mahema, akuweta ng’ombe.

21 Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.

22 Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama.

23 Lameki ndipo anati kwa akazi ake,

Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;

inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga:

Ndapha munthu wakundilasa ine,

ndapha mnyamata wakundipweteka ine.

24 Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,

koma Lameki makumi asanu ndi awiri.

Kubadwa kwa Seti

25 NdipoAdamuanadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m’malo mwa Abele amene Kaini anamupha.

26 Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/4-ee2753885b65a822279db0f4483aa4e7.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 5

Mbumba ya Seti

1 Ili ndi buku la mibadwo yaAdamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m’chifanizo cha Mulungu;

2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.

3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m’chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.

4 Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.

5 Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.

6 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;

7 ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi:

8 masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.

9 Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani;

10 ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.

11 Masiku ake onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira.

12 Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele:

13 ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi;

14 masiku ake onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.

15 Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;

16 ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi:

17 masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira.

18 Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoki;

19 ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoki, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;

20 masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.

21 Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:

22 ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;

23 masiku ake onse a Enoki anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;

24 ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.

25 Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameki;

26 ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana aamuna ndi aakazi:

27 masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.

28 Ndipo Lameki anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;

29 namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;

30 ndipo Lameki anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi:

31 masiku ake onse a Lameki anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwalira.

32 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/5-5497e13ae5cfc699d1f1fe13e0e05f3f.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 6

Kulowerera kwa mtundu wa anthu

1 Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo,

2 kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.

3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.

4 Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

6 Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.

7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.

8 Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.

9 Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.

10 Ndipo Nowa anabala ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.

11 Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.

12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.

Chigumula

13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.

14 Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m’chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m’kati ndi kunja.

15 Kupanga kwake ndi kotere: m’litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m’mimba mwake mikono makumi asanu, m’msinkhu mwake mikono makumi atatu.

16 Uike zenera m’chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m’mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu.

17 Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m’mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m’dziko lapansi zidzafa.

18 Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m’chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.

19 Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m’chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.

20 Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.

21 Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.

22 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/6-f8f61fd7b59ea7e66b41611084360816.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 7

Nowa ndi banja lake alowa m’chingalawa

1 Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno.

2 Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.

3 Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo padziko lonse lapansi.

4 Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.

5 Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.

6 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali padziko lapansi.

7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m’chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.

8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,

9 zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m’chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.

10 Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi.

11 Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.

12 Ndipo mvula inali padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.

13 Tsiku lomwelo analowa m’chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao:

14 iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.

15 Ndipo zinalowa kwa Nowa m’chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m’mene muli mpweya wa moyo.

16 Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.

17 Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.

18 Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.

19 Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pathambo lonse.

20 Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri.

21 Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse:

22 zonse zimene m’mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.

23 Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m’chingalawa.

24 Ndipo anapambana madzi padziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/7-0561816e256894cb31a8bcb16c0aaffd.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 8

Nowa atuluka m’chingalawa

1 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m’chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;

2 ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba;

3 ndipo madzi anaphweraphwerabe padziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa.

4 Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.

5 Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.

6 Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga:

7 ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi.

8 Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba padziko lapansi;

9 koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m’chingalawamo.

10 Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m’chingalawamo;

11 ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m’kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa padziko lapansi.

12 Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabwerenso konse kwa iye.

13 Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa padziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa tsindwi lake pachingalawa, nayang’ana, ndipo taonani, padauma padziko lapansi.

14 Mwezi wachiwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi.

15 Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti,

16 Tulukamoni m’chingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.

17 Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.

18 Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye:

19 zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa padziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m’chingalawamo.

Nowa amanga guwa la nsembe

20 Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.

21 Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m’mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.

22 Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/8-99b1e5da637e353e2711fe4831689711.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 9

Mulungu achita pangano ndi Nowa

1 Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.

2 Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m’mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m’nyanja, zapatsidwa m’dzanja lanu.

3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

4 Koma nyama, m’mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

5 Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.

6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.

7 Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke m’menemo.

8 Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti,

9 Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;

10 ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng’ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m’chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi.

11 Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi.

12 Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;

13 ndiika utawaleza wanga m’mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.

14 Ndipo padzakhala pophimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m’mtambomo;

15 ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene lili ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuononga zamoyo zonse.

16 Ndipo utawo udzakhala m’mtambo; ndipo ndidzauyang’anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo padziko lapansi.

17 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za padziko lapansi.

18 Ndi ana aamuna a Nowa amene anatuluka m’chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti. Hamu ndiye atate wake wa Kanani.

19 Amenewa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.

Kuledzera kwa Nowa

20 Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wampesa:

21 namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m’kati mwa hema wake.

22 Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.

23 Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.

24 Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziwa chimene anamchitira iye mwana wake wamng’ono.

25 Ndipo anati,

Wotembereredwa ndi Kanani;

adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.

26 Ndipo anati,

Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu;

Kanani akhale kapolo wake.

27 Mulungu akuze Yafeti,

akhale iye m’mahema a Semu;

Kanani akhale kapolo wake.

28 Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu.

29 Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/9-707bb75bae01581671c82a7ae430c99a.mp3?version_id=1068—